CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 135-141
Tinapangidwa Modabwitsa Kwambiri
Davide ankaganizira za makhalidwe a Mulungu omwe amaonekera m’zinthu zimene analenga. Zimenezi zinachititsa kuti azitumikira Yehova ndi mtima wonse.
Davide atayamba kuganizira mozama zinthu zimene Yehova analenga, anayamba kutamanda Yehova
“Ndidzakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa”
“Mafupa anga sanali obisika kwa inu pamene munali kundipanga m’malo obisika, pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambiri padziko lapansi”
“Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu”