CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YAKOBO 3-5
Muzisonyeza Nzeru Yochokera kwa Mulungu
Nzeru yochokera kwa Yehova ndi yothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, ingatithandize kuti tiyambirenso kugwirizana ndi Akhristu anzathu. Zomwe timachita zimasonyeza ngati tikugwiritsa ntchito nzeru yochokera kwa Mulungu kapena ayi.
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi chaposachedwapa ndasonyeza makhalidwe ati mwa makhalidwe ali m’munsiwa? Kodi ndiyenera kuchita zotani kuti ndizitha kusonyeza makhalidwewa?’
Woyera
Wamtendere
Wololera
Wokonzeka kumvera
Wodzaza ndi chifundo ndiponso zipatso zabwino
Wopanda tsankho
Wopanda chinyengo