NKHANI YOPHUNZIRA 6
Atate Wathu Yehova Amatikonda Kwambiri
“Inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu.’”—MAT. 6:9.
NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi munthu ankayenera kuchita chiyani akafuna kulankhula ndi mfumu ya ku Perisiya?
YEREKEZERANI kuti munali ku Perisiya zaka 2,500 zapitazo. Mukufuna kukalankhula ndi mfumu ndipo mukupita kumzinda wa Susani kumene mfumuyo imakhala. Koma musanalankhule ndi mfumuyo mukufunika kupatsidwa chilolezo. Ngati mutangopita mfumuyo isanakupatseni chilolezo, mukhoza kuphedwa.—Esitere 4:11.
2. Kodi Yehova amafuna kuti tizimva bwanji pa nkhani ya kulankhula naye?
2 Timayamikira kwambiri kuti Yehova sali ngati mfumu ya ku Perisiya. Yehova ndi wamkulu komanso wofunika kwambiri kuposa mfumu iliyonse, koma amatilola kuti tizilankhula naye nthawi iliyonse. Iye amafuna kuti tizikhala omasuka kulankhula naye. Mwachitsanzo, ngakhale kuti Yehova ali ndi mayina audindo ngati Mlengi Wamkulu, Wamphamvuyonse komanso Ambuye Wamkulu, iye amafuna kuti tizilankhula naye pogwiritsa ntchito mawu oti “Atate.” (Mat. 6:9) N’zosangalatsa kuti Yehova amafuna kuti tizimva kuti tili naye pa ubwenzi ndipo amatikonda.
3. N’chifukwa chiyani tingati Yehova ndi Atate wathu, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Yehova ndi amene anatipatsa moyo choncho m’poyenera kumutchula kuti “Atate.” (Sal. 36:9) Popeza ndi Atate wathu, tiyenera kumumvera. Tikamachita zimene iye amafuna, tidzadalitsidwa kwambiri. (Aheb. 12:9) Madalitsowa akuphatikizapo moyo wosatha, kaya ndi kumwamba kapena padzikoli. Koma timadalitsidwanso ngakhale panopa. Munkhaniyi tikambirana mmene Yehova amatisonyezera chikondi panopa komanso zifukwa zimene zingatitsimikizire kuti iye sadzatisiya m’tsogolo. Koma choyamba, tiyeni tikambirane zifukwa zotitsimikizira kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda komanso amafunitsitsa kutithandiza.
YEHOVA NDI ATATE WATHU WACHIKONDI
4. N’chifukwa chiyani ena amavutika kuona Yehova ngati Atate wawo?
4 Kodi zimakuvutani kuona Yehova ngati Atate wanu? Ena amadziona kuti ndi aang’ono komanso osafunika akadziyerekezera ndi Yehova. Iwo amakayikira zoti Mulungu Wamphamvuyonse amawawerengera. Koma Atate wathu wachikondi safuna kuti tizikhala ndi maganizo amenewa. Iye anatipatsa moyo ndipo amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. Paulo ali ku Atene ananenanso mfundo imeneyi ndipo kenako ananena kuti Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:24-29) Mulungu amafuna kuti tonse tizilankhula naye momasuka ngati mmene mwana amalankhulira ndi kholo lake lachikondi.
5. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha mlongo wina?
5 Ena amavutika kuona kuti Yehova ndi Atate wawo chifukwa choti sanasonyezedwe chikondi ndi bambo awo enieni. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zomwe mlongo wina ananena. Iye anati: “Bambo anga anali ankhanza kwambiri. Nditangoyamba kuphunzira Baibulo, zinkandivuta kuona Yehova ngati Atate wanga wakumwamba. Koma nditamudziwa bwino, maganizo amenewa anasintha.” Ngati inunso zimakuvutani, dziwani kuti mukhoza kuyamba kuona kuti Yehova ndi Atate wabwino kwambiri.
6. Mogwirizana ndi Mateyu 11:27, kodi Yehova watithandiza bwanji kuti tiziona kuti iye ndi Atate wachikondi?
6 Kodi njira ina imene Yehova amatithandizira kuti tizimuona ngati bambo wathu wachikondi ndi iti? Iye anachititsa kuti mawu ndi zochita za Yesu zilembedwe m’Baibulo. (Werengani Mateyu 11:27.) Yesu ankatsanzira kwambiri Atate ake moti ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Yesu ankakonda kufotokoza mmene Yehova amachitira zinthu ngati Atate. Mwachitsanzo, m’mabuku 4 a uthenga wabwino mokha, Yesu anagwiritsa ntchito mawu oti “Atate” maulendo pafupifupi 165 ponena za Yehova. N’chifukwa chiyani Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito mawu akuti Atate ponena za Yehova? Chifukwa chimodzi n’chakuti ankafuna kuti anthu akhulupirire kuti Yehova ndi Atate wachikondi.—Yoh. 17:25, 26.
7. Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Mwana wake?
7 Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Mwana wake, Yesu? Nthawi zonse, Yehova ankamvetsera mapemphero a Yesu ndipo ankawayankha. (Yoh. 11:41, 42) Pa mayesero onse amene ankakumana nawo, Yesu ankatha kuona kuti Atate wake amamukonda komanso kumuthandiza.—Luka 22:42, 43.
8. Kodi Yehova ankasamalira bwanji Yesu?
8 Yesu anatsimikizira mfundo yoti Atate wake ndi amene anamupatsa moyo komanso kumuthandiza kuti akhalebe moyo ponena kuti: “Ine ndili ndi moyo chifukwa cha Atate.” (Yoh. 6:57) Yesu ankadalira kwambiri Atate wake ndipo ankamupatsa zofunika pa moyo. Koposa zonse, Yehova ankasamalira Yesu mwauzimu.—Mat. 4:4.
9. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi Atate wachikondi kwa Yesu?
9 Popeza Yehova ndi Atate wachikondi ankathandiza Yesu kuzindikira kuti iye sadzamusiya. (Mat. 26:53; Yoh. 8:16) Ngakhale kuti Yehova sanateteze Yesu ku zinthu zina zimene zikanamuvulaza, iye anamuthandiza kupirira mayesero. Yesu ankadziwa kuti mavuto alionse amene angakumane nawo ndi akanthawi. (Aheb. 12:2) Yehova anasonyeza kuti amakonda Yesu pomvetsera mapemphero ake, kumupatsa zofunika, kumuphunzitsa komanso kumuthandiza. (Yoh. 5:20; 8:28) Tsopano tiyeni tione zimene Atate wathu amachita potisamalira ngati mmene anachitira ndi Yesu.
KODI ATATE WATHU AMATISAMALIRA BWANJI?
10. Malinga ndi Salimo 66:19, 20, kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda?
10 Yehova amamvetsera mapemphero athu. (Werengani Salimo 66:19, 20.) Iye amafuna kuti tizipemphera mosalekeza ndipo satiikira malire pa nkhani imeneyi. (1 Ates. 5:17) Tikhoza kupemphera kwa Mulungu wathu nthawi iliyonse komanso malo alionse. Iye amakhala wokonzeka kumvetsera mapemphero athu nthawi ina iliyonse. Tikazindikira kuti Yehova amamvetsera mapemphero athu timamukonda kwambiri. M’pake kuti wolemba masalimo ananena kuti: “Mtima wanga ndi wodzaza ndi chikondi, chifukwa Yehova amamva Mawu anga.”—Sal. 116:1.
11. Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero athu?
11 Sikuti Yehova amangomva mapemphero athu, koma amayankhanso. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Chilichonse chimene tingamupemphe [Mulungu] mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yoh. 5:14, 15) N’zoona kuti mwina Yehova sangayankhe mapemphero athu m’njira imene ifeyo tikuganizira. Iye amadziwa bwino zimene tikufunikira choncho nthawi zina sangatipatse zimene tikupempha kapena angafune kuti tidikire kaye.—2 Akor. 12:7-9.
12-13. Kodi Atate wathu wakumwamba amatisamalira bwanji?
12 Yehova amatipatsa zinthu zofunika. Iye amachita zimene amafuna kuti bambo aliyense azichita. (1 Tim. 5:8) Mwachitsanzo, amapatsa ana ake zofunika pa moyo. Safuna kuti tizidera nkhawa za chakudya, zovala ndi malo ogona. (Mat. 6:32, 33; 7:11) Popeza ndi Atate wachikondi, iye wakonza zoti tizidzapeza zinthu zonse zofunika m’tsogolo.
13 Chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amatipatsa zinthu zothandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Mawu ake amatiuza zoona zake zokhudza iyeyo, zolinga zake, chifukwa chake anatilenga komanso zimene zidzachitike m’tsogolo. Yehova anasonyeza kuti amatiganizira potithandiza kuti tiphunzire za iye, kaya kuchokera kwa makolo athu kapena anthu ena. Amapitiriza kutithandiza pogwiritsa ntchito akulu komanso abale ndi alongo athu. Iye amatipatsanso malangizo kumisonkhano yampingo komwe amatiphunzitsa limodzi ndi Akhristu anzathu. Kunena zoona, pali njira zambiri zimene Yehova amasonyezera kuti amatikonda.—Sal. 32:8.
14. N’chifukwa chiyani Yehova amatiphunzitsa komanso kutipatsa chilango, nanga amachita bwanji zimenezi?
14 Yehova amatiphunzitsa. Mosiyana ndi Yesu, anthufe si angwiro. Choncho potiphunzitsa, nthawi zina Atate wathu amatipatsa chilango. Paja Mawu ake amanena kuti: “Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.” (Aheb. 12:6, 7) Yehova amatilangiza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, tikhoza kumva mfundo imene ingatithandize kusintha tikamawerenga Mawu ake kapena tikapita kumisonkhano. Apo ayi, akulu angatipatse malangizo oyenerera. Kaya malangizowo angabwere bwanji, Yehova amawapereka chifukwa choti amatikonda.—Yer. 30:11.
15. Kodi Yehova amatiteteza bwanji?
15 Yehova amatithandiza tikakumana ndi mayesero. Bambo wachikondi amathandiza mwana wake akakumana ndi mavuto. Izi n’zimenenso Atate wathu wakumwamba amachita. Iye amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti azititeteza mwauzimu. (Luka 11:13) Amatithandizanso kuti maganizo athu asamasokonezeke chifukwa cha nkhawa. Mwachitsanzo, iye watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri. Zimenezi zimatithandiza kuti tizipirira mavuto amene timakumana nawo. Taganizirani mfundo iyi: Kaya tikumane ndi zinthu zoipa bwanji, Yehova adzachotseratu vuto lililonse limene lingabwere chifukwa cha zinthuzo. Vuto lililonse limene tingakumane nalo ndi lakanthawi koma madalitso amene Yehova angatipatse ndi osatha.—2 Akor. 4:16-18.
ATATE WATHU SADZATISIYA
16. Kodi chinachitika n’chiyani Adamu atachimwa?
16 Zimene Yehova anachita Adamu atachimwa zimasonyeza kuti amatikonda kwambiri. Adamu atachimwa, anachititsa kuti iyeyo komanso anthu onse odzabadwa asakhalenso m’banja la Mulungu losangalala. (Aroma 5:12; 7:14) Koma Yehova anachita zinthu zothandiza kwambiri.
17. Kodi Yehova anachita chiyani Adamu atangochimwa?
17 Yehova anapereka chilango kwa Adamu koma nthawi yomweyo anapereka chiyembekezo kwa ana ake. Iye analonjeza kuti anthu omvera adzabwereranso m’banja lake. (Gen. 3:15; Aroma 8:20, 21) Kuti zimenezi zitheke, Yehova anakonza zoti Mwana wake adzapereke dipo. Kunena zoona, Yehova anasonyeza kuti amatikonda kwambiri pololera kuti Mwana wake wokondedwa atifere.—Yoh. 3:16.
18. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti tibwerere m’banja lake ngakhale titalakwitsa zinazake?
18 Ngakhale kuti ndife ochimwa, Yehova amafuna kuti tikhale m’banja lake ndipo saona kuti timamuvutitsa. Iye sationa kuti ndife okanika ngakhale kuti nthawi zina timamukhumudwitsa kapena kusochera pang’ono. Yesu anapereka fanizo la mwana wolowerera pofuna kutithandiza kumvetsa mmene Yehova amatikondera. (Luka 15:11-32) Bambo wamufanizoli sanasiye kuyembekezera kuti mwana wake adzabwerera. Ndipo mwanayo atabwerera, iwo anamulandira bwino. Ngati ifenso talakwitsa zinazake koma talapa, tisamakayikire kuti Yehova, yemwe ndi Atate wathu wachikondi, ndi wokonzeka ndiponso wofunitsitsa kutilandiranso.
19. Kodi Yehova adzathetsa bwanji mavuto amene Adamu anayambitsa?
19 Atate wathu adzathetsa mavuto onse amene Adamu anayambitsa. Adamu atachimwa, Yehova anakonza zoti adzatenge anthu 144,000 padzikoli kuti akakhale mafumu komanso ansembe limodzi ndi Yesu kumwamba. M’dziko latsopano, Yesu ndi odzozedwa adzathandiza anthu omvera kuti akhale angwiro. Akadzapulumuka pa mayesero omaliza, Mulungu adzapereka moyo wosatha kwa anthuwo. Pa nthawi imeneyo, Yehova adzasangalala kuona kuti dziko lonse ladzaza ndi ana ake angwiro. Zimenezitu zidzakhala zosangalatsa kwambiri.
20. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amatikonda, nanga tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
20 Yehova wasonyeza kuti amatikonda ndipo ndi Atate wabwino kwambiri. Iye amamvetsera mapemphero athu ndipo amatipatsa zinthu zonse zimene timafunikira. Amatiphunzitsa komanso kutithandiza ndipo kutsogoloku watisungira madalitso osaneneka. Timasangalala kwambiri kudziwa kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda. Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingachite posonyeza kuti nafenso timamukonda.
NYIMBO NA. 108 Chikondi Chosatha cha Mulungu
a Nthawi zambiri tikaganizira za Yehova timaona kuti ndi Mlengi wathu komanso Wolamulira Wamkulu. Koma palinso zifukwa zotichititsa kumuona kuti ndi Atate wathu wachikondi. Munkhaniyi tikambirana zifukwazo. Tikambirananso zifukwa zotitsimikizira kuti Yehova sadzatisiya.
b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Chithunzi chilichonse chikusonyeza bambo ali ndi mwana wake: (1) Akumvetsera zimene mwana akunena. (2) Akupezera mwana wake zinthu zofunika. (3) Akuphunzitsa mwana wake. (4) Akutonthoza mwana wake. Chithunzi cha dzanja la Yehova chimene chikuonekacho chikusonyeza kuti Yehova amatisamaliranso chimodzimodzi.