NKHANI YOPHUNZIRA 28
Musamakayikire Kuti Zimene Mumakhulupirira Ndi Zoona
“Pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo.”—2 TIM. 3:14.
NYIMBO NA. 56 Inuyo Panokha Muzikonda Kwambiri Choonadi
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi timakhala tikutanthauza chiyani tikamanena mawu akuti “choonadi”?
N’KUTHEKA kuti munafunsidwapo kapena munafunsapo ena mafunso ngati awa: “Kodi munaphunzira bwanji choonadi?” “Kodi munabadwira m’banja la Mboni?” “Nanga mwakhala m’choonadi kwa zaka zingati?” Koma kodi timakhala tikutanthauza chiyani tikamanena mawu akuti “choonadi”? Timagwiritsa ntchito mawuwa ponena za zimene timakhulupirira, zimene timachita polambira Mulungu komanso zimene timachita pa moyo wathu watsiku ndi tsiku. Anthu amene “ali m’choonadi” amadziwa zimene Baibulo limaphunzitsa komanso amatsatira mfundo zake. Zimenezi zimawathandiza kuti asamakhulupirire mfundo zabodza za m’zipembedzo zonyenga ndipo amakhala osangalala ngakhale ali m’dziko la Satanali.—Yoh. 8:32.
2. Mogwirizana ndi Yohane 13:34, 35, kodi n’chiyani chingakope munthu kuti ayambe kuphunzira choonadi?
2 Kodi n’chiyani chinakukopani kuti muphunzire choonadi? Mwina munakopeka ndi khalidwe labwino la anthu a Yehova. (1 Pet. 2:12) Kapena munaona chikondi chimene ali nacho. Ambiri amene amabwera kumisonkhano kwa nthawi yoyamba amaona chikondi chimenechi ndipo ndi zimene amakumbukira kwambiri kuposa zimene anamva pamisonkhano. Koma izi sizodabwitsa chifukwa Yesu ananena kuti anthu adzadziwa ophunzira ake chifukwa amakondana. (Werengani Yohane 13:34, 35.) Koma pali zinanso zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.
3. Kodi chingachitike n’chiyani ngati chikhulupiriro chathu chimangodalira chikondi chimene timaona pakati pa abale ndi alongo?
3 Chikhulupiriro chathu sichiyenera kungodalira chikondi chomwe timaona pakati pa anthu a Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Tayerekezerani kuti wokhulupirira mnzanu, mkulu kapena mpainiya wachita tchimo lalikulu. Mwinanso m’bale kapena mlongo wina wakukhumudwitsani. Kapenanso wina wayamba mpatuko ndipo akunena kuti zimene timakhulupirira si zoona. Ngati zimenezi zitachitika, kodi mungakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova? Pamenepa mfundo ndi yakuti: Ngati mumakhulupirira Yehova chifukwa cha zochita za anthu ena osati chifukwa choti muli naye pa ubwenzi wolimba, chikhulupiriro chanu sichingakhale cholimba. N’zoona kuti mmene mumaonera Yehova komanso anthu ake zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Koma n’zofunikanso kwambiri kumaphunzira Baibulo mwakhama, kumvetsa zimene mukuphunzirazo komanso kufufuza mfundo zina. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzitsimikizira kuti zomwe mukuphunzira zokhudza Yehova ndi zoona.—Aroma 12:2.
4. Mogwirizana ndi lemba la Mateyu 13:3-6, 20, 21, kodi chimachitika n’chiyani anthu ena akakumana ndi mavuto?
4 Yesu ananena kuti anthu ena amalandira choonadi “mwachimwemwe” koma akakumana ndi mavuto, chikhulupiriro chawo chimafooka. (Werengani Mateyu 13:3-6, 20, 21.) N’kutheka kuti anthuwa sadziwa kuti anthu amene amatsatira Yesu amakumana ndi mavuto. (Mat. 16:24) Mwinanso amaganiza kuti chifukwa choti ndi Akhristu ndiye kuti Mulungu aziwathetsera mavuto awo. Koma m’dzikoli n’zosatheka kumakhala osakumana ndi mavuto chifukwa zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu n’kuchititsa kuti tisamasangalale.—Sal. 6:6; Mlal. 9:11.
5. N’chiyani chimasonyeza kuti abale ndi alongo ambiri sakayikira kuti zomwe amakhulupirira ndi zoona?
5 Abale ndi alongo ambiri sakayikira kuti zomwe amakhulupirira ndi zoona. Tikutero chifukwa wokhulupirira mnzawo akachita zosayenera kapena akawakhumudwitsa, sasiya kutumikira Yehova. (Sal. 119:165) Akamakumana ndi mavuto safooka, m’malomwake chikhulupiriro chawo chimalimba. (Yak. 1:2-4) Kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba ngati chimenechi?
YESETSANI “KUMUDZIWA MULUNGU MOLONDOLA”
6. Kodi Akhristu a munthawi ya atumwi ankalimbitsa bwanji chikhulupiriro chawo?
6 Akhristu a munthawi ya atumwi ankalimbitsa chikhulupiriro chawo pophunzira Malemba komanso zimene Yesu Khristu anaphunzitsa, zomwe ndi “choonadi cha uthenga wabwino.” (Agal. 2:5) Choonadi chimenechi ndi zinthu zonse zomwe timakhulupirira monga Akhristu, kuphatikizapo mfundo zokhudza nsembe ya Yesu komanso kuukitsidwa kwake. Mtumwi Paulo ankakhulupirira kuti ziphunzitso zimenezi ndi zoona. N’chiyani chinamuthandiza kuti asamakayikire? Iye ankagwiritsa ntchito Malemba pofotokoza “ndi kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti kunali koyenera kuti Khristu avutike ndi kuuka kwa akufa.” (Mac. 17:2, 3) Akhristu a munthawi ya atumwi anakhulupirira ziphunzitso zimenezi ndipo ankadalira mzimu woyera kuti uwathandize kumvetsa Mawu a Mulungu. Iwo anafufuza kuti atsimikizire kuti ziphunzitsozi zinalidi zochokera m’Malemba. (Mac. 17:11, 12; Aheb. 5:14) Chikhulupiriro chawo sichinkangodalira mmene ankamvera mumtima mwawo ndipo sankatumikira Yehova chifukwa choti ankangosangalala kusonkhana ndi okhulupirira anzawo. M’malomwake anali ndi chikhulupiriro chifukwa choti ankayesetsa “kumudziwa Mulungu molondola.”—Akol. 1:9, 10.
7. Kodi kukhulupirira mfundo za choonadi kungatithandize bwanji?
7 Mfundo za choonadi cha m’Mawu a Mulungu sizisintha. (Sal. 119:160) Mwachitsanzo, mfundozi sizisintha ngakhale wokhulupirira mnzathu atikhumudwitse kapena achite tchimo lalikulu. Ndiponso sizisintha tikakumana ndi mavuto. Choncho tiziyesetsa kudziwa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa komanso kutsimikizira kuti ndi zoona. Tikamalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi mfundo za m’Baibulo tidzakhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. Chikhulupirirochi chingakhale ngati nangula yemwe amathandiza kuti boti lisatengedwe ndi mphepo yamkuntho. Kodi mungatsimikizire bwanji kuti zimene mumakhulupirira ndi zoona?
‘MUZIKHULUPIRIRA PAMBUYO POKHUTIRA NAZO’
8. Mogwirizana ndi lemba la 2 Timoteyo 3:14, 15, kodi Timoteyo anatsimikizira bwanji kuti mfundo zimene ankakhulupirira zinali zoona?
8 Timoteyo sankakayikira kuti zimene ankakhulupirira zinali zoona. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kutsimikizira zimenezi? (Werengani 2 Timoteyo 3:14, 15.) Amayi ake komanso agogo ake ndi omwe anamuphunzitsa “malemba oyera.” Koma mosakaikira, nayenso payekha ankachita khama kuti aphunzire malembawo. Zimenezi zinachititsa kuti ayambe ‘kukhulupirira pambuyo pokhutira’ kuti mfundo za m’malembawo ndi zoona. Kenako Timoteyo, mayi ake komanso agogo ake anaphunzitsidwa mfundo za Chikhristu. N’zosakayikitsa kuti Timoteyo anachita chidwi ndi chikondi chimene otsatira a Yesu ankasonyezana. Komanso ankafunitsitsa kukhala ndi Akhristu anzake ndiponso kumawatumikira. (Afil. 2:19, 20) Komabe sikuti ankangokhulupirira Mulungu chifukwa chokonda anthu, koma chifukwa choti anakhutira ndi mfundo za m’Baibulo zimene zinamuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Nanunso muyenera kumaphunzira Baibulo n’kufika pokhutira kuti zimene mwaphunzira zokhudza Yehova ndi zoona.
9. Kodi muyenera kutsimikizira mfundo zoyambirira za choonadi zitatu ziti?
9 Kuti tifike pokhutira ndi zimene timaphunzira, choyamba tiyenera kutsimikizira kuti mfundo zoyambirira za choonadi zitatu izi ndi zoona. Mfundo yoyamba ndi yakuti Yehova Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. (Eks. 3:14, 15; Aheb. 3:4; Chiv. 4:11) Yachiwiri ndi yakuti Baibulo ndi uthenga wochokera kwa Mulungu kupita kwa anthu. (2 Tim. 3:16, 17) Ndipo yachitatu ndi yakuti Yehova ali ndi gulu lake limene limamulambira motsogoleredwa ndi Khristu ndipo gulu limeneli ndi la Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12; Yoh. 14:6; Mac. 15:14) Kutsimikizira zimenezi sikuchita kufuna kuti munthu adziwe chilichonse chokhudza Baibulo. Cholinga chanu chizikhala choti muzigwiritsa ntchito mphamvu zanu za kuganiza kuti musamakayikire zoti zimene mumakhulupirira ndi zoona.—Aroma 12:1.
MUZIKHALA OKONZEKA KUTHANDIZA ENA KUTI AZIKHULUPIRIRA CHOONADI
10. Kuwonjezera pa kudziwa choonadi, kodi tiyeneranso kuchita chiyani?
10 Mukatsimikizira mfundo zoyambirira za choonadi zokhudza Mulungu, Baibulo komanso anthu a Mulungu, muyeneranso kudziwa mmene mungagwiritsire ntchito Malemba pothandiza ena kukhulupirira mfundozi. Tikutero chifukwa Akhristufe tili ndi udindo wophunzitsa ena choonadi chomwe timaphunzira.b (1 Tim. 4:16) Tikamayesetsa kuthandiza ena kukhulupirira kuti mfundo za m’Baibulo ndi zoona, nafenso timayamba kuzikhulupirira kwambiri.
11. Kodi tingamutsanzire bwanji Paulo pa nkhani yophunzitsa anthu?
11 Mtumwi Paulo akamaphunzitsa anthu ankagwiritsa ntchito “mfundo zokopa zokhudza Yesu, kuchokera m’chilamulo cha Mose ndi mu Zolemba za aneneri.” (Mac. 28:23) Kodi tingatsanzire bwanji Paulo tikamaphunzitsa ena choonadi? Tiyenera kuchita zambiri kuposa kungowauza zimene Baibulo limaphunzitsa. Tizithandiza ophunzira Baibulo athu kuganizira mozama mfundo za m’Malemba zimene zingawathandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Timafuna kuti anthuwo azikhulupirira mfundo za choonadi kuchokera mumtima osati chifukwa choopa kutikhumudwitsa. Ayenera kukhulupirira mfundozo chifukwa choti atsimikizira kuti zimene akuphunzira ndi choonadi chokhudza Mulungu wathu wachikondi.
12-13. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti apitirize kukonda choonadi?
12 Makolo, sitikukayikira kuti mumafuna kuti ana anu apitirize kukonda choonadi. Mwina mungamaganize kuti ana anu akamangocheza ndi anthu abwino mumpingo, ziwathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Komabe, kuti ana anu atsimikizire kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi choonadi, ayenera kuchita zinthu zinanso. Paokha, ayenera kumakonda kwambiri Mulungu komanso kukhulupirira kuti zimene amaphunzira m’Baibulo ndi zoona.
13 Kuti makolo athandize ana awo kukonda choonadi, ayenera kumawasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yophunzira Baibulo. Ayeneranso kumaganizira mozama zimene akuphunzira. Akamachita zimenezi m’pamene angakwanitse kuthandiza ana awo kuti azikonda choonadi. Makolo ayenera kuthandiza ana awo kudziwa mmene angafufuzire nkhani zina akamaphunzira, ngati mmene amachitira ndi anthu ena amene amawaphunzitsa Baibulo. Akatero, angathandize anawo kuti azikonda Yehova komanso kuti azikhulupirira kuti iye amagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu. (Mat. 24:45-47) Makolo, musamangophunzitsa ana anu mfundo zoyambirira za choonadi. Koma muziwathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba powaphunzitsanso zinthu zozama za m’Mawu a Mulungu mogwirizana ndi msinkhu komanso nzeru zawo.—1 Akor. 2:10.
MUZIPHUNZIRA MAULOSI A M’BAIBULO
14. N’chifukwa chiyani tiyenera kumaphunzira maulosi a m’Baibulo? (Onaninso bokosi lakuti “Kodi Mungafotokoze Maulosi Otsatirawa?”)
14 Maulosi a m’Baibulo ndi mbali yofunika ya Mawu a Mulungu ndipo angatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova. Kodi ndi maulosi ati amene amalimbitsa chikhulupiriro chanu? Mwina munganene kuti ndi maulosi onena za “masiku otsiriza.” (2 Tim. 3:1-5; Mat. 24:3, 7) Koma kodi ndi maulosi enanso ati amene anakwaniritsidwa omwe angalimbitse kwambiri chikhulupiriro chanu? Mwachitsanzo, kodi mungafotokoze mmene maulosi a mu Danieli chaputala 2 kapena Danieli chaputala 11 anakwaniritsidwira m’mbuyomu komanso mmene akukwaniritsidwira masiku ano?c Chikhulupiriro chanu chingalimbe kwambiri mukamaphunzira maulosi a m’Baibulo ngati amenewa. Chitsanzo ndi abale athu amene anazunzidwa ku Germany pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Ngakhale kuti abalewa sankamvetsa bwino maulosi a m’Baibulo onena za masiku otsiriza, iwo ankakhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu.
15-17. Kodi kuphunzira Baibulo kunathandiza bwanji abale athu amene ankazunzidwa pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi?
15 Pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi ku Germany, abale ndi alongo masauzande ambiri anatumizidwa kundende zozunzirako anthu. Hitler komanso Heinrich Himmler, yemwe anali mkulu wa asilikali wotchuka, ankadana kwambiri ndi a Mboni za Yehova. Mlongo wina ananena kuti Himmler anauza gulu la alongo athu, amene anali m’ndende ina yozunzirako anthu, kuti: “Yehova wanuyo akhoza kukhala kuti akulamulira kumwamba, koma pansi pano tikulamulira ndife. Tiona kuti amene atatheretu ndi ndani, inuyo kapena ifeyo.” Kodi n’chiyani chinathandiza anthu a Yehova kukhalabe okhulupirika?
16 Ophunzira Baibulowa ankadziwa kuti Ufumu wa Mulungu unali utayamba kulamulira mu 1914. Choncho sankadabwa pamene ankazunzidwa kwambiri. Komabe anthu a Yehova ankaona kuti palibe boma limene lingalepheretse cholinga cha Yehova. Iwo ankadziwa kuti Hitler sangathetse kulambira koona kapena kukhazikitsa boma lamphamvu kwambiri kuposa Ufumu wa Mulungu. Abale athuwa sankakayikira kuti ulamuliro wa Hitler udzatha.
17 Zimene abale ndi alongowa ankakhulupirira zinali zoona. Pasanapite nthawi, ulamuliro wa Nazi unatha ndipo Heinrich Himmler, amene ananena kuti “pansi pano tikulamulira ndife,” anathawa poopa kuphedwa. Pamene ankathawa, anakumana ndi m’bale Lübke, yemwe anamangidwapo ndipo anamuzindikira. Mwamanyazi, Himmler anafunsa m’baleyo kuti: “Wophunzira Baibulo, kodi chichitike n’chiyani tsopano?” M’bale Lübke anamuuza kuti a Mboni za Yehova ankadziwa kuti ulamuliro wa Nazi udzatha ndipo iwo adzamasulidwa. Himmler, yemwe poyamba ankalankhula zamwano ponena za a Mboni, anangoti kukamwa yasa, kusowa chonena. Patangopita nthawi yochepa anadzipha. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Tikamaphunzira Baibulo kuphatikizapo maulosi, tingamakhulupirire kwambiri Mulungu ndipo zimenezi zingatithandize kuti tisagonje tikamayesedwa.—2 Pet. 1:19-21.
18. Mogwirizana ndi lemba la Yohane 6:67, 68, n’chifukwa chiyani tifunika “kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri” ngati mmene Paulo analembera?
18 Tiyenera kumakondana kuti tisonyeze kuti ndife Akhristu oona. Koma timafunikanso “kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.” (Afil. 1:9) Kupanda kutero, tikhoza kutengeka ndi “mphepo iliyonse ya chiphunzitso chonyenga cha anthu,” kuphatikizapo ampatuko. (Aef. 4:14) Pamene ophunzira ena a Yesu anasiya kumutsatira, mtumwi Petulo anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri kuti Yesu anali ndi “mawu amoyo wosatha.” (Werengani Yohane 6:67, 68.) Ngakhale kuti pa nthawiyi Petulo sankamvetsa zonse zokhudza mawu a moyowa, iye anakhalabe wokhulupirika chifukwa ankadziwa kuti Yesu ndi Khristu. N’zotheka kuti nanunso muzikhulupirira kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. Mukatero, chikhulupiriro chanu chidzakhala cholimba kwambiri ndipo mudzathandizanso ena kulimbitsa chikhulupiriro chawo.—2 Yoh. 1, 2.
NYIMBO NA. 72 Tikulalikira Choonadi Chonena za Ufumu
a Nkhaniyi itithandiza kumvetsa kuti choonadi chimene chimapezeka m’Mawu a Mulungu ndi chofunika kwambiri. Ifotokozanso zimene zingatithandize kutsimikizira kuti zimene timakhulupirira ndi zoona.
b Kuti mudziwe mmene mungafotokozere kwa ena mfundo zoyambirira za choonadi, onani nkhani zakuti, “Kucheza Ndi Munthu Wina” zomwe zinatuluka mu Nsanja ya Olonda kuyambira mu 2010 mpaka mu 2015. Nkhani zina zomwe zili m’magaziniwa ndi monga: “Kodi Yesu Ndi Mulungu?” “Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira?” komanso “Kodi Mulungu Amalanga Anthu Kumoto?”
c Kuti muone mmene maulosiwa anafotokozedwera, onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, ndi ya May 2020.
d MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pakulambira kwa pabanja, makolo akuphunzira ndi ana awo maulosi onena za chisautso chachikulu.
e MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Pachisautso chachikulu banja lija silikudabwa ndi zimene zikuchitika.