NKHANI YOPHUNZIRA 4
Yehova Amadalitsa Khama Lathu Loyesetsa Kuti Tipezeke pa Chikumbutso
“Muzichita zimenezi pondikumbukira.”—LUKA 22:19.
NYIMBO NA. 19 Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. N’chifukwa chiyani timapezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse?
ZAKA pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife, zomwe zinapereka mwayi woti tidzapeze moyo wosatha. Pa usiku wake womaliza, Yesu analamula otsatira ake kuti azikumbukira chikondi chake pochita mwambo wosavuta pogwiritsa ntchito mkate ndi vinyo.—1 Akor. 11:23-26.
2 Timamvera lamulo la Yesuli chifukwa choti timamukonda kwambiri. (Yoh. 14:15) Chaka chilichonse pa nyengo ya Chikumbutso, timasonyeza kuyamikira zomwe anatichitira popemphera komanso kuganizira kwambiri tanthauzo la imfa yake. Timasangalalanso kuchita zambiri pa ntchito yolalikira n’kumalimbikitsa anthu ambiri kuti adzakhale nafe pamwambo wapaderawu. Ndipotu timakhala otsimikiza kuti tisalole chilichonse kutilepheretsa kupezeka pa Chikumbutso.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Munkhaniyi tikambirana njira zitatu zomwe anthu a Yehova akhala akusonyezera khama kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Njira zake ndi (1) kuyambiranso kuchita mwambowu m’njira imene Yesu anakhazikitsa, (2) kuitanira ena ku Chikumbutso ndiponso (3) kuchita mwambowu ngakhale pa nthawi imene pali zovuta zambiri.
KUYAMBIRANSO KUCHITA MWAMBOWU M’NJIRA IMENE YESU ANAKHAZIKITSA
4. Kodi ndi mfundo za choonadi ziti zomwe timazimvetsa pa Chikumbutso chaka chilichonse, nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kuziona mopepuka? (Luka 22:19, 20)
4 Chaka chilichonse pa Chikumbutso, timamvetsera nkhani ya m’Baibulo yomwe imayankha momveka bwino mafunso angapo. Timaphunzira chifukwa chake anthu amafunikira dipo komanso mmene limathandizira kuti machimo a anthu ambiri akhululukidwe. Timakumbutsidwa zimene mkate ndi vinyo zimaimira komanso amene ayenera kudya ndi kumwa. (Werengani Luka 22:19, 20.) Komanso timaganizira madalitso amene anthu omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padzikoli adzapeze. (Yes. 35:5, 6; 65:17, 21-23) Tisamaone mopepuka mfundo za choonadizi. Anthu mabiliyoni sazidziwa ndipo samvetsa kuti nsembe ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Iwo sachitanso mwambowu ngati mmene iye anauyambitsira. N’chifukwa chiyani zili choncho?
5. Atumwi ambiri atamwalira, kodi anthu ankachita bwanji mwambo wokumbukira imfa ya Yesu?
5 Patangopita kanthawi kuchokera pamene atumwi ambiri a Yesu anamwalira, Akhristu onyenga analowa mumpingo. (Mat. 13:24-27, 37-39) Iwo ankalankhula “zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.” (Mac. 20:29, 30) Chimodzi mwa “zinthu zopotoka” zomwe anayamba kuphunzitsa, chinali chakuti Yesu sanapereke thupi lake “kamodzi kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri,” monga mmene Baibulo limanenera, koma kuti nsembe yake iyenera kumaperekedwa mobwerezabwereza. (Aheb. 9:27, 28) Masiku ano anthu ambiri oona mtima amakhulupirira chiphunzitso chabodzachi. Iwo amasonkhana m’matchalitchi pafupipafupi, nthawi zinanso tsiku lililonse, kuti achite mwambo umene amautchula kuti “Nsembe ya Misa.”b Zipembedzo zina zimachitanso mwambo wokumbukira imfa ya Yesu mwa apo ndi apo koma anthu ambiri m’zipembedzozo sadziwa tanthauzo la nsembe ya Yesu. Choncho ena angadabwe kuti, ‘Kodi imfa ya Yesu ingachititsedi kuti machimo anga akhululukidwe?’ N’chifukwa chiyani amafunsa funsoli? Nthawi zina iwo amakhala kuti anasokonezedwa ndi anthu omwe amakayikira zoti nsembe ya Yesu ingachititse kuti machimo akhululukidwe. Ndiye kodi otsatira enieni a Yesu athandiza bwanji anthu ena pa nkhaniyi?
6. Pofika mu 1872, kodi kagulu ka Ophunzira Baibulo kanamvetsa chiyani?
6 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kagulu ka Ophunzira Baibulo kotsogoleredwa ndi Charles Taze Russell kanayamba kuphunzira Malemba mosamala kwambiri. Iwo ankafuna kudziwa zoona zenizeni zimene nsembe ya Yesu imatanthauza komanso mmene anthu ayenera kukumbukirira imfa yake. Pofika mu 1872, iwo anamvetsa zimene Baibulo limanena zoti Yesu anaperekadi dipo lowombola anthu onse. Koma sikuti iwo anangokhala nazo okha zimene anadziwazi. M’malomwake, ankauzanso ena pogwiritsa ntchito mabuku, manyuzipepala komanso magazini. Nthawi yomweyo, potsanzira Akhristu oyambirira anayamba kumasonkhana kamodzi pa chaka kuti azichita Chikumbutso.
7. Kodi zimene Ophunzira Baibulo oyambirira anafufuza zimatithandiza bwanji?
7 Zimene Akhristu oona mtimawa anafufuza zaka zambiri zapitazo, zimatithandizanso masiku ano. Motani? Mothandizidwa ndi Yehova timamvetsa choonadi chokhudza nsembe ya Yesu komanso zimene nsembeyo imakwaniritsa. (1 Yoh. 2:1, 2) Taphunziranso zimene Baibulo limafotokoza zokhudza chiyembekezo chomwe anthu omwe amasangalatsa Mulungu ali nacho, kuti ena adzakhala ndi moyo wosafa kumwamba komanso anthu mamiliyoni ambiri adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Timakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova tikamaganizira chikondi chomwe amatisonyeza komanso mmene aliyense payekha amapindulira chifukwa cha nsembe ya Yesu. (1 Pet. 3:18; 1 Yoh. 4:9) Choncho mofanana ndi abale athu okhulupirika akale, timaitanira ena kuti adzakhale nafe pamwambo wa Chikumbutso womwe umachitika mofanana ndi mmene Yesu anachitira.
KUITANIRA ENA KU CHIKUMBUTSO
8. Kodi anthu a Yehova akhala akuchita zotani kuti aziitanira anthu ku Chikumbutso? (Onani chithunzi.)
8 Kwa zaka zambiri anthu a Yehova akhala akuitanira ena ku Chikumbutso. M’chaka cha 1881, abale ndi alongo ku United States anapemphedwa kuti akasonkhane m’nyumba ya m’bale ku Allegheny, Pennsylvania kuti achite mwambo wapaderawu. M’zaka zotsatira, mipingo inauzidwa kuti mpingo uliwonse ungachite Chikumbutso paokhapaokha. Mu March 1940, ofalitsa anauzidwa kuti angathe kuitanira aliyense yemwe wasonyeza chidwi m’gawo lawo. Kwa nthawi yoyamba mu 1960, ofesi ya nthambi inatumiza kumipingo timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso. Kungochokera nthawi imeneyo, mabiliyoni a timapepalati akhala akugawidwa. N’chifukwa chiyani timachita khama chonchi poitanira anthu kumwambowu?
9-10. Kodi ndi ndani amapindula tikachita khama poitanira ena ku Chikumbutso? (Yohane 3:16)
9 Chifukwa chimodzi chomwe chimatichititsa kuitanira ena ku Chikumbutso, ndi chakuti timafuna adzaphunzire zimene Yehova ndi Yesu atichitira. (Werengani Yohane 3:16.) Timayembekezera kuti zimene adzaone komanso kumva pamwambowu zidzawalimbikitsa kuti afune kudziwa zambiri komanso akhale atumiki a Yehova. Koma palinso ena omwe amapindula.
10 Timaitaniranso anthu omwe anasiya kutumikira Yehova pofuna kuwakumbutsa kuti Mulungu amawakondabe. Ambiri amabwera tikawaitana ndipo timasangalala kwambiri kuwaona. Kupezeka pamwambowu kumawakumbutsa mmene ankasangalalira pamene ankatumikira Yehova. Taganizirani chitsanzo cha Monica.c Iye anathandizidwa kuti ayambirenso kukhala wofalitsa pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Atapezeka pa Chikumbutso mu 2021, ananena kuti: “Chikumbutsochi chinali chapadera kwambiri kwa ine. Kwanthawi yoyamba pambuyo pazaka 20 ndakwanitsa kulalikira kwa anthu komanso kuwaitanira kumwambowu. Ndinachita khama pa ntchito yoitanira anthuyi, chifukwa ndimayamikira kwambiri zimene Yehova ndi Yesu anandichitira.” (Sal. 103:1-4) Kaya anthu abwera ku Chikumbutso kapena ayi, timawaitanirabe mwakhama podziwa kuti Yehova amayamikira khama lathulo.
11. Kodi Yehova wadalitsa bwanji khama lomwe timachita poitanira anthu ku Chikumbutso? (Hagai 2:7)
11 Yehova wakhala akudalitsa kwambiri khama lathu loitanira anthu ku Chikumbutso. Mu 2021 ngakhale kuti sitinkatha kuchita zambiri chifukwa cha mliri wa COVID-19, anthu amene anapezeka pamwambowu anali okwana 21,367,603. Chiwerengerochitu ndi kuwirikiza pafupifupi kawiri ndi hafu chiwerengero cha a Mboni za Yehova padziko lonse. Komabe sikuti Yehova amachita chidwi ndi kuchuluka kwa anthu omwe apezeka pamwambowu. M’malomwake, amachita chidwi ndi munthu aliyense payekha. (Luka 15:7; 1 Tim. 2:3, 4) Sitimakayikira kuti Yehova amatithandiza kupeza anthu a mtima wabwino kudzera muntchito yoitanira anthu ku Chikumbutsoyi.—Werengani Hagai 2:7.
KUCHITA CHIKUMBUTSO NGAKHALE PA NTHAWI YOVUTA
12. Kodi ndi mavuto ati omwe angachititse kuti zikhale zovuta kuchita Chikumbutso? (Onani chithunzi.)
12 Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza tidzakumana ndi mavuto ambiri monga kutsutsidwa ndi achibale, kuzunzidwa, nkhondo, miliri ndi ena ambiri. (Mat. 10:36; Maliko 13:9; Luka 21:10, 11) Nthawi zina mavuto amenewa amachititsa kuti zikhale zovuta kuti tichite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Kodi abale ndi alongo athu achita zotani polimbana ndi mavuto ngati amenewa, nanga Yehova wawathandiza bwanji?
13. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Artem chifukwa cholimba mtima komanso kukhala wotsimikiza kuti achite Chikumbutso ali m’ndende?
13 Kumangidwa. Abale athu omwe ali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo, amachita zonse zomwe angathe kuti akumbukire imfa ya Yesu. Taganizirani chitsanzo cha Artem. Pa nthawi ya Chikumbutso cha mu 2020, iye anaikidwa muselo yaing’ono kwambiri (masikweya mita 17) yomwe munkakhala akaidi 5 pa nthawi imodzi. Ngakhale zinali choncho, anakwanitsa kupeza zizindikiro za pa Chikumbutso ndiponso anakonza zoti akambe nkhani n’cholinga choti apindule. Koma akaidi anzake ankasuta komanso ankakonda kutukwana. Ndiye kodi iye anatani? Anawapempha kuti ngati angakwanitse, kwa ola limodzi lokha asasute kapena kutukwana. Artem anadabwa kuti anzakewo anavomera. Iye anati: “Ndinafuna kuwauza za Chikumbutso.” Ngakhale kuti iwo sankafuna kumva zokhudza mwambowu, atamva ndiponso kuona Artem akuchita mwambo wa Chikumbutso, anafuna kumva zambiri.
14. Kodi abale anayesetsa kutani kuti achite Chikumbutso ngakhale kuti kunali mliri wa COVID-19?
14 Mliri wa COVID-19. Mliriwu utayambika, anthu a Yehova sanathenso kuchita Chikumbutso pamasom’pamaso. Koma izi sizinawalepheretse kuchita mwambowu.d Mipingo ya m’madera omwe kuli intaneti inachita mwambowu kudzera pa vidiyokomfelensi. Koma bwanji za anthu mamiliyoni omwe ali m’madera amene kulibe intaneti? M’mayiko ena anakonza zoulutsa nkhani ya Chikumbutso pa TV kapena pa wailesi. Kuwonjezera pamenepo maofesi a nthambi anajambula nkhaniyi mu m’zilankhulo zoposa 500 kuti ngakhale anthu akutali kwambiri achite Chikumbutso. Ndipo abale okhulupirika anakapereka nkhanizi kumaderawa.
15. Kodi tikuphunzira chiyani kwa wophunzira Baibulo wina dzina lake Sue?
15 Kutsutsidwa ndi achibale. Vuto lalikulu limene ena amakumana nalo pa nkhani yochita Chikumbutso ndi kutsutsidwa ndi achibale. Taganizirani zimene zinachitikira wophunzira Baibulo wina dzina lake Sue. Mu 2021, kutatsala tsiku limodzi kuti mwambo wa Chikumbutso uchitike, Sue anauza amene ankamuphunzitsa Baibulo kuti sakwanitsa kuchita nawo chifukwa ankatsutsidwa ndi anthu a m’banja lake. Mphunzitsi wakeyo anamuwerengera Luka 22:44. Kenako anamufotokozera kuti tikamakumana ndi mavuto tiyenera kutengera chitsanzo cha Yesu popemphera kwa Yehova komanso kumukhulupirira kwambiri. Tsiku lotsatira, Sue anakonza zizindikiro zoti agwiritse ntchito ndipo anaonera pulogalamu yapadera ya Kulambira kwa M’mawa ya pa jw.org. Madzulo ake ali yekha m’chipinda chake, anachita nawo Chikumbutso kudzera pa foni. Pambuyo pake Sue analembera mphunzitsi wakeyo kuti: “Munandilimbikitsa kwambiri dzulo. Ndinachita zonse zomwe ndikanatha kuti ndichite Chikumbutso ndipo Yehova anandithandiza kwambiri. Sindingathe kufotokoza mmene ndikusangalalira ndipo ndikuthokoza kwambiri.” Kodi inunso mukuona kuti Yehova angakuthandizeni mutakumana ndi mavuto ngati amenewa?
16. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yehova adzadalitsa khama lathu kuti tidzapezeke pa Chikumbutso? (Aroma 8:31, 32)
16 Yehova amayamikira kwambiri khama lomwe timachita kuti tikumbukire imfa ya Yesu. Sitikayikira kuti adzatidalitsa tikamayamikira zimene anatichitira. (Werengani Aroma 8:31, 32.) Choncho tiyeni tikhale otsimikiza kuti tidzapezeke pa Chikumbutso chaka chino komanso kuwonjezera zimene timachita potumikira Yehova pa nyengoyi.
NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo
a Lachiwiri pa 4 April 2023, anthu mamiliyoni padziko lonse adzapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Khristu. Ambiri kadzakhala koyamba kupezekapo. A Mboni ena omwe anali akhama koma anasiya kusonkhana zaka zambiri m’mbuyomo adzapezekanso pamwambowu. Enanso adzafunika kulimbana ndi mavuto ambiri kuti apezekepo. Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, mungakhale wotsimikiza kuti Yehova adzasangalala chifukwa choti mwayesetsa kuti mupezekepo.
b Anthuwo amakhulupirira kuti pamwambowu mkate ndi vinyo zimasanduka thupi komanso magazi enieni a Khristu. Iwo amaganiza kuti thupi ndi magazi a Yesu zimaperekedwa nsembe pa nthawi iliyonse imene munthu akupanga mwambowu.
c Mayina ena asinthidwa.
d Onaninso nkhani za pa jw.org zakuti, “Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2021.”
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kuyambira m’ma 1960 timapepala toitanira ku Chikumbutso takhala tikukonzedwa ndipo tsopano timapezeka tosindikizidwa komanso tapazipangizo zamakono.
f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pachithunzichi, abale ndi alongo akuchita Chikumbutso pa nthawi yomwe kuli zipolowe.