Kodi Babulo Wamkulu N’chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Babulo Wamkulu amene amatchulidwa m’buku la Chivumbulutso amaimira zipembedzo zonse zabodza zomwe Mulungu amadana nazo.a (Chivumbulutso 14:8; 17:5; 18:21) Ngakhale kuti zipembedzozi n’zosiyanasiyana, zonse zimasokoneza anthu ndipo siziwathandiza kuti azilambira Yehova yemwe ndi Mulungu woona.—Deuteronomo 4:35.
Kodi Babulo Wamkulu tingamudziwe bwanji?
Mawu akuti Babulo Wamkulu Ndi Ophiphiritsa. Baibulo limamutchula kuti “mkazi” komanso “hule lalikulu” lomwe ‘dzina lake lachinsinsi ndi lakuti: Babulo Wamkulu.’ (Chivumbulutso 17:1, 3, 5) Buku la Chivumbulutso limafotokoza zinthu pogwiritsa ntchito “zizindikiro.” Choncho m’pomveka kunena kuti Babulo Wamkulu sakuimira mkazi weniweni. (Chivumbulutso 1:1) Baibulo limanenanso kuti mkaziyo wakhala “pamadzi ambiri” omwe amaimira “mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero.” (Chivumbulutso 17:1, 15) Ndiye n’zosatheka kuti mkazi weniweni achite zimenezi.
Babulo Wamkulu amapezeka padziko lonse. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limamutchula kuti ndi “mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.”—Chivumbulutso 17:18.
Babulo Wamkulu akuimira zipembedzo osati magulu andale kapena amalonda. Anthu amumzinda wakale wa Babulo ankakonda kwambiri “zamatsenga.” (Yesaya 47:1, 12, 13; Yeremiya 50:1, 2, 38) Zimene anthuwo ankachita zokhudza chipembedzo zinkatsutsana kwambiri ndi zimene Yehova Mulungu amafuna. (Genesis 10:8, 9; 11:2-4, 8) Olamulira a ku Babulo anali odzimva ndipo ankadziona kuti ndi apamwamba kuposa Mulungu. (Yesaya 14:4, 13, 14; Danieli 5:2-4, 23) Nawonso anthu amene ali mu Babulo Wamkulu amakonda kuchita “zamizimu.”—Chivumbulutso 18:23.
Babulo Wamkulu sangakhale magulu andale chifukwa “mafumu a dziko lapansi” adzalira Babulo Wamkuluyo akadzawonongedwa. (Chivumbulutso 17:1, 2; 18:9) Sangakhalenso amalonda chifukwa Baibulo limamusiyanitsa ndi ‘amalonda a padziko lapansi.’—Chivumbulutso 18:11, 15.
Babulo Wamkulu akuimira zipembedzo zabodza. Zipembedzo zabodzazi sizithandiza anthu kukhala pa ubwenzi ndi Yehova yemwe ndi Mulungu woona. Koma zimachititsa anthu kuti azilambira milungu ina. Baibulo limanena kuti kuchita zimenezi kuli ngati kuchita “chiwerewere” ndi milungu ina. (Ekisodo 34:15, 16; Levitiko 20:6) Anthu a m’zipembedzo zabodza amakhulupirira zinthu monga zoti kuli Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndiponso Mulungu Mzimu Woyera. Amakhulupiriranso kuti mzimu wa munthu suufa komanso amagwiritsa ntchito mafano polambira Mulungu. Zonsezi ndi zimene anthu a ku Babulo wakale ankakhulupirira ndiponso kuchita. Anthu a m’zipembedzo zabodza amakonda kwambiri zinthu za m’dzikoli. Baibulo limanena kuti kuchita zimenezi kuli ngati kuchita chigololo.—Yakobo 4:4.
Zipembedzo zabodzazi zili ndi chuma komanso ndi zodzionetsera. Zimenezi n’zofanana ndi zimene Baibulo limanena zoti Babulo Wamkulu wavala “zovala zofiirira ndi zofiira kwambiri ” komanso kuti ‘wadzikongoletsa ndi golide, ndi mwala winawake wamtengo wapatali ndiponso ngale.’ (Chivumbulutso 17:4) Babulo Wamkulu n’kuchimake kwa “zonyansa za padziko lapansi.” Zimenezi zikutanthauza kuti Babulo Wamkulu amaphunzitsa komanso kuchita zinthu zosalemekeza Mulungu. (Chivumbulutso 17:5) Mawu akuti “mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero” akuimira anthu onse amene ali mu Babulo Wamkulu.—Chivumbulutso 17:15.
Babulo Wamkulu ali ndi mlandu wamagazi a “onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 18:24) Zipembedzozi zakhala zikulimbikitsa anthu kuti azimenya nkhondo komanso zalephera kuphunzitsa anthu mfundo zoona zokhudza Yehova, yemwe ndi Mulungu wachikondi. (1 Yohane 4:8) Izi zachititsa kuti anthu ambiri aphedwe. Choncho anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu ayenera ‘kutuluka mwa iye,’ kapena kusiya kusiya chipembedzo chabodza.—Chivumbulutso 18:4; 2 Akorinto 6:14-17.
a Onani nkhani yakuti, “Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?”