23 Choncho Mulungu anaseseratu chamoyo chilichonse chimene chinali padziko lapansi, kuyambira munthu, nyama, nyama zokwawa komanso zamoyo zouluka mumlengalenga. Zonsezi anazisesa padziko lapansi.+ Nowa yekha komanso amene anali naye limodzi mʼchingalawacho, anapulumuka.+