27 Akamumwetsa madziwo, ngati iye anadzidetsa pogona ndi mwamuna wina, madzi a tembererowo azikhala chinthu chowawa akalowa mʼthupi mwake. Zikatero mimba yake izitupa ndipo ntchafu yake izifota. Mkaziyo azikhala chitsanzo cha munthu wotembereredwa pakati pa anthu a mtundu wake.