7 Koma iye wandiuza kuti, ‘Udzakhala ndi pakati ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Ndiye usamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, ndipo usadye chilichonse chodetsedwa, chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri wa Mulungu kuchokera tsiku limene adzabadwe mpaka tsiku limene adzafe.’”