17 Pamapeto pake, Samisoni anamuululira zonse. Anamuuza kuti: “Mʼmutu mwanga simunadutsepo lezala, chifukwa ndine Mnaziri wa Mulungu kuyambira tsiku limene ndinabadwa.+ Atandimeta, mphamvu zanga zikhoza kutha, ndipo ndingafooke nʼkukhala ngati anthu ena onse.”