27 Davide ndi asilikali ake anapita nʼkukapha Afilisiti 200. Ndiyeno Davide anabweretsa makungu awo akunsonga ndipo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Choncho Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+