9 Tsoka kwa amene akulimbana ndi amene anamupanga,
Chifukwa iye ali ngati phale
Limene lili pakati pa mapale ena amene ali pansi.
Kodi dongo lingafunse woumba mbiya kuti: “Kodi ukupanga chiyani?”+
Kapena kodi chinthu chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?