20 Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa, ndidzamubweretsera tsoka ndipo adzafa.+ Ngati sunamuchenjeze, adzafa chifukwa cha tchimo lake ndipo zabwino zimene ankachita sizidzakumbukiridwa, koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera kwa iwe.+