8 Amene anapanga gulu la nyenyezi la Kima ndi gulu la nyenyezi la Kesili,+
Amene amachititsa mdima wandiweyani kukhala kuwala kwa mʼmamawa,
Amene amachititsa masana kukhala ngati mdima wausiku,+
Amenenso amasonkhanitsa madzi amʼnyanja
Nʼkuwakhuthulira pansi,+
Dzina lake ndi Yehova.