30 Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, pamene Davide ndi asilikali ake anali kubwerera ku Zikilaga+ tsiku lachitatu, Aamaleki+ anaukira anthu a kum’mwera ndi a mumzinda wa Zikilaga ndi kufunkha zinthu zawo. Iwo anathira nkhondo mzindawo ndi kuutentha ndi moto.