8 “Taona, ukukhala pafupi ndi Simeyi+ wa ku Bahurimu,+ mwana wa Gera M’benjamini. Iyeyu ananditemberera temberero lopweteka+ tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu.+ Ndi iyeyu amene anabwera kudzakumana nane pa Yorodano,+ choncho ndinamulumbirira pamaso pa Yehova kuti: ‘Sindidzakupha ndi lupanga.’+