10 Ndiyeno munaonetsa Farao zizindikiro ndi zozizwitsa zomukhaulitsa pamodzi ndi atumiki ake onse ndi anthu onse okhala m’dziko lake.+ Munatero chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepo munadzipangira dzina+ kufikira lero.