Mawu a M'munsi
a Posonyeza mkwiyo chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo, Yesu ankatsanzira Yehova, amene ndi “wokonzeka kusonyeza mkwiyo wake” pa zoipa zilizonse. (Nahumu 1:2) Mwachitsanzo, Yehova atauza anthu ake osamvera kuti anasandutsa nyumba yake kukhala “phanga la achifwamba,” anati: “Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zidzatsanulidwa pamalo awa.”—Yeremiya 7:11, 20.