Mawu a M'munsi
a Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti mawu akuti “khungu kusinthanitsa ndi khungu” amatanthauza kuti chifukwa cha kudzikonda, Yobu akanalolera kuti khungu kapena moyo wa ana ake ndiponso ziweto zake ziwonongeke pofuna kuteteza khungu kapena moyo wake. Ena amanena kuti mawuwa amatanthauza kuti munthu angalolere kuti khungu lake liwonongeke pofuna kupulumutsa moyo wake. Mwachitsanzo, munthu amatha kupherera chibakera ndi mkono mpaka mkonowo kuvulala n’cholinga choti asamenyedwe mutu. Kaya mawu okuluwikawa ankatanthauza chiyani, mfundo yake ndi yakuti Yobu akanalolera kupereka chilichonse kuti ateteze moyo wake.