Mawu a M'munsi
c Mwachitsanzo, pa msonkhano wina pomwe atsogoleri azipembedzo za Chipulotesitanti anachita ku America mu 1918, ananena kuti bungwe la League of Nations ndi bungwe landale lomwe likuimira Ufumu wa Mulungu padziko lapansi. M’chaka cha 1965, atsogoleri a zipembedzo za Chibuda, Chikatolika, Orthodox, Chihindu,Chisilamu,Chiyuda,Chipulotesitanti anachita msonkhano ku San Francisco n’cholinga choti athandize komanso kupempherera bungwe la United Nations. Mu 1979, Papa Yohane Paulo Wachiwiri, ananena kuti akukhulupirira kuti bungwe la United Nations “lidzakhalabe lamphamvu kwambiri padziko lonse ndipo lidzathandiza pokhazikitsa mtendere ndiponso chilungamo mpaka kalekale.”