Lingaliro la Baibulo
Chigololo—Kukhululukira Kapena Kusakhululukira?
“KHULULUKIRANI, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.” (Marko 11:25) Mawu amenewo a Yesu amadzutsa mafunso ena ovuta mu nkhani ya ukwati wogwedezeka chifukwa cha chigololo: Kodi mkazi wopanda liwongo amene ali Mkristu ayenera kukhululukira mwamuna wake ndi kuchititsa ukwatiwo kupitiriza?a Ngati wasankha chisudzulo, kodi akuika kaimidwe kake ndi Mulungu kukhala pa ngozi? Tiyeni tione mmene Baibulo limathandizira kuyankha mafunso ameneŵa.
Kodi Muyenera Kukhululukira Nthaŵi Zonse?
Kodi mawu a Yesu akuti, “khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu,” amatanthauza kuti zivute zitani Mkristu ayenera kukhululukira—kuphatikizapo pamene wa mu ukwati achita chigololo? Mawu a Yesu ayenera kumvedwa mothandizidwa ndi ndemanga zina zimene ananena ponena za chikhululukiro.
Mwachitsanzo, timaphunzira za lamulo lofunika la kukhululukira m’mawu a Yesu olembedwa pa Luka 17:3, 4 kuti: “Akachimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire. Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kaŵiri patsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kaŵiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.” Zoonadi wina atachita tchimo lalikulu, wochimwiridwayo akulimbikitsidwa kuyesa kukhululukira ngati pali kulapa koona. Yehova mwiniyo amaona nkhaniyi mwa njira imeneyi; kuti tikhululukiridwe ndi Mulungu, tiyenera kulapa moona mtima.—Luka 3:3; Machitidwe 2:38; 8:22.
Komabe, zimenezi zimasonyezanso kuti ngati wa mu ukwati wachigololo ali wosalapa, akumakana kuvomereza tchimo lake, wa mu ukwati wopanda liwongoyo angakhale ndi chifukwa chabwino chosankhira kusakhululukira.—Yerekezerani ndi 1 Yohane 1:8, 9.
Chikhululukiro—Bwanji Nanga za Zotulukapo Zake?
Bwanji ngati wachigololoyo alapa? Pamene munthu alapa, pamakhala maziko a chikhululukiro. Koma kodi kukhululukira kumatanthauza kuti wochita cholakwayo sangavutike ndi zotulukapo zilizonse za njira yake yolakwayo? Lingalirani za zitsanzo zina za chikhululukiro cha Yehova.
Pamene Aisrayeli anapanduka atamvetsera zonena za azondi khumi amene anadza ndi mbiri yoipa ponena za dziko la Kanani, Mose anachonderera Yehova kuti: “Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa.” Yehova anayankha kuti: “Ndakhululukira monga mwa mawu ako.” Kodi zimenezi zinatanthauza kuti ochimwawo sanakhale ndi zotulukapo zilizonse za machitidwe awo? Yehova anapitiriza kuti: “Anthu onse awa . . . osamvera mawu anga; sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo awo.” (Numeri 14:19-23) Yehova anakwaniritsa mawu ake; mbadwo wa achikulire umenewo—kusiyapo Yoswa ndi Kalebi—sunaone Dziko Lolonjezedwa.—Numeri 26:64, 65.
Mofananamo, pamene mneneri Natani anadzudzula Mfumu Davide chifukwa cha tchimo lake ndi Bateseba, Davide wolapayo anavomereza kuti: “Ndinachimwira Yehova.” Ndiyeno Natani anauza Davide kuti: “Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu.” (2 Samueli 12:13) Komabe, ngakhale kuti Yehova anakhululukira Davide, iyeyo anavutika ndi zotulukapo za tchimo lake kwa moyo wake wonse.—2 Samueli 12:9-14; onaninso 2 Samueli, chaputala 24.
Zitsanzo zimenezi za kukhululukira kwa Mulungu zimasonyeza phunziro lofunika: Sitingachimwe ndiyeno nkusalangidwa. (Agalatiya 6:7, 8) Komabe, ngakhale kuti wochimwa wolapayo angakhululukidwe, sangapeŵe zotulukapo za njira yake yolakwayo. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti mkazi wopanda liwongo angakhululukire mwamuna wachigololoyo—m’lingaliro la kuleka kumkwiyira—komabe nasankha kusudzula mwamunayo?
Chikhululukiro ndi Chisudzulo
Mkati mwa utumiki wake, Yesu, panthaŵi zitatu ananena za chisudzulo. (Mateyu 5:32; 19:3-9; Luka 16:18) Chochititsa chidwi nchakuti, palibe ngakhale kamodzi m’makambitsirano ameneŵa pamene Yesu anatchula za chikhululukiro. Mwachitsanzo, monga momwe timapezera pa Mateyu 19:9, iye anati “Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo.” Mwa kunena kuti “kosakhala chifukwa cha chigololo,” Yesu anali kusonyeza kuti chigololo chingapatse mphamvu wa mu ukwati wopanda liwongoyo, kapena “chifukwa” cha Malemba cha kusudzulira wina. Komabe, Yesu sananene kuti wopanda liwongoyo ayenera kusudzula. Komabe, anasonyeza bwino kuti mkaziyo angathe kutero.
Ukwati uli pangano limene limamangirira anthu aŵiri pamodzi. (Aroma 7:2) Komabe pamene mmodzi wa iwo ali wosakhulupirika, panganolo lingathetsedwe. M’zochitika zotero wa mu ukwati wopanda liwongo kwenikweni amayang’anizana ndi zosankha ziŵiri. Choyamba, kodi mkaziyo ayenera kukhululukira? Monga momwe taonera, chinthu chachikulu pano nchakuti kaya wachigololoyo walapa moona mtima kapena ayi. Pamene pali kulapa, wa mu ukwati wopanda liwongo m’kupita kwa nthaŵi angakhululukire—m’lingaliro la kuleka kukwiya.
Chosankha chachiŵiri nchakuti, kodi mkaziyo ayenera kusudzula mwamunayo? Kodi nchifukwa ninji funso limeneli liyenera kubuka ngati iyeyo wakhululukira mwamunayo?b Chabwino, bwanji ngati mkaziyo ali ndi nkhaŵa zomveka zonena za chitetezero chake ndi cha ana ake, makamaka ngati mwamunayo anali wankhanza kumbuyoko? Kapena bwanji ngati akuwopa kuyambukiridwa ndi nthenda yachiwerewere? Kapena bwanji ngati mkaziyo ali wotsimikizira kwambiri kuti chifukwa chakuti wamnyenga, sadzamkhulupiriranso mu unansi wa mwamuna ndi mkazi? M’mikhalidwe yotero kungakhale koyenera kwa mkazi wopanda liwongoyo kukhululukira mwamuna wake wochimwayo (m’lingaliro la kuleka kukwiya) komabe nasankha kumsudzula chifukwa chakuti sakufunanso kupitiriza kukhala naye. Kuleka kukwiya kungathandize mkaziyo kupitiriza ndi moyo wake. Kungathandizirenso ulemu kukhalapo pakati pa mkaziyo ndi mwamuna wachigololoyo pa zochita zawo zilizonse za mtsogolo zimene angafunikire kuchitira pamodzi.
Kusudzula wa mu ukwati wosakhulupirika kapena ayi ndi chosankha cha munthu mwini, chosankha chimene wa mu ukwati wopanda liwongo ayenera kupanga atapenda mosamalitsa ndi mwapemphero zinthu zonse zoloŵetsedwamo. (Salmo 55:22) Ena sayenera kuuza wa mu ukwati wopanda liwongo kapena kumuumiriza kusankha imodzi ya njira ziŵirizi. (Yerekezerani ndi Agalatiya 6:5.) Kumbukirani kuti, Yesu sananene chimene wa mu ukwati wopanda liwongo ayenera kuchita. Pamenepo, nkwachionekere kuti Yehova samaipidwa ndi awo amene amasankha kusudzula pa zifukwa zoyenera za Malemba.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti mu nkhaniyi tidzatchula wa mu ukwati wopanda liwongoyo kukhala “mkazi,” mfundo zofotokozedwazo zimagwiranso ntchito pamene wopanda liwongoyo ali mwamuna Wachikristu.
b Mwa kuyambanso kugonana, mkazi wopanda liwongoyo adzakhala akusonyeza kuti wasankha kuyanjana ndi mwamuna wake wolakwayo. Motero iye adzathetsa chifukwa chilichonse cha Malemba cha chisudzulo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Life