MUTU 4
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro?
“Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani. Kondani gulu lonse la abale, opani Mulungu, lemekezani mfumu.”—1 PETULO 2:17.
1, 2. (a) Kodi tiyenera kumvera ulamuliro wa ndani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’mutuwu?
MULI mwana, mwina panali zinthu zina zimene makolo anu ankakuuzani kuti muchite koma inuyo simunkafuna. Munkakonda makolo anuwo, ndipo munkadziwa kuti muyenera kuwamvera. Komabe mwina nthawi zina simunkafuna kuwamvera.
2 Tikudziwa kuti Yehova, yemwe ndi Atate wathu, amatikonda. Iye amatisamalira ndipo nthawi zonse amatipatsa zofunika kuti tizisangalala ndi moyo. Amatipatsanso malangizo kuti zinthu zizitiyendera bwino ndipo nthawi zina amagwiritsa ntchito anthu kuti atipatse malangizowo. Anthufe tiyenera kumvera ulamuliro wa Yehova. (Miyambo 24:21) Koma kodi n’chifukwa chiyani nthawi zina zimakhala zovuta kulemekeza ulamuliro? Nanga n’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizimvera anthu audindo? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekezera ulamuliro wa Yehova?—Onani Mawu Akumapeto 9.
N’CHIFUKWA CHIYANI ZIMAKHALA ZOVUTA KULEMEKEZA ULAMULIRO?
3, 4. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti anthu akhale ochimwa? (b) N’chiyani chimachititsa kuti tizivutika kumvera ulamuliro?
3 Anthufe timabadwa ndi mtima wosafuna kumvera. Mtima umenewu unayamba pamene Adamu ndi Hava anachimwa. Ngakhale kuti anthu awiri oyambirirawa analengedwa angwiro, iwo sanamvere ndipo anasonyeza kuti sankafuna kuti Mulungu aziwalamulira. Kungoyambira nthawi imeneyo, munthu aliyense amabadwa wochimwa. Chifukwa cha zimenezi timavutika kumvera ulamuliro wa Yehova komanso anthu audindo. Chinanso chimene chimapangitsa kuti anthufe tizivutika kumvera ulamuliro ndi chakuti anthu amene Yehova amawagwiritsa ntchito kuti azititsogolera nawonso si angwiro.—Genesis 2:15-17; 3:1-7; Salimo 51:5; Aroma 5:12.
4 Popeza anthufe si ife angwiro, n’zosavuta kuyamba kukhala ndi mtima wonyada. Munthu akakhala wonyada zimakhala zovuta kuti azitsatira malangizo. Mwachitsanzo, kale ku Isiraeli Yehova anasankha Mose kuti azitsogolera anthu ake. Koma munthu wina dzina lake Kora, yemwe anali atatumikira Yehova kwa nthawi yaitali, anayamba mtima wonyada ndipo anasiya kulemekeza Mose. Mose ankatsogolera anthu a Mulungu, koma sanali wonyada. Ndipotu Baibulo limati anali wodzichepetsa kwambiri kuposa aliyense pa nthawiyo. Koma Kora anakana kuti Mose azimutsogolera. Iye anachititsanso kuti anthu ambiri asiye kumvera Mose n’kukhala kumbali yake. Koma kodi Kora ndi anthu enawo zinawathera bwanji? Onse anaphedwa. (Numeri 12:3; 16:1-3, 31–35) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza kuti kunyada n’koopsa.—2 Mbiri 26:16-21; onani Mawu Akumapeto 10.
5. Fotokozani zitsanzo za anthu amene anagwiritsa ntchito mphamvu molakwika.
5 Nthawi zambiri munthu akakhala ndi udindo amayamba kuchita zinthu zosayenera. Kuyambira kale anthu akhala akugwiritsa ntchito udindo mosayenera. (Werengani Mlaliki 8:9.) Mwachitsanzo, pamene Yehova ankasankha Sauli kuti akhale mfumu ya Isiraeli, Sauliyo anali munthu wabwino kwambiri komanso wodzichepetsa. Koma kenako anayamba kunyada komanso nsanje. Izi zinapangitsa kuti azifuna kupha Davide ngakhale kuti Davideyo anali wosalakwa. (1 Samueli 9:20, 21; 10:20-22; 18:7-11) Patapita nthawi Davide anakhala mfumu ndipo anali mfumu yabwino kwambiri. Koma kenako nayenso anayamba kugwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika. Iye anagona ndi Batiseba yemwe anali mkazi wa Uriya ndipo pofuna kubisa tchimo lakeli anachititsa kuti Uriya aphedwe ku nkhondo.—2 Samueli 11:1-17.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KULEMEKEZA ULAMULIRO WA YEHOVA?
6, 7. (a) Kodi timachita chiyani chifukwa chokonda Yehova? (b) N’chiyani chingatithandize kuti tizimvera Yehova nthawi zonse?
6 Timalemekeza ulamuliro wa Yehova chifukwa chakuti timamukonda. Popeza timakonda Yehova kuposa chilichonse komanso aliyense, timafuna kumusangalatsa. (Werengani Miyambo 27:11; Maliko 12:29, 30.) Kuyambira kale mu Edeni, Satana amafuna kuti anthu aziganiza kuti Yehova salamulira bwino. Iye amafuna kuti tiziganiza kuti Yehova alibe ufulu wotiuza zoyenera kuchita. Koma zimenezi si zoona. Timaona kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona. Limati: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse.”—Chivumbulutso 4:11.
7 Muli mwana, munaphunzitsidwa kuti muzimvera makolo anu ngakhale pamene simukufuna. N’chimodzimodzinso ndi kumvera Yehova. Si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kuti tizimumvera. Koma popeza timamukonda komanso timamulemekeza, timayesetsa kuti tizimumvera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yesu. Iye ankamvera Yehova, ngakhale kuti nthawi zina kuchita zimenezi kunali kovuta kwambiri. N’chifukwa chake pa nthawi ina anauza Atate wake kuti: “Chifuniro chanu chichitike, osati changa.”—Luka 22:42; onani Mawu Akumapeto 11.
8. Kodi Yehova amatitsogolera bwanji? (Onani bokosi lakuti, “Muzimvera Malangizo.”)
8 Masiku ano Yehova amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana potitsogolera. Mwachitsanzo, anatipatsa Baibulo komanso akulu mumpingo. Timasonyeza kuti timalemekeza ulamuliro wa Yehova tikamamvera anthu amene akutitsogolera. Tikamakana kuwamvera ndiye kuti tikukana kuti Yehova azititsogolera. Pamene Aisiraeli anakana Mose, Yehova anaona kuti akukana iyeyo.—Numeri 14:26, 27; onani Mawu Akumapeto 12.
9. Kodi chikondi chingatithandize bwanji kuti tizimvera malangizo?
9 Tikamalemekeza ulamuliro timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu. Kuti timvetse mfundo imeneyi, taganizirani chitsanzo ichi: Pakachitika ngozi zadzidzidzi, anthu opereka thandizo amafunika kugwira ntchito mogwirizana kuti apulumutse anthu ambiri. Kuti zimenezi zitheke, pamafunika munthu wina wowatsogolera ndipo aliyense amafunika kutsatira malangizo. Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu wina sakutsatira malangizowo n’kumangochita zimene akufuna? Ngakhale zolinga zake zitakhala zabwino, zimene akuchitazo zikhoza kubweretsa mavuto kwa anzake. Mofanana ndi zimenezi, ngati sititsatira malangizo ochokera kwa Yehova komanso kwa anthu audindo, zingachititse kuti anthu ena akumane ndi mavuto. Koma tikamamvera Yehova timasonyeza kuti timamulemekeza komanso timakonda abale athu.—1 Akorinto 12:14, 25, 26.
10, 11. Kodi tikambirana chiyani?
10 Zilizonse zimene Yehova amatiuza kuti tizichita ndi zothandiza kwa ifeyo. Choncho, tikamalemekeza dongosolo limene Yehova anakhazikitsa m’banja, mumpingo komanso tikamalemekeza akuluakulu a boma zinthu zimayenda bwino.—Deuteronomo 5:16; Aroma 13:4; Aefeso 6:2, 3; Aheberi 13:17.
11 Tikamvetsa chifukwa chake Yehova amafuna kuti tizilemekeza anthu audindo, zingakhale zosavuta kuti tiziwalemekeza. Tiyeni tikambirane bwinobwino zimene tingachite posonyeza kuti timalemekeza dongosolo limene Yehova anakhazikitsa m’banja komanso mumpingo. Tikambirananso zimene tingachite posonyeza kuti timalemekeza akuluakulu a boma.
TIZILEMEKEZA DONGOSOLO LIMENE YEHOVA ANAKHAZIKITSA M’BANJA
12. Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amalemekeza ulamuliro wa Yehova?
12 Yehova ndi amene anayambitsa banja ndipo aliyense anam’patsa udindo wake. Aliyense akamakwaniritsa udindo wake, banja limayenda bwino ndipo onse amasangalala. (1 Akorinto 14:33) Yehova anakonza zoti mwamuna akhale mutu wa banja. Izi zikusonyeza kuti amafuna kuti mwamuna azisamalira ndiponso kutsogolera banja lake mwachikondi. Mwamuna adzayankha kwa Yehova mmene amasamalirira banja lake. Mwamuna wachikhristu ayenera kukhala wokoma mtima komanso wachikondi pochita zinthu ndi banja lake ngati mmene Yesu amachitira ndi mpingo. Akamachita zimenezi amasonyeza kuti amalemekeza Yehova.—Aefeso 5:23; onani Mawu Akumapeto 13.
13. Kodi mkazi angakwaniritse bwanji udindo wake m’banja?
13 Nayenso mkazi ali ndi udindo wofunika kwambiri m’banja. Iye amathandiza mwamuna wake kuti akhale mutu wa banja wabwino. Komanso amathandizana ndi mwamuna wakeyo kuphunzitsa bwino ana. Chitsanzo chake chabwino chimathandiza kuti ana ake azilemekeza bambo awo. (Miyambo 1:8) Mkazi wabwino amalemekeza mwamuna wake komanso amathandiza kuti zimene mwamunayo wasankha ziyende bwino. Akakhala kuti sakugwirizana ndi zinazake, amafotokoza maganizo ake mokoma mtima komanso mwaulemu. Ngati mkazi wachikhristu ali pa banja ndi mwamuna yemwe si wa Mboni amakumana ndi mavuto ambiri. Koma ayenera kupitirizabe kukonda mwamuna wakeyo komanso kumulemekeza. Izi zingathandize kuti tsiku lina mwamunayo adzayambe kulambira Yehova.—Werengani 1 Petulo 3:1.
14. Kodi ana angasonyeze bwanji kuti amalemekeza Yehova?
14 Yehova amaona kuti ana ndi a mtengo wapatali ndipo amafunika kuwateteza komanso kuwatsogolera. Makolo amasangalala ana awo akamawamvera. Ana akamamvera, amasonyeza kuti amalemekeza Yehova ndipo Yehovayo amasangalala. (Miyambo 10:1) Pali mabanja ambiri amene ana amaleredwa ndi mayi kapena bambo okha. Izi zingakhale zovuta kwa makolowo komanso anawo. Koma anawo akakhala omvera zinthu zimayendako bwino. Komabe banja lililonse limakumana ndi mavuto. Koma aliyense m’banja akamatsatira malangizo a Yehova, banjalo limakhala losangalala. Zikatere, Yehova amalemekezeka chifukwa ndi amene anayambitsa banja.—Aefeso 3:14, 15.
TIZILEMEKEZA DONGOSOLO LIMENE YEHOVA ANAKHAZIKITSA MUMPINGO
15. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza dongosolo limene Yehova anakhazikitsa mumpingo?
15 Yehova amatitsogolera pogwiritsa ntchito mpingo wachikhristu ndipo anapatsa Yesu udindo woyang’anira mpingo. (Akolose 1:13) Nayenso Yesu anapatsa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” udindo woti azisamalira anthu a Mulungu padzikoli. (Mateyu 24:45-47) Masiku ano, Bungwe Lolamulira ndi limene lili “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Bungwe Lolamulira limatipatsa chakudya pa nthawi yoyenera kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Padziko lonse, akulu ndi atumiki othandiza komanso oyang’anira madera amathandiza mpingo ndipo amalandira malangizo kuchokera ku Bungwe Lolamulira. Abale onsewa ali ndi udindo wotisamalira ndipo amayankha kwa Yehova mmene amachitira ndi udindo wawowu. Choncho tikamalemekeza abale amenewa, ndiye kuti tikulemekeza Yehova.—Werengani 1 Atesalonika 5:12; Aheberi 13:17; onani Mawu Akumapeto 14.
16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti akulu ndi atumiki othandiza amasankhidwa ndi mzimu woyera?
16 Akulu ndi atumiki othandiza amathandiza kuti anthu a mumpingo azikhala okhulupirika komanso ogwirizana. Komabe mofanana ndi ifeyo, abale amenewa si angwiro. Koma kodi amasankhidwa bwanji? Abale amenewa amayenera kukwaniritsa zimene Malemba amanena. (1 Timoteyo 3:1-7, 12; Tito 1:5-9) Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera pothandiza anthu amene analemba Baibulo kuti afotokoze zimene m’bale ayenera kuchita kuti ayenerere udindo. Komanso akulu akafuna kusankha mtumiki wothandiza kapena mkulu, amapempha Yehova kuti awapatse mzimu woyera kuti uwathandize. Choncho Yehova ndi Yesu ndi amene amatsogolera mipingo. (Machitidwe 20:28) Abale amene anaikidwa kuti azitithandiza komanso kutisamalira, ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.—Aefeso 4:8.
17. Kodi nthawi zina mlongo angafunike kutani posonyeza kuti amalemekeza dongosolo limene Yehova anakhazikitsa?
17 Nthawi zina sipangakhale mkulu kapena mtumiki wothandiza woti atsogolere zinazake pampingo. Zikatere, m’bale wina wobatizidwa angathandize. Koma ngati palibenso m’bale aliyense wobatizidwa, mlongo angatsogolere. Koma popeza akugwira ntchito imene imayenera kugwiridwa ndi m’bale, ayenera kuvala chinachake kumutu, kaya mpango kapena chipewa. (1 Akorinto 11:3-10) Zimenezi zimasonyeza kuti amalemekeza dongosolo limene Yehova anakhazikitsa m’banja komanso mumpingo.—Onani Mawu Akumapeto 15.
TIZILEMEKEZA AKULUAKULU A BOMA
18, 19. (a) Kodi tikuphunzira chiyani palemba la Aroma 13:1-7? (b) Tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza akuluakulu a boma?
18 Yehova walola kuti maboma azilamulira ndipo tiyenera kuwalemekeza. Mabomawa amakonza zoti pakhale mayiko komanso madera n’cholinga choti azigwira bwino ntchito yawo komanso azitha kupereka zinthu zofunika kwa nzika zawo. Akhristu amatsatira malangizo a pa Aroma 13:1-7. (Werengani.) Timalemekeza “olamulira akuluakulu” komanso timatsatira malamulo a m’dziko lathu kapena akudera limene tikukhala. Malamulowa angakhudze banja lathu, bizinezi yathu kapena katundu wathu. Mwachitsanzo, timalipira misonkho komanso boma likatiuza kuti tilembe mafomu kapena makalata alionse, timamvera ndiponso timayesetsa kulemba zoona zokhazokha. Koma kodi tingatani ngati a boma atiuza kuti tichite zosemphana ndi malamulo a Mulungu? Mtumwi Petulo ananena kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”—Machitidwe 5:28, 29.
19 Tiyeneranso kusonyeza ulemu tikamalankhula ndi akuluakulu a boma, monga oweruza milandu kapena apolisi. Nawonso achinyamata ayenera kulemekeza aphunzitsi awo komanso anthu ena ogwira ntchito kusukulu. Tikakhala kuntchito tizilemekeza mabwana athu ngakhale zitakhala kuti anthu ena sawalemekeza. Tikamachita zimenezi, timakhala kuti tikutsanzira mtumwi Paulo yemwe ankalemekeza akuluakulu a boma ngakhale kuti nthawi zina zinali zovuta. (Machitidwe 26:2, 25) Komanso kaya anthu akutichitira zabwino kapena ayi, timayesetsabe kukhala aulemu.—Werengani Aroma 12:17, 18; 1 Petulo 3:15.
20, 21. Tikamalemekeza ena, kodi zotsatira zake zimakhala zotani?
20 Padzikoli anthu ambiri salemekezana. Koma anthu a Yehovafe timayesetsa kuti tizilemekeza aliyense. Timatsatira malangizo a mtumwi Petulo akuti: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.” (1 Petulo 2:17) Tikamachita zinthu mwaulemu, anthu amadziwa kuti timawalemekeza. Yesu anati: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:16.
21 Tikamasonyeza ulemu m’banja, mumpingo komanso tikamalemekeza anthu ena onse, anthu ena angayambe kuphunzira za Yehova chifukwa choona chitsanzo chathu chabwino. Tikamalemekeza ena, timasonyeza kuti timalemekeza Yehova komanso timamukonda. Ndipo zimenezi zimasangalatsa Yehova.