Lipoti la Olengeza Ufumu
Anapeza Chifuno cha Moyo
YESU amati amadziŵa nkhosa zake. (Yohane 10:14) Ngati munthu ali ndi mtima wabwino ndipo amakonda mtendere ndi chilungamo, ameneyo adzakopeka ndi otsatira a Yesu. Munthu woteroyo adzapeza chifuno cha moyo, monga momwe anachitira mkazi wina m’Belgium. Nayi nkhani yake:
“Pamene Mboni za Yehova zinagogoda pakhomo panga, ndinali wopsinjika maganizo kwambiri moti ndinali kulingalira za kudzipha. Ndinakonda zimene Mboni zinanena ponena za chothetsera mavuto a dziko lodwalali koma sindinakonde kumva kuti Mulungu adzakhala ndi mbali m’kuchita chimenecho. Ndinali nditaleka kupita kutchalitchi kwa zaka zisanu ndi zitatu, chifukwa chakuti ndinanyansidwa ndi chinyengo chimene ndinawona kumeneko. Komabe kwa Mbonizo, ndinawona mbali zina za chowonadi mwa zimene zinanena ndipo ndinazindikira kuti, ndiiko komwe, nkovuta kukhala ndi moyo wopanda Mulungu.
“Mwachisoni, pambuyo pa maulendo awo angapo, ndinaleka kuwonana ndi Mboni. Ndinamva kukhala wothedwa nzeru. Ndinkasuta mapaketi aŵiri andudu patsiku ndipo ndinayamba ngakhale kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa. Pofuna kulankhulana ndi agogo anga aamuna akufa, ndinadziloŵetsa m’kukhulupirira mizimu. Ndinkachita mantha chotani nanga pamene ndinkavutisidwa ndi ziŵanda usiku ndili ndekha! Zimenezi zinapitiriza kwa miyezi yambiri. Madzulo aliwonse ndinkachita mantha polingalira kuti ndinali ndekha.
“Ndiyeno, tsiku lina ndinakawongola miyendo, ndikumadzera ndi njira ina yosakhala ya masiku onse, ndipo ndinafika pamalo amene anali kumangidwapo chinyumba chachikulu. Ndinadabwa kuwona gulu lalikulu la anthu pamenepo. Nditafika pafupi, ndinawona kuti zinali Mboni za Yehova zikumanga Nyumba Yaufumu. Ndinakumbukira maulendo amene Mboni zinafika panyumba panga, ndipo ndinalingalira kuti dziko likhoza kukhala labwino chotani nanga ngati anthu onse anakhala ngati amenewa.
“Ndinakhumbadi kuti Mbonizo zibwerenso kunyumba kwanga, motero ndinalankhula kwa ena ogwira ntchito panyumbapo. Ndinapemphera kwa Mulungu, ndipo patapita masiku khumi mwamuna amene ankandifikira poyamba anafikanso pakhomo panga. Iye anati tipitirize phunziro lathu la Baibulo, ndipo ndinavomera mwachisangalalo. Panthaŵi yomweyo anandiitanira kumisonkhano ku Nyumba Yaufumu. Ndinavomera. Sindinawonepo zimene ndinawona kumeneko! Ndinafunafuna kwanthaŵi yaitali anthu amene amakondana ndi achimwemwe. Ndipo tsopano ndinawapeza!
“Kuchokera pamenepo ndinapita kumisonkhano yonse. Patapita pafupifupi milungu itatu, ndinaleka chizoloŵezi choipa cha kusuta. Ndinataya mabuku a kukhulupirira nyenyezi ndi marekodi anga anyimbo zausatana, ndipo ndinali kumva kuti ziŵanda zinali kundisiya. Ndinagwirizanitsa moyo wanga ndi miyezo ya Yehova ya m’Baibulo, ndipo patapita miyezi itatu ndinayamba kulalikira mbiri yabwino. Pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi ndinabatizidwa. Masiku aŵiri nditabatizidwa, ndinayamba upainiya wothandiza.
“Ndimayamikira Yehova pazabwino zonse zimene wandichitira. Moyo wanga tsopano uli ndi chifuno. Inde, dzina la Yehova ndilo linga lolimba m’limene ndinapeza chisungiko ndi chitetezo. (Miyambo 18:10) Ndimamvadi mofanana ndi wamasalmo pamene analemba Salmo 84:10 kuti: ‘Pakuti tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa.’”
Mkazi wamtima wofatsa ameneyu anapeza chifuno cha moyo. Akhozanso kutero aliyense amene afunafuna Yehova ndi mtima wabwino.