Mutu 34
Chinsinsi Chochititsa Mantha Chinaululika
1. (a) Kodi Yohane anachita chiyani ataona hule lalikulu lija litakwera pachilombo chochititsa mantha, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezo? (b) Kodi Akhristu odzozedwa masiku ano amachita chiyani akaona zinthu zokwaniritsa masomphenya aulosiwa zikuchitika?
KODI Yohane anachita chiyani ataona hule lalikulu lija komanso chilombo chochititsa mantha chimene linakwera? Iye akuyankha kuti: “Nditamuona mkaziyo, ndinadabwa kwambiri.” (Chivumbulutso 17:6b) Zimene Yohane anaonazi zinali zodabwitsa kwambiri moti munthu sakanatha kuziganizira. Komabe Baibulo likusonyeza kuti n’zimene zinachitika. Yohane anaona hule la makhalidwe oipali litakwera pachilombo choopsa chofiira kwambiri m’chipululu. (Chivumbulutso 17:3) Akhristu odzozedwa masiku ano nawonso akudabwa kwambiri pamene zinthu zokwaniritsa masomphenya amenewa zikuchitika. Anthu m’dzikoli akanaona zimenezi nawonso akananena kuti ‘N’zodabwitsa!’ ndipo olamulira m’dzikoli nawonso akanadabwa n’kunena kuti ‘Zatheka bwanji zimenezi?’ Koma masomphenyawa akukwaniritsidwa mochititsa chidwi kwambiri masiku ano. Anthu a Mulungu agwira kale ntchito yaikulu imene yathandiza kukwaniritsa masomphenyawa. Zimenezi zikuwatsimikizira kuti posachedwapa masomphenyawa akwaniritsidwa onse.
2. (a) Kodi mngelo uja anamuuza chiyani Yohane, ataona kuti akudabwa? (b) Kodi n’chiyani chaululidwa kwa Akhristu odzozedwa, ndipo zimenezi zachitika motani?
2 Mngelo uja anaona kuti Yohane akudabwa kwambiri. Yohane akupitiriza kufotokoza kuti: “Koma mngelo uja anandifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani ukudabwa? Ndikuuza chinsinsi cha mkazi ameneyu, ndi cha chilombo chimene wakwerapo, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10.’” (Chivumbulutso 17:7) Tsopano mngelo uja anali atatsala pang’ono kuulula chinsinsi. Iye anafotokozera Yohane, amene anali wodabwa kwambiri, mbali zosiyanasiyana za masomphenyawo komanso zinthu zochititsa chidwi zimene zinali pafupi kuchitika. Mofanana ndi zimenezi, Akhristu odzozedwa nawonso akuthandizidwa kumvetsa maulosi masiku ano. Izi zili choncho chifukwa chakuti Akhristu odzozedwawa ali tcheru pamene akugwira ntchito yawo motsogoleredwa ndi angelo. M’mbuyomu, Yosefe anali wokhulupirika ndipo ankakhulupirira kuti ‘Mulungu ndiye amamasulira maloto’ kapena masomphenya. Mofanana ndi mtumiki ameneyu, ifenso timakhulupirira zimenezi. (Genesis 40:8; yerekezerani ndi Danieli 2:29, 30.) Anthu a Mulungu ali pamalo abwino kwambiri owathandiza kumvetsa bwino zinthu, chifukwa Yehova akuwauza tanthauzo la masomphenyawo ndiponso akuwafotokozera mmene akukhudzira moyo wawo. (Salimo 25:14) Pa nthawi yoyenera, iye anathandiza atumiki akewo kumvetsa tanthauzo la chinsinsi chimenechi, cha mkazi ndi chilombo.—Salimo 32:8.
3, 4. (a) Kodi N. H. Knorr anakamba nkhani ya onse ya mutu wotani mu 1942, ndipo m’nkhaniyo anafotokoza kuti chilombo chofiira kwambiri chikuimira chiyani? (b) Kodi M’bale Knorr anafotokozera mawu ati amene mngelo anauza Yohane?
3 Kuyambira pa September 18 mpaka 20, 1942, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itafika pachimake, Mboni za Yehova ku United States zinachita msonkhano waukulu wa mutu wakuti “Dziko Latsopano Lolamulidwa ndi Mulungu.” Msonkhanowu unachitikira ku Cleveland, m’chigawo cha Ohio, ndipo anthu m’mizinda ina yoposa 50 anamvetsera msonkhanowu, umene unalumikizidwa pa telefoni. Choncho anthu onse amene anamvetsera msonkhanowu analipo okwana 129,699. Msonkhanowu unachitikanso m’malo ena padziko lonse lapansi kumene akanatha kutero ngakhale kuti inali nthawi ya nkhondo. Pa nthawiyo, anthu ambiri a Yehova ankayembekezera kuti pamapeto pa nkhondoyo payambika nkhondo ya Mulungu ya Aramagedo. Chotero iwo anali ndi chidwi kwambiri ndi nkhani ya onse imene inakambidwa pamsonkhanowo, ya mutu wakuti, “Kodi Padzikoli Padzakhala Mtendere?” Anthu ankadzifunsa kuti n’chifukwa chiyani N. H. Knorr, pulezidenti watsopano wa bungwe la Watch Tower Society, ankalankhula za mtendere pamene zochitika za padzikoli zinkasonyezeratu kuti mitundu ya anthu singakhale pa mtendere?a Chifukwa chake chinali chakuti Akhristu odzozedwa anali ‘kuganizira mozama, kuposa nthawi zonse,’ Mawu a Mulungu aulosi.—Aheberi 2:1; 2 Petulo 1:19.
4 Kodi nkhani yakuti “Kodi Padzikoli Padzakhala Mtendere?” inathandiza bwanji anthu kumvetsa ulosi wa m’buku la Chivumbulutso? M’bale N. H. Knorr anafotokoza momveka bwino kuti chilombo chofiira kwambiri chotchulidwa pa Chivumbulutso 17:3 chikuimira bungwe la League of Nations. Iye anafotokozanso kuti bungwe limeneli zinthu sizidzaliyendera bwino kwenikweni, mogwirizana ndi mawu otsatira amene mngelo uja anauza Yohane, akuti: “Chilombo chimene waona, chinalipo, tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho, ndipo chidzapita ku chiwonongeko.”—Chivumbulutso 17:8a.
5. (a) Kodi mawu akuti ‘chilombo chija chinalipo’ koma “tsopano palibe” anakwaniritsidwa bwanji? (b) Kodi N. H. Knorr anayankha bwanji funso lakuti, “Kodi bungwe la League of Nations likhala kuphompho mpaka kalekale?”
5 ‘Chilombo chija chinalipo,’ kutanthauza bungwe la League of Nations limene linakhazikitsidwa pa January 10, 1920, ndipo mayiko amene anakhalapo m’bungweli anali okwana 63. Koma motsatizanatsatizana, mayiko a Japan, Germany ndi Italy anachoka m’bungweli ndiponso dziko limene kale linkatchedwa Soviet Union linachotsedwamo. Mu September 1939, wolamulira wankhanza wa chipani cha Nazi ku Germany anayambitsa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse.b Bungwe la League of Nations linalephera kukhazikitsa mtendere padziko lapansi. Choncho linatha ntchito moti linangokhala ngati laponyedwa kuphompho. Pofika mu 1942 bungweli linali lisakugwiranso ntchito. Pa nthawi yoyenerera imeneyi, osati pa nthawi ya m’mbuyo kapena pa nthawi ina yake m’tsogolo, Yehova anaululira anthu ake tanthauzo lonse la masomphenyawa. Pamsonkhano wakuti “Dziko Latsopano Lolamulidwa ndi Mulungu,” N. H. Knorr ananena mogwirizana ndi ulosi umenewu kuti ‘chilombo chija tsopano palibe.’ Kenako iye anafunsa kuti, “Kodi bungwe la League of Nations likhala kuphompho mpaka kalekale?” Poyankha, iye anagwira mawu a pa Chivumbulutso 17:8, ndipo anati: “Bungwe loimira mgwirizano wa mayiko lidzayambiranso.” Zimenezi zinachitikadi, ndipo zinasonyeza kuti Mawu a ulosi a Yehova ndi oona.
Chinatuluka Kuphompho
6. (a) Kodi chilombo chofiira kwambiri chija chinatuluka liti kuphompho, ndipo chinatuluka ndi dzina latsopano liti? (b) N’chifukwa chiyani tikunena kuti bungwe la United Nations likuimira chilombo chofiira kwambiri chimene chinatuluka kuphompho?
6 Chilombo chofiira kwambiri chija chinatulukadi kuphompho. Pa June 26, 1945, mayiko 50 anagwirizana kuti avomereze chigamulo chokhazikitsira bungwe la United Nations. Mayikowa anagwirizana zimenezi ku San Francisco, m’dziko la United States pa mwambo umene panali chisangalalo chachikulu kwambiri. Cholinga cha bungwe latsopanoli chinali “kukhazikitsa bata ndi mtendere padziko lonse.” Bungwe la United Nations linkafanana kwambiri ndi bungwe la League of Nations. Buku lina linati: “Bungwe la United Nations (UN) limafanana m’njira zina ndi bungwe la League of Nations, limene linakhazikitsidwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha . . . Mwachitsanzo, mayiko ambiri amene anayambitsa nawo bungwe la UN ndi amenenso anayambitsa bungwe la League of Nations. Mofanana ndi bungwe la League of Nations, bungwe la UN linakhazikitsidwa kuti lithandize kukhazikitsa mtendere pakati pa mayiko. Ndipo nthambi zikuluzikulu za UN n’zofanana ndi za League of Nations.” (The World Book Encyclopedia) Choncho bungwe la UN likuimira chilombo chofiira kwambiri chimene chinatuluka kuphompho. M’bungweli muli mayiko pafupifupi 192 ndipo akuposa mayiko 63 amene anali mu League of Nations. Komanso bungweli limagwira ntchito zambiri kuposa bungwe la League of Nations.
7. (a) Kodi anthu okhala padziko lapansi achita chiyani podabwa ndi chilombo chofiira kwambiri chimene chinatuluka kuphompho chija ndiponso pochigomera? (b) Kodi bungwe la UN lalephera kukwaniritsa cholinga chiti, ndipo yemwe anali mlembi wamkulu wa bungweli anati chiyani pa mfundo imeneyi?
7 Poyamba, anthu ankayembekezera kuti bungwe la UN liwathandiza kwambiri. Zimenezi zinakwaniritsa mawu amene mngelo uja ananena, akuti: “Anthu okhala padziko lapansi akaona kuti chilombocho chinalipo, tsopano palibe, komabe chidzakhalapo, adzadabwa kwambiri [pochigomera]. Koma mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Chivumbulutso 17:8b) Anthu okhala padziko lapansi amagomera bungwe latsopanoli, limene likulu lake lili m’chinyumba chachikulu mumzinda wa New York, pafupi ndi mtsinje wa East. Koma bungwe la UN lalephera kukhazikitsa bata ndi mtendere weniweni padziko lapansi. M’zaka zambiri za m’ma 1900, mtendere umene unali padzikoli unangokhalapo chifukwa chakuti mayiko amene ali ndi zida za nyukiliya ankaopana, podziwa kuti ngati dziko limodzi litayambitsa nkhondo ya nyukiliya ndiye kuti dziko lonse lapansi likhoza kuwonongekeratu. Panopa mayiko akupitirizabe mpikisano wawo wopanga zida zankhondo zoopsa. Mu 1985, bungweli litayesetsa kwa zaka pafupifupi 40 kuti likhazikitse mtendere, Javier Pérez de Cuéllar amene pa nthawiyo anali mlembi wamkulu wa bungweli, anati: “Tikukhala m’nthawi imene kuli anthu ochita zinthu monyanyira komanso zigawenga zambiri, ndipo sitikudziwa chochita.”
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani bungwe la UN silingathe kuthetsa mavuto a anthu, ndipo mogwirizana ndi mawu a Mulungu, kodi n’chiyani chidzachitikire bungwe limeneli posachedwapa? (b) N’chifukwa chiyani anthu amene anayambitsa bungwe la UN ndiponso anthu amene amagomera bungweli mayina awo sanalembedwe “mumpukutu wa moyo” wa Mulungu? (c) Kodi Ufumu wa Yehova udzakwanitsa kuchita chiyani?
8 Bungwe la UN silingathetse mavuto a anthu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amene anapereka moyo kwa anthu onse si amene anakhazikitsa bungwe la UN. Bungweli silidzakhalitsa, chifukwa Mawu a Mulungu akuti, ‘lidzapita ku chiwonongeko.’ Mayina a anthu amene anayambitsa bungwe la UN komanso anthu amene amaligomera aja sanalembedwe mumpukutu wa moyo wa Mulungu. N’zosatheka kuti anthu ochimwa, amenenso amafa ndipo amanyoza dzina la Mulungu, akwaniritse zolinga za Yehova Mulungu pogwiritsa ntchito bungwe la UN. Izi zili choncho chifukwa Mulungu ananena kuti adzakwaniritsa zolinga zimenezo kudzera mu Ufumu wa Khristu, osati kudzera mwa anthu.—Danieli 7:27; Chivumbulutso 11:15.
9 N’kunyoza Mulungu komanso si zoona kunena kuti bungwe la UN likulowa m’malo mwa Ufumu wa Mulungu. Wolamulira wa ufumu umenewu ndi Yesu Khristu, yemwe ndi Mesiya komanso Kalonga wa Mtendere, ndipo ufumu wakewo sudzatha. (Yesaya 9:6, 7) Ngakhale bungwe la UN litakhazikitsa mtendere kwa kanthawi, nkhondo zikhoza kuyambiranso pasanapite nthawi yaitali. Izi n’zimene anthu ochimwa amakonda kuchita ndipo “mayina awo sanalembedwe mumpukutu wa moyo kuyambira pa kukhazikitsidwa kwa dziko.” Ufumu wa Yehova umene wolamulira wake ndi Khristu ndi umene udzabweretse mtendere wosatha padziko lapansi. Komanso nsembe ya dipo ya Yesu idzathandiza kuti Mulungu aukitse anthu akufa amene akuwakumbukira, olungama ndi osalungama omwe. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Amene adzaukitsidwe ndi anthu onse amene akhala okhulupirikabe ngakhale pamene Satana ndi mbewu yake anali kuwaukira, komanso ena amene adzayambe kumvera Mulungu m’tsogolo muno. N’zachidziwikire kuti mumpukutu wa moyo wa Mulungu simudzakhala mayina a anthu amene amaumirira kwambiri ku Babulo Wamkulu komanso anthu amene akupitiriza kulambira chilombo.—Ekisodo 32:33; Salimo 86:8-10; Yohane 17:3; Chivumbulutso 16:2; 17:5.
Bungweli Silidzabweretsa Bata ndi Mtendere
10, 11. (a) Kodi bungwe la UN linalengeza chiyani mu 1986, ndipo zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi ndi magulu angati a zipembedzo amene anasonkhana ku Assisi, m’dziko la Italy kuti apempherere mtendere, ndipo kodi Mulungu amamva mapemphero otero? Fotokozani.
10 Pofuna kuti anthu akhale ndi chiyembekezo chachikulu, bungwe la United Nations linalengeza kuti chaka cha 1986 chinali “Chaka cha Mtendere Padziko Lonse,” ndipo mutu waukulu umene bungweli linkayendera m’chakachi unali wakuti, “Kuteteza Mtendere Ndiponso Tsogolo la Anthu.” Mayiko amene anali pa nkhondo anapemphedwa kuti asiye kaye kumenyana, ngakhale kwa chaka chimodzi chokha. Kodi iwo anatani? Bungwe lina lochita kafukufuku pa nkhani zokhazikitsa mtendere padziko lonse (International Peace Research Institute) linanena kuti anthu 5 miliyoni anaphedwa pa nkhondo m’chaka cha 1986 chokha. Ngakhale kuti mayiko ena anapanga ndalama zapadera zachitsulo komanso masitampa apadera pokondwerera chakachi, mayiko ambiri sanachite chilichonse pofuna kulimbikitsa mtendere m’chaka chimenechi. Komabe, zipembedzo za m’dzikoli, zimene nthawi zonse zimafuna kuti zizikondedwa ndi bungwe la UN, zinalengeza za chaka chimenechi m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, pa January 1, 1986, Papa Yohane Paulo Wachiwiri anayamikira kwambiri ntchito ya bungwe la UN ndipo ananena kuti akufuna kuti chaka chatsopanocho chikhale cha mtendere. Ndipo pa October 27 m’chakachi, iye anasonkhanitsa atsogoleri a zipembedzo zambiri za m’dzikoli ku Assisi, m’dziko la Italy kuti akapempherere mtendere.
11 Kodi Mulungu amayankha mapemphero opempherera mtendere ngati amenewo? Kuti tiyankhe funso limeneli, tifunika kudziwa kaye kuti atsogoleri amenewo ankapemphera kwa Mulungu wake uti. Ngati mukanawafunsa, gulu lililonse likanapereka yankho losiyana ndi linzake. Kodi pali milungu mamiliyoni ambirimbiri imene ingamve ndi kuyankha mapemphero operekedwa m’njira zosiyanasiyana? Anthu ambiri amene anali kumapemphero amenewa amalambira mulungu amene Matchalitchi Achikhristu amakhulupirira kuti ndi milungu itatu mwa Mulungu mmodzi.c Abuda, Ahindu ndi zipembedzo zina ankapemphera mobwerezabwereza kwa milungu yosawerengeka. Pamsonkhanowu panali magulu 12 a zipembedzo zimene zinaimiridwa ndi atsogoleri otchuka monga Bishopu Wamkulu wa Angilikani wa ku Canterbury, mtsogoleri wa Abuda wotchedwa Dalai Lama, mtsogoleri wa tchalitchi cha Orthodox cha ku Russia, mtsogoleri wa gulu la chipembedzo cha Chishinto ku Tokyo, atsogoleri a zipembedzo zamakolo za ku Africa, komanso amwenye awiri a ku America amene anavala zipewa zokhala ndi nthenga. Atsogoleri amenewa anavala zovala zowala za mitundu yosiyanasiyana zimene zinkaoneka bwino kwambiri pa TV. Pa nthawi inayake, gulu limodzi linapemphera mosalekeza kwa maola 12. (Yerekezerani ndi Luka 20:45-47.) Koma kodi Mulungu anamvadi mapemphero amenewo, kapena anangothera m’mitambo imene inalipo tsiku limenelo? Mulungu sanamve mapemphero amenewo pa zifukwa zotsatirazi:
12. N’chifukwa chiyani Mulungu sanayankhe mapemphero opempherera mtendere a atsogoleri a zipembedzo za m’dzikoli?
12 Mosiyana ndi anthu amene ‘akuyenda m’dzina la Yehova,’ pa atsogoleri onse achipembedzo amene anali pamsonkhanowo panalibe ngakhale mmodzi amene ankapemphera kwa Yehova, Mulungu wamoyo, amene dzina lake likupezeka nthawi zoposa 7,000 m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. (Mika 4:5; Yesaya 42:8, 12)d Monga gulu, iwo sankapemphera kwa Mulungu m’dzina la Yesu, ndipo ambiri mwa iwo sankakhulupirira n’komwe Yesu Khristu. (Yohane 14:13; 15:16) Pakati pawo panalibe chipembedzo ngakhale chimodzi chimene chinkachita chifuniro cha Mulungu, chomwe ndi kulalikira padziko lonse kuti Ufumu wa Mulungu umene ukubwerawo ndi womwe udzathetse mavuto a anthu, osati bungwe la UN. (Mateyu 7:21-23; 24:14; Maliko 13:10) Zipembedzo zawo zambiri zakhala zikulowerera pa nkhondo zoopsa m’mbiri ya anthu, kuphatikizapo nkhondo ziwiri zapadziko lonse zomwe zachitika m’zaka za m’ma 1900. Choncho Mulungu akuuza zipembedzo zimenezi kuti: “Ngakhale mupereke mapemphero ambiri, ine sindimvetsera. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.”—Yesaya 1:15; 59:1-3.
13. (a) N’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti atsogoleri a zipembedzo za m’dzikoli akugwirizana ndi bungwe la UN polimbikitsa mtendere? (b) Kodi pamapeto pa mawu amene anthu akunena, akuti “kuli mtendere,” padzachitika chiyani pokwaniritsa Mawu a Mulungu aulosi?
13 N’zochititsa chidwi kuti atsogoleri a zipembedzo za m’dzikoli akugwirizana ndi bungwe la United Nations pa nthawi ino polimbikitsa mayiko kuti akhazikitse mtendere. Atsogoleri a zipembedzowa akufuna kugwiritsa ntchito bungwe la UN kuti zinthu ziwayendere bwino, makamaka masiku ano pamene anthu ambiri akuchoka m’zipembedzo zawozo. Mofanana ndi atsogoleri osakhulupirika a mu Isiraeli wakale, iwo akufuula kuti, “‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.” (Yeremiya 6:14) N’zodziwikiratu kuti iwo adzapitiriza kunena kuti kuli mtendere, ndipo pamapeto pake zimenezi zidzakwaniritsa ulosi wa mtumwi Paulo wakuti: “Tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku. Pamene azidzati: ‘Bata ndi mtendere!’ chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati, ndipo sadzapulumuka.”—1 Atesalonika 5:2, 3.
14. Kodi mawu akuti “Bata ndi mtendere!” anganenedwe mwanjira yotani ndipo tingapewe bwanji kupusitsidwa?
14 M’zaka zaposachedwapa, andale akhala akugwiritsa ntchito mawu akuti “bata ndi mtendere” pofotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene iwo akuchita pofuna kukhazikitsa mtendere. Kodi zinthu zimenezo, zimene atsogoleri am’dzikoli akuchita, zikusonyeza kuti lemba la 1 Atesalonika 5:3 layamba kukwaniritsidwa? Kapena kodi Paulo ankatanthauza kuti padzachitika chinthu chinachake chapadera kwambiri chimene anthu padziko lonse adzachite nacho chidwi? Kawirikawiri timamvetsa bwino matanthauzo a maulosi a m’Baibulo pamene maulosiwo akwaniritsidwa, kapena ali mkati mokwaniritsidwa. Choncho tiyenera kuyembekezera kaye tisanadziwe mayankho a mafunso amenewa. Pakali pano, Akhristu akudziwa kuti ngakhale zitaoneka kuti mayiko akhazikitsadi bata ndi mtendere, kwenikweni palibe chimene chingasinthe. Anthu adzakhalabe odzikonda ndipo zinthu monga chidani, uchigawenga, kutha kwa mabanja, chiwerewere, matenda, chisoni komanso imfa zidzapitiriza kuchitika. Choncho kuti musapusitsike ndi mawu alionse onena za “bata ndi mtendere,” muyenera kukhala tcheru ndi kuzindikira tanthauzo la zochitika m’dzikoli komanso muyenera kumvera mawu ochenjeza opezeka m’maulosi a m’Mawu a Mulungu.—Maliko 13:32-37; Luka 21:34-36.
[Mawu a M’munsi]
a J. F. Rutherford anamwalira pa January 8, 1942, ndipo N. H. Knorr ndi amene anakhala pulezidenti wa bungwe la Watch Tower Society.
b Pa November 20, 1940, mayiko a Germany, Italy, Japan ndi Hungary anasainirana pangano loti akhazikitse bungwe la League of Nations latsopano. Patapita masiku anayi akuluakulu a Katolika ku Vatican anaulutsa pawailesi mwambo wa Misa ndiponso pemphero lopempherera kuti zipembedzo zibweretse mtendere ndi dongosolo latsopano lochitira zinthu. Koma bungwe latsopano limeneli silinapite patali.
c Chikhulupiriro chakuti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi chinachokera ku Babulo wakale kumene anthu ankalambira milungu imene inkakhala itatu nthawi zonse. Milungu imeneyi inali Shamashi mulungu wa dzuwa, Sini mulungu wa mwezi ndi Ishitara mulungu wa nyenyezi. Aiguputo nawonso ankachita zomwezi polambira Osirisi, Isisi ndi Horasi. Ndipo zithunzi za Ashuri, mulungu wamkulu wa Asuri, zimasonyeza kuti anali ndi mitu itatu. Potengera zimenezi, m’matchalitchi a Katolika mumapezeka zifaniziro za Mulungu wa mitu itatu.
d Potanthauzira mawu akuti Yehova Mulungu, buku lina lotanthauzira mawu limene linasindikizidwa mu 1993 linati, Yehova Mulungu ndi “Mulungu yekhayo amene Mboni za Yehova zimalambira ndi kuvomereza kuti ndiye Mulungu woona.”—Webster’s Third New International Dictionary.
[Bokosi patsamba 250]
Chaka Chimene Ankati ‘N’chamtendere’ Chinalibe Mtendere
Ngakhale kuti bungwe la UN linanena kuti chaka cha 1986 chikhale Chaka cha Mtendere Padziko Lonse, mayiko anapitiriza mpikisano wopanga zida zoopsa zankhondo. M’munsimu muli mfundo zochokera m’buku lina, zofunika kuziganizira mofatsa (World Military and Social Expenditures 1986):
Mu 1986 mayiko ndi mabugwe padziko lonse anagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 900,000 miliyoni pogula zida zankhondo, kulipira asilikali ndi kuchitira zinthu zina zokhudzana ndi nkhondo.
Ndalama zimene zinkagwiritsidwa ntchito pa ola limodzi padziko lonse pa zinthu zokhudzana ndi nkhondo, zinali zokwanira kupereka katemera kwa anthu mamiliyoni atatu ndi hafu amene ankafa chaka chilichonse chifukwa cha matenda amene akanatha kuwapewa.
Padziko lonse, munthu mmodzi mwa anthu asanu alionse anali pa umphawi wadzaoneni. Anthu onsewa, omwe ankavutika ndi njala, zikanatheka kuwadyetsa kwa chaka chimodzi pogwiritsa ntchito ndalama zimene mayiko padziko lonse ankawononga pa nkhondo kwa masiku awiri okha.
Mphamvu za mabomba a nyukiliya amene mayiko anali nawo zinali zowirikiza maulendo 160 miliyoni kuposa mphamvu zimene zinatuluka, fakitale yopanga magetsi a nyukiliya itaphulika ku Chernobyl.
Zikanatheka kuphulitsa bomba la nyukiliya lamphamvu kwambiri kuwirikiza maulendo 500 kuposa bomba limene linaphulitsidwa ku Hiroshima mu 1945.
Mabomba a nyukiliya amene mayiko ali nawo angawononge malo aakulu kuwirikiza maulendo 1 miliyoni kuposa mzinda wa Hiroshima. Mabomba amenewa ali ndi mphamvu zowirikiza maulendo 2,700 kuposa mabomba amene anagwiritsidwa ntchito pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse pamene anthu 38 miliyoni anafa.
Nkhondo zinkachitika pafupipafupi ndipo zinkakhala zoopsa kwambiri. Mwachitsanzo, anthu amene anafa pa nkhondo m’zaka za m’ma 1700 analipo 4.4 miliyoni, amene anafa m’zaka za m’ma 1800 analipo 8.3 miliyoni ndipo amene anafa m’zaka 86 zoyambirira za m’ma 1900 analipo 98.8 miliyoni. Kuchokera m’zaka za m’ma 1700, chiwerengero cha anthu amene akhala akufa pa nkhondo chawonjezereka mofulumira kwambiri kuwirikiza maulendo oposa 6, kuposa mmene chiwerengero cha anthu padziko lonse chikuwonjezekera. M’zaka za m’ma 1900, pa nkhondo iliyonse pankafa anthu ochuluka kuwirikiza maulendo 10 poyerekezera ndi anthu amene ankafa pa nkhondo iliyonse m’zaka za m’ma 1800.
[Zithunzi patsamba 247]
Mogwirizana ndi ulosi wonena za chilombo chofiira kwambiri, bungwe la League of Nations linaponyedwa kuphompho pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, koma kenako linatuluka kuphomphoko ndi dzina lakuti United Nations
[Zithunzi patsamba 249]
Pogwirizana ndi mfundo ya UN yakuti chaka cha 1986 chikhale “Chaka cha Mtendere,” atsogoleri oimira zipembedzo zosiyanasiyana za padziko lapansi anasonkhana ku Assisi, m’dziko la Italy n’kumapemphera, koma palibe aliyense wa iwo amene anapemphera kwa Yehova, Mulungu wamoyo