Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mboni zambiri za Yehova zimakumbukira tsiku lawo laukwati. Kukondwerera tsiku lakubadwa nchikumbutso cha tsiku lako lakubadwa. Choncho nkukondwereranji masiku aukwati koma osati akubadwa?
Kunena zoona, palibe kufunika kwakuti Mkristu azikondwerera zonse ziŵiri. Komabe, zimenezo sizikutanthauza kuti zinthu ziŵirizi zikufanana kapena kuti Akristu ayenera kuona zinazo (chikumbutso cha tsiku laukwati) mmene amaonera mapwando a masiku akubadwa.
Monga mwaonera, zonse ziŵiri ndi zikumbutso chifukwa chakuti “chikumbutso chapachaka [anniversary]” ndicho ‘kufikanso kwa pachaka kwa tsiku limene chinachake chinachitika.’ Chingakhale chikumbutso cha chochitika chilichonse—tsiku limene munachita ngozi yagalimoto, tsiku limene munaona mwezi utada, tsiku limene munapita kukasambira ndi a m’banja mwanu, ndi zina zotero. Nzachidziŵikire kuti Akristu samapanga “chikumbutso” chilichonse kukhala tsiku lapadera kapena kukhala ndi phwando polikumbukira. Munthu ayenera kuona kuti chochitikacho chikuloŵetsamo chiyani ndi kusankha kuti choyenera nchiti.
Mwachitsanzo, Mulungu analangiza Aisrayeli molunjika kuti chaka chilichonse azikondwerera tsiku limene mngelo wake anapitirira nyumba za Aisrayeli ku Igupto ndi kusamuka kwa anthu ake kumene kunatsatirapo mu 1513 B.C.E. (Eksodo 12:14) Pamene Ayuda, kuphatikizapo Yesu, anakumbukira chochitikacho chaka ndi chaka, anali kumvera malangizo a Mulungu, ndipo sanachite zimenezo mwa kukhala ndi phwando kapena kupatsana mphatso. Ayuda anaonanso kupatulidwanso kwa kachisi monga tsiku lachikumbutso chapadera. Ngakhale kuti Baibulo silinalamule kuti azikumbukira chochitika chachikulu m’mbiri chimenechi, Yohane 10:22, 23 akusonyeza kuti Yesu sanatsutse chikumbutsocho. Ndiponso, Akristu ali ndi msonkhano wapadera patsiku lokumbukira imfa ya Yesu. Ndithudi, amachita zimenezo pomvera lamulo lolunjika lopezeka m’Mawu a Mulungu.—Luka 22:19, 20.
Nanga bwanji za chikumbutso cha tsiku laukwati? M’maiko ena amuna ambiri ndi akazi awo amakumbukira tsiku limene anakwatirana, makonzedwe amene Mulungu anayambitsa. (Genesis 2:18-24; Mateyu 19:4-6) Tikudziŵa kuti Baibulo silimanena kuti ukwati ngwoipa. Yesu anapezeka paphwando laukwati ndi kuchitapo kanthu kuti chochitikacho chikhale chosangalatsa.—Yohane 2:1-11.
Choncho sizingakhale zachilendo ngati mwamuna ndi mkazi wake apatula nthaŵi patsiku lokumbukira ukwati wawo kuti akumbukire mmene anasangalalira tsikulo ndi kukumbukira chosankha chawo chogwirira ntchito pamodzi kuti zinthu ziyende bwino. Kaya akumbukira chochitika chosangalatsa chimenechi paokha, ali aŵiriŵiri, kapena akhala ndi achibale angapo kapena mabwenzi apafupi nchosankha chawo. Chochitikachi sichiyenera kukhala mpata wokhalira ndi phwando lalikulu. Patsikuli Akristu ayenera kutsogozedwa ndi mapulinsipulo amene amagwira ntchito masiku onse a moyo wawo. Choncho kaya munthu akumbukira kapena sakumbukira tsiku laukwati wake ndi nkhani yaumwini.—Aroma 13:13, 14.
Nangano bwanji za kukumbukira tsiku lakubadwa? Kodi Baibulo limanenapo kalikonse pa kukumbukira tsiku limeneli?
Eya, kuchiyambi kwa zaka za zana lino, Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo, ankasunga masiku akubadwa. Ochuluka a iwo anali ndi timabuku totchedwa Daily Heavenly Manna (Mana Akumwamba a Tsiku ndi Tsiku). M’timabukuti munali lemba la Baibulo la tsiku lililonse, ndipo Akristu ambiri anali kuikamo tizithunzi ta Ophunzira Baibulo anzawo pamasiku awo akubadwa. Ndiponso Nsanja ya Olonda yachingelezi ya February 15, 1909, inasimba kuti pamsonkhano waukulu ku Jacksonville, Florida, U.S.A., Mbale Russell, pulezidenti wa Sosaite panthaŵiyo anambweretsa papulatifomu. Chifukwa? Anapatsidwa mabokosi a zipatso za mpesa, zinanazi, ndi malalanje mosayembekezereka monga mphatso ya tsiku lake lakubadwa. Zimenezo zikutisonyeza zina zimene zinkachitika kale. Kuti mudziŵe chifukwa chake, kumbukirani kuti nthaŵiyo, Ophunzira Baibulo anali kusunganso December 25 monga tsiku lakubadwa kwa Yesu. Ndiponso unali mwambo kukhala ndi mgonero wa Krisimasi ku likulu ku Brooklyn.
Ndithudi, anthu a Mulungu akula mwauzimu pazinthu zambiri chiyambire pamenepo. M’ma 1920, kuwonjezeka kwa kuunika kwa choonadi kunatheketsa abale kuona zotsatirazi:
Yesu sanabadwe pa December 25, deti lochokera kuchipembedzo chachikunja. Baibulo limatilangiza kukumbukira tsiku la kufa kwa Yesu, osati tsiku la kubadwa kwake kapena kubadwa kwa munthu wina aliyense. Kuchita zimenezi nkogwirizana ndi Mlaliki 7:1 ndi choonadi chakuti chofunika kwambiri ndi chitsiriziro cha moyo wa munthu wokhulupirika osati kubadwa kwake. Baibulo silinenapo za mtumiki wokhulupirika aliyense amene anakondwerera tsiku lake lakubadwa. Ilo limanena za mapwando a masiku akubadwa a anthu akunja, likumasonyeza kuti pamapwandowo panachitika zinthu zankhanza. Tiyeni tione chiyambi cha zikumbutso zimenezo za masiku akubadwa.
Choyamba ndi chikumbutso cha tsiku lakubadwa la Farao wa m’tsiku la Yosefe. (Genesis 40:20-23) Pamenepa, nkhani yonena za mapwando a masiku akubadwa mu Encyclopædia of Religion and Ethics ya Hastings imayamba kuti: “Mwambo wokumbukira tsiku lakubadwa ngwogwirizana ndi kuŵerengera nthaŵi, ndipo, malinga ndi zochitika zake, ngwogwirizana ndi miyambo yakalekale yachipembedzo.” Kenako, insaikulopediyayo ikugwira mawu wodziŵa za mbiri ya Igupto Bwana J. Gardner Wilkinson, amene analemba kuti: “Mwaigupto aliyense ankaona tsiku, ndipo ngakhale ola la kubadwa kwake kukhala lofunika kwambiri; mwinanso monga momwe zinalili ku Perisiya, munthu aliyense anali kukumbukira tsiku lake lakubadwa pochita phwando lalikulu, kulandira mabwenzi ake ndi zosangalatsa zonse zakomweko, ndi zakudya zochuluka monyanyira.”
Phwando lina la tsiku lakubadwa lotchulidwa m’Baibulo ndi la Herode, pamene Yohane Mbatizi anadulidwa mutu. (Mateyu 14:6-10) The International Standard Bible Encyclopedia (ya mu 1979) ikufotokozapo kuti: “Agiriki amene anakhalako Chihelene chisanayambe anali kukondwerera masiku akubadwa a milungu ndi a anthu otchuka. Mawu achigiriki akuti genéthlia ankatanthauza mapwando ameneŵa, pamene mawu akuti genésia anatanthauza phwando lokumbukira tsiku lakubadwa la munthu wotchuka amene anamwalira. Pa 2 Amakabeo 6:7 tikupezapo nkhani yonena za genéthlia wa mwezi uliwonse wa Antiochus IV, pamene Ayuda anali kuwakakamiza ‘kudyako nsembe.’ . . . Pamene Herode anakondwerera tsiku lake lakubadwa, iye anali kutsatira mwambo wa Ahelene; palibe umboni wakuti Aisrayeli amene anakhalako Chihelene chisanayambe anakondwerera masiku akubadwa.”
Inde, Akristu oona lerolino samangodera nkhaŵa za chiyambi cha mwambo wina uliwonse ndi kugwirizana kwake ndi zachipembedzo kumene ungakhale nako, komanso samafuna kunyalanyaza maumboni oonekeratu amene ali m’Mawu a Mulungu. Zimenezi zikuphatikizapo mfundo yonena kuti zikondwerero za masiku akubadwa zokhazo zolembedwa m’Baibulo ndi za anthu akunja pamenenso panachitika zinthu zankhanza. Chifukwa cha zimenezo, Malemba akusonyeza bwino lomwe kuti kukondwerera masiku akubadwa nkoipa, choonadi chimene Akristu oona mtima amachisamala.
Ndiye chifukwa chake, pamene kuli kwakuti ndi nkhani yaumwini ngati Akristu asankha kukumbukira tsiku laukwati wawo, pali zifukwa zomveka zimene Akristu ofikapo samakondwerera masiku akubadwa.