NKHANI YOPHUNZIRA 23
“Dzina Lanu Liyeretsedwe”
“Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo mpaka kalekale.”—SAL. 135:13.
NYIMBO NA. 10 Tamandani Yehova Mulungu Wathu
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. Kodi A Mboni za Yehovafe timakonda kukambirana nkhani zochititsa chidwi ziti?
PALI nkhani zofunika ziwiri zomwe zimakhudza tonsefe. Nkhani zake ndi zokhudza ulamuliro wa Yehova komanso kuyeretsedwa kwa dzina lake. A Mboni za Yehovafe timakonda kukambirana nkhani zochititsa chidwi zimenezi. Komatu nkhani ya ulamuliro wa Mulungu komanso kuyeretsedwa kwa dzina lake n’zogwirizana.
2 Tonsefe tinaphunzira kuti dzina la Mulungu ndi loyenera kuyeretsedwa. Tinaphunziranso kuti tiyenera kuvomereza kuti ulamuliro wa Yehova ndi umene uli wabwino kwambiri. Choncho nkhani zonse ziwirizi ndi zofunika kwambiri.
3. Kodi dzina la Yehova limaphatikizapo chiyani?
3 Dzina la Yehova limaphatikizapo zonse zokhudza Mulungu komanso mmene amalamulirira. Ndiye tikamanena kuti dzina la Yehova ndi lofunika kuyeretsedwa, timakhala tikuvomereza kuti ulamuliro wake ndi umene uli wabwino kwambiri. Dzina la Yehova limagwirizana kwambiri ndi mmene amalamulirira monga Wolamulira Wamphamvuyonse.—Onani bokosi lakuti “Mbali za Nkhani Yaikulu Kwambiri.”
4. Kodi Salimo 135:13 limanena zotani zokhudza dzina la Mulungu, nanga tikambirana mayankho a mafunso ati?
4 Dzina la Mulungu lakuti Yehova ndi lapadera kwambiri. (Werengani Salimo 135:13.) Koma n’chifukwa chiyani dzina la Mulungu lili lofunika kwambiri? Kodi dzinali linadetsedwa bwanji? Nanga kodi Mulungu amayeretsa bwanji dzina lakeli? Ndipo kodi ifeyo tingachite chiyani poteteza dzinali kuti lisapitirize kudetsedwa? Tiyeni tikambirane mayankho a mafunso amenewa.
KODI DZINA NDI LOFUNIKA BWANJI?
5. Kodi anthu ena angakhale ndi funso lotani akamva zoti dzina la Mulungu likufunika kuyeretsedwa?
5 “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Yesu anasonyeza kuti kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu ndi mfundo yofunika kuikumbukira tikamapemphera. Koma kodi ankatanthauza chiyani? Mawu akuti kuyeretsa palembali amatanthauza kuchititsa chinthu kukhala chopatulika. Koma mwina ena angafunse kuti, ‘Kodi dzina la Yehova si loyera kale, ndiye lingafunikenso kuliyeretsa?’ Kuti tiyankhe bwino funsoli, tiyenera kuganizira zimene dzina limatanthauza.
6. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti dzina likhale lofunika kwambiri?
6 Dzina si mawu amene timangogwiritsa ntchito potchulira munthu kapena chinthu chinachake basi. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi chuma chochuluka.” (Miy. 22:1; Mlal. 7:1) N’chifukwa chiyani dzina lili lofunika kwambiri chonchi? Chifukwa dzina lingatanthauzenso mbiri ya munthu komanso zimene ena amadziwa zokhudza munthuyo. Choncho kalembedwe kapena katchulidwe ka dzina si zofunika kwenikweni. Chofunika ndi zomwe anthu amaganiza akamva dzinalo.
7. Kodi anthu adetsa bwanji dzina la Mulungu?
7 Anthu akamanenera Yehova zinthu zabodza, amakhala akuipitsa mbiri yake. Akamachita zimenezi amakhalanso kuti akudetsa dzina lake. Dzina la Mulungu komanso mbiri yake zinadetsedwa kwa nthawi yoyamba m’munda wa Edeni. Tiyeni tione mmene zinachitikira komanso zomwe tingaphunzirepo.
KODI DZINA LA MULUNGU LINADETSEDWA BWANJI?
8. Kodi Adamu ndi Hava ankadziwa chiyani, nanga tingakhale ndi mafunso ati?
8 Adamu ndi Hava ankadziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova komanso ankadziwa zambiri zokhudza Yehovayo. Ankadziwa kuti iye ndi Mlengi wawo yemwe anawapatsa moyo, malo okongola oti azikhala komanso banja labwino. (Gen. 1:26-28; 2:18) Koma kodi anapitiriza kuganizira zinthu zonse zimene Yehova anawachitira? Kodi anasonyezabe kuti amamukonda komanso kumuyamikira? Mayankho a mafunsowa anadziwika pamene mdani wa Mulungu anawayesa.
9. Mogwirizana ndi Genesis 2:16, 17 ndi 3:1-5, kodi Yehova anauza chiyani Adamu ndi Hava, nanga Satana anapotoza bwanji zimene Yehova ananenazi?
9 Werengani Genesis 2:16, 17 ndi 3:1-5. Satana anachititsa njoka kuoneka ngati ikulankhula pamene anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Funsoli linali ndi mfundo inayake yabodza imene inachititsa Hava kuyamba kuganiza zolakwika zokhudza Mulungu. Mulungu ananena kuti anthuwo akhoza kudya zipatso za mtengo uliwonse kupatulapo umodzi. Panali mitengo yambirimbiri yomwe Adamu ndi Hava akanatha kudya zipatso zake. (Genesis 2:9) Pamenepa Yehova anasonyeza kuti ndi Mulungu wopatsa. Koma iye anauza Adamu ndi Hava kuti asadye zipatso zamtengo umodzi wokha. Choncho Satana anapotoza dala zimene Yehova ananena. Iye ankafuna kuti Adamu ndi Hava aziona kuti Mulungu ndi woumira. N’kutheka kuti Hava anayamba kuganiza kuti, ‘Kapenatu Mulungu akutimana zinazake.’
10. Kodi Satana anadetsa bwanji dzina la Mulungu, nanga zotsatira zake zinali zotani?
10 Pamene Satana ankafunsa funsoli, Hava anali adakali ndi mtima womvera Yehova. Poyankha, iye anafotokoza momveka bwino zimene Mulungu anawauza. Anawonjezeraponso kuti sankayenera ngakhale pang’ono kukhudza mtengo umene anawaletsawo. Iye anamvetsa bwino chenjezo la Mulungu kuti ngati sangamumvere, adzafa. Koma Satana anayankha kuti: “Kufa simudzafa ayi.” (Gen. 3:2-4) Iye sikuti anangotsutsa zimene Yehova ananena, koma anayamba kudetsa dzina la Mulungu pouza Hava kuti Yehova ndi wabodza. Pamenepatu iye anakhala Mdyerekezi kapena kuti wonenera ena zoipa. Satana anakwanitsadi kupusitsa Hava chifukwa anamukhulupirira. (1 Tim. 2:14) Hava anayamba kukhulupirira kwambiri Satana kuposa Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti Hava asankhe kuchita zinthu molakwika kwambiri. Iye anasankha kusamvera Yehova moti anadya chipatso chimene anamuletsa. Pambuyo pake, anapatsanso Adamu chipatsocho.—Gen. 3:6.
11. Kodi makolo athu oyamba akanatha kuchita chiyani, koma kodi iwo anatani?
11 Tangoyesani kuganizira zimene Hava akanauza Satana. Bwanji ngati akanamuuza kuti: “Sindikukudziwa, ine ndimadziwa Yehova amene ndi Atate wanga komanso ndimamukonda ndi kumukhulupirira kwambiri. Zinthu zonse zomwe tili nazozi anatipatsa ndi iyeyo. Ndiye iweyo ukundiuza kuti Mulungu ndi woipa? Choka apa!” Kodi mukuganiza kuti Yehova akanamva bwanji kumva Hava akulankhula mawu amenewa osonyeza kuti amamukhulupirira kwambiri? (Miy. 27:11) Koma n’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava analephera kukhala okhulupirika. Chifukwa chakuti chikondi chawo kwa Mulungu chinali chitachepa, sakanathanso kuteteza dzina lake kuti lisadetsedwe.
12. Kodi Satana anachititsa bwanji Hava kuti ayambe kukayikira, nanga Adamu ndi Hava analephera kuchita chiyani?
12 Monga taonera, Satana anachititsa Hava kuti ayambe kukayikira. Chifukwa choti Satana analankhula zoipa zokhudza Mulungu, Hava anayamba kukayikira ngati Mulungu alidi wabwino. Pamapeto pake, Adamu ndi Hava analephera kuteteza dzina la Yehova kuti lisadetsedwe. Iwo anakopekadi ndi zonena za Satana ndipo anasankha kuti asakhalenso kumbali ya Mulungu. Masiku anonso, Satana amagwiritsa ntchito njira ngati imeneyi. Iye amadetsa dzina la Mulungu pomunenera zoipa. Anthu amene amakhulupirira mabodza akewo, sachedwa kukopeka n’kuyamba kukana njira zolungama za Mulungu.
YEHOVA AMAYERETSA DZINA LAKE
13. Kodi lemba la Ezekieli 36:23 limafotokoza bwanji mfundo yaikulu ya uthenga wa m’Baibulo?
13 Kodi Yehova amangolola kuti dzina lake lizidetsedwa koma iye osachitapo kanthu? Ayi. Baibulo limafotokoza zimene Yehova wachita posonyeza kuti zinthu zoipa zimene Satana anamunenera m’munda wa Edeni, zinali zabodza. (Gen. 3:15) Mwachidule tingafotokoze kuti mfundo yaikulu ya uthenga wa m’Baibulo ndi yakuti, Yehova amayeretsa dzina lake komanso adzabwezeretsa chilungamo ndi mtendere padziko lapansi, pogwiritsa ntchito Ufumu wolamuliridwa ndi Mwana wake. M’Baibulo muli mfundo zimene zimatithandiza kumvetsa mmene Yehova amachitira zimenezi.—Werengani Ezekieli 36:23.
14. Kodi zimene Yehova wachita pa nkhani ya m’munda wa Edeni zathandiza bwanji kuti ayeretse dzina lake?
14 Satana wakhala akuyesetsa kuti alepheretse cholinga cha Yehova koma walephera. Baibulo limafotokoza zimene Yehova wachita ndipo limasonyeza kuti iye ndi Atate wachikondi komanso Wolamulira wabwino. N’zoona kuti kusamvera kwa Satana komanso onse amene ali kumbali yake kumam’pweteka kwambiri. (Sal. 78:40) Komabe zimene wachita pa nkhaniyi, zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru, woleza mtima ndiponso wachilungamo. Wasonyezanso mphamvu zake m’njira zambiri. Koposa zonse, wasonyeza kuti ndi Mulungu wachikondi. (1 Yoh. 4:8) Yehova akupitirizabe kuyeretsa dzina lake.
15. Kodi Satana akuchita zotani masiku ano pofuna kudetsa dzina la Mulungu, ndipo zimenezi zakhala ndi zotsatirapo zotani?
15 Masiku ano, Satana akupitirizabe kudetsa dzina la Mulungu. Iye amachititsa kuti anthu azikayikira ngati Mulungu alidi wamphamvu, wachilungamo, wanzeru komanso wachikondi. Mwachitsanzo, amayesetsa kuchititsa anthu kukhulupirira kuti Yehova si Mlengi. Kwa anthu amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu, Satana amawachititsa kuona kuti malamulo a Mulungu si achilungamo ndipo ndi opanikiza. Amaphunzitsanso anthu kuti Mulungu ndi wankhanza ndipo amawotcha anthu. Anthu akakhulupirira mabodza amenewa, kumakhala kosavuta kuti ayambe kukana ulamuliro wolungama wa Yehova. Mpaka pamene adzawonongedwe, Satana apitirizabe kudetsa dzina la Yehova komanso kukopa anthu kuti asakhale kumbali ya Mulungu. Koma kodi iye adzapambana?
MUNGATHANDIZE KUYERETSA DZINA LA YEHOVA
16. Kodi inuyo mungasankhe kuchita chiyani mosiyana ndi zimene Adamu ndi Hava anachita?
16 Yehova amapereka mwayi kwa anthu opanda ungwiro kuti athandize nawo kuyeretsa dzina lake. Choncho n’zotheka kuchita zosiyana ndi zimene Adamu ndi Hava anachita. Ngakhale kuti mukukhala m’dziko limene anthu amanyoza komanso kudetsa dzina la Mulungu, muli ndi mwayi woteteza dzina lake ndi kuuza anthu zoona zokhudza iyeyo. Mungathandize ena kudziwa kuti Yehova ndi woyera, wolungama, wabwino komanso wachikondi. (Yes. 29:23) Mungasonyeze kuti muli kumbali ya Ufumu wa Mulungu ndipo mungathandize ena kudziwa kuti ndi ulamuliro wake wokha umene udzabweretse mtendere m’chilengedwe chonse.—Sal. 37:9, 37; 146:5, 6, 10.
17. Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu kudziwa dzina la Atate wake?
17 Tikamateteza dzina la Mulungu timakhala tikutsanzira Yesu Khristu. (Yoh. 17:26) Yesu anathandiza anthu kudziwa dzina la Atate wake. Sikuti iye ankangogwiritsa ntchito dzinali koma anathandizanso anthu kuti amudziwe bwino Mulungu. Mwachitsanzo, anatsutsa zonena za Afarisi zomwe zinkapangitsa anthu ena kuona kuti Yehova ndi wankhanza, wopanda chifundo komanso saganizira anthu. Yesu anathandiza anthu kudziwa kuti Atate wake amachita zinthu moganizira ena, ndi wachifundo, wachikondi komanso wokhululuka. Anathandizanso anthu kudziwa bwino mmene Yehova alili chifukwa tsiku lililonse ankasonyeza makhalidwe amene anatengera kwa Atate wake.—Yoh. 14:9.
18. Kodi tingatani kuti tisonyeze kuti zoipa zimene otsutsa amanena zokhudza Mulungu ndi zabodza?
18 Mofanana ndi Yesu, nafenso tingauze anthu ena zimene tikudziwa zokhudza Yehova komanso kuwaphunzitsa kuti iyeyo ndi Mulungu wachikondi ndiponso wokoma mtima. Tikamachita zimenezi, timakhala tikusonyeza kuti zoipa zimene otsutsa amamunenera ndi zabodza. Timayeretsa dzina la Mulungu tikamathandiza anthu kuti aziliona kuti ndi loyera. Ngakhale kuti si ife angwiro, tingathe kutsanzira Yehova. (Aef. 5:1, 2) Tikamalankhula komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi makhalidwe a Yehova, timathandiza kuyeretsa dzina lake. Timayeretsanso dzinali tikamaphunzitsa anthu kuti adziwe zoona zokhudza Mulungu.b Zimenezi zimasonyezanso kuti anthu opanda ungwiro akhoza kukhala okhulupirika kwa Mulungu.—Yobu 27:5.
19. Kodi lemba la Yesaya 63:7 limatithandiza bwanji kuona cholinga chathu chachikulu pophunzitsa anthu?
19 Palinso zina zimene tingachite kuti tiyeretse dzina la Mulungu. Nthawi zambiri tikamaphunzira Baibulo ndi ena, timafotokoza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira ndipo zimenezi n’zoona. Komabe ngakhale kuti ndi zofunika kuphunzitsa anthu malamulo a Mulungu, cholinga chathu chachikulu ndi kuwathandiza kuti ayambe kumukonda komanso kukhala okhulupirika kwa iye. Choncho tiyenera kuwathandiza kuti adziwe makhalidwe abwino a Yehova komanso kuti amudziwe kuti ndi wotani. (Werengani Yesaya 63:7.) Tikamaphunzitsa anthu mwa njira imeneyi, tidzakwaniritsa cholinga chathu chowathandiza kuti akhale okhulupirika kwa Yehova ndipo adzayamba kumukonda komanso kumumvera.
20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
20 Ndiye kodi tingatani kuti zochita zathu komanso mmene timaphunzitsira zizithandiza anthu ena kuganiza zabwino zokhudza Yehova ndiponso kufuna kukhala naye pa ubwenzi? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli.
NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndinu Yehova
a Kodi ndi nkhani yofunika iti imene imakhudza anthu komanso angelo? N’chifukwa chiyani ili yofunika, nanga imatikhudza bwanji? Kumvetsa mayankho a mafunso amenewa kungatithandize kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova.
b M’mbuyomu, m’mabuku athu tinkafotokoza kuti dzina la Yehova silifunika kutsimikiziridwa kuti ndi loyera chifukwa palibe amene anatsutsapo kuti Yehova siwoyenera kukhala ndi dzina limeneli. Koma pamsonkhano wapachaka wa 2017, panakambidwa nkhani imene inasintha kafotokozedwe ka mfundo imeneyi. Tcheyamani ananena kuti: “Sikulakwa kunena kuti timapempherera kuti dzina la Yehova litsimikiziridwe kuti ndi loyera chifukwa mbiri yake ikufunika kuti iyeretsedwe.”—Onani JW Broadcasting ya January 2018 pa jw.org®. Pitani pa LIBRARY > JW BROADCASTING®.
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Satana anadetsa dzina la Mulungu pouza Hava kuti Mulungu ndi wabodza. Kwa zaka zambiri Satana wakhala akuphunzitsa zinthu zabodza monga zakuti Mulungu ndi wankhanza komanso kuti sanalenge anthu
d MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale akuchititsa phunziro la Baibulo ndipo akufotokozera wophunzirayo makhalidwe a Mulungu.