Chiphunzitso Chaumulungu Chilimbana ndi Ziphunzitso za Ziŵanda
“Ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda.”—1 TIMOTEO 4:1.
1. Kodi Akristu ali pakati pa nkhondo iti?
TAYEREKEZERANI kukhala ndi moyo wanu wonse m’dera la nkhondo. Kodi kupita kukagona mulikumva mfuti zikulira ndi kudzuka mabomba akuphulika kungakhale kotani? Mwachisoni, m’madera ena a dziko, ndimmenedi anthu akukhalira. Komabe, m’lingaliro lauzimu, Akristu onse amakhala otero. Ali pakati pa nkhondo yaikulu imene yakhala ikumenyedwa kwa zaka pafupifupi 6,000 ndipo yakulirapo kwambiri m’masiku athu. Kodi nkhondo yanthaŵi yaitali imeneyi ndiiti? Nkhondo ya chowonadi ndi mabodza, ya chiphunzitso chaumulungu ndi ziphunzitso za ziŵanda. Sindiko kukuza zinthu ndi pakamwa—malinga ndi zochita za mtsogoleri wa mbali ina yotsutsayo—kuitcha nkhondo yankhalwe ndi yakupha koposa m’mbiri ya anthu.
2. (a) Malinga ndi kunena kwa Paulo, kodi ndimbali ziŵiri ziti zimene zikulimbana? (b) Kodi Paulo anatanthauzanji pamene anati “chikhulupiriro”?
2 Mtumwi Paulo anatchula mbali ziŵiri zomenyana m’nkhondo imeneyi pamene analembera Timoteo kuti: “Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda.” (1 Timoteo 4:1) Onani kuti ziphunzitso za ziŵanda zikakhala zosonkhezera kwambiri “m’masiku otsiriza.” Poonera zinthu m’tsiku la Paulo, ife tikukhala ndi moyo m’nthaŵi imeneyo. Onaninso chimene chikutsutsa ziphunzitso za ziŵanda, ndicho “chikhulupiriro.” Panopo, “chikhulupiriro” chikutanthauza chiphunzitso chaumulungu, chozikidwa pa mawu a Mulungu ouziridwa mwaumulungu opezeka m’Baibulo. Chikhulupiriro chotero chili chopatsa moyo. Chimaphunzitsa Mkristu kuchita chifuniro cha Mulungu. Ndicho chowonadi chimene chimatsogolera kumoyo wamuyaya.—Yohane 3:16; 6:40.
3. (a) Kodi nchiyani chimachitikira ophedwa m’nkhondo yapakati pa chowonadi ndi mabodza? (b) Kodi ndani amene ali kumbuyo kwa ziphunzitso za ziŵanda?
3 Alionse amene amataya chikhulupiriro amaphonya moyo wosatha. Ali ophedwa m’nkhondoyo. Nchotulukapo chatsoka chotani nanga cha kudzilola kusochezedwa ndi ziphunzitso za ziŵanda! (Mateyu 24:24) Kodi ndimotani mmene ife patokha tingapeŵere kukhala ophedwawo? Mwa kukana kwa mtu wagalu ziphunzitso zonama zimenezi, zimene zimangotumikira chifuno cha “mkulu wa ziŵanda,” Satana Mdyerekezi. (Mateyu 12:24) Mwachidziŵikire, ziphunzitso za Satana zili mabodza, pakuti Satana ndiye “atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Talingalirani mmene mwamachenjera anagwiritsira ntchito bodza kusocheretsa makolo athu oyambirira.
Ziphunzitso za Ziŵanda Zivumbulidwa
4, 5. Kodi ndibodza lanji limene Satana anauza Hava, ndipo nchifukwa ninji linali chinthu choipa kwambiri?
4 Zochitikazo nzolembedwa m’Baibulo pa Genesis 3:1-5. Akumagwiritsira ntchito njoka, Satana anafika kwa mkaziyo Hava namfunsa kuti: “Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Funsolo likuoneka kukhala lopanda chiŵembu, koma talipendaninso. “Eya! kodi anatitu?” Satana akumveka wodabwa, monga ngati akunena kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji Mulungu anganene zimenezi?’
5 Mosadziŵa, Hava anasonyeza kuti zinalidi motero. Mkaziyo anadziŵa chiphunzitso chaumulungu pankhaniyi, kuti Mulungu anali atauza Adamu kuti akafa ngati akadya mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa. (Genesis 2:16, 17) Mwachionekere funso la Satana linadzutsa chidwi mwa iye, chotero anamvetsera pamene Satana anafika pamfundo yeniyeni: “Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai.” Nchinthu choipitsitsa chotani nanga kuchinena! Satana anaimba mlandu Yehova, Mulungu wa chowonadi, Mulungu wa chikondi, Mlengi, wa kunena bodza kwa ana Ake aumunthu!—Salmo 31:5; 1 Yohane 4:16; Chivumbulutso 4:11.
6. Kodi ndimotani mmene Satana anakayikiritsa ubwino ndi uchifumu wa Yehova?
6 Koma Satana ananenanso zina. Iye anapitiriza kuti: “Chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” Malinga ndi kunena kwa Satana, Yehova Mulungu—amene anagaŵira makolo athu oyambirira zochuluka—anafuna kuwamana kanthu kena kabwino koposa. Anafuna kuwaletsa kukhala onga milungu. Motero, Satana anakayikiritsa ubwino wa Mulungu. Ndiponso anachirikiza kudzikhutiritsa kwaumwini ndi kunyalanyaza mwadala malamulo a Mulungu, akumanena kuti kuchita mwanjirayi kukakhala kopindulitsa. Kwenikweni, Satana anakayikiritsa uchifumu wa Mulungu pa chilengedwe Chake, akumanena kuti Mulungu analibe kuyenera kwa kuika malire pa zochita za munthu.
7. Kodi ndiliti pamene ziphunzitso za ziŵanda zinayamba kumveka?
7 Ndi mawu amenewo a Satana, ziphunzitso za ziŵanda zinayamba kumveka. Ziphunzitso zoipa zimenezi zikali kuchirikiza miyezo yoipa yofanana ndi imeneyo. Monga momwedi anachitira m’munda wa Edene, Satana, wogwirizana tsopano ndi mizimu ina yopanduka, akali kukayikiritsa kuyenera kwa Mulungu kwa kukhazikitsa miyezo ya zochita. Akali kutsutsa uchifumu wa Yehova ndipo amayesa kusonkhezera anthu kusamvera Atate wawo wakumwamba.—1 Yohane 3:8, 10.
8. Kodi nchiyani chimene Adamu ndi Hava anataya m’Edene, koma ndimotani mmene Yehova anakhalira wowona?
8 Mumkangano woyambirira umenewo m’nkhondo ya chiphunzitso chaumulungu ndi ziphunzitso za ziŵanda, Adamu ndi Hava anapanga chosankha cholakwika ndipo anataya chiyembekezo cha moyo wosatha. (Genesis 3:19) Patapita zaka zambiri ndipo matupi awo atayamba kufooka, iwo anatsimikizira kwenikweni ponena za amene ananena bodza ndi amene ananena zowona m’Edene kalelo. Komabe, zaka mazana ambiri iwo asanafe mwakuthupi, anakhala oyamba kuphedwa m’nkhondo yapakati pa chowonadi ndi bodza pamene anaweruzidwa kukhala osayenerera moyo ndi Mlengi wawo, Magwero a moyo. Panali panthaŵiyo pamene anafa mwauzimu.—Salmo 36:9; yerekezerani ndi Aefeso 2:1.
Ziphunzitso za Ziŵanda Lerolino
9. Kodi ziphunzitso za ziŵanda zakhala zachipambano motani m’zaka mazana ambiri?
9 Monga kwalembedwa m’buku la Chivumbulutso, mtumwi Yohane anatengeredwa ndi mzimu ku “tsiku la Ambuye,” limene linayamba mu 1914. (Chivumbulutso 1:10) Panthaŵiyo Satana ndi ziŵanda zake anachotsedwa kumwamba naponyedwa kudziko lapansi—kugonjetsedwa kwakukulu kwa wotsutsa ameneyu wa Mlengi wathu Wamkulu. Liwu lake silinamvekenso kumwamba kuneneza atumiki a Yehova mosalekeza. (Chivumbulutso 12:10) Komabe, kodi nchipambano chotani chimene ziphunzitso za ziŵanda zinakhala nacho padziko lapansi kuyambira pa Edene? Cholembedwacho chimati: “Chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Dziko lonse linali litanyengezedwa ndi mabodza a Satana! Mposadabwitsa kuti Satana amatchedwa “[wolamulira, NW] wa dziko ili”!—Yohane 12:31; 16:11.
10, 11. Kodi ndim’njira zotani zimene Satana ndi ziŵanda zake alili okangalika lerolino?
10 Kodi Satana anavomereza kugonjetsedwa kwake atapitikitsidwa kumwamba? Kutalitali! Iye anatsimikiza mtima kupitiriza kulimbana ndi chiphunzitso chaumulungu ndi awo amene amachimamatira. Pambuyo pa kupitikitsidwa kwake kumwamba, Satana anapitiriza nkhondo yake: “Chinjoka [Satana] chinakwiya ndi mkazi, nichinachoka kumka kuchita nkhondo ndi otsala a mbewu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.”—Chivumbulutso 12:17.
11 Kuwonjezera pa kulimbana ndi atumiki a Mulungu, Satana akudzaza dziko ndi manenanena ake okopa, akumayesayesa kusungitsa ulamuliro wake pa mtundu wa anthu. Mu amodzi a masomphenya ake a m’Chivumbulutso a tsiku la Ambuye, mtumwi Yohane anaona zilombo zitatu zolusa zimene mophiphiritsira zinaimira Satana, gulu lake landale la padziko lapansi, ndi ulamuliro waukulu wa dziko lonse wa m’nthaŵi yathu. M’kamwa mwa zitatuzi, munatuluka achule. Kodi ameneŵa anaimira chiyani? Yohane akulemba kuti: “Ali mizimu ya ziŵanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kumka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Moonekera bwino, ziphunzitso za ziŵanda zikugwira ntchito kwambiri m’dziko lapansi. Satana ndi ziŵanda zake akali kulimbana ndi chiphunzitso chaumulungu, ndipo adzapitiriza kutero kufikira ataletsedwa mokakamizidwa ndi Yesu Kristu, Mfumu Yaumesiya.—Chivumbulutso 20:2.
Kudziŵa Ziphunzitso za Ziŵanda
12. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kotheka kukaniza ziphunzitso za ziŵanda? (b) Kodi ndimotani mmene Satana amayesera kukwaniritsa chifuno chake pa atumiki a Mulungu?
12 Kodi anthu owopa Mulungu angakanize ziphunzitso za ziŵanda? Angaterodi pazifukwa ziŵiri. Choyamba, chifukwa chakuti chiphunzitso chaumulungu chili champhamvu koposa; ndipo chachiŵiri, chifukwa Yehova wavumbula machenjera a Satana kotero kuti tiwakanize. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera, “sitikhala osadziŵa machenjerero ake.” (2 Akorinto 2:11) Tidziŵa kuti Satana amagwiritsira ntchito zizunzo monga njira imodzi yokwaniritsira chifuno chake. (2 Timoteo 3:12) Komabe, mochenjera kwambiri, amayesa kusonkhezera maganizo ndi mitima ya awo amene amatumikira Mulungu. Anasocheretsa Hava naika zikhumbo zolakwa mumtima mwake. Amayesa kuchita zimodzimodzizo lerolino. Paulo analembera Akorinto kuti: “Ndiwopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Hava ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuwona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.” (2 Akorinto 11:3) Talingalirani mmene waipitsira kalingaliridwe ka mtundu wonse wa anthu.
13. Kodi ndimabodza otani amene Satana wauza mtundu wa anthu kuyambira pa Edene?
13 Kwa Hava, Satana anaimba Yehova mlandu wa kunama ndipo anati anthu angakhale ngati milungu ngati samvera Mlengi wawo. Mkhalidwe wauchimo wa anthu lerolino umatsimikizira kuti Satana, osati Yehova, ndiye amene anali wabodza. Anthu lerolino sali milungu ayi! Komabe, Satana anawonjezera pa bodza loyambiriralo mabodza ena. Anayambitsa lingaliro lakuti moyo wa munthu uli wosafa. Motero iye monyengerera anapereka kwa anthu chiyembekezo cha kukhala ngati milungu mwanjira ina. Ndiyeno, ndi chiphunzitso chonyenga chimenecho monga maziko, anachirikiza ziphunzitso za moto wa helo, purigatoriyo, kukhulupirira mizimu, ndi kulambira makolo akufa. Anthu mamiliyoni mazanamazana akali akapolo a mabodza ameneŵa.—Deuteronomo 18:9-13.
14, 15. Kodi chowonadi chonena za imfa ndi chiyembekezo cha mtsogolo cha munthu nchotani?
14 Ndithudi, zimene Yehova anauza Adamu zinali zowona. Adamu anafadi pamene anachimwira Mulungu. (Genesis 5:5) Pamene Adamu ndi mbadwa zake anafa, anakhala miyoyo yakufa, yosadziŵa kanthu ndi yosachitha kanthu. (Genesis 2:7; Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Chifukwa cholandira choloŵa cha uchimo kwa Adamu, miyoyo yonse yaumunthu imafa. (Aroma 5:12) Komabe, kalelo m’Edene, Yehova analonjeza kudza kwa mbewu imene ikagonjetsa ntchito za Mdyerekezi. (Genesis 3:15) Mbewuyo inali Yesu Kristu, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Yesu anafa wopanda uchimo, ndipo moyo wake woperekedwa nsembe unakhala dipo lowombola mtundu wa anthu kumkhalidwe wawo wakufa. Awo amene momvera asonyeza chikhulupiriro mwa Yesu ali ndi mpata wa kulandira moyo wosatha umene Adamu anataya.—Yohane 3:36; Aroma 6:23; 1 Timoteo 2:5, 6.
15 Dipo ndilo chiyembekezo chenicheni cha mtundu wa anthu, osati lingaliro losamveka bwino lakuti moyo umapulumuka imfa. Ichi ndichiphunzitso chaumulungu. Chili chowonadi. Ndiponso chili chisonyezero chabwino koposa cha chikondi ndi nzeru za Yehova. (Yohane 3:16) Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga pakudziŵa chowonadi chimenechi ndi kumasulidwa ku ziphunzitso za ziŵanda m’nkhani zimenezi!—Yohane 8:32.
16. Kodi ndizotulukapo zotani zimene zimakhalapo m’kupita kwa nthaŵi pamene anthu atsatira nzeru zawozawo?
16 Mwa mabodza ake m’munda wa Edene, Satana analimbikitsa Adamu ndi Hava kukalimira kukhala osadalira Mulungu ndi kudalira nzeru za iwo eni. Lerolino, timaona zotulukapo zake zokhalapo m’kupita kwa nthaŵi mwa upandu, mavuto azachuma, nkhondo ndi chisalungamo chofala zimene zili m’dziko lerolino. Nchifukwa chake Baibulo limati: “Nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu”! (1 Akorinto 3:19) Komabe, anthu ochuluka amasankha kuvutika mmalo mwa kumvetsera mosamalitsa ziphunzitso za Yehova. (Salmo 14:1-3; 107:17) Akristu, amene alandira chiphunzitso chaumulungu, amapeŵa kugwidwa ndi msamphawo.
17. Kodi ndi “chotchedwa chizindikiritso konama” chotani chimene Satana wachirikiza, ndipo zipatso zake nzotani?
17 Paulo analembera Timoteo kuti: “Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kuleŵa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chotchedwa chizindikiritso konama; chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro.” (1 Timoteo 6:20, 21) “Chizindikiritso” chimenecho chimatanthauza ziphunzitso za ziŵanda. M’tsiku la Paulo, zikuonekera kuti chinatanthauza malingaliro ampatuko amene ena m’mipingo anali kuchirikiza. (2 Timoteo 2:16-18) Pambuyo pake, zotchedwa chizindikiritso konama, zonga Gnosticism ndi filosofi Yachigiriki, zinaipitsa mpingo. M’dziko lerolino, nthanthi za kukana kukhalako kwa Mulungu, kukayikira kukhalako kwa Mulungu, chisinthiko, ndi chisulizo cha ophunzira pa Baibulo zili zitsanzo za chotchedwa chizindikiritso konama, monga momwe malingaliro osakhala a m’malemba a ampatuko amakono alili. Zipatso za chotchedwa chizindikiritso konama zimaoneka m’kunyonyotsoka kwa makhalidwe, kusalemekeza ulamuliro kofala, kusawona mtima, ndi dyera zimene zili mbali yaikulu ya dongosolo la zinthu la Satana.
Kumamatira ku Chiphunzitso Chaumulungu
18. Kodi ndani lerolino amene afunafuna chiphunzitso chaumulungu?
18 Ngakhale kuti Satana wakhala akudzaza dziko lapansi ndi ziphunzitso za ziŵanda kuyambira pa Edene, nthaŵi zonse pakhala ena amene afunafuna chiphunzitso chaumulungu. Oterowo ali okwanira mamiliyoni lerolino. Amaphatikizapo Akristu odzozedwa otsalira amene ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kulamulira ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba ndi khamu lalikulu lomakula la “nkhosa zina” amene chiyembekezo chawo chili cha kulandira gawo la padziko lapansi la Ufumuwo. (Mateyu 25:34; Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:3, 9) Lerolino, ameneŵa asonkhanitsidwa pamodzi m’gulu limodzi la padziko lonse limene mawu a Yesaya amasonyako: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.”—Yesaya 54:13.
19. Kodi kuphunzitsidwa ndi Yehova kumaphatikizapo chiyani?
19 Kuphunzitsidwa ndi Yehova kumatanthauza zoposa kungodziŵa chiphunzitso chowona—ngakhale kuti kumeneko nkofunika. Yehova amatilangiza mmene tingakhalire ndi moyo, mmene tingagwiritsirire ntchito chiphunzitso chaumulungu m’miyoyo yathu. Mwachitsanzo, timakaniza dyera, makhalidwe oipa, ndi mzimu wa kudzigangira zimene zili zofala kwambiri m’dziko lotizinga. Timazindikira zimene kulondola chuma kodzivulaza m’dzikoli kumatanthauza—kuli kwakupha. (Yakobo 5:1-3) Sitimaiŵala konse chiphunzitso chaumulungu chotchulidwa m’mawu a mtumwi Yohane kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.”—1 Yohane 2:15.
20, 21. (a) Kodi nchiyani chimene Satana amagwiritsira ntchito pakuyesayesa kwake kuchititsa khungu anthu? (b) Kodi ndimadalitso otani amene amadza kwa awo amene amamamatira ku chiphunzitso chaumulungu?
20 Chiyambukiro cha ziphunzitso za ziŵanda pa mikhole yake chimasonyezedwa ndi mawu a Paulo kwa Akorinto akuti: ‘[Satana] wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawaŵalire.’ (2 Akorinto 4:4) Satana akufunanso kuchititsa khungu Akristu owona m’njira imodzimodziyo. Kalelo m’Edene, anagwiritsira ntchito njoka kusocheretsa mmodzi wa atumiki a Mulungu. Lerolino, amagwiritsira ntchito akanema ndi maprogramu apawailesi yakanema achiwawa kapena achisembwere. Amagwiritsira ntchito wailesi, mabuku, ndi nyimbo. Chida champhamvu chimene ali nacho ndicho mayanjano oipa. (Miyambo 4:14; 28:7; 29:3) Nthaŵi zonse zindikirani zimene zinthuzo kwenikweni zili—machenjera ndi ziphunzitso za ziŵanda.
21 Kumbukirani, mawu a Satana m’Edene anali mabodza; mawu a Yehova anakhala owona. Chiyambire masiku oyambirira amenewo, zinthu zapitirizabe choncho. Satana nthaŵi zonse wakhala wabodza, ndipo chiphunzitso chaumulungu chakhala chowona mosalephera. (Aroma 3:4) Ngati timamatira ku Mawu a Mulungu, nthaŵi zonse tidzakhala kumbali yopambana m’nkhondo yapakati pa chowonadi ndi bodza. (2 Akorinto 10:4, 5) Pamenepa, tiyeni titsimikize mtima kukana ziphunzitso zonse za ziŵanda. Tikatero tidzapirira kufikira nthaŵi imene nkhondo ya pakati pa chowonadi ndi bodza idzatha. Chowonadi chidzakhala chitapambana. Satana adzachotsedwa, ndipo chiphunzitso chaumulungu ndicho chokha chimene chidzamvedwa padziko lapansi.—Yesaya 11:9.
Kodi Mungathe Kufotokoza?
◻ Kodi ndiliti pamene ziphunzitso zauchiŵanda zinayamba kumveka?
◻ Kodi ena a mabodza ochirikizidwa ndi Satana ndi ziŵanda zake ndiati?
◻ Kodi ndim’njira zotani zimene Satana alili wokangalika kwambiri lerolino?
◻ Kodi Satana amagwiritsira ntchito chiyani kuchirikiza ziphunzitso za ziŵanda?
◻ Kodi ndimadalitso otani amene amadza kwa awo amene amamamatira ku chiphunzitso chaumulungu?
[Chithunzi patsamba 9]
Chiphunzitso chauchiŵanda chinayamba kumveka m’munda wa Edene
[Chithunzi patsamba 10]
Chiphunzitso chaumulungu chonena za dipo ndi Ufumu chimapereka chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu