Chenjerani ndi “Mawu a Alendo”
“Mlendo sizidzam’tsata, koma zidzam’thaŵa; chifukwa sizidziŵa mawu a alendo.”—YOHANE 10:5.
1, 2. (a) Kodi Mariya anatani Yesu atamuitana dzina lake, ndipo zimene zinachitikazi zimatsimikizira motani mawu amene Yesu ananena m’mbuyomo? (b) N’chiyani chimene chimatithandiza kuyandikana kwambiri ndi Yesu?
YESU atauka kwa akufa, anaona mkazi wina ataimirira pafupi ndi manda opanda kanthu amene Yesuyo anali ataikidwamo. Iye anam’dziŵa bwino mkaziyo kuti ndi Mariya wa Magadala. Zaka pafupifupi ziŵiri ndi theka m’mbuyomo, Yesu anachotsa ziŵanda mwa mkaziyo. Kuyambira panthaŵi imeneyo, Mariya anatsagana ndi Yesu ndi atumwi ake, ndipo anali kuwatumikira pa zosoŵa zawo. (Luka 8:1-3) Koma tsiku limene Yesu anam’pezali, Mariya anali kulira poti anali ndi chisoni chachikulu chifukwa analipo pamene Yesu anali kufa, ndipo apa thupi la Yesu linali litasoŵa. Choncho Yesu anam’funsa kuti: “Mkazi, uliranji? Ufuna yani?” Poganizira kuti munthuyo ndiye mwiniwake wa mundawo, Mariya anayankha kuti: “Mbuye ngati mwam’nyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzam’chotsa.” Ndiyeno Yesu uja ananena kuti: “Mariya.” Nthaŵi yomweyo anam’zindikira chifukwa cha mmene Yesu anam’lankhulira ndipo anafuula mosangalala kuti “Mphunzitsi,” nam’kupatira.—Yohane 20:11-18.
2 Nkhani imeneyi ikutsimikizira bwino kwambiri zimene Yesu ananena m’mbuyomo zisanachitike zimenezi. Nthaŵi imeneyo anafotokoza kuti iye ali ngati mbusa ndipo otsatira ake ali ngati nkhosa, ndiponso ananena kuti mbusa amaitana nkhosa zake mayina ndipo nkhosazo zimadziŵa mawu ake. (Yohane 10:3, 4, 14, 27, 28) Indedi, mofanana ndi mmene nkhosa zimazindikirira mbusa wawo, Mariya anazindikira Kristu, Mbusa wake. Nawonso otsatira a Yesu masiku ano amam’zindikira iye. (Yohane 10:16) Mofanana ndi mmene khutu la nkhosa limazindikirira mawu a mbusa wake ndipo limathandiza nkhosayo kuyandikana naye kwambiri, kuzindikira kwauzimu kumatithandiza kutsatira bwinobwino mapazi a Yesu Kristu, Mbusa wathu Wabwino.—Yohane 13:15; 1 Yohane 2:6; 5:20.
3. Kodi fanizo la Yesu la khola la nkhosa likubweretsa mafunso ena otani m’maganizo mwathu?
3 Koma malinga ndi fanizo limeneli, nzeru imene nkhosa ili nayo yozindikira mawu a munthu imathandiza nkhosayo kudziŵa bwenzi lake komanso mdani wake. Mfundo imeneyi n’njofunika kwambiri chifukwa ife tili ndi adani ochenjera kwambiri. Kodi adani amenewo ndani? Kodi amachita zotani? Nanga tingadziteteze bwanji? Kuti tidziŵe mayankho a mafunso ameneŵa, tiyeni tionenso zina zimene Yesu ananena m’fanizo lake la khola la nkhosa.
‘Iye Wosaloŵa Pakhomo’
4. Malinga ndi fanizo la mbusa, kodi nkhosazo zimatsata ndani, nanga ndani amene sizim’tsata?
4 Yesu anati: “Iye wakuloŵera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa. Iyeyu, wapakhomo am’tsegulira ndi nkhosa zimva mawu ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha mayina awo, nazitsogolera kunja. Pamene adatulutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zim’tsata iye; chifukwa zidziŵa mawu ake. Koma mlendo sizidzam’tsata, koma zidzam’thaŵa; chifukwa sizidziŵa mawu a alendo.” (Yohane 10:2-5) Onani kuti Yesu anatchula liwu lakuti “mawu” katatu. Kaŵiri ananena za mawu a mbusa, koma kachitatu, ananena za “mawu a alendo.” Kodi apa Yesu akunena za mlendo wotani?
5. Kodi n’chifukwa chiyani sitichereza mlendo ngati amene akutchulidwa mu Yohane chaputala 10?
5 Pano Yesu sakunena mlendo amene tiyenera kum’chereza—mawu amene m’chinenero choyambirira cha Baibulo amatanthauza “kukonda alendo.” (Ahebri 13:2) M’fanizo la Yesu, mlendoyo si munthu woti wachita kuitanidwa ayi chifukwa ‘saloŵa m’khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina.’ Iye ndiye “wakuba ndi wolanda.” (Yohane 10:1) Kodi woyamba kutchulidwa m’Mawu a Mulungu kuti anakhala wakuba ndi wolanda ndi ndani? Ndi Satana Mdyerekezi. Umboni wa zimenezi timaupeza m’buku la Genesis.
Nthaŵi Yoyamba Imene Mawu a Mlendo Anamveka
6, 7. Kodi ndi zifukwa ziti zabwino zimene Satana akutchedwera mlendo ndi wakuba?
6 Genesis 3:1-5 amafotokoza nthaŵi yoyamba imene mawu a mlendo anamveka padziko lapansi. Nkhaniyo imanena kuti Satana anafika kwa mkazi woyamba, Hava, kudzera mwa njoka namuuza zosokeretsa. Zoona, sikuti nkhani imeneyi imachita kutchuliratu kuti Satana ndiye “mlendo.” Koma zochita zake zimasonyeza kuti m’njira zambiri iye anali ngati mlendo amene Yesu anamufotokoza m’fanizo lake lolembedwa mu Yohane chaputala 10. Tiyeni tione kufanana kwina kwa mlendoyo ndi Satana.
7 Yesu ananena kuti mlendoyo amafika m’khola la nkhosa zimene akufuna kubazo mozembera. Satananso anafika kwa mkaziyo mozembera, pogwiritsa ntchito njoka. Machenjera ameneŵa anavumbula mmene Satana alili, kuti iye ndi mbava yachinyengo. Ndiponso, cholinga cha mlendo m’khola la nkhosazo ndi kuba nkhosa za mwiniwake. Ndipotu mlendoyo ndi woipa kuposa wakuba, popeza chinanso chimene iye akufuna ndi “kupha, ndi kuwononga.” (Yohane 10:10) Satananso anali wakuba. Mwa kunyenga Hava, iye anaba kukhulupirika kwake kumene kunayenera kupita kwa Mulungu. Chinanso, Satana anadzetsa imfa pa anthu, choncho ali wambanda.
8. Kodi Satana anapotoza motani mawu a Yehova ndiponso zolinga Zake?
8 Chinyengo cha Satana chinaoneka m’njira imene anapotozera mawu a Yehova ndiponso zolinga Zake. Iye anafunsa Hava kuti: ‘Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?’ Apa Satana anaonetsa ngati kuti akudabwapo, kukhala ngati akunena kuti: ‘Zingatheke bwanji Mulungu kukhala wonyanyira choncho?’ Kenako anapitiriza kuti: “Adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu.” Taonani mawu akewo akuti: “Adziŵa Mulungu.” Kunena kwina, Satana anali kunena kuti: ‘Zimene Mulungu akudziŵa inenso ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa zolinga zake, ndipo si zabwino ayi.’ (Genesis 2:16, 17; 3:1, 5) N’zachisoni kuti Hava ndi Adamu sanapeŵe mawu a mlendo ameneyu. Koma iwo anamvera mawuwo nadzetsa tsoka pa iwo ndi ana awo onse.—Aroma 5:12, 14.
9. N’chifukwa chiyani masiku ano tikuyembekeza kumva mawu a alendo?
9 Masiku ano Satana amagwiritsa ntchito njira ngati zimenezi pofuna kusokeretsa anthu a Mulungu. (Chivumbulutso 12:9) Iye ndiye “atate wake wa bodza,” ndipo anthu amene, mofanana ndi iyeyo, amayesa kusokeretsa atumiki a Mulungu ali ana ake. (Yohane 8:44) Tiyeni tione njira zina zimene mawu a alendo ameneŵa amamvekera masiku ano.
Mmene Mawu a Alendo Amamvekera Masiku Ano
10. Kodi imodzi mwa njira zimene mawu a alendo akumvekera ndi yotani?
10 Mawu onyenga. Mtumwi Paulo anati: “Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo.” (Ahebri 13:9) Kodi anali kunena ziphunzitso zotani? Popeza kuti ziphunzitso zimenezo ‘tingatengedwe’ nazo, n’zachionekere kuti Paulo anali kunena ziphunzitso zimene zingatifooketse mwauzimu. Kodi ndani amene akulankhula ziphunzitso zachilendo zimenezi? Paulo anauza gulu la akulu achikristu kuti: “Mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:30) Indedi, masiku ano mofanana ndi masiku a Paulo, anthu ena amene kale anali mumpingo wachikristu akuyesa kusokeretsa nkhosa mwa kulankhula “zokhotakhota”—zinthu zomveka ngati zoona ndiponso mabodza enieni. Mogwirizana ndi zimene mtumwi Petro ananena, iwo amagwiritsa ntchito “mawu onyenga”—mawu ofanana ndi choonadi koma opandiratu ntchito ngati ndalama zachinyengo.—2 Petro 2:3.
11. Kodi mawu opezeka pa 2 Petro 2:1, 3 amavumbula motani njira zimene ampatuko amagwiritsa ntchito ndi zolinga zawo?
11 Petro anapitiriza kuvumbula njira zimene ampatuko amagwiritsa ntchito mwa kunena kuti “adzaloŵa nayo m’seri mipatuko yotayikitsa.” (2 Petro 2:1, 3) Mofanana ndi wakuba m’fanizo la Yesu la khola la nkhosa amene ‘saloŵa m’khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina,’ ampatuko amati akamafika kwa ife amafika chozemba. (Agalatiya 2:4; Yuda 4) Kodi cholinga chawo n’chiyani? Petro akuti: “Adzakuyesani malonda.” Indedi, zilizonse zimene ampatuko anganene, cholinga chenicheni cha mbavazo ndicho ‘kuba, ndi kupha, ndi kuwononga.’ (Yohane 10:10) Chenjerani ndi alendo oterowo!
12. (a) Kodi mawu a alendo angamveke bwanji m’mayanjano athu? (b) Kodi njira imene Satana anagwiritsa ntchito ikufanana bwanji ndi imene alendo amagwiritsa ntchito masiku ano?
12 Mayanjano oipa. Mawu a alendo angamveke kudzera mwa anthu amene timayanjana nawo. Mayanjano oipa angawononge makamaka achinyamata. (1 Akorinto 15:33) Kumbukirani kuti Satana anasankha Hava amene anali wamng’onopo ndi wosadziŵa zambiri pakati pa anthu aŵiri oyambawo. Chifukwa cha zonena za Satana, Hava anakhulupirira kuti Yehova anam’patsa ufulu wochepa kwambiri, ngakhale kuti zimenezo sizinali zoona chifukwa Hava anapatsidwa ufulu wambiri. Yehova anakonda anthu amene iye anawalenga ndipo anali kuwasamala. (Yesaya 48:17) Masiku anonso alendo amayesa kukukopani inu achinyamata mwa kunena kuti makolo anu achikristu amakupatsani ufulu wochepa kwambiri. Kodi alendo ngati amenewo angakukhudzeni motani? Mtsikana wina wachikristu anavomereza kuti: “Kwa kanthaŵi ndithu chikhulupiriro changa chinafooka chifukwa cha anzanga kusukulu. Iwo ankangokhalira kundiuza kuti chipembedzo changa chimaletsa zambiri ndipo n’chonyanyira.” Koma zoona zake n’zoti makolo anu amakukondani. Choncho pamene anzanu kusukulu akuyesa kukulimbikitsani kuti musamakhulupirire makolo anu, musanyengedwe ngati Hava.
13. Kodi Davide anatsatira langizo liti lanzeru, ndipo njira imodzi imene ife tingatengere chitsanzo chake n’njotani?
13 Wamasalmo Davide ananenapo za mayanjano oipa. Iye anati: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu otyasika,” kapena kuti anthu amene amabisa khalidwe lawo. (Salmo 26:4) Kodi apanso mukutha kuona mmene alendo alili? Amadzibisa ngati mmene Satana anadzibisira mwa kugwiritsa ntchito njoka. Masiku ano, anthu ena okonda zachiwerewere amadzibisa ndipo amabisa zolinga zawo mwa kugwiritsa ntchito Intaneti. Pamalo ochezera ndi anthu ena pa Intanetipo, anthu achikulire ofuna kuchita zachiwerewere ndi ana angadzionetse ngati ndi achinyamata pofuna kukukopani. Achinyamatanu, khalani ochenjera kwambiri kuti musapweteke mwauzimu.—Salmo 119:101; Miyambo 22:3.
14. Kodi nthaŵi zina mawu a alendo amafalitsidwa motani m’manyuzipepala, pa TV, ndi pawailesi?
14 Kunenezedwa mabodza. Ngakhale kuti nkhani zina m’manyuzipepala zimanena chilungamo za Mboni za Yehova, nthaŵi zina a manyuzipepala, TV, ndi wailesi amalola kufalitsa mawu abodza onenedwa ndi alendo. Mwachitsanzo, m’dziko lina nkhani ina inanena zabodza zoti a Mboni anali kumbali ya boma la Hitler nthaŵi imene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inali kuchitika. Kudziko linanso kunanenedwa nkhani yoneneza a Mboni kuti ndiwo akuphwanya zinthu m’matchalitchi. M’mayiko ena anafalitsa nkhani m’manyuzipepala, pa TV, ndi pawailesi zoneneza a Mboni kuti amakana kupatsa ana awo mankhwala kuti achire ndiponso kuti amalekerera dala machimo aakulu amene anthu awo amachita. (Mateyu 10:22) Ngakhale atineneze zimenezo, alipo anthu ena oona mtima amene amatidziŵa bwino kwambiri ndipo amadziŵa kuti limenelo ndi bodza.
15. N’chifukwa chiyani kuli kupanda nzeru kukhulupirira zonse zimene zimanenedwa m’manyuzipepala, pa TV, ndi pawailesi?
15 Kodi tiyenera kuchita chiyani tikamva zonenanena zofalitsidwa ndi mawu a alendo ngati amenewo? Tiyenera kutsatira langizo lopezeka pa Miyambo 14:15 lakuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” Ndi kupanda nzeru kukhulupirira kuti zonse zimene zimanenedwa m’manyuzipepala, pa TV, ndi pawailesi n’zoona. Ngakhale kuti si nkhani zonse za m’dzikoli zimene timazikayikira, timadziŵa kuti ‘dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.’—1 Yohane 5:19.
“Yesani Mawu Ouziridwawo”
16. (a) Kodi khalidwe la nkhosa zenizeni limatsimikizira motani kuti mawu a Yesu opezeka pa Yohane 10:4 ndi oona? (b) Kodi Baibulo limatilimbikitsa kuchita chiyani?
16 Koma kodi tingadziŵe bwanji kuti amene takumana nayeyo ndi bwenzi lathu kapena mdani wathu? Yesu ananena kuti nkhosa zimatsata mbusa “chifukwa zidziŵa mawu ake.” (Yohane 10:4) Nkhosa zikamatsata mbusa sizim’tsata chifukwa cha maonekedwe ake koma chifukwa cha mawu ake. Buku lina lofotokoza za mayiko otchulidwa m’Baibulo limasimba zoti mlendo wina ananena kuti nkhosa zimadziŵa mbusa wawo chifukwa cha zimene wavala, osati mawu ake. Koma mbusa wina anati zimadziŵa mawu a mbusa wawo. Pofuna kutsimikizira zimenezi, mbusayo anasinthana zovala ndi mlendoyo. Mlendoyo atavala zovala za mbusayo, anaitana nkhosazo koma sizinam’tsate. Sizinadziŵe mawu ake. Koma pamene mbusayo anaziitana, nthaŵi yomweyo zinam’tsatira ngakhale kuti sanavale ngati mbusa. Choncho, munthu atha kuoneka ngati mbusa, koma kwa nkhosa, zimenezo sizitanthauza kuti iye ndi mbusadi. Pamenepa tinganene kuti nkhosa zimayesa mawu a amene akuziitanayo, n’kuwayerekeza ndi mawu a mbusa wawo. Mawu a Mulungu amatiuza kuti tizichita zofanana ndi zimenezi, pamene amati “yesani mawu ouziridwawo kuona ngati achokera kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1, NW; 2 Timoteo 1:13) Kodi chingatithandize n’chiyani kuchita zimenezi?
17. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiwadziŵe bwino mawu a Yehova? (b) Tikadziŵa Yehova timatha kuchita chiyani?
17 Choncho, ngati tiwadziŵa bwino kwambiri mawu a Yehova, kapena kuti uthenga wake, ndiye kuti sitingavutike kuzindikira mawu a mlendo. Baibulo limafotokoza mmene tingadziŵire zimenezo. Limati: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu mmenemo.” (Yesaya 30:21) “Mawu” amenewo amene timawamva kumbuyo kwathu amachokera m’Mawu a Mulungu. Tikamaŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi iliyonse, zili ngati timamva mawu a Yehova, Mbusa wathu Wamkulu. (Salmo 23:1) Chotero, pamene tiphunzira kwambiri Baibulo, m’pamenenso timawadziŵa bwino mawu a Mulungu. Chifukwa chodziŵa bwino mawu a Mulunguwo, alendo akamalankhula timatha kuzindikira nthaŵi yomweyo mawu awo.—Agalatiya 1:8.
18. (a) Kodi kudziŵa mawu a Yehova kumaphatikizapo chiyani? (b) Malinga ndi Mateyu 17:5, n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera mawu a Yesu?
18 Kodi kudziŵa mawu a Yehova kumaphatikizaponso chiyani? Kuwonjezera pa kumva, kumaphatikizapo kuchita zimene munthu wamvazo. Taonaninso lemba la Yesaya 30:21. Mawu a Mulungu amati: “Njira ndi iyi.” Inde, mwa kuphunzira Baibulo, timamva malangizo a Yehova. Kenako, Yehova akulamula kuti: “Yendani inu mmenemo.” Iye amafuna kuti ife tichite zimene tamvazo. Ndiye tikamagwiritsa ntchito zimene tikuphunzira, timaonetsa kuti tikumva mawu a Yehova ndipo tikuchita zimene akunena. (Deuteronomo 28:1) Ndiponso kumvera mawu a Yehova kumatanthauza kumvera mawu a Yesu, chifukwa chakuti Yehova mwiniwakeyo anatiuza kuchita zimenezo. (Mateyu 17:5) Kodi Yesu, Mbusa Wabwino, amatiuza kuchita chiyani? Amatiphunzitsa kuti tizipanga ophunzira ndi kukhulupirira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45; 28:18-20) Tikamvera mawu akewo tidzapeza moyo wosatha.—Machitidwe 3:23.
“Zidzam’thaŵa”
19. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikamva mawu a alendo?
19 Choncho, kodi tiyenera kuchita chiyani tikamva mawu a alendo? Tiyenera kuchita zimene nkhosa zimachita. Yesu anati: “Mlendo sizidzam’tsata, koma zidzam’thaŵa.” (Yohane 10:5) Zimene tiyenera kuchitazo zili paŵiri. Choyamba, ‘sitidzam’tsata’ mlendoyo. Inde, timakana mlendoyo kwamtuwagalu. Ndipotu m’Chigiriki cha m’Baibulo, lemba limeneli limagwiritsa ntchito mawu okana amphamvu kwambiri m’chinenerocho. (Mateyu 24:35; Ahebri 13:5) Chachiŵiri, tiyenera ‘kum’thaŵa,’ kapena kuti kum’peŵa. Umu ndi mmene tiyenera kuchitira ndi anthu amene ziphunzitso zawo sizigwirizana ndi mawu a Mbusa Wabwino.
20. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikakumana ndi (a) ampatuko onyenga, (b) mayanjano oipa, ndiponso (c) tikamva nkhani zotineneza mabodza m’manyuzipepala, pa TV, ndi pawailesi?
20 Ndiyetu tikakumana ndi anthu amene amalankhula zampatuko, tizichita zimene Mawu a Mulungu amanena. Amati: ‘Yang’anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.’ (Aroma 16:17; Tito 3:10) N’chimodzimodzinso ndi Akristu achinyamata amene ayenera kulimbana ndi mayanjano oipa. Iwo ayenera kutsatira malangizo amene Paulo anapereka kwa Timoteo wachinyamata, akuti: ‘Thaŵa zilakolako za unyamata.’ Ndipo akatineneza mabodza m’nkhani za m’nyuzipepala, pa TV, ndi pawailesi, tizikumbukira langizo lina limene Paulo anapereka kwa Timoteo. Iye anati: ‘[Iwo amene amamvera mawu a alendo] adzapatukira kutsata nthano zachabe. Koma iwe, khala maso m’zonse.’ (2 Timoteo 2:22; 4:3-5) Ngakhale mawu a alendo amveke okoma chotani, ife timathaŵa chilichonse chimene chingawononge chikhulupiriro chathu.—Salmo 26:5; Miyambo 7:5, 21; Chivumbulutso 18:2, 4.
21. Kodi amene amakana mawu a alendo adzapeza mphoto yotani?
21 Mwa kunyansidwa ndi mawu a alendo, Akristu odzozedwa ndi mzimu amalabadira mawu a Mbusa Wabwino opezeka pa Luka 12:32. Pamenepo Yesu amawauza kuti: “Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.” Nazonso “nkhosa zina” zikuyembekezera mwachidwi kumva mawu a Yesu akuti: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” (Yohane 10:16; Mateyu 25:34) Tidzapeza mphoto yosangalatsa kwambiri tikamakana “mawu a alendo.”
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Satana amafanana bwanji ndi mlendo amene Yesu anam’fotokoza m’fanizo lake la khola la nkhosa?
• Kodi masiku ano mawu a alendo amamveka m’njira zotani?
• Kodi tingawazindikire motani mawu a alendo?
• Kodi tiyenera kuchita chiyani tikamva mawu a alendo?
[Chithunzi patsamba 15]
Mariya anazindikira Kristu
[Chithunzi patsamba 16]
Mlendo amafika kwa nkhosa mozembera
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi timachita chiyani tikamva mawu a alendo?