Mutu 7
Moyo Wokhutiritsa—N’chifukwa Chiyani Uli Wosoŵa Choncho?
1, 2. Kodi Mulungu analetseranji kudya za “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa”?
N’CHIFUKWA chiyani anthu ambiri amavutikira pachabe osapeza cholinga chenicheni chokhalira ndi moyo? “Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duŵa, nafota; athaŵa ngati mthunzi, osakhalitsa.” (Yobu 14:1, 2) Chinthu chimene chinawononga ziyembekezo zabwino za anthu onse chinachitika kwa anthu aŵiri oyambirira m’Paradaiso.
2 Kuti banja la anthu onse lipeze chimwemwe chenicheni, iwo ayenera kukhala paubale wabwino ndi Mulungu—ubale wodzifunira, osati woumirizidwa ayi. (Deuteronomo 30:15-20; Yoswa 24:15) Yehova amafuna kumvera ndi kulambira kochokera mumtima, komanso kwachikondi. (Deuteronomo 6:5) Choncho, m’munda wa Edene, Yehova anapereka lamulo limene linapatsa mwayi munthu woyamba kuti asonyeze kukhulupirika kwake kochokera pansi pa mtima. “Mitengo yonse ya m’munda udyeko,” anatero Mulungu kwa Adamu, “koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Kunali kuyesedwa kosavuta. Yehova analetsa Adamu kudya chipatso cha mtengo umodzi wokha pa mitengo yonse ya m’mundamo. Mtengo umenewo unaimira ulamuliro wa Mlengi wanzeru zonse wonena chimene chili chabwino ndi chimene chili choipa. Mwamuna woyambayo anakauza mkazi wake, amene Yehova anam’patsa monga “wom’thangatira,” za lamulo la Mulungu limenelo. (Genesis 2:18) Onse aŵiri anakhutira ndi dongosolo limenelo—kukhala pansi pa ulamuliro wa Mulungu—pogonjera chifuniro chake mokondwa ndi kusonyeza chikondi chawo kwa Mlengi wawo ndi Mpatsi wa Moyo.
3-6. Kodi n’chiyani chinachitikira banja la anthu kuti miyoyo yawo ikhale yovutitsa ndi yotopetsa?
3 Ndiyeno tsiku lina njoka inalankhula kwa Hava ndi kum’funsa kuti: “Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava anayankha kuti iwo analetsedwa kudya zipatso za ‘mtengo [wokhawo] umene unali m’kati mwa munda,’ mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa, kuti ‘asafe.’—Genesis 3:1-3.
4 Kodi njoka imeneyi inali ndani? Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limaitcha “njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Kodi Mulungu ndiye analenga Satana Mdyerekezi? Ayi, ntchito za Yehova ndi zangwiro ndi zabwino. (Deuteronomo 32:4) Wolengedwa wauzimu ameneyu anadzipanga yekha kukhala Mdyerekezi, kutanthauza “Woneneza,” ndi Satana, kutanthauza “Wotsutsa.” ‘Chilakolako chake cha iye mwini chinam’koka,’ chilakolako chofuna kutenga malo a Mulungu, ndipo anakhala ndi cholinga chopandukira Mlengi.—Yakobo 1:14.
5 Satana Mdyerekezi anapitiriza kulankhula kwa Hava nati: “Kufa simudzafayi; chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:4, 5) Satana anachititsa kuti kudya zipatso za mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa kuoneke kokhumbirika. Kwenikweni iye anatanthauza kuti: ‘Mulungu akukubisirani kanthu kena kabwino. Ingodyanitu za mtengowu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu ndiponso mudzakhoza kudzisankhira nokha zabwino ndi zoipa.’ Lerolino, Satana akugwiritsabe ntchito kalingaliridwe kameneka pofuna kulepheretsa ambiri kuti asatumikire Mulungu: ‘Ingochitani zimene mukufuna,’ iye amatero. ‘Iŵalani za udindo wanu kwa Uyo amene anakupatsani moyo.’—Chivumbulutso 4:11.
6 Basi pamenepo zipatso za mtengo uja zinaoneka zosiririka ndi zosakanika! Hava anathyola chipatso chija, nadya, napatsa china mwamuna wake. Ngakhale kuti Adamu anadziŵa bwino lomwe zotsatira zake, iye anamvera mawu a mkazi wake nadyanso chipatso chija. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Kwa mkaziyo, Yehova anapereka chiweruzo ichi: “Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” Ndipo kwa mwamunayo anati: “Nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo: m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” Tsopano zinawatsalira okha Adamu ndi Hava kuti adzipezere okha chimwemwe ndi moyo wokhutira m’njira imene anaifuna eni akewo. Kodi iwo akathadi kupeza moyo wokhutiritsa mwa nzeru yaumunthu mosayendera chifuniro cha Mulungu? Ntchito yawo yosangalatsa yosamalira munda wokongola wa Paradaiso ndi youfutukulira kumalekezero a dziko lapansi inatha. M’malo mwake anakhala ndi ntchito yotopetsa ndi yokhaulitsa kungoti akhale ndi moyo basi, popanda kuchita chilichonse cholemekeza Mlengi wawo.—Genesis 3:6-19.
7. Kodi n’chiyani chimachitika kwa munthu akamwalira?
7 M’tsiku limene anadya zipatso za mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa, banja laumunthu loyambiriralo linafa m’maso mwa Mulungu ndipo linaloŵa panjira ya ku imfa yakuthupi. Kodi chinachitika kwa iwo n’chiyani atamwalira potsirizira pake? Baibulo limatiunikira za mkhalidwe wa akufa. “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, sadzalandira mphoto; pakuti angoiŵalika.” (Mlaliki 9:5; Salmo 146:4) Munthu akamwalira, sipakhalanso chinthu china chotchedwa “mzimu” chimene chimakhalabe ndi moyo. Chilango cha uchimo ndi imfa, osati chizunzo chosatha m’helo woyaka moto ayi. Ndiponso, imfa siitsegulira munthu khomo la ku mtendere wamuyaya kumwamba ayinso.a
8. N’chifukwa chiyani tonse timafa?
8 Mmene chiwaya chophikira keke chotiwama chimatulutsira keke yotiwamanso, ndi mmenenso mwamuna ndi mkazi opanda ungwiro anaberekera ana opandanso ungwiro. Baibulo limafotokoza mkhalidwe umenewu kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Choncho, tonsefe timabadwa mu uchimo, ndipo timakhala opanda pake. Moyo unakhala wogwetsa ulesi ndi wotopetsa kwa ana a Adamu. Koma kodi ilipo njira yotulukira m’tsoka limeneli?
[Mawu a M’munsi]
a Mudzapeza mfundo zosangalatsa zonena za akufa m’kabuku kachingelezi kakuti: What Happens to Us When We Die?, kofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.