NKHANI YOPHUNZIRA 10
Chikundiletsa Kubatizidwa N’chiyani?
“Filipo ndi nduna ija, anatsika ndi kulowa m’madzimo ndipo anaibatiza.”—MAC. 8:38.
NYIMBO NA. 52 Kudzipereka Monga Mkhristu
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi zimene Adamu ndi Hava anachita zinabweretsa mavuto otani?
KODI inuyo mumaona kuti ndi ndani amene ayenera kutiuza kuti ichi n’choyenera, ichi n’cholakwika? Pamene Adamu ndi Hava anadya chipatso cha mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa, anasonyeza kuti sankakhulupirira Yehova komanso mfundo zake. Iwo anaona kuti angathe kumasankha okha kuti izi n’zabwino, izi n’zoipa. (Gen. 3:22) Koma zotsatira zake zinali zoipa kwambiri. Iwo anataya ubwenzi wawo ndi Yehova, mwayi wokhala ndi moyo wosatha ndipo anapatsira ana awo uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Zimene anasankha zinabweretsa mavuto osaneneka.
2-3. (a) Kodi nduna ya ku Itiyopiya inatani Filipo atailalikira? (b) Kodi munthu akabatizidwa amapeza madalitso ati, nanga tikambirana mafunso ati?
2 Zimene Adamu ndi Hava anachita n’zosiyana ndi zimene nduna ya ku Itiyopiya inachita italalikiridwa ndi Filipo. Ndunayi inayamikira kwambiri zimene Yehova ndi Yesu anaichitira ndipo sinachedwe kubatizidwa. (Mac. 8:34-38) Tikadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa, ngati mmene anachitira munthu wa ku Itiyopiyayu, timasonyezanso kuti timayamikira zimene Yehova ndi Yesu atichitira. Timasonyezanso kuti timadalira Yehova ndipo timazindikira mfundo yoti iye ndi woyenera kutiuza kuti izi n’zoyenera izi n’zolakwika.
3 Pali madalitso ambiri amene timapeza chifukwa chotumikira Mulungu. Mwachitsanzo, tili ndi chiyembekezo chodzapeza zinthu zonse zimene Adamu ndi Hava anataya monga moyo wosatha. Tikamakhulupirira Yesu Khristu, Yehova amatikhululukira machimo athu ndipo timakhala ndi chikumbumtima chabwino. (Mat. 20:28; Mac. 10:43) Timakhalanso m’banja la atumiki a Mulungu n’kumayembekezera madalitso ambirimbiri. (Yoh. 10:14-16; Aroma 8:20, 21) Anthu ena amadziwa bwinobwino za madalitso amenewa koma safuna kuchita zinthu ngati mmene inachitira nduna ya ku Itiyopiya ija. Kodi chimawalepheretsa kubatizidwa n’chiyani? Nanga angathane bwanji ndi mavuto amene amawalepheretsawo?
MAVUTO AMENE AMALEPHERETSA ANTHU KUBATIZIDWA
4-5. Kodi Avery ndi Hannah anali ndi mavuto otani?
4 Kudzikayikira. M’bale wina dzina lake Avery anabadwira m’banja la Mboni. Bambo ake ndi mkulu wabwino komanso amasamalira bwino banja lawo. Koma Avery sankafuna kubatizidwa. Pofotokoza chifukwa chake, iye anati: “Ndinkaona kuti sindingakwanitse kuchita zinthu ngati mmene bambo anga amachitira.” Iye ankaonanso kuti ngati angapatsidwe maudindo sangakwanitse kuwasamalira bwino. Iye anati: “Ndinkaona kuti sindingathe kupemphera pagulu, kukamba nkhani kapena kutsogolera anthu mu utumiki wakumunda.”
5 Mlongo wina wazaka 18, dzina lake Hannah, ankadzikayikiranso kwambiri. Iye anakuliranso m’banja la Mboni. Koma ankakayikira zoti angakwanitse kumatsatira mfundo za Yehova pa moyo wake. Hannah ankadziona kuti ndi munthu wachabechabe. Zinafika poti nthawi zina ankadzivulaza ndipo izi zinkangowonjezera mavuto. Iye anati: “Zimene ndinkachitazi sindinauze aliyense ngakhale makolo anga. Ndinkaganiza kuti Yehova sangandikondenso chifukwa cha zimene ndinkadzichitirazi.”
6. N’chiyani chinkalepheretsa Vanessa kuti abatizidwe?
6 Anthu ocheza nawo. Mlongo wina wazaka 22 dzina lake Vanessa anati: “Ndinali ndi mnzanga wapamtima ndipo tinkacheza limodzi kwa zaka pafupifupi 10.” Koma mnzakeyu sanasangalale atamva kuti Vanessa akufuna kubatizidwa. Zimenezi zinamupweteka kwambiri moti ananena kuti: “Zimandivuta kupeza anzanga, ndiye ndinkaopa kuti ndikasiya kucheza naye sindidzapezanso mnzanga wina wapamtima.”
7. Kodi Makayla ankaopa chiyani, nanga mantha akewa anayamba bwanji?
7 Kuopa kuti adzalakwitsa zinthu. Chitsanzo china ndi cha mtsikana wina dzina lake Makayla. Iye ali ndi zaka 5, mchimwene wake anachotsedwa mumpingo. Ndipo pamene ankakula ankaona mavuto amene anabwera m’banja lawo chifukwa cha zochita za mchimwene wakeyo. Makayla anati: “Ndinkaopa kuti nanenso ndikabatizidwa ndidzalakwitsa zinazake n’kuchotsedwa ndipo makolo anga adzakhumudwa kwambiri.”
8. Kodi vuto la Miles linali lotani?
8 Kuopa kutsutsidwa. Bambo a Miles ndi mayi ake omupeza ndi a Mboni koma mayi ake enieni si a Mboni. Iye anati: “Ndakhala ndi mayi anga kwa zaka 18 koma ndinkaopa kuwauza kuti ndikufuna kubatizidwa. Ndinaona zomwe anachita pa nthawi imene bambo anga anakhala a Mboni. Ndinkaopa kuti adana nazo kwambiri ndipo ndizunzika.”
KODI MUNGATHANE BWANJI NDI MAVUTO AMENEWA?
9. Kodi chingachitike n’chiyani munthu akazindikira chikondi ndi kuleza mtima kwa Yehova?
9 Adamu ndi Hava analephera kutumikira Yehova chifukwa choti sankamukonda kwambiri. Koma Yehova anawalolabe kupitiriza kukhala ndi moyo, kubereka ana komanso kusankha okha njira yolerera ana awowo. Pasanapite nthawi yaitali, zinaonekeratu kuti zimene anasankha zinali zopusa kwambiri. Mwana wawo woyamba anapha m’bale wake ndipo anthu ambiri anali achiwawa komanso odzikonda. (Gen. 4:8; 6:11-13) Koma Yehova anakonza njira yopulumutsira ana a Adamu ndi Hava amene ankafunitsitsa kumutumikira. (Yoh. 6:38-40, 57, 58) Apatu tingati Yehova anasonyeza chikondi komanso kuleza mtima. Mukamaphunzira zokhudza makhalidwe amenewa mudzayamba kukonda kwambiri Yehova. Mtima womukondawu udzakuthandizani kuti mudzipereke kwa Yehova n’kumapewa kuchita zimene Adamu ndi Hava anachita.
10. Kodi kuganizira lemba la Salimo 19:7 kungakuthandizeni bwanji kuti muzitumikira Yehova?
10 Pitirizani kuphunzira za Yehova. Munthu akamaphunzira kwambiri za Yehova sakayikira zoti akhoza kumutumikira bwinobwino. Avery amene tamutchula uja anati: “Ndinalimba mtima nditawerenga komanso kuganizira kwambiri lonjezo la pa Salimo 19:7.” (Werengani.) Avery ataona umboni wa zimene zili palembali anayamba kukonda kwambiri Yehova. Zimenezi zikusonyezeratu kuti munthu akamakonda Yehova amafunitsitsa kumusangalatsa komanso kumutumikira. Hannah amene tamutchula kale uja anati: “Kuphunzira Baibulo komanso kusinkhasinkha kunandithandiza kuzindikira kuti Yehova sasangalala ndikamadzivulaza.” (1 Pet. 5:7) Kenako Hannah anayamba kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Yak. 1:22) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anati: “Nditaona kuti kumvera Yehova kukundithandiza, ndinayamba kumukonda kwambiri. Panopa sindikayikira ngakhale pang’ono kuti Yehova azindithandiza pa nthawi iliyonse imene ndikufunikira thandizo.” Hannah anasiya kudzivulaza ndipo anadzipereka kwa Yehova kenako anabatizidwa.
11. Kodi n’chiyani chinathandiza Vanessa kuti akhale ndi anzake abwino, nanga ife tikuphunzirapo chiyani?
11 Muzisankha bwino anthu ocheza nawo. Vanessa amene tamutchula kale uja anazindikira kuti mnzake ndi amene ankamulepheretsa kubatizidwa. Choncho anasiya kucheza naye. Komatu si zokhazi zimene anachita. Anapezanso anzake atsopano mumpingo. Mlongoyu ananena kuti chitsanzo cha Nowa ndi banja lake n’chimene chinamuthandiza. Iye anati: “Nowa ndi banja lake ankakhala limodzi ndi anthu osakonda Yehova koma iwowo ankagwirizana m’banja lawo.” Vanessa anabatizidwa kenako anayamba upainiya. Iye anati: “Chitsanzo chimenechi chandithandiza kuti ndipeze anzanga mumpingo wathu komanso m’mipingo ina yachikhristu.” Kuti nanunso mupeze anzanu apamtima, muyenera kugwira mwakhama ntchito imene Yehova watipatsa.—Mat. 24:14.
12. Kodi Adamu ndi Hava analibe mantha ati, nanga zotsatira zake zinali zotani?
12 Mantha anu azikhala oyenera. Kunena zoona, mantha ena ndi abwino. Mwachitsanzo, ndi bwino kuopa kukhumudwitsa Yehova. (Sal. 111:10) Adamu ndi Hava akanakhala ndi mantha amenewa si bwenzi atachimwa. Iwo atachita zimene Mulungu anawaletsa, maso awo anatseguka, kutanthauza kuti anazindikira kuti ndi ochimwa. Kuyambira pamenepo, chimene akanapatsira ana awo ndi uchimo ndi imfa basi. Chifukwa chozindikira vuto lawoli, anayamba kuchita manyazi kuti sanavale ndipo anasoka masamba n’kuvala.—Gen. 3:7, 21.
13-14. (a) Malinga ndi 1 Petulo 3:21, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa kwambiri imfa? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda Yehova?
13 Taona kuti tiyenera kuopa Yehova moyenera koma sitiyenera kuopa kwambiri imfa. Yehova wakonza kale njira yotithandiza kuti tidzapeze moyo wosatha. Ngati tachimwa n’kulapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova amaiwala nkhaniyo. Iye amatikhululukira chifukwa choti timakhulupirira nsembe ya Mwana wake. Njira yaikulu imene timasonyezera kuti tili ndi chikhulupiriro ndi kudzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa.—Werengani 1 Petulo 3:21.
14 Anthufe tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kukonda Yehova. Sikuti amangotipatsa zofunika pa moyo wathu tsiku lililonse koma amatiphunzitsanso mfundo zoona zokhudza iyeyo komanso zolinga zake. (Yoh. 8:31, 32) Iye watipatsanso mpingo wachikhristu kuti uzititsogolera komanso kutithandiza. Amatithandizanso kuti tipirire mavuto amene timakumana nawo panopa komanso watipatsa chiyembekezo choti tidzakhale ndi moyo wosatha tili angwiro. (Sal. 68:19; Chiv. 21:3, 4) Tikaganizira zinthu zambiri zimene Yehova watichitira chifukwa cha chikondi timalimbikitsidwa kuti nafenso tizimukonda. Ndiyeno kukonda Yehova kumatithandiza kuti tizikhala ndi mantha oyenera n’kumaopa kumukhumudwitsa.
15. N’chiyani chinathandiza Makayla kuti asiye kuopa kuti adzalakwitsa zinazake?
15 Makayla amene tamutchula kale uja anasiya kuopa kuti adzalakwitsa zinazake atazindikira kuti Yehova amakhululuka ndi mtima wonse. Iye anati: “Ndinazindikira kuti tonsefe ndi ochimwa ndipo tikhoza kulakwitsa zinthu zina. Koma ndinazindikiranso kuti Yehova amatikonda ndipo angatikhululukire chifukwa cha dipo.” Kukonda Yehova kunamuthandiza kuti adzipereke kwa iye n’kubatizidwa.
16. Kodi Miles anathandizidwa bwanji kuti asaope kutsutsidwa?
16 Miles, amene ankaopa kuti mayi ake adzakwiya akamva zoti akufuna kubatizidwa, anapempha thandizo kwa woyang’anira dera. Miles anati: “Mayi a woyang’anira derayo sanali a Mboni. Choncho iye anandithandiza kuganizira mfundo zimene ndingakauze mayi anga kuti adziwe kuti si bambo anga amene akundikakamiza kuti ndibatizidwe koma ndasankha ndekha.” Mayi ake a Miles anakwiyadi atamva zimene mwana wawo anasankha. Izi zinachititsa kuti achoke pakhomo pa mayi akewo, koma sanasinthe maganizo ake. Iye anati: “Ndinakhudzidwa kwambiri nditazindikira zinthu zabwino zambirimbiri zimene Yehova wandichitira. Kuganizira kwambiri za dipo la Yesu kunandithandiza kuzindikira kuti Yehova amandikonda kwambiri. Mfundo imeneyi inandithandiza kuti ndidzipereke kwa Yehova ndi kubatizidwa.”
MUSASINTHE MAGANIZO ANU
17. Kodi tili ndi mwayi wotani?
17 Pamene Hava anadya chipatso choletsedwa, anasonyeza kuti sankafuna kutsogoleredwa ndi Atate ake. Nayenso Adamu atadya chipatsochi anasonyeza kuti sankayamikira zinthu zabwino zambirimbiri zimene Yehova anamuchitira. Tonsefe tili ndi mwayi wosonyeza kuti sitigwirizana ndi zimene Adamu ndi Hava anasankha. Tikabatizidwa, timasonyeza kuti timavomereza kuti Yehova ndi woyenera kutiuza kuti izi n’zabwino, izi n’zoipa. Timasonyezanso kuti timakonda Yehova komanso kumukhulupirira.
18. Kodi mungatani kuti zinthu zizikuyenderani bwino potumikira Yehova?
18 Munthu akabatizidwa, nkhani tsopano imakhala yoti aziyendera mfundo za Yehova tsiku lililonse osati zake. Izi n’zimene anthu mamiliyoni ambiri akuchita masiku ano. Nanunso mukhoza kuchita zimenezi. Chinsinsi chake ndi kuyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu, kusonkhana nthawi zonse komanso kuchita khama pouza ena mfundo zokhudza Atate wanu zimene mwaphunzira. (Aheb. 10:24, 25) Mukafuna kusankha zochita, muziganizira malangizo amene Yehova wapereka kudzera m’Mawu ake ndi gulu lake. (Yes. 30:21) Mukamachita zimenezi, zinthu zidzakuyenderani bwino.—Miy. 16:3, 20.
19. Kodi tiyenera kupitiriza kuzindikira chiyani, nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?
19 Mukamazindikira ubwino wotsatira malangizo a Yehova m’pamene mumayambanso kumukonda kwambiri ndiponso kukonda mfundo zake. Zikatero, chilichonse chimene Satana angakunyengerereni nacho sichidzakupangitsani kuti musiye Yehova. Kodi mukuganiza kuti mungamve bwanji mutakhala zaka zina 1000 kuchokera panopa? Mudzaona kuti munachita bwino kwambiri kudzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa.
NYIMBO NA. 28 Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova
a Kusankha kuti mubatizidwe kapena ayi ndi nkhani yaikulu kwambiri kuposa nkhani ina iliyonse. Munkhaniyi tikambirana chifukwa chake tikunena zimenezi. Ithandizanso anthu amene akufuna kubatizidwa kuthana ndi mavuto amene angawalepheretse kuchita zimenezi.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kudzikayikira: Wachinyamata akuopa kuyankha
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Anzathu: Mlongo ali ndi mnzake amene amamupangitsa kuti asabatizidwe ndipo akuchita manyazi ataona a Mboni anzake.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kuopa kulakwitsa: Mtsikana akuopa kulakwitsa zinthu chifukwa choti mchimwene wake anachotsedwa.
e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kutsutsidwa: Mnyamata akuopa kupemphera chifukwa chakuti mayi ake, omwe si Mboni, akumuyang’ana.
f MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kudzikayikira: Wachinyamata akuphunzira kwambiri payekha
g MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Anzathu: Mlongo akuyamba kunyadira kuti ndi wa Mboni za Yehova.
h MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kuopa kulakwitsa: Mtsikana wayamba kukonda choonadi ndipo wabatizidwa.
i MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kutsutsidwa: Mnyamata walimba mtima ndipo akufotokozera mayi ake, omwe si Mboni, zimene amakhulupirira.