Mavuto A Banja—Chizindikiro cha Nthaŵi
MAVUTO a banja—ambiri amawalingalira kukhala chizindikiro chakuti malamulo amwambo a ukwati ndi kulera ana zakhala zachikale. Ena amawawona kukhala chotulukapo cha kusintha kwa ndale za dziko, zachuma, ndi kakhalidwe ka chitaganya. Ndiponso ena amawawona kukhala ngozi inanso ya luso la zopangapanga lamakono. Kwenikweni mavuto amene mabanja amalimbana nawo lerolino amasonyeza kanthu kena ka tanthauzo lalikulu kwambiri. Tamvani mawu a m’Baibulo pa 2 Timoteo 3:1-4:
“Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”
Kodi mawuŵa samafika pamuzu penipeni pa mavuto a lerolino? Mavuto a banja la lerolino mwachiwonekere ndiwo chotulukapo cha mikhalidwe yonenedweratu kudzachitika m’masiku otsiriza a dziko lino. Ndipo pali umboni wotsimikizirika wakuti nyengo ino ya mavuto inayamba mu 1914.a Chiyambire pamenepo, chisonkhezero cha cholengedwa chauzimu champhamvu yoposa ya anthu chotchedwa Satana Mdyerekezi makamaka chakhala chakupha.—Mateyu 4:8-10; 1 Yohane 5:19.
tatsekerezedwa kuchigawo cha dziko lapansi chiyambire 1914, Satana wakhala ali “nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:7-12) Popeza kuti Satana ndiye mdani wolumbilirana wa Mulungu “amene kuchokera kwa iye fuko lonse la m’mwamba ndi la padziko alitcha dzina,” kodi nkodabwitsa kuti dziko lapansi lakhala malo aupandu kwa mabanja? (Aefeso 3:15) Satana ngwotsimikizira kuchotsa anthu onse kwa Mulungu. Kodi ndim’njira ina itinso yabwino kwambiri imene akanachitira zimenezi kuposa mwa kugwiritsira ntchito mavuto kuukira mabanja?
Kudzatofunikira zoposa nthanthi zachiphamaso za akatswiri otchuka kutetezera mabanja pakuukiridwa koposa kwaumunthu koteroko. Komabe, Baibulo ponena za Satana limati: “Sitikhala osadziŵa machenjerero ake.” (2 Akorinto 2:11) Pali mlingo wakutiwakuti wa chitetezero m’kudziŵa njira zina zenizeni zimene amaukira nazo.
Ndalama ndi Ntchito
Chitsenderezo cha chuma ndicho chimodzi cha zida zamphamvu za Satana za kuukira. Zino ndizo “nthaŵi zoŵaŵitsa,” kapena monga momwe Revised Standard Version imanenera 2 Timoteo 3:1 kuti, “nthaŵi ya mavuto.” M’maiko osatukuka, mavuto onga ngati kusoŵeka kwa ntchito, malipiro ochepa, ndi kuchepa kwa zofunika zazikulu kumachititsa mavuto ambiri m’mabanja. Komabe, ngakhale ku United States wolemerayo, zitsenderezo za chuma ziri ndi chiyambukiro chachikulu. Kufufuza kwina kwa United States kunavumbula kuti ndalama ndizo chimodzi cha zochititsa mkangano m’banja. Bukhu lakuti Secrets of Strong Families limafotokoza kuti “nthaŵi, chisamaliro, [ndi] nyonga” zoperekedwa m’kukwaniritsa zofunikira za ntchito zingakhalenso “mdani wosadziŵika” amene amanyonyotsola thayo la muukwati.
Mikhalidwe yakakamiza ziŵerengero zazikulu za akazi kuloŵa ntchito. Mlembi wina Vance Packard akusimba kuti: “Pakali pano, osachepera pagawo limodzi mwa anayi a makanda a ku Amereka ndi ana ongoyamba kumene kuyenda a pansi pa zaka zitatu ali ndi amayi amene amagwira ntchito yapambali ya mtundu wina wakutiwakuti.” Kusamalira zofunika zimene ziri pafupifupi zosatheka kuzikwaniritsa za ana aang’ono ndiponso kugwira ntchito kungakhale mchitidwe wosakondweretsa ndi wotopetsa—wokhala ndi ziyambukiro zoipa kwa makolo ndi ana omwe. Packard akuwonjezera kuti chifukwa cha kuchepa kwa makonzedwe a chisamaliro choyenera cha ana mu United States, “lerolino ana mamiliyoni oŵerengeka samasamaliridwa bwino m’zaka zawo zoyambirira.—Our Endangered Children.
Kaŵirikaŵiri malo ogwirirako ntchito enieniwo amafooketsa chimvano cha banja. Antchito ambiri amakokeredwa m’machitachita achisembwere ndi ogwira nawo ntchito. Ndiponso ena amatanganitsidwa m’kufunafuna chipambano kosaphula kanthuko ndi kunyanyala moyo wabanja kaamba ka kupititsa patsogolo ntchito yodzisankhira. (Yerekezerani ndi Mlaliki 4:4.) Mwamuna wina anakhala womwerekera kwambiri muntchito yake monga wosatsa malonda mwakuti mkazi wake anadzifotokoza kukhala “kholo lokwatiŵa koma lolera lokha ana.”
Zomangira za Muukwati Zofooketsedwa
Chigwirizano cha ukwati chenichenicho chaaukiridwanso. Likutero bukhu lakuti The Intimate Environment: “Kalero, chiyembekezo chinali chakuti okwatirana akakhalira limodzi kusiyapo ngati mmodzi wa okwatiranawo wapalamula mlandu waukulu molakwira ukwati—chigololo, nkhanza, kunyalanyaza kwakukulu. Tsopano anthu ambiri amawona chifuno cha ukwati kukhala cha kudzikhutiritsa.” Inde, ukwati umawonedwa monga mankhwala ochiritsira kupanda chimwemwe, kusungulumwa, kapena kusukidwa—osati monga kukhulupirika kwa munthu wina m’moyo wonse. Tsopano lino chifuno chimakhala pazimene mungapeze muukwati, osati pazimene mungapatse muukwati. (Siyanitsani ndi Machitidwe 20:35.) “Kusintha kwakukulu kumeneku m’mapindu aukwati” kwafooketsa kwambiri zomangira za ukwati. Pamene alephera kupeza zowakhutiritsazo, kaŵirikaŵiri okwatiranawo amatembenukira kuchisudzulo monga yankho lofulumira.
‘M’masiku otsiriza’ ano athu amafotokozedwa mwaulosi m’Baibulo kukhala “akukhala nawo mawonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.” (2 Timoteo 3:4, 5) Akatswiri ambiri amalingalira kuti kunyonyotsoka kwa makhalidwe m’chipembedzo kwakhala ndi mbali m’kululuza ukwati. M’bukhu lake lakuti The Case Against Divorce, Dr. Diane Medved analemba kuti: “Malinga ndi zipembedzo zochuluka, Mulungu anati ukwati unayenera kukhala wachikhalire. Pamene mumakayikira Mulungu kapena simumkhulupirira Iye, pamenepo mumachita zimene mufuna.” Monga chotulukapo, pamene ukwati uli ndi mavuto, okwatiranawo samafunafuna zothetsera zoyenerera. “Amangothetsa ukwatiwo.”
Achichepere Aukiridwa
Ana akuvutika ndi zitsenderezo za lerolino. Ziŵerengero zazikulu mochititsa mantha za ana zimamenyedwa mwachiwawa ndi kutukwanidwa kapena kuipitsidwa mwa kugonedwa ndi makolo awo. Kupyolera mwa chisudzulo, mamiliyoni owonjezereka amamanidwa chisonkhezero chachikondi cha makolo aŵiri, ndipo kupwetekedwa mtima ndi chisudzulo cha makolo kaŵirikaŵiri zimakhalapo m’moyo wawo wonse.
Achichepere amakanthidwa ndi zisonkhezero zamphamvu. Podzafika zaka 14 zakubadwa wachichepere wa ku Amereka amakhala atawona kuphedwa kwa anthu 18,000 ndi mitundu ina yosaŵerengeka ya chiwawa, kugonana kosaloleka, nkhanza, ndi upandu mwakungowonerera wailesi yakanema. Nyimbo zirinso ndi mphamvu pa achichepere, ndipo zambiri za izo nzoluluza, zachisembwere, kapena zokhaladi ndi mawu ausatana. Masukulu amaphunzitsa achichepere nthanthi zonga za chisinthiko zimene zimaluluzitsa kukhulupirira Mulungu ndi Baibulo. Chitsenderezo cha anzawo chimasonkhezera ambiri kudziloŵetsa m’kugonana asanakonzekere ukwati ndi kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa kapena mankhwala oledzeretsa.
Mizu ya Mavuto a Banja
Chifukwa cha chimenecho chiukiro pamabanja nchachikulu ndipo chingakhale chowononga. Kodi nchiyani chimene chingathandizire mabanja kupulumuka? Mlangizi wa banja John Bradshaw akupereka lingaliro lakuti: “Malamulo athu olerera ana sanasinthidwe mwamphamvu m’zaka 150 zapitazi. . . . Chikhulupiriro changa nchakuti malamulo akale sakugwiranso ntchito.” Komabe, malamulo ambiri opangidwa ndi anthu sali yankho. Yehova Mulungu ndiye Woyambitsa banja. Amadziŵa bwino kwambiri koposa wina aliyense mmene mbali ya moyo wa banja iliri yofunika kaamba ka chimwemwe chathu ndi zimene zimafunika kupangitsa banja kukhala lachimwemwe ndi lolimba. Kodi ziyenera kutidabwitsa kuti Mawu ake, Baibulo, amapereka yankho la mavuto a banja?
Bukhu lakalelo limafotokoza mmene moyo wa banja unakhotera. Anthu okwatirana oyambawo, Adamu ndi Hava, anaikidwa m’kakonzedwe ka munda wokongola ndi kupatsidwa chitokoso chopereka mphotho cha kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso wadziko lonse. Mulungu analamula kuti Adamu anali kudzakhala mutu wabanja. Hava anafunikira kuchita mogwirizana ndi umutu wake monga “womthangatira,” kapena ‘womkwaniritsa.’ Koma Hava anapandukira kakonzedwe kameneka. Analanda umutu wa mwamuna wake ndi kusamvera chiletso chimodzi chokhacho chimene Mulungu anawaikira. Pamenepo Adamu anavula umutu wake ndi kugwirizana naye m’chipanduko chimenechi.—Genesis 1:26–3:6.
Ziyambukiro zowononga za kupandukira kakonzedwe ka Mulungu kameneka zinawonekera nthaŵi yomweyo. Posakhalanso oyera ndi opanda chifukwa, Adamu ndi Hava anayankha mwamanyazi ndi liwongo. Adamu, amene poyambirirapo anafotokoza mkazi wake m’mawu a ndakatulo yachikondi, tsopano ndi mawu amphwayi anamtchula kuti ‘mkazi amene munandipatsa.’ Mawu osasangalatsa amenewo analidi chiyambi cha mavuto a m’banja. Zoyesayesa zosaphula kanthu za Adamu kuti apeze umutu wake zikachititsa ‘kulamulira mkaziyo.’ Nayenso Hava, akakhala ‘akukhumba’ mwamuna wake, mwinamwake m’njira yomkitsa kapena yosadekha.—Genesis 2:23; 3:7-16.
Mosadabwitsa, mavuto a muukwati wa Adamu ndi Hava anali ndi chiyambukiro chowononga pa mbadwa zawo. Mwana wawo wachisamba, Kaini, anakhala munthu wambanda wouma mtima. (Genesis 4:8) Lameki, mbadwa ya Kaini, anawonjezera kunyonyotsoka kwa moyo wa banja mwa kukhala munthu wamitala woyamba m’mbiri. (Genesis 4:19) Motero Adamu ndi Hava anapatsira osati kokha choloŵa cha uchimo ndi imfa komanso mtundu wa banja lodwala umene wakhala mkhalidwe wa mtundu wa anthu chiyambire pamenepo. M’masiku otsiriza ano, kusagwirizana kwa banja kwafika pamlingo waukulu kuposa ndi kale lonse.
Mabanja Amene Amapita Patsogolo
Komabe, simabanja onse amene amagonjera kuzitsenderezo za lerolino. Mwachitsanzo, mwamuna wina, amakhala ndi mkazi wake ndi ana ake aakazi aŵiri m’chitaganya chaching’ono mu United States. Ngakhale kuti anansi awo ambiri ali ndi mpata wa mbadwo pakati pa makolo ndi ana awo, iyeyo ndi mkazi wake alibe, samada nkhaŵa ndi kuti ana awo aakaziwo angafune kuyesa mankhwala oledzeretsa kapena kugonana. Madzulo a Lolemba, pamene ana ena amakhala akuwonerera wailesi yakanema, banja lawo lonselo limasonkhana pagome m’chipinda chochezera kudzakambitsirana za m’Baibulo. “Madzulo a Lolemba ndiwo apadera kwa ife kuti tisonkhane ndi kukambitsirana,” iye akufotokoza motero. “Ana athu aakaziwo amakhala omasuka kulankhula nafe mavuto a kukhosi kwawo.”
Kumbali ina, pali kholo lina lolera ana lokha mu New York City limene limasangalalanso ndi mgwirizano wabanja wosawonekawonekawo ndi ana ake aŵiri aakazi. Kodi chinsinsi chake nchiyani? “Timatseka TV kufikira pakutha kwa mlungu,” iye akufotokoza motero. “Timakambitsirana lemba la tsiku la m’Baibulo. Timapatulanso pambali madzulo amodzi a kukambitsirana Baibulo ndi banja.”
Mabanja onse aŵiriwo ndi a Mboni za Yehova. Amatsatira uphungu wa mabanja woperekedwa m’Baibulo—ndipo umagwira ntchito. Komabe, siokhawo. Pali mazana zikwi zambiri za mabanja ofanana nawo amene akupindula mwa kugwiritsira ntchito malamulo a moyo wabanja opezeka m’bukhu limenelo.b Kodi malamulo amenewo nchiyani? Kodi angakupindulitseni motani ndi banja lanu? M’kuyankha tikukupemphani kuŵerenga nkhani zoyambira patsamba lotsatiralo.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani mutu 18 wa bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, kaamba ka umboni wina wakuti masiku otsiriza anayamba mu 1914, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Mwanjira ya phunziro lapanyumba la Baibulo laulere, Mboni za Yehova zimapereka chithandizo chaumwini m’kugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo m’banja. Zikhoza kuwonedwa mwa kulembera ofalitsa magazini ano.
[Chithunzi patsamba 4]
Mikhalidwe ya kusoŵa imachititsa chipsinjo chachikulu m’mabanja a m’maiko osatukuka
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzithunzi cha U.S. Navy
[Chithunzi patsamba 7]
Mwa kugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo, mabanja ambiri amakaniza zitsenderezo za lerolino