Achinyamata, Yesetsani Kulimbitsa Chikhulupiriro Chanu
“Chikhulupiriro ndicho . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.”—AHEB. 11:1.
1, 2. Kodi achinyamata ambiri amadzifunsa funso liti, nanga m’Baibulo muli malangizo otani?
MTSIKANA wina wa ku Britain anauza mtsikana wa Mboni kuti: “Zoona munthu wabwinobwinowe umakhulupirira zoti kuli Mulungu?” M’bale wina wachinyamata wa ku Germany analemba kuti: “Aphunzitsi anga amati nkhani ya m’Baibulo yonena kuti Mulungu analenga zinthu, ndi nthano chabe. Iwo amadabwa akaona kuti ana ena sakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.” Mtsikana wina wa Mboni wa ku France anati: “Aphunzitsi a kusukulu kwathu amadabwa akamva kuti pali ana ena amene amakhulupirirabe Baibulo.”
2 Masiku ano anthu ambiri sakhulupirira kuti kuli Mulungu. Ngati ndinu wachinyamata wa Mboni kapena mukuphunzira Baibulo, mwina mumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingamutsimikizire bwanji munthu kuti kuli Mlengi?’ Akhristufe timalimbikitsidwa kuti tiziganizira kwambiri zimene tamva kapena kuwerenga, kuti tidziwe ngati zili zoona kapena ayi. Paja Baibulo limati: “Kuganiza bwino kudzakuyang’anira.” Kuganiza bwino kungakuthandizeni kuti muzikana mfundo zabodza komanso kuti muzikhulupirira kwambiri Yehova.—Werengani Miyambo 2:10-12.
3. Kodi m’nkhaniyi tikambirana chiyani?
3 Kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chenicheni amafunika kudziwa zolondola zokhuza Mulungu. (1 Tim. 2:4) Choncho mukamaphunzira Baibulo kapena mabuku athu, musamathamange. Muzigwiritsa ntchito luso lanu lakuganiza n’cholinga choti muzindikire “tanthauzo” la zimene mukuwerengazo. (Mat. 13:23) M’nkhaniyi tiona kuti kuchita zimenezi kungakuthandizeni kutsimikizira kuti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse komanso kuti Baibulo ndi Mawu ake.
KODI MUNGALIMBITSE BWANJI CHIKHULUPIRIRO CHANU?
4. (a) Kodi munthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina amafanana bwanji ndi amene amakhulupirira kuti zinachita kulengedwa? (b) Koma kodi aliyense ayenera kuchita chiyani?
4 Mwina anthu ena anakuuzanipo kuti: “Ndimakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina chifukwa choti asayansi amanena choncho. N’chifukwa chiyani inu mumakhulupirira kuti kuli Mulungu ngati munamuonapo?” N’zoona kuti palibe munthu amene anaonapo Mulungu kapena kuona zinthu zikulengedwa. (Yoh. 1:18) Koma anthu amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, nawonso amakhulupirira zinthu zoti sanazionepo. Palibe wasayansi kapena munthu aliyense amene anaona chamoyo chikusintha n’kukhala chinthu china. Mwachitsanzo, palibe anaonapo buluzi akusintha n’kukhala mkango. (Yobu 38:1, 4) Choncho kaya munthu amakhulupirira zotani, ayenera kufufuza mokwanira komanso kugwiritsa ntchito luso lakuganiza kuti apeze umboni wa zimene amakhulupirirazo. Ponena za chilengedwe, mtumwi Paulo anati: “Chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu.”—Aroma 1:20.
5. Kodi gulu la Yehova limatithandiza bwanji kuti tizifufuza zinthu n’kuzidziwa bwino?
5 “Kuzindikira” kumatanthauza kudziwa zinthu zimene si zoonekeratu. (Aheb. 11:3) Choncho anthu ozindikira akaona kapena kumva zinthu amaziganizira kwambiri. Mwachitsanzo, tingathe kuona Mlengi wathu ndi maso achikhulupiriro tikaona zimene asayansi atulukira masiku ano. (Aheb. 11:27) Gulu la Yehova limatipatsa zinthu zambiri zotithandiza pa nkhani imeneyi. Zinthu zake ndi monga mavidiyo, mabuku komanso timabuku. (Mwachitsanzo pali vidiyo yakuti, The Wonders of Creation Reveal God’s Glory, buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You? komanso timabuku takuti, Was Life Created? ndi The Origin of Life—Five Questions Worth Asking.) Mfundo zinanso zothandiza zimapezeka m’magazini athu. Mwachitsanzo, mu Galamukani! nthawi zambiri mumakhala nkhani zofunsa asayansi komanso anthu ena omwe amafotokoza zimene zinawathandiza kuti ayambe kukhulupirira zoti kuli Mulungu. Mumakhalanso nkhani zakuti, “Kodi Zinangochitika Zokha?” ndipo zimafotokoza zinthu zachilengedwe zochititsa chidwi kwambiri. Masiku ano asayansi akamapanga zinthu zawo amayesetsa kutengera zam’chilengedwezi.
6. (a) Kodi zinthu zofufuzira zomwe tili nazo zingatithandize bwanji? (b) Kodi zinthu zimenezi zakuthandizani bwanji inuyo?
6 M’bale wina wazaka 19 wa ku United States anafotokoza zokhudza timabuku timene tatchula m’ndime 5. Anati: “Timabukuti ndinatiwerenga kambirimbiri ndipo tandithandiza kwabasi.” Mlongo winanso wa ku France analemba kuti: “Nkhani zakuti, ‘Kodi Zinangochitika Zokha?’ zimandisangalatsa kwambiri. Zimasonyeza kuti akatswiri akamapanga zinthu amayesetsa kutsanzira zimene zili m’chilengedwechi komabe safikapo.” Makolo ena a ku South Africa omwe ali ndi mwana wazaka 15 anati: “Mwana wathu akalandira Galamukani! amayamba n’kuwerenga nkhani zofunsa akatswiri amene anayamba kukhulupirira kuti kuli Mulungu.” Nanga inuyo mumakonda nkhani ziti? Kodi mumagwiritsa ntchito zinthu zonse zimene tili nazo kuti chikhulupiriro chanu chikhale ngati mtengo wa mizu yozika kwambiri pansi? Chikhulupiriro choterocho chingakuthandizeni kuti musamatengeke ndi ziphunzitso zabodza, zomwe tingaziyerekezere ndi mphepo.—Yer. 17:5-8.
KODI MUNGATANI KUTI MUZIKHULUPIRIRA KWAMBIRI BAIBULO?
7. N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti tizigwiritsa ntchito luntha la kuganiza?
7 Kodi n’kulakwa kufunsa mafunso okhudza Baibulo? Ayi. Yehova amafuna kuti tizigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza” kuti tizindikire ngati mfundo inayake ili yoona. Iye safuna kuti tizingokhulupirira zinthu chifukwa choti ena amazikhulupirira. Kodi inuyo mumagwiritsa ntchito luntha la kuganiza kuti mudziwe zolondola? Munthu akadziwa zolondola, m’pamene amakhala ndi chikhulupiriro cholimba. (Werengani Aroma 12:1, 2; 1 Timoteyo 2:4.) Kuti zimenezi zitheke, ndi bwino kusankha nkhani zinazake n’kufufuza zimene Baibulo limanena pa nkhanizo.
8, 9. (a) Kodi anthu ena amakonda kufufuza nkhani ziti m’Baibulo? (b) Kodi anthu ena apindula bwanji chifukwa choganizira kwambiri zimene aphunzira?
8 Anthu ena amasankha kuti afufuze maulosi a m’Baibulo kapena umboni woti ndi lolondola pa nkhani za sayansi kapena mbiri yakale. Ulosi wina wochititsa chidwi ndi wopezeka pa Genesis 3:15. Vesi limeneli limafotokoza mwachidule nkhani yaikulu m’Baibulo. Nkhani yake ndi yokhudza ulamuliro wa Yehova komanso mmene Ufumu udzayeretsere dzina lake. Pavesi limodzi lokhali Mulungu anafotokoza mophiphiritsira mmene adzathetsere mavuto onse amene anayamba mu Edeni. Kodi mungachite zinthu ziti pophunzira vesili? Mwina mungayambe ndi kulemba mzere wosonyeza nthawi. Kenako pamzerepo mungalembe mavesi komanso zinthu zimene Mulungu ananena pang’onopang’ono zosonyeza kuti ulosiwu udzakwaniritsidwa. Mukaona kugwirizana kwa malembawo, mungayambe kukhulupirira kwambiri kuti aneneri ndiponso anthu amene analemba Baibulo ‘ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera.’—2 Pet. 1:21.
9 M’bale wina wa ku Germany anachita chidwi kuona kuti buku lililonse la m’Baibulo lili ndi mfundo zina zokhudza Ufumu. Iye anati: “Zimenezi n’zodabwitsa chifukwa Baibulo linalembedwa ndi anthu osiyanasiyana okwana 40. Ndipotu ambiri mwa anthu amenewa anakhalako nthawi zosiyana ndipo sankadziwana n’komwe.” Mlongo wina wa ku Australia anachita chidwi atawerenga nkhani ya Pasika mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 2013. Mwambo umenewu ukugwirizana kwambiri ndi ulosi wa pa Genesis 3:15 komanso kubwera kwa Mesiya. Mlongoyu anati: “Kuphunzira za dipo kwandithandiza kudziwa kuti Yehova ndi wodabwitsa. N’zochititsa chidwi kuti iye anakonza zoti Aisiraeli azichita mwambowu ndipo zonse n’kudzakwaniritsidwa ndi Yesu. Nditafatsa n’kuiganizira nkhaniyi ndinaona kuti Yehova amakwaniritsa maulosi m’njira yodabwitsa.” N’chifukwa chiyani mlongoyu anamva chonchi? Iye anaganizira kwambiri zimene anawerenga n’kuzindikira “tanthauzo lake.” Izi zinamuthandiza kuti alimbitse chikhulupiriro chake komanso azikonda kwambiri Yehova.—Mat. 13:23.
10. Kodi kuona mtima kwa olemba Baibulo kumatithandiza bwanji kukhulupirira zimene analemba?
10 Olemba Baibulo anali olimba mtima komanso achilungamo. Kuganizira mfundo imeneyi kumalimbitsanso chikhulupiriro chathu. Tikutero chifukwa chakuti olemba mbiri akale ankalemba zotamanda dziko lawo ndi atsogoleri awo. Koma aneneri a Yehova ankanena zoona nthawi zonse. Iwo ankalemba zolakwa zimene anthu awo kapena mafumu awo ankachita. (2 Mbiri 16:9, 10; 24:18-22) Ankafotokozanso zimene iwowo komanso atumiki ena a Mulungu analakwitsa. (2 Sam. 12:1-14; Maliko 14:50) M’bale wina wa ku Britain anati: “Kuona mtima kotereku n’kosowa kwambiri ndipo kumatithandiza kutsimikizira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu.”
11. Kodi timadziwa bwanji kuti mfundo za m’Baibulo ndi zothandiza?
11 Ambiri amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu akaona mmene mfundo zake zimathandizira anthu. (Werengani Salimo 19:7-11.) Mlongo wina wa ku Japan analemba kuti: “Pamene aliyense m’banja lathu ankatsatira mfundo za m’Baibulo tinkasangalala. Tinkakondana kwambiri, tinkagwirizana komanso tinkakhala mwamtendere.” Mfundozi zimatitetezanso kuti tipewe miyambo ya zipembedzo zonyenga komanso kukhulupirira zamizimu. (Sal. 115:3-8) Tinganene kuti anthu amene amakhulupirira zoti kulibe Mlengi amaona zinthu zam’chilengedwe ngati milungu yawo. Iwo amaganiza kuti tsogolo lawo lonse lili m’manja mwawo. Koma vuto ndi lakuti sapereka chiyembekezo chilichonse kwa anthu.—Sal. 146:3, 4.
KODI MUNGAFOTOKOZERE BWANJI ENA ZIMENE MUMAKHULUPIRIRA?
12, 13. Kodi tingakambirane bwanji ndi anthu zokhudza chilengedwe kapena Baibulo?
12 Kodi mungatani kuti muthandize munthu amene mukukambirana naye zokhudza chilengedwe kapena Baibulo? Musafulumire kuganiza kuti mukudziwa zimene munthuyo amakhulupirira. Pali anthu ena amene amakhulupirira zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina, koma amakhulupiriranso kuti Mulungu alipo. Amakhulupirira kuti Mulungu anangochititsa kuti zinthu zina zisinthe n’kukhala zamoyo zosiyanasiyana. Ndiye pali ena amene amakhulupirira kuti mfundo yakuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina ikanakhala yabodza, si bwenzi ikuphunzitsidwa kusukulu. Pomwe ena anasiya kukhulupirira kuti kuli Mulungu chifukwa choti anakhumudwa ndi zimene zipembedzo zimachita. Choncho musanayambe kukambirana ndi munthu zokhudza mmene moyo unayambira, ndi bwino kumufunsa kaye mafunso kuti mudziwe zimene amakhulupirira. Mukamamvetsera pamene iye akufotokoza, zingapangitse kuti nayenso amvetsere inuyo mukamafotokoza.—Tito 3:2.
13 Kodi mungatani ngati munthu wanena kuti ndinu wopusa chifukwa mumakhulupirira kuti kuli Mlengi? Mwina mungamufunse kuti: ‘Kodi inuyo mumakhulupirira kuti moyo unayamba bwanji?’ Ndiyeno munganene kuti, ‘Mogwirizana ndi sayansi, ngati zamoyo zinayambira ku zinthu zina, ndiye kuti chinthu choyambacho chinafunika kupanganso zinthu zina.’ Katswiri wina anatchula zimene ziyenera kuchitika kuti chamoyo chisinthe n’kukhala chinthu china. Anati chingafunike kukhala ndi (1) khungu lochiteteza, (2) mphamvu zoti chizigwiritsa ntchito, (3) malangizo okhudza maonekedwe ndi kakulidwe komanso (4) chikhale choti chingathe kupanga zinthu zina. Katswiriyu ananenanso kuti: “Komatu munthu amagoma akaona mmene moyo unayambira, ngakhale wa tinthu ting’onoting’ono.”
14. Fotokozani zimene mungachite pokambirana mwachidule ndi munthu amene sakhulupirira kuti kuli Mlengi.
14 Ngati mukuona kuti simungathe kufotokoza zambiri pa nkhaniyi, mukhoza kungotchula mfundo yosavuta imene Paulo ananena. Iye anati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheb. 3:4) Chitsanzo chimenechi ndi chothandiza kwambiri. Tikaona chinthu chopangidwa mwaluso timadziwa kuti payenera kukhala winawake amene anachipanga. Mungathenso kugwiritsa ntchito buku kapena kabuku pokambirana ndi munthuyo. Mwachitsanzo, mlongo wina anagwiritsa ntchito timabuku tomwe tatchula poyamba tija pokambirana ndi mnyamata amene ankakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha ndipo ankati kulibe Mulungu. Patadutsa mlungu umodzi, mnyamatayo anati: “Tsopano ndayamba kukhulupirira kuti kuli Mulungu.” Kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndipo panopa ndi m’bale.
15, 16. Kodi mungakambirane bwanji mfundo za m’Baibulo ndi anthu, ndipo cholinga chanu chiyenera kukhala chiyani?
15 Mungathenso kugwiritsa ntchito njira yosavuta pokambirana ndi anthu amene amakayikira kuti Baibulo ndi lolondola. Yesani kudziwa zimene amakhulupirira ndipo kenako pezani nkhani zimene zingawachititse chidwi. (Miy. 18:13) Ngati amakonda sayansi, mungakambirane nawo mfundo zosonyeza kuti Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi. Ena angachite chidwi ndi mfundo zosonyeza kuti maulosi a m’Baibulo amakwaniritsidwa komanso Baibulo ndi lolondola pa nkhani ya mbiri yakale. Njira inanso n’kuwasonyeza mfundo za m’Baibulo zothandiza ngati zimene zimapezeka mu ulaliki wa Yesu wapaphiri.
16 Musaiwale kuti cholinga chanu ndi kuwafika pamtima osati kuwina mkangano. Choncho akamalankhula muzimvetsera. Muzifunsa mafunso abwino komanso muzilankhula mokoma mtima ndi mwaulemu, makamaka mukamalankhula ndi achikulire. Mukatero nawonso angamvetsere zimene mukunena. Angaonenso kuti zimene mukuwaphunzitsazo mukuzidziwa bwino ngakhale kuti ndinu wachinyamata. Koma ngati munthuyo akungofuna kuti muzitsutsana kapena ngati akukunyozani, ndi bwino kungomusiya.—Miy. 26:4.
INUYO PANOKHA MUZIKONDA CHOONADI
17, 18. (a) N’chiyani chingakuthandizeni kuti inuyo panokha muzikonda choonadi? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
17 Kuti munthu akhale ndi chikhulupiriro cholimba pamafunika zambiri osati kungodziwa mfundo zina za m’Baibulo. Choncho muzichita khama kufufuza mfundo za m’Mawu a Mulungu ngati mmene munthu amafufuzira chuma chobisika. (Miy. 2:3-6) Muzigwiritsa ntchito bwino Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani komanso zinthu zina zofufuzira. (Tikunena zinthu monga Watchtower Library ya pa DVD, LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower ndiponso Watch Tower Publications Index.) Ndi bwinonso kukonza zoti muwerenge Baibulo lonse mwina pomatha chaka chimodzi. Kunena zoona, kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kumathandiza kwambiri kuti chikhulupiriro chilimbe. Izi n’zimene zinathandiza woyang’anira dera wina pa nthawi imene anali wachinyamata. Iye anati: “Kuwerenga Baibulo lonse kunandithandiza kuti nditsimikizire zoti ndi lochokeradi kwa Mulungu. Ndinayamba kumvetsa nkhani za m’Baibulo zimene ndinaphunzira ndili mwana. Izi zinandithandiza kwambiri kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.”
18 Makolo ali ndi udindo waukulu pothandiza ana awo kuti azikonda kwambiri Yehova komanso kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Tidzakambirana nkhani imeneyi m’mutu wotsatira.