Mapangano Ophatikizapo Chifuno Chosatha cha Mulungu
“Yehova . . . akumbukira chipangano chake kosatha, mawuwo anawalamulira, mibadwo zikwi.”—SALMO 105:7, 8.
1, 2. Nchifukwa ninji tinganene kuti ambiri a ife tayambukiridwa ndi pangano?
MWACHIDZIŴIKIRE kwenikweni pangano lakuyambukirani inu—nthaŵi yanu ya kumbuyo, ya pakali pano, ndi ya mtsogolo. ‘Pangano lotani?’ inu mungadabwe tero. Mu nkhaniyi, uli ukwati, popeza kuti ambiri a ife ndife mbadwa za ukwati ndipo ambiri a ife ndife okwatira nafenso. Ngakhale awo omwe sanakwatirebe angaganizire ponena za madalitso a ukwati wachimwemwe mtsogolo.
2 Mazana angapo apitawo mneneri wa Chihebri Malaki analemba ponena za “mkazi wa ubwana wako,” “mnzako mkazi wa pangano lako.” (Malaki 2:14-16) Iye anakhoza kutcha ukwati pangano, popeza kuti limenelo ndi pangano kapena kumvana kwa lamulo, makonzedwe pakati pa mbali ziŵiri a kuchita chinachake mogwirizana. Kugwirizana kwa ukwati kuli pangano la mbali ziŵiri mu limene mbali ziŵirizo zimavomerezana kukhala mwamuna ndi mkazi, kulandira mathayo kulinga kwa wina ndi mnzake ndi kuyang’ana kutsogolo ku mapindu osatha.
3. Nchifukwa ninji mapangano ena angatiyambukire kuposa chikwati?
3 Ukwati ungawonekere kukhala pangano lokhala ndi kugwirizana kokulira kwaumwini pa ife, ndipo komabe Baibulo limakambitsirana mapangano a tanthauzo lokulira kwenikweni. M’kusiyanitsa mapangano a m’Baibulo ndi aja a zipembedzo zosakhala za m’Baibulo, encyclopedia imodzi yanena kuti kokha m’Baibulo “ndi mmene kulongosoka kwa unansi pakati pa Mulungu ndi anthu ake kumakhala m’dongosolo lomvekera bwino ndi tanthauzo lotheratu la chilengedwe chonse.” Inde, mapangano amenewa amaphatikizapo chifuno chosatha cha Mlengi wathu wachikondi. Monga mmene mudzawonera, kulandira kwanu madalitso osaneneka kwagwirizanitsidwa ndi mapangano amenewa. ‘Koma ndimotani mmene chimenecho chiriri tero?’ inu muli ndi chifukwa chofunsira.
4. Ndi pangano loyambirira liti limene limalozera ku chifuno chosatha cha Mulungu?
4 Inu mudziŵa bwino lomwe za zotulukapo zowawa pamene Adamu ndi Hava anakana ulamuliro wa Mulungu. Ife tinaloŵa kupanda ungwiro kuchokera kwa iwo, nsonga imene iri kumbuyo kwa kudwala kumene tavutika nako, ndi kumene kumatsogolera ku imfa. (Genesis 3:1-6, 14-19) Tingakhale oyamikira, ngakhale kuli tero, kuti chimo lawo silikanasintha chifuno cha Mulungu cha kudzaza dziko lapansi ndi alambiri owona osangalala ndi umoyo wosatha ndi chimwemwe. M’chigwirizano ndi ichi, Yehova anapanga pangano lolembedwa pa Genesis 3:15: “Ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Ndipo idzalalira mutu wako ndipo iwe udzalalira chitende chake.” Ngakhale kuli tero, ukulu ndi chinenero chophiphiritsira cha ndemanga imeneyi chinasiya mafunso ambiri osayankhidwa. Ndimotani mmene Yehova akakwaniritsira lonjezo la pangano limeneli?
5, 6. (a) Ndi njira iti imene Mulungu anagamulapo kugwiritsira ntchito m’kuchita chifuno chake? (b) Nchifukwa ninji tiyenera kukhala okondweretsedwa m’njira ya Mulungu ya kuchitira ichi?
5 Mulungu kenaka anasankha kukonzekera kaamba ka mpambo wapadera wa mapangano aumulungu, umene, ndi pangano la mu Edeni, umapanga asanu ndi aŵiri mwa onse. Aliyense wa ife woyembekezera kusangalala ndi madalitso osatha ayenera kumvetsetsa mapangano amenewa. Ichi chimaphatikizapo kudziŵa ndi liti ndi mmene iwo anapangidwira, ndani amene anaphatikizidwa, chimene zolinga zawo kapena utali zinali, ndi mmene mapanganowo amagwirizanirana lina ndi linzake m’chifuno cha Mulungu cha kudalitsa mtundu wa anthu omvera ndi moyo wosatha. Ino ndi nthaŵi yoyenerera kubwereramo mu mapangano amenewa, popeza kuti pa March 22, 1989, mipingo ya Akristu idzasonkhana kukumbukira Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, chomwe chimaphatikizapo mwachindunji mapangano amenewa.
6 Ndithudi, kwa anthu ena lingaliro la mapangano lingamveke losakondweretsa, lokhudza lamulo, lokhala ndi chikondwerero chochepera cha umunthu. Lingalirani, ngakhale ndi tero, chimene Theological Dictionary of the Old Testament ikunena: “Mawu kaamba ka ‘pangano’ mu Near East wakale limodzinso ndi m’dziko la Chigriki ndi Chiroma . . . akuperekedwa mogwirizana ndi zigawo ziŵiri za matanthauzo: lumbiro ndi ntchito kumbali imodzi, chikondi ndi ubwenzi ku mbali ina.” Tingawone mbali zonse ziŵiri—lumbiro ndi ubwenzi—monga magwero a mapangano a Yehova.
Pangano la Abrahamu—Maziko kaamba ka Madalitso Osatha
7, 8. Ndi mtundu wotani wa pangano umene Yehova anapanga ndi Abrahamu? (1 Mbiri 16:15, 16)
7 Kholo Abrahamu, “atate wa onse okhala ndi chikhulupiriro,” anali “bwenzi la Yehova.” (Aroma 4:11; Yakobo 2:21-23) Mulungu analumbira kwa iye ndi lumbiro, akumakhazikitsa pangano lomwe liri maziko ku kulandira kwathu madalitso osatha.—Ahebri 6:13-18.
8 Pamene Abrahamu anali mu Uri, Yehova anamuuza iye kusamukira ku dziko lina, lomwe linatembenukira kukhala Kanani. Pa nthaŵi imeneyo Yehova analonjeza Abrahamu kuti: “Ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu ndipo ndidzakudalitsa iwe ndi kubukitsa dzina lako; . . . ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.”a (Genesis 12:1-3) Pambuyo pake, Mulungu pang’onopang’ono anawonjezera tsatanetsatane ku chimene timalankhula molondola kukhala pangano la Abrahamu: Mbewu ya Abrahamu, kapena oloŵa m’malo, akakhoza kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa; mbewu yake ikatsogolera ku mbadwa zosaŵerengeka; Abrahamu ndi Sara akakhala magwero a mafumu.—Genesis 13:14-17; 15:4-6; 17:1-8, 16; Salmo 105:8-10.
9. Ndimotani mmene timadziŵira kuti tingakhale ophatikizidwa m’pangano la Abrahamu?
9 Mulungu analitcha ilo “pangano langa pakati pa ine ndi iwe [Abrahamu].” (Genesis 17:2) Koma ife motsimikizirika tiyenera kudzimva kuti miyoyo yathu ndi yolowetsedwamo, popeza kuti Mulungu pambuyo pake anakulitsa panganolo, akumanena kuti: “Kudalitsa ndidzakudalitsa iwe [ndi] kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja; ndipo mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo. M’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:17, 18) Ife ndife mbali ya mitundu imeneyo; dalitso lothekera liri mtsogolo kaamba ka ife.
10. Ndi chidziŵitso chotani chomwe tikupeza mu pangano ndi Abrahamu?
10 Tiyeni tipume kuti tilingalire chomwe tingaphunzire kuchokera ku pangano la Abrahamu. Mofanana ndi pangano la mu Edeni lisanakhale ilo, iri limalozera ku “mbewu” yomadzayo, mwakutero kulingalira kuti mbewuyo ikakhala ndi mzere wa umunthu. (Genesis 3:15) Umenewo ukakhala mzere wa Semu, kufika kwa Abrahamu, ndipo kupyolera mwa mwana wake wamwamuna Isake. Mzera umenewu ukaphatikizapo ufumu, ndipo ukakhoza mwa njira inayake kulola kaamba ka dalitso osati kokha kwa banja limodzi koma anthu a maiko onse. Ndimotani mmene pangano limenelo linakwaniritsidwira?
11. Ndimotani mmene kukwaniritsidwa kwenikweni kwa pangano la Abrahamu kunadzera?
11 Mbadwa za Abrahamu kupyolera mwa Yakobo, kapena Israyeli, zinachuluka kukhala mtundu waukulu. Monga mbewu yosaŵerengeka yeniyeni ya Abrahamu, iwo anali odzipereka ku kulambira kowona kwa Mulungu wa Abrahamu, Isake, ndi Yakobo. (Genesis 28:13; Eksodo 3:6, 15; 6:3; Machitidwe 3:13) Kaŵirikaŵiri Aisrayeli anapatuka kuchoka pa kulambira kowona, komabe “Yehova anasonyeza kwa iwo chiyanjo ndipo anali ndi chifundo kwa iwo . . . chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo; ndipo sanafune kuwawononga iwo.” (2 Mafumu 13:23; Eksodo 2:24; Levitiko 26:42-45) Ngakhale pambuyo pakuti Mulungu analandira mpingo Wachikristu monga anthu ake, iye anapitirizabe kwa kanthaŵi kusonyeza chiyanjo chapadera kwa Aisrayeli monga anthu omwe anali mbewu yeniyeni ya Abrahamu.—Danieli 9:27.
Mbewu Yauzimu ya Abrahamu
12, 13. Ndimotani mmene Yesu anatsimikizira kukhala mbali yoyambirira ya mbewu m’kukwaniritsidwa kwauzimu kwa pangano la Abrahamu?
12 Pangano la Abrahamu linali ndi kukwaniritsidwa kwinakwake, kwauzimu. Kukwaniritsidwa kwakukulu kumeneku sikukanakhala kowonekera nthaŵi ya Yesu isanadze, koma tingakhale achimwemwe kuti kuli komvekera m’nthaŵi yathu. Tiri ndi kulongosola kwa kukwaniritsidwa kwake m’Mawu a Mulungu. Paulo akulemba kuti: “Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Sanena: ‘Ndipo kwa zimbewu,’ ngati kunena zambiri, komatu ngati kunena imodzi: ‘Ndipo kwa mbewu yako,’ ndiye Kristu.”—Agalatiya 3:16.
13 Inde, mbewuyo ikabwera kokha kupyolera mwa mzera umodzi wokha, kapena banja, chimene chinali chowona ndi Yesu, wobadwa monga Myuda wa kuthupi, mbadwa yeniyeni ya Abrahamu. (Mateyu 1:1-16; Luka 3:23-34) Kuwonjezerapo, iye anali mbali ya banja la Abrahamu Wamkulu kumwamba. Kumbukirani kuti ndi chikhulupiriro chozama kholo Abrahamu linali lofunitsitsa kupereka nsembe mwana wake wamwamuna Isake ngati Mulungu anafuna chimenecho. (Genesis 22:1-18; Ahebri 11:17-19) Mofananamo, Yehova anatumiza Mwana wake wobadwa yekha ku dziko lapansi kukakhala nsembe ya dipo kaamba ka mtundu wa anthu omvera. (Aroma 5:8; 8:32) Chotero nchomvekera chifukwa chimene Paulo anazindikiritsira Yesu Kristu monga mbali yokulira ya mbewu ya Abrahamu mogwirizana ndi pangano limeneli.
14. Ndi iti yomwe iri mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu, ndipo kodi ichi chikutsogolera ku kukambitsirana kotani?
14 Paulo anapitirizabe kusonyeza kuti Mulungu akakhoza ‘kuchulukitsa mbewu ya Abrahamu’ m’kukwaniritsidwa kwauzimu. Iye analemba kuti: “Ngati muli a Kristu, muli mbewu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.” (Genesis 22:17; Agalatiya 3:29) Oterowo ali Akristu odzozedwa ndi mzimu a 144,000 omwe amapanga mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamuyo. Iwo sali otsutsana ndi mbali yoyambirira ya mbewuyo koma “ali a Kristu.” (1 Akorinto 1:2; 15:23) Timadziŵa kuti ambiri a iwo sangapeze makolo awo kufika kwa Abrahamu, popeza kuti iwo ali ochokera ku mitundu yosakhala Yachiyuda. Chokulira koposa m’kukwaniritsidwa kwauzimu, ngakhale ndi tero, iwo sali mwachibadwa mbali ya banja la Abrahamu Wamkulu, Yehova; m’malomwake, iwo amachokera ku banja lopanda ungwiro la Adamu wochimwa. Chotero tidzafunikira kuwona kuchokera ku mapangano otsatira mmene iwo angayenerere kukhala mbali ya “mbewu ya Abrahamu.”
Pangano la Chilamulo Lowonjezeredwa Mosakhalitsa
15-17. (a) Nchifukwa ninji pangano la Chilamulo linawonjezeredwa ku pangano la Abrahamu? (b) Ndimotani mmene Chilamulo chinakwaniritsira zolinga zimenezi?
15 Pambuyo pa kupanga kwa Mulungu pangano la Abrahamu monga sitepi lokulira kulinga ku kukwaniritsa chifuno chake, ndimotani mmene mzere wa Mbewuyo ukachinjirizidwira kuchoka ku kuipitsidwa kapena kuthetsedwa kufikira nthaŵi ya kuwonekera kwake? Pamene Mbewuyo inafikadi, ndimotani mmene olambira owona akaizindikirira iyo? Paulo akuyankha mafunso oterowo mwa kulozera nzeru ya Mulungu m’kuwonjezera kosakhalitsa kwa pangano la Chilamulo. Mtumwiyo akulemba kuti:
16 “Nanga, Chilamulo, tsono? Chinawonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe. . . . Momwemo Chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.”—Agalatiya 3:19, 24.
17 Pa Phiri la Sinai, Yehova anapanga pangano lapadera pakati pa iyemwini ndi Israyeli—pangano la Chilamulo, ndi Mose monga nkhoswe yake.b (Agalatiya 4:24, 25) Anthu anavomera kukhala m’pangano limeneli, ndipo linapangidwa kugwira ntchito ndi mwazi wa ng’ombe ndi mbuzi. (Eksodo 24:3-8; Ahebri 9:19, 20) Ilo linapatsa Israyeli malamulo a teokratiki ndi ndandanda ya boma lolungama. Panganolo linaletsa kukwatirana ndi akunja kapena kugawana m’kachitidwe kachisembwere ndi kulambira konyenga kwa chipembedzo. Ilo chotero linachinjiriza Aisrayeli ndipo linali magwero m’kusungirira mzere wa mbewuyo kukhala wosaipitsidwa. (Eksodo 20:4-6; 34:12-16) Koma popeza kuti palibe m’Israyeli wopanda ungwiro yemwe akakhoza kusunga Chilamulocho kotheratu, icho chinapanga machimo kuwonekera. (Agalatiya 3:19) Icho chinalozanso ku chifuno kaamba ka wansembe wangwiro, wosatha ndi kaamba ka nsembe yomwe sikafunikira kubwerezedwa chaka ndi chaka. Chilamulocho chinali monga namkungwi yemwe anatsogoza mwana kwa mlangizi wofunika, yemwe akakhala Mesiya, kapena Kristu. (Ahebri 7:26-28; 9:9, 16-22; 10:1-4, 11) Pamene ilo linafikiritsa chifuno chake, pangano la Chilamulo likatha.—Agalatiya 3:24, 25; Aroma 7:6; onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga,” tsamba 31.
18. Ndi chiyembekezo chowonjezereka chotani chomwe chinaphatikizidwa ndi pangano la Chilamulo, koma kodi nchifukwa ninji chinali chovuta kuchimvetsetsa?
18 Pamene ankapanga pangano losakhalitsa limeneli, Mulungu anatchulanso cholinga chochititsa nthumanzi ichi: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera . . . Ndipo ndidzakuyesera ufumu wanga wansembe ndi mtundu wopatulika.” (Eksodo 19:5, 6) Ndi chiyembekezo chotani nanga! Mtundu wa mafumu-ansembe. Ngakhale ndi tero, ndimotani mmene chimenechi chikakhalira? Monga mmene Chilamulo pambuyo pake chinalunjikitsira, fuko lolamulira la (Yuda) ndi fuko la unsembe (Levi) anapatsidwa mathayo osiyana. (Genesis 49:10; Eksodo 28:43; Numeri 3:5-13) Palibe munthu yemwe akakhoza kukhala ponse paŵiri wolamulira wamba ndi wansembe. Ndiponso, mawu a Mulungu pa Eksodo 19:5, 6 anapereka chifukwa chokhulupirira kuti mu mkhalidwe wina wosavumbulutsidwa, aja okhala mu pangano la Chilamulo akakhala ndi mwaŵi wa kupereka ziwalo za “ufumu wa ansembe ndi mtundu wopatulika.”
Pangano la Ufumu wa Davide
19. Ndimotani mmene ufumu unalozedwerako m’pangano limeneli?
19 M’kupita kwa nthaŵi Yehova anawonjezera pangano lina lomwe mowonjezereka linamveketsa bwino mmene iye akakwaniritsira chifuno chake, ku dalitso lathu losatha. Tawona kuti pangano la Abrahamu linalozera kutsogolo ku ufumu pakati pa mbewu yeniyeni ya Abrahamu. (Genesis 17:6) Pangano la Chilamulo linayembekezeranso mafumu pakati pa anthu a Mulungu, popeza kuti Mose anawuza Israyeli kuti: “Mutakalowa [m’Dziko Lolonjezedwa] ndipo mukanena kuti, ‘Tidziikire mfumu monga amitundu onse akutizinga’; mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha. . . . Simuyenera kudziikira mlendo.” (Deuteronomo 17:14, 15) Ndimotani mmene Mulungu akakonzekera kaamba ka mfumu yoteroyo, ndipo ndimotani mmene iyo ikanyamulira pangano la Abrahamu?
20. Ndimotani mmene Davide ndi mzera wake amabwerera m’chithunzichi?
20 Ngakhale kuti mfumu yoyambirira ya Israyeli inali Sauli wa fuko la Benjamini, iye anatsatiridwa ndi Davide wolimba mtima ndi wokhulupirika wa Yuda. (1 Samueli 8:5; 9:1, 2; 10:1; 16:1, 13) Mkati mwa kulamulira kwa Davide, Yehova anasankha kupanga pangano ndi Davide. Poyamba Iye ananena kuti: “Ine ndidzaukitsa mbewu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m’matumbo mwako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthaŵi zonse.” (2 Samueli 7:12, 13) Monga momwe zasonyezedwera pamenepo, mwana wamwamuna wa Davide Solomo anakhala mfumu yotsatira, ndipo anagwiritsiridwa ntchito kumanga nyumba, kapena kachisi, kaamba ka Mulungu mu Yerusalemu. Komabe, panali zowonjezereka.
21. Pangano la Ufumu wa Davide linapanga makonzedwe kaamba ka chiyani?
21 Yehova anapitirizabe kupanga pangano iri ndi Davide: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthaŵi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthaŵi zonse.” (2 Samueli 7:16) Mowonekera, Mulungu chotero ankakhazikitsa kulamulira kwa ufumu kaamba ka Israyeli m’banja la Davide. Iwo sunafunikire kukhala kokha kupatsirana kokhazikika kwa mafumu a Davide. Potsirizira pake, winawake mu mzere wa Davide akadza kukalamulira “ku nthaŵi yonse, ndi mpando wachifumu wake [ukakhala] ngati dzuŵa pamaso pa [Mulungu].”—Salmo 89:20, 29, 34-36; Yesaya 55:3, 4.
22. Ndimotani mmene pangano la Davide limagwirizanirana ku mzere wa Mbewu, ndipo ndi chotulukapo chotani?
22 Chotero, chiri chachiwonekere, kuti pangano la Davide mowonjezereka linachepetsa mzere wa Mbewu. Ngakhale Ayuda a m’zana loyamba anazindikira kuti Mesiya akayenera kukhala mbadwa ya Davide. (Yohane 7:41, 42) Yesu Kristu, mbali yoyambirira ya mbewu ya pangano la Abrahamu, anayenerera kukhala Wolowa m’malo wosatha wa Ufumu wa Davide umenewu, monga mmene mngelo anachitira umboni. (Luka 1:31-33) Yesu chotero anapeza kuyenera kwa kulamulira pa Dziko Lolonjezedwa, ufumu wa pa dziko lapansi pa umene Davide analamulira. Ichi chiyenera kuwonjezera chidaliro chathu mwa Yesu; iye akulamulira, osati mwa kugonjetsa kosakhala kwa lamulo, koma kupyolera m’kakonzedwe ka lamulo kokhazikitsidwa, pangano laumulungu.
23. Ndi mafunso otani ndi nkhani zomwe zifunikirabe kuthetsedwa?
23 Talingalira kokha anayi a mapangano aumulungu ochitira umboni za mmene Mulungu anakonzera kuti akwaniritse chifuno chake cha kubweretsa madalitso osatha ku mtundu wa anthu. Mwachidziŵikire, inu mungawone kuti chithunzithunzichi sichiri chokwanira. Mafunso akukhalabe: Popeza kuti anthu anapitirizabe opanda ungwiro, ndi wansembe uti kapena nsembe imene ikasintha chimenecho kosatha? Ndimotani mmene anthu akayenerera kukhala mbali ya mbewu ya Abrahamu? Kodi pali chifukwa cha kukhulupirira kuti kuyenera kwa ulamuliro kukafutukuka kuphatikizapo zoposa kokha gawo wamba la pa dziko lapansi? Ndimotani mmene mbewu ya Abrahamu, ponse paŵiri mbali yoyambirira ndi yachiŵiri, ikabweretsera madalitso ku “mitundu yonse ya pa dziko lapansi,” kuphatikizapo aliyense wa ife? Tiyeni tiwone.
[Mawu a M’munsi]
a Iri ndi pangano la munthu mmodzi, popeza kuti kokha mbali imodzi (Mulungu) akulowetsedwa m’kuchita kachitidwe kake.
b “Lingaliro la pangano linali mbali yapadera ya chipembedzo cha Israyeli, yokhayo yofuna kukhulupirika kotheratu ndi kuthetsa kuthekera kwa kukhulupirika kuŵiri kapena kochulukira konga komwe kunaloledwa m’zipembedzo zina.”—Theological Dictionary of the Old Testament, Volyumu II, tsamba 278.
Kodi Yankho Lanu N’lotani?
◻ Ndimotani mmene pangano la Abrahamu linakhazikitsira maziko kaamba ka kulandira kwathu madalitso osatha?
◻ Nchiyani chomwe chinali mbewu yeniyeni, yakuthupi ya Abrahamu? Mbewu yophiphiritsira?
◻ Nchifukwa ninji pangano la Chilamulo linawonjezeredwa m’pangano la Abrahamu?
◻ Ndimotani mmene pangano la Ufumu wa Davide linapititsira patsogolo chifuno cha Mulungu?
[Chithunzi patsamba 13]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Pangano la mu Edeni Genesis 3:15
Pangano la Abrahamu
Mbewu yoyamba
Mbewu yachiŵiri
Madalitso osatha
[Chithunzi patsamba 14]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Pangano la mu Edeni Genesis 3:15
Pangano la Abrahamu
Pangano la Chilamulo
Pangano la Ufumu wa Davide
Mbewu yoyamba
Mbewu yachiŵiri
Madalitso osatha
[Chithunzi patsamba 10]
Kuti apange chifuno chake m’malo mwa mtundu wa anthu, Mulungu anapanga pangano ndi Abrahamu wokhulupirika