Moyo Watsopano wa Makolo Athu Akufa
KODI Mawu a Mulungu, Baibulo, amaphunzitsa kuti aliyense mwachibadwa amapitiriza kukhala ndi moyo m’dziko la mizimu pa imfa? Ayi, silimatero. Baibulo limapereka chiyembekezo cha moyo chabwino koposa pambuyo pa imfa, koma osati m’njira imene ambiri amalilingalirira.
Lingalirani zimene Baibulo limanena ponena za kholo lathu loyamba, Adamu. Yehova anamuumba “ndi dothi lapansi.” (Genesis 2:7) Adamu anali ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha mwachimwemwe pa dziko lapansi. (Genesis 2:16, 17) Komabe, iye anapandukira Mlengi wake wachikondi, ndipo chifukwa chake imfa inadza.
Kodi nkuti kumene Adamu anapita pa imfa? Mulungu anati kwa iye: “Udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”—Genesis 3:19.
Kodi Adamu anali kuti Yehova asanamlenge ndi fumbi? Kunalibe. Iye sanakhaleko. Chotero pamene Yehova anati Adamu ‘adzabwerera kunthaka,’ iye anangotanthauza kuti Adamu sakakhalanso ndi moyo, monga ngati fumbi. Adamu ‘sanawolokere kwina’ kuti akakhale woyambitsa dziko la mizimu ya makolo akufa. Iye sanawolokere ku moyo wachimwemwe kumwamba kapena ku mavuto osatha ku malo a chizunzo. Kusamuka kokha kumene anachita kunali kuchoka kumoyo kumka ku mkhalidwe wopanda moyo, kuchokera ku mkhalidwe wa kukhalako kumka ku mkhalidwe wa kusakhalako.
Bwanji nanga za anthu onse? Kodi mbadwa za Adamu nazonso zimaleka kukhalako pa imfa? Baibulo limayankha: “Onse [anthu ndi nyama zomwe] apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.”—Mlaliki 3:19, 20.
Mkhalidwe wa Akufa
Inde, akufa alibe moyo, sakhoza kumva, kuona, kulankhula, kapena kuganiza. Mwachitsanzo, Baibulo limati: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi, . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano.” Baibulo limanenanso kuti: “Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”—Mlaliki 9:5, 6, 10.
Motero, malinga ndi kunena kwa Mawu a Mulungu, anthu amadziŵa kuti adzafa akali ndi moyo. Komabe, pamene imfa ichitika, sadziŵa kanthu bi. Samaima pambali pa mtembo wawo, akumapenyerera zimene zikuuchitikira. Mumkhalidwe wa kusakhalakowo mulibe chikondwerero kapena zopweteka, ndiponso mulibe chisangalalo kapena chisoni. Awo amene afa samadziŵa za kupita kwa nthaŵi. Mkhalidwe wawo uli wosadziŵa chilichonse woposa mkhalidwe wa tulo.
Yobu, mtumiki wa Mulungu m’nthaŵi zakale, anadziŵa kuti anthu samakhalabe ndi moyo atafa. Iye anazindikiranso kuti popanda kuloŵererapo kwa Mulungu, sipangakhale chiyembekezo cha kubwereranso ku moyo. Yobu anati: “Munthu akufa atachita liondeonde inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti? Agona pansi, osaukanso.” (Yobu 14:10, 12) Ndithudi Yobu sanayembekezere kuti pamene adzafa adzagwirizana ndi makolo ake m’dziko la mizimu.
Chiyembekezo cha Chiukiriro
Popeza kuti amoyo amaleka kukhalako pa imfa, funso lofunika kwambiri ndilo limene Yobu anadzutsa pamene anapitiriza kufunsa kuti: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” Yobu mwiniyo anapereka yankho ili: “Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga [nthaŵi ya kumanda], mpaka kwafika kusandulika kwanga. Mukadaitana [Yehova], ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.”—Yobu 14:14, 15.
Mwa mawu ena, ngakhale ngati Yobu anali kudzaloŵa mu mkhalidwe wa kusakhalako, Mulungu sakanamuiŵala. Yobu anali ndi chikhulupiriro chakuti idzafika nthaŵi pamene Yehova Mulungu ‘adzamuitana’ kudzakhalanso ndi moyo mwa chiukiriro.
Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anasonyeza kuti chiyembekezo cha Yobu cha chiukiriro chinali chenicheni. Yesu anasonyeza kuti akufa angathe kuukitsidwa. Motani? Mwa kukuchita iye mwiniyo! Iye panalibe kuti aukitse Yobu, koma pamene anali pa dziko lapansi Yesu anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wina wamasiye wa ku mzinda wa Nayini. Yesu anaukitsanso mwana wamkazi wazaka 12 wa mwamuna wina wotchedwa Yairo. Ndipo anaukitsa bwenzi lake Lazaro, amene anali wakufa kwa masiku anayi.—Luka 7:11-15; 8:41, 42, 49-56; Yohane 11:38-44.
Kuwonjezera pa kuchita zozizwitsa zimenezi, Yesu analankhula za chiukiriro china chachikulu cha mtsogolo. Iye anati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Pambuyo pake, mtumwi Paulo, amene Yehova anamgwiritsira ntchito kuukitsa mnyamata wina, nayenso anasonyeza chikhulupiriro pa chiukiriro cha mtsogolo. Iye anati: “Ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 20:7-12; 24:15.
Maumboni a Malemba ameneŵa onena za chiukiriro cha mtsogolo samanena za moyo wopitirizabe m’dziko la mizimu. Amasonyeza za nthaŵiyo pamene miyandamiyanda ya akufa idzakhalanso ndi moyo m’thupi lanyama pa dziko lapansi pompano. Oukitsidwa ameneŵa sadzakhala anthu amene sadzakumbukira moyo wawo wapapitapo pa dziko lapansi. Sadzabadwanso kachiŵiri monga makanda. M’malo mwake, adzakhala anthu amodzimodziwo amene iwo anali pamene anafa, okhala ndi zikumbukiro ndi umunthu umodzimodziwo. Adzadzizindikira ndipo ena adzawazindikira. Chidzakhala chisangalalo chotani nanga pamene anthu ameneŵa agwirizananso ndi mabwenzi awo ndi mabanja awo! Ndipo kudzakhala kokondweretsa chotani nanga kukumananso ndi makolo athu akufa!
Chiukiriro cha Moyo Wakumwamba
Kodi Yesu sananene kuti ena adzapita kumwamba? Inde, iye anatero. Pa usikuwo asanaphedwe, iye anati: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. . . . Ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso.” (Yohane 14:2, 3) Yesu anali kulankhula kwa atumwi ake okhulupirika, koma mawu akewo samatanthauza kuti anthu onse abwino amapita kumwamba.
Yesu anasonyeza kuti awo amene amaukitsidwira kumwamba ayenera kufitsa zofunika zake zina m’malo mwa kungokhala munthu wabwino. Chofunika chimodzi ndicho kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Yehova ndi zifuno zake. (Yohane 17:3) Zofunika zina ndizo kusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu ndi kumvera Mulungu. (Yohane 3:16; 1 Yohane 5:3) Ndipo chofunika chinanso ndicho ‘kubadwa mwatsopano’ monga Mkristu wobatizidwa wodzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Yohane 1:12, 13; 3:3-6) Chofunika chinanso cha moyo wakumwamba ndicho kupirira monga momwe Yesu anachitira, kusonyeza kukhulupirika kwa Mulungu ngakhale kufikira imfa.—Luka 22:29; Chivumbulutso 2:10.
Pali chifukwa chake chofunira zofunika zapamwamba kwambiri zimenezo. Awo oukitsidwira kumwamba ali ndi ntchito ina yofunika yoti akachite. Yehova anadziŵa kuti maboma a anthu sadzayendetsa zinthu bwino pa dziko lapansi. Chotero anakonza boma lakumwamba, kapena Ufumu, umene ukalamulira anthu. (Mateyu 6:9, 10) Yesu akakhala Mfumu ya Ufumu umenewo. (Danieli 7:13, 14) Anthu ena osankhidwa pa dziko lapansi ndi kuukitsidwira kumwamba akalamulira naye. Baibulo linaneneratu kuti oukitsidwa ameneŵa anali kudzakhala “ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo [anali kudzachita] ufumu padziko.”—Chivumbulutso 5:10.
Kodi anthu ambirimbiri adzakwaniritsa zofunika za chiukiriro chakumwamba? Ayi. Pa chifukwa chosakhala chawo, ochuluka a amene agona mu imfa samayenerera. Ambiri anali ndi mwaŵi wochepa wa kuphunzira choonadi chonena za Yehova ndi zifuno zake ndipo ena analibe. Iwo anakhala ndi moyo ndi kufa osadziŵa chilichonse ponena za Yesu Kristu kapena za Ufumu wa Mulungu.
Yesu anatchula awo amene anali kudzapita kumwamba kuti “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Pambuyo pake kunavumbulidwa kuti chiŵerengero cha awo “ogulidwa kuchokera kudziko” okalamulira ndi Kristu kumwamba chidzakhala 144,000. (Chivumbulutso 14:1-3; 20:6) Pamene kuli kwakuti 144,000 ili chiŵerengero chachikulu mokwanira kudzaza “malo . . . ambiri” amene Yesu anatchula, chimenechi nchochepa pamene chiyerekezeredwa ndi anthu miyandamiyanda amene abadwa kwa Adamu.—Yohane 14:2.
Zochitika Chiukiriro cha pa Dziko Lapansi Chisanakhale
Tiyeni tione zimene tafotokoza kufikira pano. Malinga ndi kunena kwa Baibulo, awo amene amafa ngopanda moyo mu imfa kufikira pamene aukitsidwa ndi Yehova Mulungu. Ena amaukitsidwira ku moyo wakumwamba, kumene adzalamulira ndi Yesu Kristu mu boma la Ufumu. Anthu ochuluka adzaukitsidwa kukhala pa dziko lapansi, monga nzika za Ufumu umenewo.
Yehova adzakwaniritsa mbali ina ya chifuno chake cha dziko lapansi mwa chiukiriro cha pa dziko lapansi. Yehova analilenga kuti “akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Linali kudzakhala kwawo kwa anthu kwachikhalire. Chifukwa chake, wamasalmo anaimba kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.”—Salmo 115:16.
Chiukiriro cha moyo wa pa dziko lapansi chisanayambe, zinthu zambiri ziyenera kusintha. Mwina mungavomereze kuti sichinali chifuno cha Mulungu kuti dziko lapansi lidzazidwe ndi nkhondo, kuipitsa, upandu, ndi chiwawa. Mavuto ameneŵa amabweretsedwa ndi anthu amene samalemekeza Mulungu ndi malamulo ake olungama. Chotero, Ufumu wake ‘udzawononga iwo akuwononga dziko’—sitepe yaikulu yokwaniritsira chifuniro chake pa dziko lapansi. (Chivumbulutso 11:18) Ufumuwo udzawononga anthu onse oipa, ukumasiya olungama kukhalabe ndi moyo kosatha pa dziko lapansi.—Salmo 37:9, 29.
Paradaiso pa Dziko Lapansi
Awo amene adzaukitsidwa pa dziko lapansi loyeretsedwa adzakhala anthu ofatsa, achifundo amene amachita zabwino. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:5.) Pansi pa uyang’aniro wachikondi wa Ufumu wa Mulungu, adzakhala ndi moyo wachimwemwe m’chisungiko. Baibulo limafotokoza chithunzi cha mkhalidwe wokondweretsa umenewu umene udzakhalako: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
Inde, dziko lapansi lidzasandulizidwa paradaiso. (Luka 23:43) Tangoganizirani kuti zimenezo zidzatanthauzanji! Sikudzakhalanso zipatala ndi nyumba zosungiramo okalamba. Mu Paradaiso, awo amene tsopano akuvutika ndi ukalamba adzakhalanso olimba ndi athanzi labwino. (Yobu 33:25; Yesaya 35:5, 6) Sikudzakhalanso nyumba zokonzeramo mitembo, manda, ndi miyala ya pamanda yolembedwapo maina. Mwa Ufumu wake, Yehova ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse.’ (Yesaya 25:8) Ndithudi madalitso otero angatanthauze moyo watsopano kwa ife ndi kwa makolo athu akufa.
[Chithunzi patsamba 7]
Awo amene adzaukitsidwa pa dziko lapansi adzakhala nzika za Ufumuwo