Ziyembekezo za Paradaiso Ziri Zotsimikizirika Mosasamala Kanthu za Kusamvera kwa Anthu
1. Ndi kupita kwa nthaŵi, ndi kuti kumene mwamuna ndi mkazi oyambirira akuwonedwa ndipo m’malo ozungulira otani?
NTHAŴI yapita. Mwamuna ndi mkazi oyamba salinso amaliseche mosadziŵa. Iwo ali ovekedwa—ndi zovala zazitali za chikopa cha nyama. Iwo ali kokha kunja kwa poloŵera pa munda wangwiro wa Edene. Kumsana kwawo kukuloza ku mundawo. Iwo akuyang’ana pa chochitika kutsogolo kwawo. Iwo akuwona kokha nthaka yosalimidwa. Momvekeradi ilo liribe dalitso la Mulungu pa ilo. Patsogolo pawo pangawonedwe minga ndi mitula. Kodi iri sidziko lapansi limene iwo analamulidwa kugonjetsa? Inde, koma mwamuna ndi mkazi oyamba sali kunja kumeneko tsopano kaamba ka chifuno cha kufutukula munda wa Edene ku dziko losasamalidwa loterolo.
2. Nchifukwa ninji mwamuna ndi mkazi sakuyesera kuloŵanso m’munda wa Paradaiso?
2 Pa kawonedwe kosiyana koteroko, nchifukwa ninji iwo sakubwerera ndi kuloŵanso m’munda wa Paradaiso? Chikulingaliridwa mopepuka, koma yang’anani pa chomwe chiri kumbuyo kwawo poloŵera pa mundawo. Zolengedwa zomwe sanawonepo ndi kale lonse, ngakhale mkati mwa mundawo, makerubi, ndi lupanga lamoto lomwe likuzungulira ponsepo. Mwamuna ndi mkaziyo sakakhoza kudutsa zimenezi ali amoyo kuloŵa m’mundamo!—Genesis 3:24.
3. Nchiyani chomwe chinachitika kusintha mkhalidwe wa okwatirana aŵiri oyambirira mofulumira chotero?
3 Nchiyani chomwe chachitika? Sichiri chinsinsi chocholoŵanacholoŵana kotero kuti n’kuzizwitsa sayansi kwa zaka zikwi zingapo. Icho chalongosoledwa mopepuka. Mwamuna ndi mkazi oyamba anafunikira kuzindikira ziyembekezo zozizwitsa zimene lamulo la Mulungu linakhazikitsa pamaso pawo pa tsiku la ukwati wawo koma pa mlingo wakuti amvere Atate wawo wakumwamba m’nkhani yaing’ono koposa. Chimvero chawo changwiro chinafunikira kuyesedwa ndi kuletsa chakudya chimodzi: Iwo sanafunikire kudya chipatso cha “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 2:16, 17) Ngati iwo anatero motsutsana ndi malamulo a Mulungu, iwo akafa ndithu. Chimenecho ndi chimene Adamu, monga mneneri wa Mulungu, anawuza mkazi wake, cholengedwa chocheperako chaumunthu. Koma modabwitsa, na·chashʹ uja, njoka ija, inakana kuwona kwa chimene Mulungu anawuza Adamu m’chenjezo Lake motsutsana ndi kudya ku mtengo woletsedwa “wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa.” Njokayo inanyenga mkaziyo m’kukhulupirira kuti kuswa lamulo la Mulungu ndi kudya chipatso choletsedwa kukatulukapo m’kukhala kwake wofanana ndi Mulungu ndi kumpangitsa iye kukhala wodziimira payekha kuchoka kwa Mulungu m’kugamula chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa.—Genesis 3:1-5.
Palibe Cholembera cha Nthanthi
4, 5. Ndimotani mmene mtumwi Paulo akusonyezera kuti cholembera cha kunyenga kwa mkazi woyambirira kochitidwa ndi njoka sichinali nthanthi?
4 Chozizwitsa? Kodi icho chikumvekera mokulira monga nthanthi, nkhani yopekedwa yosazikidwa pa zenizeni ndipo chotero yosalandirika ku maganizo a achikulire owunikiridwa a lerolino? Ayi, osati ku mlembi woŵerengedwa mofalabe, mlembi wokhulupirika, mtumwi wosankhidwa mwapadera, yemwe anadziŵa kulondola kwa chimene analemba. Ku mpingo wa Akristu achikulire mu mzinda wa nzeru zakudziko wa Korinto, mtumwi Paulo ameneyu analemba kuti: “Koma ndiwopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsyidwe kusiyana nako kuwona mtima ndi kuyera mtima ziri kwa Kristu.”—2 Akorinto 11:3.
5 Paulo sakakhoza mpang’ono pomwe kulozera ku nthanthi, nkhani yopeka, ndi kugwiritsira ntchito yoteroyo monga chinthu choyerekeza kupanga nsonga yake ndi Akorinto amenewo, omwe anali ozoloŵerana bwino lomwe ndi nthanthi za chipembedzo chachikunja cha Chigriki. Akumagwira mawu kuchokera m’Malemba a Chihebri owuziridwa, omwe iye analengeza kukhala “mawu a Mulungu,” mtumwi Paulo anatsimikizira kuti “njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake.” (1 Atesalonika 2:13) Kuwonjezerapo, pamene anali kulembera kwa woyang’anira Wachikristu yemwe anapatsidwa thayo la kuphunzitsa “chitsanzo cha mawu a moyo,” mtumwi Paulo ananena kuti: “Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva; ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analoŵa m’kulakwa.”—2 Timoteo 1:13; 1 Timoteo 2:13, 14.
6. (a) Ndimotani mmene kuchimwa kwa Adamu molimbana ndi Mulungu kunasiyanira ndi kuja kwa mkazi? (b) Nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti mkazi sanali kungopeka nkhani ponena za njoka?
6 Kunyengedwa kwa mkaziyo kochitidwa ndi njoka kuli chenicheni, osati nthanthi, motsimikizirika mongadi momwe zotulukapo za kusamvera kwake mwa kudya chipatso choletsedwa ziri zenizeni zotsimikizirika za m’mbiri. Pambuyo pa kuloŵa mu uchimo koteroko molimbana ndi Mulungu, iye anasonkhezera mwamuna wake kugaŵana ndi iye m’kudya, koma kudya kwake sikunali chifukwa chakuti iye nayenso ananyengedwa kotheratu. (Genesis 3:6) Kulongosola kwa kuŵerengera kwawo kwa pambuyo pake kwa Mulungu kumanena kuti: “Ndipo anati mwamunayo, mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya. Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.” (Genesis 3:12, 13) Mkaziyo sanali kupanga nkhani ponena za na·chashʹ ameneyo, njoka imeneyo, ndipo Yehova Mulungu sanachite ndi kulongosola kwake monga kopeka, nthanthi. Iye anachita ndi njoka imeneyo monga chiwiya m’kunyenga mkaziyo kuchimwa motsutsana ndi Iye, Mulungu wake ndi Mlengi. Chikakhala kutali ndi ulemu wa Mulungu kuchita ndi njoka ya nthanthi wamba.
7. (a) Ndimotani mmene cholembera cha Baibulo chimalongosolera kuchita kwa chiweruzo kwa Mulungu ndi njokayo? (b) Ndimotani mmene njoka yomwe inanyenga mkazi woyambirira ingatinyengerenso ife? (Phatikizanipo ndemanga kuchokera ku mawu am’munsi.)
7 Polongosola kachitidwe ka chiweruzo ka Mulungu pa njoka imeneyo m’munda wa Edene, cholemberacho chimanena kuti: “Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m’thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako: ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:14, 15) Khothi labwino lirilonse limachita ndi nsonga ndi kusanthula umboni weniweni, osati zopeka. Yehova Mulungu sanali kudzipanga iyemwini kukhala wopusa, wopanda nzeru, mwa kulunjikitsa chigamulo chake cha chiweruzo ku njoka ya nthanthi koma anali kupereka chiweruzo pa cholengedwa chenicheni, chokhalapo chomwe chinali choŵerengera. Chikakhala, osati choseketsa, koma chomvetsa chifundo ngati njoka yofananayo ikatinyenga ife m’kuganiza kuti iyo sinakhaleko nkomwe, kuti iyo inali kokha nthanthi, kuti iyo sinaŵerengere kaamba ka chirichonse choipa pa dziko lapansi.a
8. Ndi chiweruzo chotani chimene Mulungu anapereka kwa mkazi, ndipo ndi zotulukapo zotani kwa ana ake aakazi ndi zidzukulu zazikazi?
8 Kuchita ndi ndemanga ya mkazi yomwe inaphatikizapo njoka kukhala yeniyeni, cholembera chokhudza mkazi wa mwamunayo chikunena kuti: “Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” (Genesis 3:16) Palibe chirichonse chofanana ndi ichi chomwe chinaphatikizidwa m’dalitso la Mulungu pa ukwati wake kwa Adamu pamene Mulungu ananena kwa iwo kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Lamulo lodalitsidwa limenelo kwa okwatirana aŵiri angwiro aumunthu linasonyeza kukhala ndi pakati kochulukira kaamba ka mkazi koma popanda kusauka kulikonse ndi kuwawidwa kopambanitsa kwa pobala ndipo kunalibe kutsendereza kwa mwamuna pa iye. Chiweruzo chimenechi cholengezedwa pa mkazi wochimwa chinafunikira kuyambukira ana ake aakazi ndi zidzukulu zake ku mibadwo mibadwo.
Lamulo la Mulungu Likulitsidwa mwa Kupereka Chilango pa Adamu
9, 10. (a) Ndi chenjezo lotani limene Mulungu anapereka molunjika kwa Adamu, ndipo kodi nchiyani chomwe chikakhala chotulukapo ngati Mulungu anasungirira ku chilango chimenecho? (b) Ndi chiweruzo chotani chimene Mulungu anapereka molimbana ndi Adamu?
9 Ndi mikhalidwe yosintha yotani, ngakhale ndi tero, imene mkazi anafunikira kugaŵana ndi mwamuna yemwe iye anakopa kutsagana naye m’kuchimwa? Kwa mwamuna ameneyu, Mulungu anali atanena mwachindunji kuti: “Koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Kodi Mulungu, Woweruza, akasungirira kuzenga mlandu kotsirizira koteroko kaamba ka kudya kokha kwa Adamu chidutswa cha chipatso? Ganizirani ponena za chimene kuperekedwa kwa chilango chimenecho kukatanthauza! Mwa iko kokha kukawononga chiyembekezo chija chosangalatsa moyo chimene Adamu ndi Hava anakhala nacho pa tsiku lawo laukwati, chiyembekezo cha kudzaza dziko lonse lapansi ndi mbadwa zawo, ndi fuko la anthu angwiro lokhala m’paradaiso wa pa dziko lapansi mwa mtendere kosatha mu unyamata wosatha, mu unansi wa mtendere ndi Mulungu wawo ndi Atate wakumwamba! Motsimikizirika, Mulungu sakagonjetsa chifuno chake chozizwitsa kaamba ka mtundu wa anthu ndi kaamba ka mudzi wa munthu wa pa dziko lapansi mwa kungoika mosamalitsa chilango cha imfa pa makolo aumunthu oyambirira a mtundu wonse wa anthu! Koma mvetserani ku lamulo laumulungu monga momwe lalembedwera mowonekera m’cholembera cha Baibulo:
10 “Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mawu a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m’thengo: m’thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti mmenemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”—Genesis 3:17-19.
11. Ndi nsonga zotani m’chigwirizano ndi chimvero zimene zimasonyeza kuyenerera kwa chiweruzo cha Mulungu motsutsana ndi Adamu?
11 Chiweruzo chimenecho chinatanthauza kuperekedwa kwa chilango cha imfa pa munthu mosasamala kanthu za zotulukapo ku chifuno cha Mulungu cha kukhala ndi paradaiso pa dziko lapansi lodzazidwa ndi amuna ndi akazi angwiro okhala pamodzi mwachikondi ndi mwa mtendere ndi kulima ndi kusamalira kosatha kaamba ka munda wa Paradaiso ya padziko lonse lapansi. Mwamunayo anali atamvetsera ku liwu la mkazi wake m’malo mwa liwu la Mulungu lomwe linamuuza iye kusadya “mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa” woletsedwawo. Ndipo ngati iye sanamvere liwu la Mulungu ndi Mlengi, kodi iye akaphunzitsa mokhazikika ana ake kuchita tero? Kodi chitsanzo chake chikakhala nsonga yokambitsirana m’kuphunzitsa iwo kumvera Yehova Mulungu?—Yerekezani ndi 1 Samueli 15:22.
12, 13. (a) Ndimotani mmene chimo la Adamu likayambukirira ana ake? (b) Nchifukwa ninji Adamu sanayenerere kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso kapena ngakhale pa dziko lapansi nkomwe?
12 Kodi ana a Adamu akakhala okhoza kusunga lamulo la Mulungu mwangwiro, monga mmene iyemwini mu ungwiro wake waumunthu pa nthaŵi ina anali wokhoza kutero? Mwa kugwira ntchito kwa malamulo a chibadwa, kodi iye sakakhoza kupatsira kwa ana ake chifooko chake ndi chikhoterero cha kusamvera liwu la Mulungu ndi kumvetsera ku liwu lina lake? Zenizeni za m’mbiri yakale zimapereka yankho ku mafunso amenewa.—Aroma 5:12.
13 Kodi mwamuna woteroyo amene, kokha chifukwa cha cholengedwa chaumunthu, anatembenuka kuchoka pa kumvera kwangwiro kwa Mulungu m’kulongosoledwa kwa chikondi changwiro kaamba ka Mulungu anayenerera kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso kapena ngakhale pa dziko lapansi nkomwe? Kodi chikakhala chachisungiko kumulola iye kukhala ndi moyo pa dziko lapansi kosatha? Kodi kuloledwa kwake kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi mu uchimo wake kukakulitsa lamulo la Mulungu ndi kusonyeza chilungamo Chake chotheratu, kapena kodi iko kukaphunzitsa kusalemekeza lamulo la Mulungu ndi kutanthauza kuti mawu a Mulungu anali osadalirika?
Kuthamangitsidwa Kuchoka m’Munda wa Edene
14. Ndimotani mmene cholembera cha Baibulo chimalongosolera kutenga kwa Mulungu kachitidwe kolimbana ndi Adamu ndi mkazi wake?
14 Cholembera cha Baibulo chimatiwuza ife m’njira imene Mulungu anagamulira nkhani zimenezi: “Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo. Ndipo anati Yehova Mulungu, Tawonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziŵa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthaŵi zonse, Yehova Mulungu anamtulutsa iye m’munda wa Edene, kuti alime nthaka mmene anamtenga iye. Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika makerubi cha kum’mawa kwake kwa munda wa Edene, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.”—Genesis 3:21-24.
15. (a) Ndimotani mmene Mulungu anasonyezera kulingalira kaamba ka kudzimva kwa manyazi kumene Adamu ndi mkazi wake anadzimva pa kukhala amaliseche? (b) Ndimotani mmene okwatirana aŵiri oyambirira anapitikitsidwira m’munda wa Edene? (c) Ndi mikhalidwe yosinthika yotani imene inayang’anizana ndi Adamu ndi mkazi wake kunja kwa munda wa Edene?
15 Woweruza waumulunguyo anasonyeza kulingalira kaamba ka kudzimva amanyazi kumene Adamu ndi mkazi wake ochimwa tsopano anadzimva pa kukhala amaliseche. Mwanjira inayake yosalongosoledwa, iye anapereka kaamba ka iwo zovala zazitali za zikopa kuloŵa m’malo zovala zamasamba a mkuyu zosokedwa pamodzi zimene iwo anadzipangira iwo eni. (Genesis 3:7) Zovala za zikopa zikakhoza kukhala kwa nthaŵi yaitali ndi kuwapatsa iwo chitetezero chowonjezereka molimbana ndi minga ndi mitula ndi zinthu zina zovulaza zokhala kunja kwa munda wa Edene. Chifukwa cha kukhala ndi chikumbumtima choipa pambuyo pochimwa, iwo anali atayesera kubisala kuchoka pamaso pa Mulungu pakati pa mitengo ya m’munda wa Edene. (Genesis 3:8) Tsopano, pambuyo pa kuzengedwa mlandu, iwo anamva mtundu winawake wa chitsenderezo chaumulungu m’kukhala atathamangitsidwa kuchoka m’mundamo ndi Mulungu. Iwo atathamangitsidwira cha kum’mawa, ndipo mofulumira anadzipeza iwo eni kunja kwa mundawo, ataletsedwa kosatha ku uwo. Iwo sakakhoza nkomwe kugwira ntchito kukulitsa munda umenewo ndi kufalitsa mkhalidwe wake wa Paradaiso kumalekezero a dziko lapansi. Kuchokera pa nthaŵiyo kupitirizabe, iwo akadya mkate wopangidwa kuchokera ku zomera za m’munda, koma sizikakhoza kuwakhutitsa iwo kosatha m’moyo wamunthu. Iwo analetsedwa ku “mtengo wa moyo.” Pambuyo pa nthaŵi ina—kwa utali wotani?—iwo afunikira kufa!
Chifuno Choyambirira cha Yehova Chosagonjetsedwa
16. Nchiyani chomwe Mulungu sanafune kuchita, ndipo nchifukwa ninji?
16 Kodi Mulungu tsopano anagamulapo kuwononga dziko lapansi, limodzi ndi mwezi ndi dzuŵa ndi nyenyezi, m’kutentha chilengedwe chonse chifukwa chakuti zolengedwa ziŵiri zimenezi zochokera ku nthaka zinali zitamuchimwira iye? Ngati iye anati achite chinthu chimenecho, kodi ichi sichikatanthauza kuti iye wagonjetsedwa m’chifuno chake chaulemerero, zonsezo chifukwa cha chimene na·chashʹ anayambitsa? Kodi njoka yokha ikakhoza kuswa chifuno chonse cha Mulungu? Iye anali atakhazikitsa chifuno chake kwa Adamu ndi Hava pa tsiku lawo laukwati pamene anawadalitsa iwo ndi kuwauza iwo chimene chifuniro chake chinali kaamba ka iwo: kudzaza dziko lonse lapansi ndi fuko la anthu angwiro, mwa kukhala ndi dziko lonse kugonjetsedwera ku ungwiro wa m’munda wa Edene, ndi kukhala ndi mtundu wonse wa anthu wokhala ndi chigonjero cha zolengedwa zamoyo zochepera zonse pa dziko lapansi ndi m’madzi ake. Masomphenya ozizwitsa a chifuno cha Mulungu anakwaniritsidwa, kukonzekera kumene iye anapanga ndi masiku akulenga asanu ndi limodzi a ntchito a nthaŵi yoposa zaka zikwi zingapo! Kodi chifuno chofunikira kutamandidwa chimenechi tsopano chinafunikira kusiyidwa osazindikiridwa kokha chifukwa cha njoka ndi kutaika kwa okwatirana aŵiri aumunthu oyambirira? Kutalitali!—Yerekezani ndi Yesaya 46:9-11.
17. Nchiyani chomwe Mulungu anagamulapo kuchita m’chigwirizano ndi tsiku limeneli lachisanu ndi chiŵiri, ndipo chotero ndimotani mmene tsikuli lidzathera?
17 Linali lidakali tsiku lopuma, tsiku lachisanu ndi chiŵiri, la Yehova Mulungu. Iye anali atagamulapo kudalitsa tsiku limenelo ndipo analipanga ilo kukhala loyera. Iye sakalola chirichonse kulipanga ilo kukhala tsiku lotembereredwa, ndipo temberero lirilonse lomwe likupangidwa ndi winawake kudza pa tsiku limenelo la kupuma kwake iye akaloŵereramo ndi kulisintha ilo kukhala dalitso, kupangitsa tsikulo kutha lodalitsidwa. Ilo likasiya dziko lonse lapansi kukhala malo oyera, kukhala ndi chifuniro cha Mulungu chitachitidwa pansi pano pa dziko lapansi monga momwe zimachitidwira kumwamba, ndipo chimenechi ndi fuko la anthu angwiro.—Yerekezani ndi Mateyu 6:10.
18, 19. (a) Nchifukwa ninji mbadwa zovutika za okwatirana aŵiri oyambirira ochimwa zikasangalalira? (b) Nchiyani chomwe madanga owonjezereka a Nsanja ya Olonda adzakambitsirana?
18 Mulungu sanadzimve wokhumudwitsidwa. Iye sanasiye chifuno chake. Iye anagamulapo kudzisonyeza iyemwini kukhala Mmodzi wodalirika kotheratu amene ponse paŵiri amapanga zifuno ndi kuzichita mokwanira monga momwe wafunira, ndi ulemerero wonse ukumapita kwa iyemwini. (Yesaya 45:18) Mbadwa zopanda ungwiro, zovutika za anthu aŵiri ochimwa oyambirira zikakhoza kusangalala ndi kuyang’ana kutsogolo ku kuchita kwa Mulungu mokhulupirika kwa chifuno chake choyambirira ndi phindu losatha kwa iwo. Kalekale, zaka zikwi zingapo za tsiku la kupuma kwake zapita, ndipo mbali yotsirizira ya tsiku limenelo limene lidzakhala ndi dalitso lake lapadera liyenera kukhala pafupi. “Madzulo” a tsiku lake la kupuma akupita, ndipo mofanana ndi masiku onse olenga asanu ndi limodzi apitawo, “m’mawa” muyenera kudza. Pamene “m’mawa” mmenemo mufikira ungwiro wake ndi kudzipangitsa kukhala mowonekera kwa apenyereri onse a kukwaniritsidwa kwa ulemerero kwa chifuno chosasinthika cha Mulungu, chidzakhala chothekera kuliika ilo m’cholembedwa: ‘Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachisanu ndi chiŵiri.’ Chiyembekezo chozizwitsa ndithudi!
19 Zonsezi ziri zosangalatsa kulingalira ponena za izo! Ndipo m’madanga owonjezereka a Nsanja ya Olonda, zambiri zidzanenedwa ponena za ziyembekezo zodabwitsa za Paradaiso yomwe iri kutsogolo kaamba ka anthu omvera, okonda lamulo la Mulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Pa Chibvumbulutso 12:9, Satana Mdyerekezi akuzindikiritsidwa kukhala “njoka yokalambayo”; ndipo pa Yohane 8:44, Yesu Kristu akulankhula za iye kukhala “atate wabodza.”
Nchiyani Chomwe Mukanena?
◻ Nchifukwa ninji okwatirana aumunthu aŵiri oyambirira anataya mudzi wawo wa Paradaiso?
◻ Nchifukwa ninji timadziŵa kuti kunyengedwa kwa Hava kupyolera m’njoka sikunali nthanthi?
◻ Ndi chilango chotani chimene Mulungu analengeza kwa mkazi?
◻ Ndi chilango chotani chimene Mulungu analengeza kwa Adamu, ndipo nchifukwa ninji ichi chinakulitsa lamulo la Mulungu?
◻ Nchifukwa ninji Mulungu sanadzimve wokhumudwitsidwa kulinga ku chifuno chake cha kukhala ndi dziko lapansi lodzazidwa ndi anthu angwiro m’Paradaiso?