MUTU 1
“Ngakhale Kuti Anafa, Iye Akulankhulabe”
1. N’chiyani chinachititsa kuti banja la Adamu ndi Hava lisamathenso kulowa m’munda wa Edeni, nanga Abele ankalakalaka chiyani?
ABELE anayang’ana nkhosa zake zimene zinkadya m’mbali mwa phiri. Ndiye mwina anaponyanso maso ake kutsogolo kwambiri ndipo chapatali anaona kuwala kwa moto. Abele ankadziwa kuti pamalo amenewo panali lupanga loyaka moto lomwe linkazungulira mosalekeza kutchinga njira yopita kumunda wa Edeni. Poyamba makolo ake ankakhala m’mundawo koma pa nthawiyi, iwo kapenanso ana awo, sakanatha kukhalamonso. Ndiyeno yerekezerani kuti tsopano ndi madzulo ndipo kunja kukuwomba kamphepo kayaziyazi. Abele akuyang’anitsitsa kumwamba ndipo akuyamba kuganizira za Mlengi wake. Kodi zidzathekanso kuti anthu akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu ngati mmene zinalili poyamba? Abele ankalakalaka zimenezi zitachitika.
2-4. Kodi Abele akulankhula bwanji kwa ife masiku ano?
2 Baibulo limanena kuti Abele akulankhulabe masiku ano. Kodi inuyo mungathe kumva zolankhula zake? Mwina mungaganize kuti zimenezo n’zosatheka chifukwa iye anafa. Ndipotu mwana wachiwiri wa Adamu ameneyu anamwalira zaka pafupifupi 6,000 zapitazo ndipo anasanduka fumbi. Komanso ponena za akufa, Baibulo limaphunzitsa kuti: “Sadziwa chilichonse.” (Mlal. 9:5, 10) Kuwonjezera pamenepo, m’Baibulo mulibe mawu aliwonse amene Abele analankhula. Ndiye kodi iye angatilankhule bwanji?
3 Mtumwi Paulo anauziridwa ndi Mulungu kulemba mawu awa ponena za Abele: “Mwa chikhulupiriro chimenecho, ngakhale kuti anafa, iye akulankhulabe.” (Werengani Aheberi 11:4.) Onani kuti lembali likusonyeza kuti Abele akulankhulabe mwa chikhulupiriro chake. Abele anali munthu woyamba kusonyeza chikhulupiriro. Anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba moti tikhoza kutengera chitsanzo chake ngakhale masiku ano. Ngati tingaphunzire za Abele komanso kutsanzira chikhulupiriro chake, ndiye kuti tingati iye akulankhulabe kwa ife zinthu zothandiza kwambiri.
4 Koma zimene zinalembedwa m’Baibulo zokhudza Abele n’zochepa kwambiri. Ndiye kodi tingaphunzire bwanji za iye? Tiyeni tione.
Anakhala ndi Moyo pa Nthawi Yomwe Anthu Anali Atangolengedwa Kumene
5. Kodi mawu a Yesu oti Abele anakhalako “pamene dziko linakhazikika” akutanthauza chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)
5 Abele anabadwa pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anthu oyambirira analengedwa. Yesu ananena za Abele kuti anakhalapo “pamene dziko linakhazikika.” (Werengani Luka 11:50, 51.) Pamenepa Yesu sankanena dziko lenileni koma ankatanthauza anthu amene ali ndi chiyembekezo choti adzawomboledwa. Ngakhale kuti Abele anali munthu wachinayi kukhalapo, zikuoneka kuti iye anali woyamba kuonedwa ndi Mulungu kuti angathe kuwomboledwa.a Choncho n’zoonekeratu kuti Abele sanakule ndi anthu achitsanzo chabwino.
6. Kodi Abele anali ndi makolo otani?
6 Ngakhale kuti pa nthawiyo anthu anali atangolengedwa kumene, iwo anali atayamba kale kukumana ndi mavuto. Adamu ndi Hava, omwe anali makolo a Abele, anali okongola komanso amphamvu. Koma iwo anali anthu ochimwa ndipo ankadziwa bwino mfundo imeneyi. Poyamba anali angwiro komanso anali ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha. Koma kenako anapandukira Yehova Mulungu ndipo anathamangitsidwa m’Paradaiso m’munda wa Edeni. Chifukwa choti iwo anachita zinthu mwadyera, osaganizira ubwino wa ana awo, anataya mwayi wokhala angwiro komanso wokhala ndi moyo wosatha.—Gen. 2:15–3:24.
7, 8. Kodi Hava ananena mawu ati Kaini atabadwa, ndipo mwina ankaganiza chiyani ponena mawu amenewa?
7 Atathamangitsidwa m’munda wa Edeni, Adamu ndi Hava anayamba kuvutika. Komabe pamene mwana wawo woyamba anabadwa, anamutchula kuti Kaini kapena kuti “Woberekedwa” ndipo Hava anati: “Ndabereka mwana wamwamuna ndi thandizo la Yehova.” Mawu akewa akusonyeza kuti mwina ankaganizira za lonjezo limene Yehova ananena m’munda wa Edeni pamene analosera kuti mkazi adzabereka “mbewu” yomwe idzawononge Satana amene anachititsa kuti iye ndi mwamuna wake achimwire Mulungu. (Gen. 3:15; 4:1) Mwina Hava ankaganiza kuti iyeyo ndiye anali mkazi amene Mulungu anatchula ndipo Kaini ndiye “mbewu” yolonjezedwa.
8 Ngati iye ankaganizadi zimenezi ndiye kuti ankalakwitsa kwambiri. Komanso ngati iye ndi mwamuna wake ankauza Kaini zimenezi, ndiye kuti anachititsa Kainiyo kukhala ndi maganizo olakwika. Kenako Hava anaberekanso mwana wina ndipo pa nthawiyi sananene mawu osonyeza kuti ananyadira. Mwana wachiwiriyu, anamutchula kuti Abele, dzina lomwe mwina limatanthauza “Mpweya Wotuluka M’mphuno” kapena “Zachabechabe.” (Gen. 4:2) N’kutheka kuti anamutchula dzina limeneli posonyeza kuti ankadalira kwambiri Kaini kusiyana ndi Abeleyo.
9. Kodi makolo a masiku ano angaphunzire chiyani kwa makolo athu oyambirira?
9 Masiku ano, makolo angaphunzire zambiri kuchokera kwa makolo oyambirirawa. Kodi mawu ndiponso zochita zanu zimachititsa kuti ana anu akhale onyada komanso odzikonda? Kapena kodi mumawaphunzitsa kukonda Yehova Mulungu komanso kuti akhale naye pa ubwenzi? N’zomvetsa chisoni kuti makolo oyambawa analephera udindo wawo. Komabe panali chiyembekezo choti ana awo ena adzachita zinthu mwanzeru.
N’chiyani Chinathandiza Abele Kukhala Ndi Chikhulupiriro Cholimba?
10, 11. Kodi Kaini ndi Abele ankagwira ntchito zotani, nanga Abele anakhala ndi khalidwe lotani?
10 N’zodziwikiratu kuti pamene anyamatawa ankakula, Adamu ankawaphunzitsa ntchito. Kaini anali mlimi ndipo Abele anali m’busa.
11 Koma Abele anachitanso zinthu zina zofunika kwambiri. M’kupita kwa nthawi iye anasonyeza khalidwe labwino kwambiri la chikhulupiriro, limene Paulo analemba pambuyo pake. Kumbukirani kuti pa nthawiyo panalibe munthu wachitsanzo chabwino amene Abele akanatsanzira. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti azikhulupirira kwambiri Yehova Mulungu? N’kutheka kuti zinthu zitatu zotsatirazi n’zimene zinamuthandiza.
12, 13. Kodi chilengedwe cha Yehova chiyenera kuti chinathandiza bwanji Abele kukhala ndi chikhulupiriro cholimba?
12 Chilengedwe. N’zoona kuti Yehova anali atatemberera nthaka ndipo zimenezi zinachititsa kuti panthaka pazimera minga ndi zitsamba zobaya. Izi zinapangitsa kuti nthakayo isamatulutse zakudya zambiri ngati poyamba. Komabe inkatha kutulutsa chakudya cha anthu chokwanira. Komanso Mulungu sanatemberere nyama, mbalame, nsomba, mapiri, nyanja, mitsinje, mlengalenga, mitambo, dzuwa, mwezi komanso nyenyezi. Choncho Abele ankatha kuona zinthu ngati zimenezi, zomwe zinali umboni woti Yehova Mulungu, yemwe analenga zonse, ndi wachikondi, wanzeru komanso wabwino. (Werengani Aroma 1:20.) N’zoonekeratu kuti kuganizira kwambiri za makhalidwe a Mulungu komanso zomwe iye analenga, kunamuthandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.
13 Abele ankaganizira kwambiri za Yehova. Yerekezani kuti mukumuona ali kuubusa akuweta nkhosa zake. Abusa ankayenda kwambiri ndipo nthawi zambiri ankayenda m’malo amapiri, m’zigwa komanso m’mbali mwa mitsinje. Ankayenda m’malo amenewa kufunafuna msipu wobiriwira, akasupe a madzi komanso malo abwino oti nkhosa zawo zipume. Pa zolengedwa zonse, nkhosa zinkaoneka kuti sizingayende zokha koma zinkafunika munthu woti azizitsogolera komanso kuziteteza. Abele ankaona kuti nayenso ankafunika kuti Mulungu, yemwe ndi wamphamvu kuposa anthu, azimutsogolera, kumuteteza komanso kumusamalira. N’zosakayikitsa kuti iye ankanena zimenezi akamapemphera ndipo izi zinathandiza kuti chikhulupiriro chake chipitirize kulimba.
14, 15. Kodi malonjezo a Yehova anathandiza bwanji Abele kukhala ndi mfundo zambiri zoziganizira?
14 Malonjezo a Yehova. Adamu ndi Hava ayenera kuti anafotokozera ana awo zimene zinachitika m’munda wa Edeni zomwe zinachititsa kuti athamangitsidwe m’mundamo. Zimenezinso zinachititsa kuti Abele akhale ndi zambiri zoganizira.
15 Yehova ananena kuti nthaka idzakhala yotembereredwa. Abale ankaona minga ndi zitsamba zobaya zomwe zinkasonyeza kukwaniritsidwa kwa mawu amene Mulungu ananenawa. Yehova ananenanso kuti Hava azidzavutika akakhala ndi pakati komanso pobereka. Pamene abale ake ena ankabadwa, Abele ayenera kuti anaona izi zikuchitikadi. Yehova anadziwiratu kuti Hava azidzasowa chikondi ndi chisamaliro cha Adamu, mwamuna wake, komanso Adamuyo azidzamulamulira. Abele anaona zinthu zoterezi zikuchitikadi. Zonsezi zinathandiza Abele kuzindikira kuti mawu a Yehova ndi odalirika kwambiri. Choncho, Abele anali ndi zifukwa zomveka zokhulupirira lonjezo la Mulungu lonena za “mbewu” imene idzathetse mavuto onse amene anayambira mu Edeni.—Gen. 3:15-19.
16, 17. Kodi Abele ayenera kuti anaphunzira chiyani kuchokera kwa akerubi?
16 Angelo. Pa nthawiyo panalibe anthu achitsanzo chabwino oti Abele atengere. Komabe padziko lapansi panali angelo omwe Abele akanatha kutengera chitsanzo chawo. Pamene Adamu ndi Hava anathamangitsidwa m’munda wa Edeni, Yehova anaonetsetsa kuti iwo kapena ana awo asabwererenso m’munda umenewo. Pofuna kuteteza malowa kuti anthu asalowemonso, Yehova anaika angelo okhala ndi udindo wapamwamba kwambiri otchedwa akerubi. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linkazungulira mosalekeza.—Werengani Genesis 3:24.
17 Tangoganizani mmene Abele ankamvera ali mnyamata akaona akerubi amenewa. Popeza akerubiwa anali ndi matupi a anthu, Abele ankatha kuwaona ndipo ankaona kuti anali amphamvu kwambiri. Komanso akaona ‘lupangalo,’ limene linkayaka moto ndiponso kuzungulira nthawi zonse, Abele ankazindikira kuti Yehova ndi Mulungu wodabwitsa kwambiri. Pamene iye ankakula anaona kuti akerubiwa anali okhulupirika kwambiri chifukwa sanasiye ntchito yawoyi kapena kutopa nayo. Iwotu anakhala zaka zambirimbiri akuteteza malowa. Choncho Abele anaphunzira kuti akerubi amenewo ankatumikira Yehova Mulungu ndi mtima wonse. Anaonanso kuti iwo anali okhulupirika komanso omvera kusiyana ndi anthu a m’banja lake. N’zosakayikitsa kuti chitsanzo cha angelowa chinam’thandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.
18. Kodi ndi zinthu ziti masiku ano zomwe zingatithandize kukhala ndi chikhulupiriro?
18 Kuganizira chitsanzo cha angelo, malonjezo a Yehova komanso zimene chilengedwe chimaphunzitsa, kunathandiza Abele kuti apitirizebe kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Ndiyetu n’zoonekeratu kuti tonsefe, makamaka achinyamata, tingaphunzire zambiri pa chitsanzo cha Abele. Chitsanzo cha Abele chingathandize achinyamata kudziwa kuti angathe kukhulupirira kwambiri Yehova Mulungu ngakhale zitakhala kuti makolo ndiponso abale awo sakonda Yehova. Masiku ano, ife tili ndi zinthu zambiri zimene zingatithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Tili ndi zinthu monga Baibulo lonse, chilengedwe, komanso zitsanzo zambiri za anthu achikhulupiriro kusiyana ndi mmene zinalili ndi Abele.
N’chifukwa Chiyani Mulungu Anasangalala Ndi Nsembe ya Abele?
19. Kodi m’kupita kwa nthawi Abele anazindikira mfundo yotani?
19 Pamene chikhulupiro cha Abele chinkakula, iye anayamba kufuna kuchita zinthu zosonyeza chikhulupiriro chakecho. Koma kodi munthu angapereke chiyani kwa Mlengi wa chilengedwe chonse, popeza Mulungu sasowa kanthu? M’kupita kwa nthawi Abele anazindikira mfundo yakuti, ngati ndi zolinga zabwino, atapereka kwa Yehova zinthu zabwino kwambiri, Yehovayo adzasangalala kwambiri.
20, 21. Kodi Kaini ndi Abele anapereka nsembe zotani, ndipo Yehova anatani?
20 Abele anakonza zopereka nsembe ya nkhosa. Iye anasankha zonenepa bwino komanso zoyamba kubadwa ndipo atazipha, anatenga mbali zabwinozabwino n’kuzipereka nsembe. Pa nthawiyi, nayenso Kaini anafuna kuti Mulungu amukonde komanso amudalitse, choncho iyenso anapereka nsembe ya zokolola zake. Koma mosiyana ndi Abele, iye analibe maganizo abwino. Kusiyana kumeneku kunaonekera kwambiri pamene iwo ankapereka nsembe zawo.
21 Onse anagwiritsa ntchito guwa la nsembe ndi moto popereka nsembe zawo. Mwina anamanga maguwa awowo pafupi ndi malo amene panali akerubi aja, omwe pa nthawiyo ankaimira Yehova padziko lapansi. Baibulo limati: “Yehova anakondwera ndi Abele ndipo analandira nsembe yake.” (Gen. 4:4) Baibulo silinena kuti Yehova anachita chiyani posonyeza kuti wasangalala ndi nsembe ya Abele.
22, 23. N’chifukwa chiyani Yehova anasangalala ndi nsembe ya Abele?
22 Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti Mulungu asangalale ndi nsembe ya Abeleyo? Kodi zinthu zimene anagwiritsa ntchito popereka nsembeyo ndi zomwe zinasangalatsa Yehova? Abele anapereka nyama yamoyo komanso anakhetsa magazi a nyamayo. Kodi iye ankadziwa kuti nsembe yotereyi idzakhala yofunika kwambiri m’tsogolo? Patapita zaka zambiri, Mulungu anagwiritsa ntchito nsembe ya mwana wankhosa wopanda chilema kuimira nsembe ya Mwana wake wangwiro, “Mwanawankhosa,” amene magazi ake osalakwa anali kudzakhetsedwa. (Yoh. 1:29; Eks. 12:5-7) Sitikudziwa zimene Abele ankadziwa ndiponso kuganiza pa nthawiyo. Koma n’kutheka kuti iye sankadziwa zoti m’tsogolo Yehova adzagwiritsa ntchito nsembe za nyama komanso sankadziwa kuti adzazigwiritsa ntchito bwanji.
23 Koma zimene tikudziwa ndi zakuti, Abele anapereka kwa Yehova zinthu zabwino kwambiri. Yehova anasangalala osati ndi nsembe yokhayo, komanso ndi Abeleyo. Kukonda Yehova komanso chikhulupiriro n’zimene zinachititsa Abele kupereka nsembe yake.
24. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti nsembe ya Kaini payokha sinali yolakwika? (b) Kodi zochita za Kaini zikufanana bwanji ndi za anthu ambiri masiku ano?
24 Koma zinali zosiyana ndi Kaini. Yehova “sanakondwere naye Kaini ndi nsembe yake m’pang’ono pomwe.” (Gen. 4:5) Sikuti Yehova sanakondwere ndi nsembe ya Kaini chifukwa choti inali ya zokolola. Tikutero chifukwa patapita nthawi, Chilamulo cha Mulungu chinkalola anthu kupereka nsembe ya zokolola. (Lev. 6:14, 15) Ponena za Kaini, Baibulo limati: “Zochita zake zinali zoipa.” (Werengani 1 Yohane 3:12.) Koma mofanana ndi anthu ambiri masiku ano, Kaini ankaganiza kuti maonekedwe akunja osonyeza ngati ndi wodzipereka kwa Mulungu angachititse kuti Mulungu asangalale naye. Pasanapite nthawi, zochita za Kaini zinasonyeza kuti analibe chikhulupiriro komanso sankakonda Yehova.
25, 26. Kodi Yehova anamuchenjeza Kaini za chiyani, komabe Kainiyo anachita zotani?
25 Kaini ataona kuti Yehova sanakondwere naye, kodi anafuna kuphunzira pa chitsanzo cha Abele? Ayi ndithu. M’malomwake anayamba kudana kwambiri ndi m’bale wakeyo ngakhale kuti sanaonetsere zimenezi. Koma Yehova anaona zimene zinali mumtima mwa Kaini ndipo moleza mtima anamuuza kuti asinthe. Anamuchenjeza kuti zochita zakezo zingamupangitse kuchita tchimo lalikulu ndipo anamuuza kuti akasintha, ‘amuyanja.’—Gen. 4:6, 7.
26 Kaini sanamvere zimene Mulungu anamuuzazi ndipo anauza Abele kuti apite naye kumunda. Atafika kumeneko, Kaini anakantha Abele n’kumupha. (Gen. 4:8) Choncho tingati Abele anali munthu woyamba kuphedwa pa zifukwa zachipembedzo. Abele anafa koma sikuti nkhani yake inathera pompo.
27. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Abele ali m’gulu la anthu omwe adzaukitsidwe? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzaonane ndi Abele?
27 Mophiphiritsa, magazi a Abele analirira Yehova Mulungu kuti amubwezerere. Mulungu anaonetsetsa kuti chilungamo chachitika ndipo analanga Kaini woipayo chifukwa cha tchimo lake. (Gen. 4:9-12) Chofunika kwambirinso n’chakuti mbiri ya chikhulupiriro cha Abele imatiphunzitsa kanthu masiku ano. Iye anakhala moyo zaka mwina 100 zokha, zomwe ndi nthawi yochepa poyerekeza ndi mmene anthu ankakhalira pa nthawiyo. Koma pa zaka zimenezi, Abele ankaonetsetsa kuti akukhala moyo wokondweretsa Mulungu. Iye anamwalira akudziwa kuti Atate wake wakumwamba, Yehova, ankamukonda ndiponso ankakondwera naye. (Aheb. 11:4) Choncho, tikukhulupirira kuti Yehova akumukumbukira ndipo adzamuukitsa m’paradaiso padziko lapansi. (Yoh. 5:28, 29) Kodi mudzaonana naye? Mungadzaonane naye ngati mukumvetsera pamene iye akulankhula komanso ngati mutatsanzira chikhulupiriro chake.
a Palembali mawu akuti “pamene dziko linakhazikika” amanena za kuberekana kwa anthu, choncho lembali likunena za ana a anthu oyambirira. Nanga n’chifukwa chiyani Yesu ananena za Abele kuti anakhalapo “pamene dziko linakhazikika” pomwe woyamba kubadwa anali Kaini? N’chifukwa choti zochita za Kaini zinasonyeza kuti anali wopandukira Yehova Mulungu. Mofanana ndi makolo ake, zikuoneka kuti Kaini sali m’gulu la anthu odzaukitsidwa komanso kuwomboledwa ku uchimo ndi imfa.