-
Kodi Kukonda Mulungu Kumatanthauzanji?Nsanja ya Olonda—1996 | June 15
-
-
Anadziŵa kuti makolo awo analengedwa angwiro ndi kuti chifuno choyambirira cha Yehova chinali chakuti anthu akhale ndi moyo kosatha. Mwinamwake Adamu ndi Hava anawafotokozera za munda wokongola wa Edene, ndipo mwa njira ina yake ayenera kuti anafotokoza chifukwa chake anapitikitsidwa m’mudzi wa paradaiso umenewo. Kaini ndi Abele angakhale atadziŵanso za ulosi wa Mulungu wolembedwa pa Genesis 3:15. Mwa ulosi umenewo Yehova anasonyeza chifuno chake cha kuwongolera zinthu panthaŵi yake kuti aja omkonda ndi osonyeza kukhulupirika kwa iye akapindule.
Kuphunzira za Yehova ndi mikhalidwe yake kungakhale kutakulitsa mwa Kaini ndi Abele chikhumbo cha kupeza chiyanjo cha Mulungu. Chotero iwo anafikira Yehova mwa kupereka nsembe kwa iye. Nkhaniyo m’Baibulo imati: “Panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova. Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe.”—Genesis 4:3, 4.
-
-
Kodi Kukonda Mulungu Kumatanthauzanji?Nsanja ya Olonda—1996 | June 15
-
-
Kodi nchifukwa ninji Yehova anakana nsembe ya Kaini? Kodi panali cholakwika ndi nsembe yake? Kodi Yehova anakwiya chifukwa chakuti Kaini anapereka nsembe “zipatso za nthaka” m’malo mwa nsembe ya nyama? Si zimenezo kwenikweni. Pambuyo pake, Mulungu analandira mokondwa nsembe za dzinthu ndi zipatso zina za nthaka kuchokera kwa ambiri a olambira ake. (Levitiko 2:1-16) Chotero, malinga ndi umboni, panali cholakwika china ndi mtima wa Kaini. Yehova anatha kusanthula mtima wa Kaini namchenjeza kuti: “Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake.”—Genesis 4:6, 7.
-