TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO
Anapulumutsidwa “Pamodzi ndi Anthu Ena 7”
TAYEREKEZERANI kuti mukumuona Nowa ndi banja lake atakhala pansi moyandikana, ali m’chingalawa kunja kukugwa chimvula. M’chingalawamo muli mdima ngakhale kuti ayatsa nyale. Akumva chiphokoso chochititsa mantha cha mvula yomwe ikuwomba pamwamba komanso m’mbali mwa chingawalacho.
N’zosakayikitsa kuti ali m’chingalawamo, Nowa ankasangalala kwambiri akayang’ana ana ake, azipongozi ake komanso mkazi wake yemwe anali wokhulupirika. Ngakhale kuti nthawi imeneyi inali yochititsa mantha kwambiri, Nowa sankadandaula chifukwa anthu onse amene ankawakonda kwambiri anali otetezeka m’chingalawacho. Nowa ayenera kuti anapemphera pothokoza Yehova kuti wawapulumutsa ndipo ayenera kuti anapemphera mokweza kuti banja lake limve.
Nowa anali ndi chikhulupiriro cholimba. N’chifukwa chake Yehova anamuteteza limodzi ndi banja lake pa nthawi ya chigumula. (Aheberi 11:7) Koma kodi anafunika kukhalabe ndi chikhulupiriro pa nthawi imene anali m’chingalawamo? Inde, ndipo ifenso tifunika kukhalabe ndi chikhulupiriro makamaka m’nthawi yovuta ino. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Nowa.
“MASIKU 40, USANA NDI USIKU”
Mvula inapitiriza kugwa kwa “masiku 40, usana ndi usiku.” (Genesis 7:4, 11, 12) Pa nthawi imeneyi madzi ankangowonjezereka ndipo Nowa ankaona kuti Yehova akuteteza anthu okonda chilungamo ndi kuwononga anthu oipa.
Chigumulacho chinathetsa zachiwawa zomwe zinkachitika nthawi imeneyo. Angelo ena, omwe anatengera khalidwe la Satana lodzikonda, “sanasunge malo awo oyambirira” akumwamba. Iwo anabwera padziko lapansi kudzagona ndi akazi ndipo anawaberekera ana omwe ankatchedwa Anefili. (Yuda 6; Genesis 6:4) Satana ayenera kuti ankasangalala kwambiri kuona angelowo akuchimwira Yehova komanso akulimbikitsa anthu kuchita zachiwawa.
Koma pamene madzi a chigumula ankawonjezereka, angelo oipawo anasiya matupi awo aumunthu n’kubwereranso kumwamba ndipo kuchokera panthawiyi sakanathanso kuvala matupi a anthu. Iwo anasiya akazi ndi ana awo kuti afe limodzi ndi anthu onse pa chigumulacho.
Zaka 600 zimenezi zisanachitike, Yehova anagwiritsa ntchito Inoki kuchenjeza anthu kuti adzawononga anthu onse oipa komanso osalambira Mulungu. (Genesis 5:24; Yuda 14, 15) Kungoyambira nthawi imeneyo, anthu anapitiriza kuchita zoipa, kuwononga dziko komanso kuchita zachiwawa. Choncho nthawi inakwana yoti awonongedwe. Kodi Nowa ndi banja lake ankasangalala kuti Mulungu akuwononga anthu oipa?
Ayi sankasangalala, ngakhalenso Mulungu wawo, yemwe ndi wachifundo, sankasangalala. (Ezekieli 33:11) Yehova anali atawapatsa mwayi woti apulumuke. Anatuma Inoki kuti awachenjeze komanso anatuma Nowa kuti amange chingalawa. Pa nthawi yonse imene Nowa ndi banja lake ankamanga chingalawa anthu ankaona. Kuwonjezera pamenepo, Yehova anauza Nowa kuti akhale “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petulo 2:5) Nowa ankachenjezanso anthu za chiwonongeko ngati mmene Inoki anachitira. Koma kodi anthuwo anamvera? Yesu, yemwe ankaona zimene zinkachitika ali kumwamba, ananena kuti: “Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo.”—Mateyu 24:39.
Tangoganizani mmene Nowa ndi banja lake ankamvera masiku 40, kuchokera pamene Yehova anatseka chitseko cha chingalawacho. Pamene chimvula chinkakhuthuka, Nowa ndi banja lake ayenera kuti ankathandizana pogwira ntchito zosiyanasiyana monga kusamalira nyama zomwe zinali m’chingalawamo. Kenako, chingalawacho chinayamba kugwedezeka n’kuyamba kusuntha. Chifukwa cha kuchuluka kwa madzi, chingalawacho chinayamba “kuyandama pamwamba kwambiri kuchokera padziko lapansi.” (Genesis 7:17) Apa Yehova anasonyeza kuti ndi Mulungu Wamphamvuyonse.
Nowa ayenera kuti ankathokoza kwambiri Yehova chifukwa chomupulumutsa ndi banja lake komanso chifukwa chowagwiritsa ntchito kuchenjeza anthu kuti asawonongedwe. Pa nthawi imene ankawachenjezayo zinkaoneka ngati palibe chimene akuchita chifukwa anthu sankawamvera. Ndipotu Nowa anali ndi achimwene, achemwali komanso achibale ake ena koma onsewo sanamumvere pamene ankawachenjeza. Ndi anthu a m’banja lake okha amene anamumvera. (Genesis 5:30) Nowa ndi banja lake ankati akaganizira za ntchito imene anaigwira yochenjeza anthu, ankaona kuti anachita zonse zomwe akanatha kuthandiza anthuwo kuti apulumuke.
Mmene Yehova anachitira zinthu m’nthawi ya Nowa ndi mmenenso akuchitira masiku ano. (Malaki 3:6) Ndipo Yesu Khristu ananenanso kuti masiku athu ano ndi ofanana ndi “masiku a Nowa.” (Mateyu 24:37) Koma nthawi yathuyi ndi yapadera komanso yovuta kwambiri chifukwa Yehova awononga dziko lonse loipali. Masiku anonso, atumiki a Mulungu akuchenjeza anthu za chiwonongeko chimene chikubwera kutsogoloku. Kodi inuyo mudzamvera kapena mudzanyalanyaza chenjezolo? Ngati munamvera kale chenjezolo, kodi mukugwira nawo ntchito yochenjezanso anthu ena? Nowa ndi banja lake anatipatsa chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi.
‘ANAPULUMUTSIDWA PAMADZI’
Pamene chingalawa chinkayandama, Nowa ndi banja lake ayenera kuti ankamva phokoso la mafunde akuwomba chingalawacho. Kodi zimenezi zinachititsa Nowa kuda nkhawa kuti chingalawacho chiphwasuka? Ayi, Nowa sankada nkhawa chifukwa Baibulo limanena kuti: “Mwa chikhulupiriro, Nowa . . . anamanga chingalawa.” (Aheberi 11:7) N’chiyani chinathandiza Nowa kukhala ndi chikhulupiriro? Yehova anali atachita pangano ndi Nowa kuti adzam’pulumutsa iyeyo pamodzi ndi banja lake pa chigumulacho. (Genesis 6:18, 19) Kodi Mulungu amene analenga chilengedwe chonse komanso zinthu zonse akanalephera kukwaniritsa lonjezo limeneli? Ayi. Nowa ankadziwa kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake ndipo zimenezi zinachitikadi, Nowa ndi banja lake ‘anapulumutsidwa pamadzi.’—1 Petulo 3:20.
Mvulayo inasiya patapita masiku 40, itagwa usana ndi usiku. Tikatengera kalendala yathu iyenera kuti inasiya mu December chaka cha 2370 B.C.E. Koma sikuti anthu amene anali m’chingalawa anatuluka nthawi yomweyo. Chingalawacho chinapitiriza kuyandama pamwamba pamadzi omwe anali atamiza mapiri ataliatali kwambiri. (Genesis 7:19, 20) Tangoganizirani ntchito yaikulu imene Nowa ndi ana ake, Semu, Hamu ndi Yafeti anali nayo pa nthawi imeneyi. Iwo ankafunika kudyetsa komanso kusamalira nyama zonse. Pa nthawi imene Nowa ankalowetsa nyamazi m’chingalawa, Mulungu anachititsa kuti nyamazo zifatse komanso kuti zisamaluse. N’kutheka kuti Mulungu anachitanso zimenezi pa nthawi yonse yomwe zinali m’chingalawacho ndipo zinathandiza kuti asamavutike kuzisamalira.a
Nowa ayenera kuti ankalemba zimene zinkachitikazo monga tsiku limene mvulayo inayamba, limene inasiya komanso kuti padziko lapansi panali madzi masiku 150. Kenako madziwo anayamba kuphwa. Tsiku lina, chingalawacho chinaima pamwamba “pamapiri a Ararati,” omwe masiku ano amapezeka ku Turkey. N’kutheka kuti zimenezi zinachitika m’mwezi wa April chaka cha 2369 B.C.E. Patapita masiku 73, cha mu June, nsonga za mapiri zinayamba kuonekera. Patatha miyezi itatu, mu September, Nowa anachotsa mbali ina ya denga la chingalawacho. Ntchito imeneyi inali yaikulu koma inathandiza kuti m’chingalawamo muziwala komanso kuti azipuma mpweya wabwino. Kenako anatulutsa khwangwala kuti adziwe ngati madzi aphwa. Khwangwalayo atabwerera Nowa anatulutsa njiwa, yomwe inkapita n’kubwerera koma kenako ulendo wina siinabwererenso chifukwa inapeza malo omanga chisa. Zimenezi zinamuthandiza kudziwa kuti madzi aphwa.—Genesis 7:24–8:13.
Ntchito zimene Nowa ankagwira tsiku lililonse sizinkamulepheretsa kuchita zinthu zauzimu zomwe zinali zofunika kwambiri. Iye ankapeza nthawi yopemphera komanso yokambirana ndi banja lake za Atate wawo wakumwamba. Nowa ankadalira Yehova kuti amuthandize pofuna kusankha zochita. Mwachitsanzo, ngakhale kuti Nowa anaona kuti ‘madzi aphweratu padziko lapansi,’ sanaganize zotsegula chitseko n’kutuluka m’chingalawacho. (Genesis 8:14) Anadikira Yehova kuti amuuze nthawi yotuluka.
Mitu ya mabanja masiku ano ingaphunzire zambiri kuchokera kwa munthu wachikhulupiriro ameneyu. Nowa ankachita zinthu mwadongosolo, moleza mtima, mwakhama komanso ankafunitsitsa kuteteza banja lake. Koma kuposa zonsezi, ankaona kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wake ndi kuchita chifuniro cha Yehova Mulungu. Tikatsanzira zimene Nowa anachita, tidzapeza madalitso pamodzi ndi anthu onse amene timawakonda.
“TSOPANO TULUKANI M’CHINGALAWAMO”
Kenako Yehova analamula Nowa kuti: “Tsopano tulukani m’chingalawamo, iweyo, mkazi wako, ana ako, ndi akazi a ana ako.” Nowa anamvera ndipo anatuluka ndi banja lake kenako nyamanso zinatuluka. Kodi nyamazo zinangotuluka mwa chipwirikiti? Ayi, chifukwa Baibulo limanena kuti: “Monga mwa magulu awo, zinatuluka m’chingalawamo.” (Genesis 8:15-19) Atatuluka, Nowa ndi banja lake ayenera kuti ankapuma mpweya wabwino ndipo anaona kuti dziko lonse linali litasintha. Anthu onse oipa kuphatikizapo Anefili komanso angelo ochimwa aja kunali kulibe.b Tsopano Nowa ndi banja lake anafunika kuyambitsanso mtundu watsopano.
Chinthu choyambirira chimene Nowa anachita ndi kupereka nsembe kwa Mulungu. Iye anamanga guwa la nsembe ndipo anatenga nyama “zosadetsedwa” n’kupereka nsembe. (Genesis 7:2; 8:20) Kodi Yehova anasangalala ndi nsembeyo?
Baibulo limanena kuti: “Yehova anamva fungo lokhazika mtima pansi.” Poyamba Yehova ankapwetekedwa mumtima chifukwa cha chiwawa chimene chinadzaza padziko lonse lapansi. Koma tsopano mtima wake unadzaza ndi chimwemwe poona kuti padziko lapansi pali banja lokhulupirika lomwe linkafunitsitsa kuchita chifuniro chake. Yehova sankayembekezera kuti anthuwa azichita chilichonse osalakwitsa chifukwa Baibulo limasonyeza kuti: “Maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira pa ubwana wawo.” (Genesis 8:21) Tiyeni tione mmene Yehova anasonyezera kuti ndi woleza mtima komanso kuti amachitira anthu chifundo.
Mulungu anachotsa temberero limene anaika panthaka. Adamu ndi Hava atangochimwa, Mulungu anatemberera nthaka, zomwe zinapangitsa kuti isamabereke bwino. Lameki anapatsa mwana wake dzina loti Nowa lomwe mwina limatanthauza “Mpumulo.” Pompatsa dzina limeneli analosera kuti Nowa adzabweretsa mpumulo kwa anthu amene ankavutika kulima nthaka imene Yehova anaitemberera. Nowa ayenera kuti anasangalala kwambiri atadziwa kuti ulosiwu wakwaniritsidwa kudzera mwa iyeyo ndipo ankadziwa kuti nthaka iyambiranso kubereka bwino. N’chifukwa chake Nowa anayamba ulimi.—Genesis 3:17, 18; 5:28, 29; 9:20.
Koma Yehova anapatsa Nowa ndi ana ake malangizo osavuta oti aziwathandiza pa moyo wawo monga akuti asamaphe munthu komanso asamadye magazi. Mulungu analonjezanso anthu kuti sadzawononganso dziko lapansi pogwiritsa ntchito madzi. Iye anaika utawaleza mumtambo pofuna kusonyeza kuti adzakwaniritsa lonjezo limeneli. Masiku ano tikaona utawaleza tizikumbukira lonjezo limene Yehova anapereka kwa anthu.—Genesis 9:1-17.
Ngati nkhani ya Nowa inali nthano chabe bwenzi kulibenso utawaleza. Koma Nowa anakhalapodi ndipo anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Chifukwa chakuti m’nthawi imeneyo anthu ankakhala ndi moyo kwa zaka zambiri, Nowa anakhala ndi moyo zaka zina 350, ndipo m’zaka zimenezi anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Pa nthawi ina Nowa anachita zinthu zolakwika kwambiri. Iye analedzera ndipo nkhaniyi inavuta kwambiri pamene mdzukulu wake Kanani anachita tchimo lalikulu. Zimenezi zinachititsa kuti banja lonse la Kanani litembereredwe. Nowa anaonanso mbadwa zake zikuchita machimo akuluakulu monga kulambira mafano komanso chiwawa chomwe chinkachitika m’nthawi ya Nimurodi. Komabe ana ena a Nowa monga Semu anapitirizabe kukhala okhulupirika.—Genesis 9:21-28; 10:8-11; 11:1-11.
Nafenso tiyenera kukhala okhulupirikabe ngakhale tikumane ndi mavuto osiyanasiyana. Anthu ena akasiya kutumikira Yehova, tiyenera kukhala okhulupirika ngati mmene Nowa anachitira. Anthu amene amapirirabe akakumana ndi mavuto, Yehova amawaona kuti ndi amtengo wapatali kwambiri. Ndipo Yesu ananenanso kuti: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.”—Mateyu 24:13.
a Anthu ena amanena kuti zikuoneka kuti Mulungu anachititsa nyama zonse kuti zikhale ngati zaulesi kapena ngati zagona n’cholinga choti zisamadye kwambiri. Kaya Mulungu anachitadi zimenezi kapena ayi, nkhani ndi yakuti anakwaniritsa lonjezo lake lakuti adzapulumutsa anthu ndi zinyama zomwe zinali m’chingalawamo.
b Chigumulacho chinawononganso Munda wa Edeni. Zimenezi zinapangitsa kuti angelo amene analondera mundawu kwa zaka 1,600, abwerere kumwamba.—Genesis 3:22-24.