Kodi Anthu Achiwawa Mumawaona Monga Momwe Mulungu Amawaonera?
Kwanthaŵi yaitali anthu achita chidwi ndi kulemekeza ziphona, zomwe zasonyeza nyonga yaikulu yakuthupi ndi kulimba mtima. Mmodzi wa ziphonazo anali ngwazi ya m’nthano ya mu Girisi wakale, Heracles, kapena kuti Hercules monga momwe aroma amam’dziŵira.
HERACLES anali ngwazi yotchuka kwambiri, womenya nkhondo wamphamvu kwambiri. Malinga n’kunena kwa nthano ina, iye anali munthu wamphamvu ngati za mulungu, mwana wa mulungu wachigiriki Zeus, ndi Alcmene, amayi ake aumunthu. Zochita zake za ungwazizo zinayamba adakali wamng’ono m’chogonekamo ana. Pamene mulungu wamkazi wansanje anatumiza njoka zikuluzikulu ziŵiri kuti zikamuphe, Heracles anazipha. Atakula anamenya nkhondo, anagonjetsa mizukwa, komanso analimbana ndi imfa kuti apulumutse bwenzi lake. Ndiponso anawononga mizinda, kugwirira akazi, kukankhira pansi mnyamata wina kuchokera pa nsanja, ndi kupha mkazi ndi ana ake.
Ngakhale kuti sanali munthu ŵeniŵeni, kuchokera m’nthaŵi yakale Heracles wopekayo wafotokozedwa m’nthano za m’mayiko akale odziŵika kwa Agiriki. Aroma ankam’lambira monga mulungu; amalonda ndi apaulendo ankapemphera kwa iye kuti alemere ndi kutetezedwa kungozi. Kwa zaka zambiri, anthu achita chidwi ndi nthano za zochita zake za ungwazizo.
Chiyambi cha Nthanozo
Kodi nkhani za Heracles ndi ngwazi zina za m’nthano zili ndi maziko m’chochitika chenicheni? M’lingaliro lina, zingakhale nawo. Baibulo limanena za nthaŵi, kale kwambiri m’mbiri ya munthu, pamene “milungu” ndi “anthu amphamvu ngati mulungu” anayendadi padziko lapansi.
Pofotokoza za nthaŵi imeneyo, Mose analemba kuti: “Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana aakazi anawabadwira iwo, kuti ana aamuna a Mulungu anayang’ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.”—Genesis 6:1, 2.
“Ana aamuna a Mulungu” amenewo sanali anthu; anali angelo, ana a Mulungu aungelo. (Yerekezani ndi Yobu 1:6; 2:1; 38:4, 7.) Wolemba Baibulo Yuda ananena kuti angelo ena “sanasunga chikhalidwe chawo choyamba, komatu anasiya pokhala pawopawo.” (Yuda 6) M’mawu ena, anasiya malo awo omwe anawapatsa mu gulu la Mulungu la kumwamba chifukwa anakonda kukhala ndi akazi okongola padziko lapansi. Yuda anawonjeza kuti angelo opanduka ameneŵa anali ngati anthu a mu Sodomu ndi Gomora, omwe ‘anadzipereka ku dama ndi kutsata zilakolako zachilendo.’—Yuda 7.
Baibulo silimalongosola mwatsatanetsatane za zochita za angelo osamvera ameneŵa. Komabe, nthano zakale za ku Girisi ndiponso za kwina kulikonse zimalongosola za milungu yaimuna ndi yaikazi yosiyanasiyana yomwe inakhala pakati pa anthu, monga yosaoneka kapena yooneka. Akavala matupi aumunthu, anali kuoneka okongola kwambiri. Anali kudya, kumwa, kugona, ndiponso ankagonana okhaokha ngakhalenso kugonana ndi anthu. Ngakhale kuti anali kulingaliridwa monga oyera ndi osakhoza kufa, iwo ankanena mabodza ndi kupusitsa anthu, kukangana ndi kumenyana, kunyengerera ndi kugwirira. Ngakhale kuti azikometsera ndi kuzikhotetsa, nthano zoterozo zingasonyeze momwedi zinthu zinalili Chigumula chotchulidwa m’buku la Baibulo la Genesis chisanachitike.
Anthu Amphamvu Akalekale, Anthu Omveka
Angelo osamvera ovala matupi aumunthuwo anagona ndi akazi, ndipo akaziwo anabala ana. Ameneŵa sanali ana wamba. Anali Anefili, mbali ina anthu, mbali ina angelo. Nkhani ya m’Baibulo imati: “Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu ataloŵa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.”—Genesis 6:4.
Liwu la Chihebri lakuti “anefili” kwenikweni limatanthauza “wogwetsa” awo amene amagwetsa ena, kapena omwe amachititsa ena kugwa, kupyolera m’ziwawa. Choncho, sizodabwitsa kuti nkhani ya m’Baibulo inanenanso kuti: “Dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.” (Genesis 6:11) Anthu amphamvu ngati mulungu a mu nthanowo, monga Heracles ndinso ngwazi yachibabulo Gilgamesh, amafanana kwambiri ndi Anefili.
Onani kuti Anefili ankawatcha kuti “anthu amphamvu” ndiponso “anthu omveka.” Mosiyana ndi munthu wolungamayo Nowa, yemwe anakhalako m’nyengo imodzimodziyo, Anefili analibe chidwi cholimbikitsa kutchuka kwa Yehova. Iwo ankangofuna kutchuka kwa iwo eni, kutamandidwa, ndi kudzipangira mbiri. Kupyolera m’zochita zamphamvu, zomwe mosakayikira zinaphatikizapo ziwawa ndi kukhetsa magazi, iwo monga mwa kulakalaka kwawo anatchukadi m’dziko lopanda umulungu loŵazingalo. Analidi ngwazi zamphamvu za m’tsiku lawo—owopedwa, kulemekezedwa, ndipo mwachionekere osagonjetseka.
Pamene kuli kwakuti Anefili ndi atate awo otha mphamvu aungelowo angakhale atasangalala ndi kutchuka pamaso pa anthu okhalako panthaŵiyo, iwo mwachionekere sanali otamandika kwa Mulungu. Njira yawo ya moyo inali yonyansa. Pachifukwa chimenechi, Mulungu anawalanga. Mtumwi Petro analemba kuti: “Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzidwe; ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi aŵiri pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.”—2 Petro 2:4, 5.
Pa Chigumula chadziko lonse, angelo opandukawo anavula matupi awo aumunthu ndi kubwerera mwamanyazi ku malo auzimu. Mulungu anawalanga mwa kuwalepheretsa kuvalanso matupi aumunthu. Anefili, ana amphamvu zoposa zaumunthu a angelo osamverawo, onse anawonongedwa. Nowa yekha ndi banja lake laling’onolo ndiwo anapulumuka Chigumulacho.
Anthu Omveka Lerolino
Lerolino, milungu ndiponso anthu amphamvu ngati mulungu palibe tsopano padziko lapansi. Komabe, ziwawa ndiye zili ponseponse. Anthu otchuka amakono amatamandidwa m’mabuku, m’mafilimu, m’wailesi yakanema, ndi m’nyimbo. Iwo saganiza n’komwe zotembenuza tsaya lina, kukondana nawo adani awo, kufunafuna mtendere, kukhululukira, kapena kupeŵa ziwawa. (Mateyu 5:39, 44; Aroma 12:17; Aefeso 4:32; 1 Petro 3:11) Mmalo mwake, anthu amphamvu amakono amachititsa anthu chidwi chifukwa cha nyonga zawo ndiponso chifukwa cha kukhoza kwawo kumenya, kulipsira okha, ndi kuchita ziwawa zoopsa pobwezera ziwawa.a
Kaonedwe ka Mulungu ka anthu otereŵa sikanasinthe chiyambire m’nthaŵi ya Nowa. Yehova sachita chidwi ndi okonda ziwawa kapena kusangalatsidwa ndi zochita zawozo. Wamasalmo anaimba kuti: “Yehova ayesa wolungama mtima: Koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.”—Salmo 11:5.
Nyonga Yamtundu Wina
Yemwe anachita zosiyana kotheratu ndi anthu amphamvu achiwawawo ndi munthu wotchuka kwambiri kuposa onse amene anakhalako, Yesu Kristu, mwamuna wamtendere. Ali padziko lapansi “sanachita chiwawa.” (Yesaya 53:9) Pamene adani ake anadza kudzam’gwira m’munda wa Getsemane, om’tsatira ake anali ndi malupanga. (Luka 22:38, 47-51) Ophunzirawo akanatha kukhazikitsa gulu la nkhondo pofuna kumuteteza kuti asaperekedwe kwa Ayuda.—Yohane 18:36.
Ndithudi, mtumwi Petro anatulutsa lupanga lake kuti atchinjirize Yesu, koma Yesu anati kwa iye: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:51, 52) Inde, chiwawa chimabala chiwawa, monga momwedi mbiri ya anthu mobwerezabwereza yasonyezera. Pambali pa kuthekera kwa kudziteteza ndi zida, Yesu anali ndi njira inanso yodzitetezera. Iye anauzanso Petro kuti: “Uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri?”—Mateyu 26:53.
M’malo moyembekezera kutetezeredwa m’njira ya chiwawa kapena kutetezedwa ndi angelo, Yesu analola kugwidwa ndi omwe anamuphawo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi chinali chakuti iye ankadziŵa kuti nthaŵi inali isanafike yakuti Atate wake wakumwamba athetse kuchita zoipa padziko lapansi. M’malo modzichitira yekha zinthu zonse, Yesu anadalira Yehova.
Kumeneku sikunali kufooka koma inali imodzi mwa nyonga zam’kati. Yesu anasonyeza chikhulupiriro cholimba chakuti Yehova anali kudzakonza zinthu bwino lomwe m’nthaŵi ndi m’njira Yakeyake. Chifukwa cha kumvera kwake, Yesu anakwezedwa pamalo apamwamba kwambiri achiŵiri kwa Yehova yekha. Mtumwi Paulo analemba ponena za Yesu kuti: “Anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda. Mwa ichinso Mulungu anam’kwezetsa Iye, nam’patsa dzina limene liposa mayina onse, kuti m’dzina la Yesu, bondo lililonse lipinde, la za m’mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.”—Afilipi 2:8-11.
Lonjezo la Mulungu Lothetsa Ziwawa
Akristu oona amakhala ndi moyo potsanzira chitsanzo ndi ziphunzitso za Yesu. Samachita chidwi kapena kutsanzira anthu akudziko otchuka ndi achiwawa. Amadziŵa kuti m’nthaŵi yoikika ya Mulungu, anthu oterowo adzasesedwa kosatha, monga momwedi zinachitikira kwa oipa a m’nthaŵi ya Nowa.
Mulungu ndi Mlengi wa dziko lapansi ndi mtundu wa anthu. Iye alinso Mfumu yoyenerera. (Chivumbulutso 4:11) Ngati woweruza waumunthu amakhala ndi mphamvu zalamulo zom’yeneretsa kupereka zigamulo zachiweruzo, Mulungu ali ndi mphamvu zoposa zochitira zimenezo. Kulemekeza kwake mfundo zake zachikhalidwe zolungamazo, komanso chikondi chake pa omwe amam’konda iyeyo, zidzam’sonkhezera kuthetsa kuipa konse ndi omwe amakuchita.—Mateyu 13:41, 42; Luka 17:26-30.
Zimenezi zidzadzetsa mtendere wosatha padziko lapansi, mtendere wozikika zolimba pa chiweruzo ndi chilungamo. Zimenezi zinaloseredwa mu ulosi wodziŵika bwino zedi wokhudza Yesu Kristu wakuti: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa pheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kumkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”—Yesaya 9:6, 7.
Choncho, pazifukwa zabwino, Akristu amamvera uphungu wouziridwa wakale lomwe wakuti: “Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.”—Miyambo 3:31, 32.
[Mawu a M’munsi]
a Anthu achiwawa m’maseŵera ambiri apavidiyo ndi m’mafilimu ambiri abodza la sayansi kaŵirikaŵiri amasonyeza mikhalidwe yoipa ndi yachiwawa imeneyi moŵirikiza.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
ANTHU AMPHAMVU AMAKONO AMACHITITSA ANTHU CHIDWI CHIFUKWA CHA NYONGA ZAWO NDIPONSO CHIFUKWA CHA KUKHOZA KWAWO KUCHITA ZIWAWA ZOOPSA KWAMBIRI POBWEZERA ZIWAWA
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Alinari/Art Resource, NY