Kuyenda ndi Mulungu—Masitepe Oyambirira
“Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”—YAKOBO 4:8.
1, 2. Kodi nchifukwa chiyani mukunena kuti kutumikira Yehova uli mwayi waukulu?
MUNTHUYO anali atavutika m’ndende zaka zambiri. Kenako anaitanidwa kukaonekera pamaso pa wolamulira dzikolo. Zinthu zinachitika mofulumira. Mwadzidzidzi, mkaidiyo anapezeka kuti akutumikira mfumu yamphamvu kwambiri padziko lonse lapansi panthaŵiyo. Amene anali mkaidiyo anapatsidwa udindo waukulu ndiponso wolemekezeka kwabasi. Yosefe—munthu amene mapazi ake anali m’matangadza nthaŵi inayake—tsopano anali kuyenda ndi mfumu!—Genesis 41:14, 39-43; Salmo 105:17, 18.
2 Lero, anthu ali ndi mwayi wotumikira winawake wamkulu kuposa Farao wa Igupto. Wam’mwambamwamba m’chilengedwe chonse akupempha onse kumtumikira. Kuchita zimenezo komanso kukhala paunansi wapafupi ndi Yehova, Mulungu wamphamvuyonse, ndi mwayi wochititsadi nthumanzi! Malemba amati iye ngwamphamvu zazikulu, waulemerero komanso wabata, wokongola, ndi waukoma. (Ezekieli 1:26-28; Chivumbulutso 4:1-3) Zochita zake zonse zimakhala zachikondi. (1 Yohane 4:8) Sanama. (Numeri 23:19) Ndipo Yehova sakhumudwitsa konse aja okhulupirika kwa iye. (Salmo 18:25) Mwa kutsatira zinthu zolungama zimene iye amafuna, tingakhale ndi miyoyo yachimwemwe ndi yatanthauzo tsopano, ndi moyo wosatha m’tsogolo. (Yohane 17:3) Kulibe wolamulira waumunthu aliyense amene angapereke madalitso ndi mwayi zofanana ndi zimenezi mpang’ono pomwe.
3. Kodi Nowa ‘anayenda ndi Mulungu’ m’njira yotani?
3 Kalekale, kholo lathu Nowa anatsimikiza mtima kutsatira chifuniro ndi cholinga cha Mulungu. Ponena za iye, Baibulo limati: “Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m’mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.” (Genesis 6:9) Mwachionekere, Nowa sanayende ndi Mulungu mmene wina angayendere ndi munthu mnzake, pakuti kulibe munthu “anaona Mulungu nthaŵi zonse.” (Yohane 1:18) M’malo mwake, Nowa anayenda ndi Mulungu m’njira yakuti anachita zimene Mulungu anamuuza kuchita. Chifukwa chakuti Nowa anapereka moyo wake pakuchita chifuniro cha Yehova, anali ndi unansi wabwino ndiponso wolimba ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Mofanana ndi Nowa, anthu mamiliyoni ambiri lero ‘akuyenda ndi Mulungu’ mwa kutsatira uphungu ndi malangizo a Yehova. Kodi munthu amayamba motani kuyenda panjirayo?
Afunika Chidziŵitso Cholongosoka
4. Kodi Yehova amawaphunzitsa motani anthu ake?
4 Kuti tiyende ndi Yehova, mpofunika kuti timdziŵe kaye. Mneneri Yesaya analosera kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake; chifukwa m’Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mawu a Yehova kuchokera m’Yerusalemu.” (Yesaya 2:2, 3) Inde, tili ndi chidaliro chakuti Yehova adzaphunzitsa onse amene akufuna kuyenda m’njira zake. Yehova wapereka Mawu ake, Baibulo, ndipo amatithandiza kulimvetsa. Njira ina imene amachitira zimenezo ndi mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Yehova akugwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika” kupereka malangizo auzimu m’zofalitsa zozikidwa pa Baibulo, misonkhano yachikristu, ndi makonzedwe a phunziro la Baibulo la panyumba laulere. Mulungu amathandizanso anthu ake kumvetsa Mawu ake mwa mzimu wake woyera.—1 Akorinto 2:10-16.
5. Nchifukwa chiyani choonadi cha m’Malemba chili chamtengo wapatali?
5 Ngakhale kuti sitilipira ndalama kuti tipeze choonadi cha Baibulo, icho nchamtengo wapatali. Pamene tiŵerenga Mawu a Mulungu, timaphunzira za Mulungu mwiniyo—dzina lake, umunthu wake, cholinga chake, ndi njira imene amachitira ndi anthu. Timaphunziranso za mayankho omasula a mafunso ofunika pamoyo akuti: Nchifukwa chiyani tili ndi moyo? Nchifukwa chiyani Mulungu amalola kuvutika? Kodi m’tsogolo muli zotani? Nchifukwa chiyani timakalamba ndi kufa? Kodi pali moyo pambuyo pa imfa? Ndiponso, timaphunzira za chifuniro cha Mulungu kwa ife, ndiko kuti, mmene tiyenera kuyendera kuti timkondweretse mokwanira. Timaphunzira kuti zimene iye amafuna nzotheka ndipo zipindulitsa kwambiri tikazichita. Popanda malangizo a Mulungu, bwenzi tisakumvetsa zinthu ngati zimenezi.
6. Kodi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chimatitheketsa kutsatira njira yotani?
6 Choonadi cha Baibulo nchamphamvu ndipo chimatisonkhezera kusintha miyoyo yathu. (Ahebri 4:12) Tisanapeze chidziŵitso cha Malemba, tinkangoyenda “monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino.” (Aefeso 2:2) Koma chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu chimatilembera njira ina kuti tizitha ‘kuyenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo.’ (Akolose 1:10) Zimasangalatsa kwambiri kutenga masitepe athu oyambirira poyenda ndi Yehova, Munthu wofunika koposa m’chilengedwe chonse!—Luka 11:28.
Masitepe Aŵiri Ofunika—Kudzipatulira ndi Ubatizo
7. Pamene tiphunzira Mawu a Mulungu, kodi ndi choonadi chiti chonena za atsogoleri aumunthu chimene timadziŵa?
7 Pamene chidziŵitso chathu cha Baibulo chikula, timayamba kuona nkhani zaumunthu ndi miyoyo yathu mothandizidwa ndi kuunika kwauzimu kwa Mawu a Mulungu. Motero timadziŵa choonadi chofunika kwambiri. Choonadi chimenecho chinatchulidwa kalekale ndi mneneri Yeremiya, yemwe analemba kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Anthu—tonsefe—tifunikira chitsogozo cha Mulungu.
8. (a) Kodi nchiyani chimasonkhezera anthu kudzipatulira kwa Mulungu? (b) Kodi kudzipatulira kwachikristu nchiyani?
8 Kumvetsa mfundo yofunika kwambiri imeneyi kumatisonkhezera kufuna chitsogozo cha Yehova. Ndipo kukonda kwathu Mulungu kumatisonkhezera kupatulira moyo wathu kwa iye. Kudzipatulira kwa Mulungu kumatanthauza kumfika m’pemphero ndi kumlonjeza mwalumbiro kuti tidzagwiritsa ntchito moyo wathu kumtumikira ndi kuyenda m’njira zake mokhulupirika. Mwa kuchita zimenezo, timatsatira chitsanzo cha Yesu, amene anadzipereka kwa Yehova motsimikiza mtima kuchita chifuniro chaumulungu.—Ahebri 10:7.
9. Nchifukwa chiyani anthu amapatulira moyo wawo kwa Yehova?
9 Yehova Mulungu sakakamiza kapena kuumiriza aliyense kuti adzipatulire kwa iye. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 9:7.) Ndiponso, Mulungu safuna kuti wina aliyense apatulire moyo wake kwa Iye chifukwa chongotengeka mtima mwakanthaŵi. Asanabatizidwe, munthu ayenera kukhala atakhala kale wophunzira, ndipo zimenezo zimafuna khama ndithu kuti apeze chidziŵitso. (Mateyu 28:19, 20) Paulo anapempha aja amene anali kale obatizidwa ‘kupereka matupi awo nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika ndi mphamvu yawo ya kulingalira.’ (Aroma 12:1, NW) Timadzipatulira kwa Yehova Mulungu mwa kugwiritsa ntchito mofananamo mphamvu yathu ya kulingalira. Titadziŵa zofunikira ndi kulingalira bwinobwino za nkhaniyo, timapatulira moyo wathu kwa Mulungu mwaufulu ndi mwachimwemwe.—Salmo 110:3.
10. Kodi kudzipatulira kumagwirizana motani ndi ubatizo?
10 Titamfika Mulungu m’pemphero mwamseri kumuuza za kufunitsitsa kwathu kuyenda m’njira zake, timatenga sitepe lotsatira. Timadziŵikitsa poyera kudzipatulira kwathu mwa kubatizidwa m’madzi. Zimenezi ndiko kulengeza poyera kuti tawinda kuchita chifuniro cha Mulungu. Kuchiyambi kwa utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu anabatizidwa ndi Yohane, motero akumatiikira chitsanzo. (Mateyu 3:13-17) Pambuyo pake, Yesu anatuma otsatira ake kupanga ophunzira ndi kuwabatiza. Chotero, kudzipatulira ndi ubatizo ali masitepe ofunika kwa aliyense wofuna kuyenda ndi Yehova.
11, 12. (a) Kodi ubatizo ungayerekezedwe motani ndi ukwati? (b) Kodi ndi kufanana kotani kumene kuli pakati pa unansi wathu ndi Yehova ndi uja wa mwamuna ndi mkazi wake?
11 Kukhala wophunzira wa Yesu Kristu wodzipatulira ndi wobatizidwa kuli ngati kukwatira. M’maiko ambiri, tsiku la ukwati lisanafike pamakhala masitepe angapo. Mwamuna ndi mkazi amakumana, kuzoloŵerana, kenako kukondana. Ndiyeno pamatsatira chitomero. Ukwati umaonetsa poyera zimene anasankha mseri—kukwatirana ndi kukhala pamodzi monga mwamuna ndi mkazi wake. Ukwati ndiwo umasonyeza poyera chiyambi cha unansi wapadera umenewo. Deti limenelo ndilo chiyambi cha banja. Mofananamo, ubatizo umakhala chiyambi cha moyo wodzipereka pakuyenda ndi Yehova mu unansi wodzipatulira.
12 Talingalirani kufanana kwinanso. Tsiku la ukwati wawo litapita, chikondi pakati pa mwamuna ndi mkazi wake chiyenera kukula ndi kulimba. Kuti akhale oyandikana kwambiri nthaŵi zonse, okwatiranawo ayenera kuyesetsa mopanda dyera kusunga ukwati wawo ndi kuulimbitsa. Ngakhale kuti sitiloŵa mu ukwati ndi Mulungu, titabatizidwa tiyenera kulimbikira kusunga unansi wapafupi ndi Yehova. Iye amaona ndi kuyamikira khama lathu pochita chifuniro chake ndipo amayandikira kwa ife. “Yandikirani kwa Mulungu,” analemba motero wophunzira Yakobo, “ndipo adzayandikira kwa inu.”—Yakobo 4:8.
Kuyenda m’Mapazi a Yesu
13. Poyenda ndi Mulungu, kodi tiyenera kutsatira chitsanzo cha yani?
13 Kuti tiyende ndi Yehova, tiyenera kutsatira chitsanzo choperekedwa ndi Yesu Kristu. Mtumwi Petro analemba kuti: “Kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.” (1 Petro 2:21) Popeza Yesu anali wangwiro ndipo ife tilibe ungwiro, sitingatsate chitsanzo chake popanda kuphonya. Komano, Yehova amafuna kuti tichite zonse zomwe tingathe. Tiyeni tipende mbali zisanu za moyo wa Yesu ndi utumiki wake zimene Akristu odzipatulira ayenera kulimbikira kutsanzira.
14. Kodi kudziŵa Mawu a Mulungu kumaphatikizapo chiyani?
14 Yesu anali ndi chidziŵitso cholongosoka komanso chachikwanekwane cha Mawu a Mulungu. Mu utumiki wake, Yesu nthaŵi zambiri anagwira mawu m’Malemba Achihebri. (Luka 4:4, 8) Inde, atsogoleri oipa achipembedzo a masiku amenewo anagwiranso Malemba. (Mateyu 22:23, 24) Kusiyana kwake kunali kwakuti Yesu anamvetsa tanthauzo la Malemba, ndipo anawagwiritsa ntchito m’moyo wake. Iye anadziŵa malembo a Chilamulo komanso cholinga chake. Pamene titsatira chitsanzo cha Kristu, ifenso tiziyesetsa kumvetsa Mawu a Mulungu, kupeza tanthauzo lake, kapena cholinga chake. Mwa kutero, tingakhale antchito ovomerezedwa ndi Mulungu okhoza ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’—2 Timoteo 2:15.
15. Kodi Yesu anapereka motani chitsanzo pa kulankhula za Mulungu?
15 Kristu Yesu anauza ena za Atate wake wakumwamba. Yesu sanangosunga chidziŵitso cha Mawu a Mulungu. Ngakhale adani ake anamutcha “Mphunzitsi,” chifukwa kulikonse kumene anapita anauza ena za Yehova ndi zolinga Zake. (Mateyu 12:38) Yesu analalikira poyera m’bwalo la kachisi, m’masunagoge, m’mizinda, ndi m’midzi. (Marko 1:39; Luka 8:1; Yohane 18:20) Anaphunzitsa mwachifundo ndi mokoma mtima, kusonyeza chikondi kwa amene anawathandiza. (Mateyu 4:23) Amene amatsatira chitsanzo cha Yesu amapezanso malo ndi njira zambiri zophunzitsira ena za Yehova Mulungu ndi zolinga zake zodabwitsa.
16. Kodi unansi wa Yesu ndi olambira Yehova anzake unali wapafupi motani?
16 Yesu anakonda kwambiri ena amene analambira Yehova. Pamene Yesu anali kulankhula kwa makamu nthaŵi ina, amayi ake ndi abale ake osakhulupirira anadza kudzalankhula naye. Nkhaniyo ya Baibulo imati: “Munthu anati kwa iye, Onani, amayi wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu. Koma iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amayi wanga ndani? Ndi abale anga ndi ayani? Ndipo anatambalitsa dzanja lake pa ophunzira ake, nati, Penyani amayi wanga ndi abale anga! Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.” (Mateyu 12:47-50) Zimenezi sizitanthauza kuti Yesu ananyanyala achibale ake, pakuti zochitika pambuyo pake zionetsa kuti sanatero. (Yohane 19:25-27) Komano, nkhani imeneyi ikugogomezera chikondi chimene Yesu anali nacho kwa okhulupirira anzake. Mofananamo lero, amene akuyenda ndi Mulungu amakonda kuyanjana ndi atumiki ena a Yehova ndipo amafika powakonda kwambiri.—1 Petro 4:8.
17. Kodi Yesu anakuona motani kuchita chifuniro cha Atate wake wakumwamba, ndipo zimenezi ziyenera kutikhudza motani?
17 Mwa kuchita chifuniro cha Mulungu, Yesu anasonyeza chikondi kwa Atate wake wakumwamba. Yesu anamvera Yehova m’zonse. Iye anati: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Kristu ananenanso kuti: “Ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye [Mulungu] nthaŵi zonse.” (Yohane 8:29) Yesu anakonda Atate wake wakumwamba kwambiri moti “anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda [“mtengo wozunzirapo,” NW].” (Afilipi 2:8) Chotero, Yehova anadalitsa Yesu, kumkweza kumpatsa malo aulamuliro ndi olemekezeka achiŵiri kwa Yehova yekha. (Afilipi 2:9-11) Monga Yesu, ife timasonyeza chikondi chathu kwa Mulungu mwa kusunga malamulo ake ndi kuchita chifuniro chake.—1 Yohane 5:3.
18. Kodi ndi motani mmene Yesu anaikira chitsanzo pankhani ya kupemphera?
18 Yesu anali munthu wokonda kupemphera. Anapemphera pa ubatizo wake. (Luka 3:21) Asanasankhe atumwi ake 12, anachezera usiku wonse kupemphera. (Luka 6:12, 13) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera. (Luka 11:1-4) Usiku imfa yake isanafike, anapempherera ophunzira akewo ndi kupemphera limodzi nawo. (Yohane 17:1-26) Pemphero linali lofunika kwambiri pamoyo wa Yesu, mmenenso liyenera kukhalira pamoyo wathu, popeza ndife otsatira ake. Ndi mwayi waukulu kulankhula kwa Mfumu ya Chilengedwe Chonse mwa pemphero! Ndiponso, Yehova amayankha mapemphero, pakuti Yohane analemba kuti: “Uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziŵa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziŵa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.”—1 Yohane 5:14, 15.
19. (a) Kodi ndi mikhalidwe iti ya Yesu imene tiyenera kutsanzira? (b) Kodi timapindula motani mwa kuphunzira za moyo ndi utumiki wa Yesu?
19 Tingaphunzire zambiri zedi mwa kupenda mosamalitsa moyo wapadziko lapansi ndi utumiki wa Yesu Kristu! Talingalirani mikhalidwe imene anaonetsa: chikondi, chifundo, kukoma mtima, nyonga, kusamala, kulolera, kudzichepetsa, kulimba mtima, ndi kusadzikonda. Tikaphunzira zambiri ponena za Yesu, chikhumbo chathu chokhala otsatira ake okhulupirika chimakulanso. Kudziŵa Yesu kumatiyandikizanso kwambiri kwa Yehova. Ndipotu Yesu anali chithunzi changwiro cha Atate wake wakumwamba. Anali kumdziŵa bwino Yehova moti anati: “Wandiona Ine waona Atate.”—Yohane 14:9.
Khulupirirani Mulungu Kuti Akuchirikizeni
20. Kodi tingakhale motani ndi chidaliro poyenda ndi Yehova?
20 Pamene ana angoyamba kuphunzira kuyenda, amadzandira. Nangano amaphunzira motani kuyenda mwachidaliro? Mwa kudzizoloŵeretsa ndi kulimbikira. Eya, amene akuyenda ndi Yehova amayesetsa kunyamula miyendo mwachidaliro ndi mosamala. Izinso zimafuna nthaŵi ndi kulimbikira. Paulo anatchula za kufunika kwa kulimbikira poyenda ndi Mulungu pamene analemba kuti: “Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.”—1 Atesalonika 4:1.
21. Pamene tikuyenda ndi Yehova, kodi tingasangalale ndi madalitso otani?
21 Ngati ndife odzipereka kwathunthu kwa Mulungu, adzatithandiza kuyendabe ndi iye. (Yesaya 40:29-31) Kulibe chimene dzikoli lingapatse munthu chimene chingafanane ndi madalitso amene iye amapatsa aja amene akuyenda m’njira zake. Iye ndiye ‘akutiphunzitsa kupindula, amene akutitsogolera m’njira yoyenera ife kupitamo. Ndipo titamvera malamulo ake mtendere wathu udzakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chathu monga mafunde a nyanja.’ (Yesaya 48:17, 18) Mwa kulabadira pempho la kuyenda ndi Mulungu ndi kuchita zimenezo mokhulupirika, tingakhale pamtendere ndi iye kosatha.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Nchifukwa chiyani uli mwayi waukulu kuyenda ndi Mulungu woona?
◻ Nchifukwa chiyani kuphunzira, kudzipatulira, ndi ubatizo ali masitepe oyambirira pa kuyenda ndi Yehova?
◻ Kodi tingawatsatire motani mapazi a Yesu?
◻ Tidziŵa bwanji kuti Yehova adzatichirikiza pamene tikuyenda naye?
[Zithunzi patsamba 13]
Kuphunzira, kudzipatulira, ndi ubatizo ndiwo masitepe oyambirira pa kuyenda ndi Mulungu