Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi nchifukwa ninji Nowa anatumiza khungubwe ndiyeno njiŵa kuchokera m’chingalawa?
Baibulo silimapereka malongosoledwe atsatanetsatane. Komabe, mukuwoneka kukhala munali nzeru inayake m’kachitidwe ka Nowa.
Kwamasiku 40 ndi usiku 40, padziko lapansi panagwa chimvumbi champhamvu, chochititsa chigumula chimene chinamiza ngakhale nsonga za mapiri kwa miyezi isanu. Ndiyeno ‘chingalawa chinaima pa mapiri a Ararati.’ (Genesis 7:6–8:4) Pambuyo pa miyezi ingapo, ‘padaoneka mitu ya mapiri,’ Nowa ‘anatulutsa khungubwe, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina.’—Genesis 8:5, 7.
Koma chifukwa ninji khungubwe? Mbalame imeneyi njamphamvu zakuuluka, ndipo ikhoza kudya zakudya zosiyanasiyana, kuphatikizapo nyama zakufa. Nowa angakhale anatumiza khungubweyo kuwona ngati akabwerera kapena akachokeratu m’chingalawa, mwinamwake akumadya zotsala za mitembo pamene madzi anaphwa ndi mtunda kuwonekera. Komabe, khungubweyo sanapitiretu. Baibulo limanena kuti anabwerera, koma silimanena kuti anabwerera kwa Nowa. Mwinamwake anabwera kudzakhala pa chingalawacho ndi kumauluka kukafuna chakudya choyandama pamadzi osefukirabe.
Pambuyo pake, Nowa anatumiza njiŵa. Timaŵerenga kuti: ‘Njiŵayo sinapeza popondapo phazi lake, nibwera kwa iye ku chingalawako.’ (Genesis 8:9) Ichi chimapereka lingaliro lakuti mwa iyo yokha, njiŵa inakhoza kuthandiza kudziŵa ngati madziwo adaphwa. Njiŵa zimasonyeza kukhulupirika kwa anthu. Nowa anayembekezera kuti njiŵayo ikabwerera, osati kudzangokhala pachingalawa, koma kwa Nowa iyemwiniyo.
Zikunenedwa kuti njiŵa zimatera kokha panthaka youma, zimauluka chamunsi m’zigwa, ndipo zimadya zomera. (Ezekieli 7:16) Grzimek’s Animal Life Encyclopedia imanena kuti: “Popeza kuti nkhunda zonse ndi njiŵa zimadya mbewu, nkovuta kuti zipeze chakudya pamene chipale chofeŵa [kapena madzi] chikuta nthaka koposa tsiku limodzi, popeza kuti zimapeza chakudya chawo panthaka.” Chotero njiŵayo iyenera kuti inabweretsa kwa Nowa umboni wakuti inapeza nthaka youma kapena zomera zomaphuka. Nthaŵi yoyamba imene Nowa anaitumiza, njiŵayo inangobwerera kwa iye m’chingalawamo. Nthaŵi yachiŵiri, njiŵayo inabwera ndi tsamba la azitona. Nthaŵi yachitatu, sinabwerere, kupereka umboni wakuti kunali kotheka ndi kwachisungiko kuti Nowa atuluke m’chingalawa.—Genesis 8:8-12.
Pamene kuli kwakuti ena angalingalire zimenezi kukhala tsatanetsatane wongochitika mwamwaŵi, chenicheni chakuti nkhaniyo njotsimikiziridwa motero, mosalongosola zonse zoloŵetsedwamo, kumasonyeza kudalirika kwa Baibulo. Chimatipatsa chifukwa chowonjezereka chakuvomereza nkhaniyo kukhala, osati yopeka, koma yolongosoka mowonadi. Kusoŵeka kwa tsatanetsatane wochuluka ndi malongosoledwe kumasonyezanso kuti pali zinthu zokondweretsa zimene Akristu okhulupirika ayenera kuyembekezera kudzafunsa Nowa pamene adzaukitsidwa kuti adzafotokoze iyemwini zifukwa ndi mmene anachitira zinthu.—Ahebri 11:7, 39.