Lingaliro la Baibulo
Kodi Akristu Ayenera Kukhalira Mbali Chilango cha Imfa?
“NCHOLAKWIKA malinga ndi makhalidwe abwino ndi mwambo.” “Nchabwino ndipo ncholungama.” Malingaliro otsutsana ameneŵa anachokera kwa atsogoleri achipembedzo aŵiri, onse odzitcha kukhala Akristu. Iwo anali kulimbana pa imodzi ya nkhani zazikulu kwambiri za masiku ano—chilango cha imfa. Nkhani ya mu nyuzipepala imene inawagwira mawu inati: “Pamene atsogoleri achipembedzo akangana pankhani ya chilango cha imfa, kumbali zonse ziŵiri amagwira mawu a Baibulo kuchirikiza malingaliro awo.”
Ena amanena kuti chilango cha imfa chimatetezera anthu opanda liwongo, chimalimbikitsa chilungamo, ndipo chimaletsa upandu waukulu. Ena amalimbikira kunena kuti ndi choipa—njira yolimbana ndi chiwawa mwa kuchita chiwawa chowonjezereka ndipo yoipa kwambiri polinganiza ndi njira yabwino yosinthira apandu, kuwathandizira kuti akhale anthu othandiza m’chitaganya.
M’zandale ku United States, mkangano umenewu ngwaukulu kwambiri, ndipo atsogoleri achipembedzo sanazengereze kuloŵereramo. Komabe, mungadzifunse kuti, ‘Kodi Baibulo limanenapo zilizonse pankhani ya chilango cha imfa?’ Zoonadi, limatero.
Kupereka “Lupanga” kwa Maulamuliro Aumunthu
Chigumula cha m’nthaŵi ya Nowa chitangotha, Yehova Mulungu ananenetsa za mtengo wa moyo wa munthu ndiyeno anati: “Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa.” (Genesis 9:6) Komabe, chimenechi sichinali chilolezo chopanda malire cha kubwezera. M’malo mwake, chinatanthauza kuti maulamuliro aumunthu oikidwapo mwalamulo kuyambira pamenepo analoledwa kupha awo amene anapha anzawo.
M’Israyeli wakale Chilamulo chimene Mulungu anapereka kudzera mwa Mose chinanena kuti chilango cha imfa chiyenera kuperekedwa pa milandu ina yaikulu. (Levitiko 18:29) Komabe, Chilamulocho chinalinso ndi makonzedwe a chiweruzo chopanda tsankhu, umboni woona ndi maso, ndi malamulo oletsa chiphuphu. (Levitiko 19:15; Deuteronomo 16:18-20; 19:15) Oweruza anafunikira kukhala amuna odzipereka ndipo ankaŵerengeredwa mlandu kwa Mulungu iye mwiniyo! (Deuteronomo 1:16, 17; 2 Mbiri 19:6-10) Motero panali njira zoletsa kugwiritsira ntchito chilango cha imfa molakwa.
Lerolino palibe boma padziko lino lapansi limene limatsatiradi chilungamo chaumulungu monga mmene Israyeli wakale anachitira. Koma m’njira zambiri maboma amakhala ngati ‘atumiki’ a Mulungu, kapena nthumwi, chifukwa chakuti amasungitsa mtendere ndi bata ndipo amapereka mautumiki ofunikira kwa anthu. Mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu kumvera “maulamuliro aakulu” ameneŵa ndiyeno anawonjezera kuti: “Ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye [maboma] sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.”—Aroma 13:1-4.
“Lupanga” limene Paulo anatchula limaimira mphamvu ya boma ya kulanga apandu—ngakhale ndi imfa. Akristu amalemekeza mphamvu imeneyo, koma kodi ayenera kulakalaka kulankhulapo pa mmene iyenera kuchitidwira?
“Lupanga” Ligwiritsiridwa Ntchito Molakwa
Maboma aumunthu mosakayikira agwiritsira ntchito “lupanga” nthaŵi zambiri chifukwa cha chilungamo. Koma ndi zoona kuti alinso ndi liwongo la kuligwiritsira ntchito molakwa. (Mlaliki 8:9) Boma la Roma wakale linali ndi liwongo la kugwiritsira ntchito “lupanga” la kupha kwachiweruzo pa atumiki a Mulungu opanda mlandu. Yohane Mbatizi, Yakobo, ndiponso ngakhale Yesu Kristu anali ena amene linapha.—Mateyu 14:8-11; Marko 15:15; Machitidwe 12:1, 2.
M’nthaŵi zamakono chinthu chofananacho chachitika. Atumiki a Yehova opanda mlandu aphedwa m’maiko osiyanasiyana—ndi gulu loombera mfuti, pa makina odulira mutu, mwa kupachikidwa, mwa zipinda za mpweya wakupha—zonse zochitidwa “mwalamulo” ndi maboma ofuna kufafaniza Chikristu. Maulamuliro onse amene akugwiritsira ntchito mphamvu molakwa adzakhala ndi mlandu kwa Mulungu. Iwo alidi ndi liwongo la mwazi!—Chivumbulutso 6:9, 10.
Lingaliro la kukhala ndi liwongo la mwazi pamaso pa Yehova Mulungu limawachititsa mantha kwambiri Akristu oona. Motero, pamene kuli kwakuti amalemekeza mphamvu ya boma ya kugwiritsira ntchito “lupanga,” iwo akudziŵa bwino lomwe mmene ilo lagwiritsiridwa ntchito molakwa. Ilo lagwiritsiridwa ntchito monga chiŵiya chozunzira ndiponso nthaŵi zina aligwiritsira ntchito mwankhanza ndi mwatsankhu kwa ena ndi kulekerera ena mosayenera.a Motero kodi ndi motani mmene Akristu ayenera kuchitira ndi mkangano wa chilango cha imfa? Kodi ayenera kuloŵamo ndi kulimbikitsa kusintha?
Uchete Wachikristu
Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo otchulidwa poyambapo, Akristu oona amayesa kukumbukira pulinsipulo lofunika kwambiri ili: Yesu Kristu anauza ophunzira ake ‘kusakhala a dziko lapansi.’—Yohane 15:19; 17:16.
Kodi Mkristu akhoza kulabadira lamulo limenelo koma nkuloŵabe mumkangano wa chilango cha imfa? Mosakayikira ayi. Ndipotu imeneyi ndi nkhani ya zamakhalidwe a anthu ndi ya ndale. Ku United States, olimbanirana mpando wandale nthaŵi zambiri amagwiritsira ntchito malingaliro awo ponena za chilango cha imfa—kaya kuchichirikiza kapena kuchitsutsa—monga njira yaikulu yochitira kampeni yawo. Amalankhula za nkhani imeneyi mogwira mtima ndipo amagwiritsira ntchito kupwetekedwa kwa malingaliro kumene nkhani imeneyi imachititsa monga chiŵiya chosonkhezerera oponya mavoti kuwakhalira mbali.
Mwinamwake funso limene Mkristu ayenera kulingalirapo ndi ili: Kodi Yesu akanadziloŵetsamo mumkangano wa mmene maboma a dziko lino amagwiritsira ntchito “lupanga”? Kumbukirani, pamene anthu akwawo anafuna kumuloŵetsa m’ndale, Yesu “anachokanso kumka ku phiri payekha.” (Yohane 6:15) Motero, zikuonekeratu kuti iye akanasiya nkhaniyi pamalo pamene Mulungu anaisiya—m’manja mwa maboma.
Moteronso lerolino, Akristu oona ayenera kukhala osamala mwa kusaloŵa mumkangano pankhaniyi. Iwo amazindikira mphamvu imene maboma ali nayo ya kuchita mmene akufunira. Koma monga atumiki achikristu amene saali mbali ya dziko, iwo sangachilikize chilango cha imfa kapena kuchirikiza kuthetsedwa kwake.
M’malo mwake, iwo amakumbukira mawu a Mlaliki 8:4 akuti: “Mawu a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani?” Inde, ‘mafumu’ a dziko kapena olamulira a ndale, apatsidwa mphamvu ya kuchita zimene akufuna. Palibe Mkristu amene ali ndi ulamuliro wa kuwadzudzula. Koma Yehova angachite zimenezo. Ndipo adzatero. Baibulo limatichititsa kuyang’ana kutsogolo kutsiku pamene Mulungu adzabweretsa chiweruzo chomaliza pa mlandu uliwonse ndi kugwiritsira ntchito “lupanga” kulikonse kolakwa m’dziko lino lakale.—Yeremiya 25:31-33; Chivumbulutso 19:11-21.
[Mawu a M’munsi]
a Mwachitsanzo, ndende za ku United States zinatsutsidwa pa kupha apandu okhala pa mzere wa imfa osaposa pa 2 peresenti chaka chilichonse. Ambiri a iwo amafa ndi zochititsa zachilengedwe osati ndi kuphedwa. Pakhalanso madandaulo onena za tsankhu—monga mmene ziŵerengero zimasonyezera kuti wakupha munthu amalandira chilango cha imfa mosakayikira ngati wophedwayo anali mzungu koposa ngati anali munthu wakuda.
[Mawu a Chithunzi patsamba 30]
The Bettmann Archive