-
“Khalani Otsanzira Mulungu”Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
-
-
Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akhristu oona kuti: “Chifukwa chake, khalani otsanzira Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu amakhulupirira kwambiri anthu amene amam’lambira. Kodi n’chifukwa chiyani amatero? Yehova Mulungu analenga munthu m’chifanizo Chake, monga mwa chikhalidwe Chake. (Genesis 1:26, 27) Motero Mulungu anapatsa anthu makhalidwe ofanana ndi makhalidwe ake.a Moti Baibulo likamalimbikitsa Akhristu kuti “khalani otsanzira Mulungu,” zili ngati kuti Yehova akuwauza kuti: ‘Sindimakukayikirani ngakhale pang’ono. Ngakhale kuti ndinu opanda ungwiro, ndikudziwa kuti mungathe ndithu kutsanzira makhalidwe anga.’
-
-
“Khalani Otsanzira Mulungu”Nsanja ya Olonda—2008 | October 1
-
-
a Lemba la Akolose 3:9, 10 limasonyeza kuti mawu akuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu amatanthauza kuti tili ndi makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. Anthu amene akufuna kukondweretsa Mulungu amalimbikitsidwa kuti avale “umunthu watsopano,” umene “ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha [Mulungu] amene anaulenga.”
-