Chikhulupiriro Chinamufulumiza ku Ntchito
PAKATIMPAKATI pa Persian Gulf ndi mzinda wa Baghdad pali mulu wosapenyeka wa njerwa za matope. Uwo uli nsanja ya payokha ikuyang’anira pa chigwa chofutukuka cha chipululu chosabala kanthu. Zopumphunthidwa ndi mphepo ya mkuntho ya fumbi, kuphikidwa ndi dzuŵa laukali, unyinji wa zowunjikidwa za pabwinjazo ziri mu mkhalidwe wosawoneka bwino wachete. Mkhalidwe wachete wochititsa mantha umenewu umaswedwa kokha ndi kulira kwa pa kanthaŵi kwa cholengedwa choyenda usiku. Izi ndi zokha zimene zinatsala za umene poyamba unali mzinda wamphamvu wa Uri.
Koma bwererani m’mbuyo zaka zikwi zinayi. Kumeneko, pa chimene pa nthaŵiyo chinali doko la kum’mawa kwa Mtsinje wa Firate, Uri uli mzinda wopita patsogolo! Nyumba zowala zopakidwa utoto woyera ndi nyumba zogulitsiramo zinthu zandandalikidwa m’makwalala ake okhotakhota. Ogulitsa ndi ogula amanenerera ponena za mitengo m’misika. Ogwira ntchito amagwira ntchito usana ndi usiku kuluka ulusi woyera ngati mkaka kuchokera ku mitolo yaikulu ya thonje. Akapolo akumayenda kutsika pansi pa malo opendekeka omagwedera a sitima ya m’madzi, akumawerama pansi pa kulemera kwa chuma chogulidwa kumaiko ena.
Zochitika zonsezi zimachitika m’mthunzi wa kachisi ya Chibabulo yaitali kwambiri yomwe imalamulira dziko lonse la mzindawo. Olambira amabwera ku malo opatulika amenewa kudzapereka ulemu kwa mulungu amene amamkhulupirira kuti anabweretsa kutukuka kwa Uri—mulungu wa mwezi Nanna kapena Sin.
Kwa munthu mmodzi, ngakhale kuli tero, fungo la nsembe zoperekedwa pamwamba pa chipilala chachikulu chimenechi liri fungo losapatulika. Dzina lake ndi Abramu (pambuyo pake Abrahamu). Pa nthaŵi imodzi, atate wake, Terah, angakhale anagawanamo mu kulambira mafano kumeneku. (Yerekezani ndi Yoswa 24:2, 14, 15.) Koma tsopano Abramu wadziŵa Mulungu wowona, Yehova. Motani? Mwachiwonekere kupyolera m’kuyanjana ndi Semu, wopulumuka wachikulire wa Chigumula cha Nowa.
Abramu mwamsanga asonyeza kuti chikhulupiriro chake mwa Yehova sichiri chopanda ntchito. Mwanjira ina yake, Mulungu tsopano ‘awonekera’ kwa Abramu. (Machitidwe 7:2-4) Yehova akulamula: “Tuluka m’dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi ku nyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.”—Genesis 12:1-3.
Kuvomereza ku Kuitanako
Kusiya Uri wopita patsogolo? Nkulekeranji, popeza kuti nyumba mu Uri kwenikweni ziri timagulu ta nyumba za njerwa zosanjikizana zikumazungulira malo amodzi apakati ochitira maseŵera zikumakhala ndi zipinda zomafika ku 14! Nchosadabwitsa kuti wolemba mbiri wa chiFrench Henri Gaubert anachipeza icho chovuta kukhulupirira kuti Abramu akanasiya “nyumba yake ku Uri ndi zipinda zake zokongoletsedwa ndi makama ndi makushoni, malo ake okhalamo osangalatsa, ozizirira m’nyengo yotentha ndi otentha m’nyengo yachisanu, nyumba yake yosungiramo zinthu yodzazidwa bwino, chitsime chake chamadzi ozizira.” Kusiya zinthu zonsezi ndi kutenga moyo monga woyendayenda? Chosakhulupirika!
Ndipo bwanji ponena za ziwalo za banja la Abramu—ena kumasalira kumbuyo? Mu Middle East, maunansi oterowo ali amphamvu kotero kuti kuchoka ku banja la munthu kuli kulakwa kofikira ku chilango cha imfa. Kodi ndimotani mmene Abramu akanayembekezeredwa kusiya zonsezi kumbuyo kaamba ka malonjezo wamba? Indedi, kodi ndimotani mmene Mulungu akanapangira munthu ameneyu—yemwe analibe mwana pa nthaŵiyo—“mtundu waukulu”? Kodi ndi kuti kumene kuli dziko lolonjezedwa limeneli?
Ngakhale ndi tero, Abramu ali mwamuna wachikhulupiriro ndipo ali ndi “chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeredwa.” (Ahebri 11:1) Iye amadziŵa kuchokera ku zochitika kale—monga ngati Chigumula cha dziko lonse—kuti mawu a Mulungu nthaŵi zonse amakhala owona. Abramu sali wovutitsidwa maganizo chifukwa chakuti sakudziŵa kwenikweni ndimotani, ndi liti, kapena ndi kuti kumene malonjezo aumulungu amenewo adzakwaniritsidwa. Kwa iye, osati nyumba yokondeka, moyo wachisungiko, kapena ngakhale unansi wa banja ziri za mtengo wapatali koposa unansi wa Yehova. Kwa Abramu, motero, pangangokhala chosankha chimodzi: Kumvera Mulungu ndi kuchoka mu Uri!
Kodi chikhulupiriro chanu mofananamo chimakufulumizani kuchita ntchito? Kaŵirikaŵiri timalimbikitsidwa kufutukula kutengamo mbali m’ntchito yolalikira. Ambiri amachita tero mwa kukhala alengezi Aufumu anthaŵi zonse. Koma kodi Akristu ena amadziletsa chifukwa chakuti iwo mwachinsinsi amakaikira lonjezo la Mulungu la kupereka kwa awo amene amafuna choyamba Ufumu? (Mateyu 6:33) Chikhulupiriro cha Abramu chinamufulumiza iye kuchita ntchito. Iye anayika pa ngozi mtsogolo mwake pa malonjezo a Mulungu!
Kuchokera ku Uri Kupita ku Harani
Abramu sakuchoka yekha. Mofanana ndi Mboni za Yehova zambiri lerolino, iye mosakaikira akugawana chowonadi cha Mulungu ndi ziwalo za banja lake. Chotero nchosadabwitsa kuti mkazi wa Abramu Sarai ndi mwana wamasiye wa mlongo wake wotchedwa Loti mofananamo akufulumizidwa kumvera chiitano cha Mulungu.a Nkulekelanji, popeza ngakhale atate wa Abramu, Tera—wolingaliridwa ndi ena kukhala wopanga mafano—akuchoka nayenso!—Genesis 11:31.
Pomalizira, banja la Abramu ndi zoweta zawo ziri kunja ku malinga a Uri. Chizindikiro kaamba ka kunyamuka chaperekedwa, ndipo magareta akhazikitsidwa m’kuyenda kolongosoka. Akumatsatira njira cha kum’mawa kwa Mtsinje wa Firate, akuyenda pansi pa dzuŵa laukali, mwachidziŵikire akumayenda ndi kukwera ku kumveka kwa mabelu omalira omangidwa m’makosi a ngamira zawo.
Iwo akuyenda chakumpoto koma kumadzulo, akumatsatira kukhota kwa Mtsinje wa Firate. Pambuyo pa masiku ochulukira kwambiri, iwo akukwaniritsa makilomita 960. Oyenda otopawo akusangalatsidwa kuwona nyumba zomangidwa ngati chisa cha njuchi zozungulira mzinda wa Harana. Iwo uli malo akulu oyimapo kaamba ka anthu a paulendo.—Genesis 11:31.
Ku Tsidya Lina la Firate
Abramu akhazikika ku Harana, mwachiwonekere chifukwa cha kulingalira kaamba ka Tera wachikulire. Koma ndi dalitso la Yehova, Abramu akhala wolemera. (Yerekezani ndi Mlaliki 5:19.) Ndi kaŵirikaŵiri chotani nanga mmene Mulungu lerolino mofananamo amaperekera madalitso akuthupi pa awo amene ‘amasiya nyumba, abale kapena alongo’ kaamba ka Ufumu!—Marko 10:29, 30.
Mu Harana, Abramu ‘anapezanso miyoyo’—gulu la antchito. (Genesis 12:5) Jerusalemu Targum ndi Chaldee Paraphrase imanena kuti iye anawatembenuza, kapena ‘kuwagonjetsera iwo ku lamulo.’ (Yerekezani ndi Genesis 18:19.) Inde, chikhulupiriro chake chikumfulumiza iye kulalikira kwa ena, monga mmene Mboni za Yehova zimachitira lerolino.
“Masiku a Tera anali zaka mazana aŵiri kudza zisanu; ndipo anafa mu Harana.” (Genesis 11:32) Abramu ali wachisoni kwambiri ndi kufa kwa atate wake. Koma pamene nyengo yokhuza maliro itha, iye kachiŵirinso apanga makonzedwe a kusamuka. “Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi aŵiri kudza zisanu pamene anatuluka mu Harana.”—Genesis 12:4.
“Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chawo chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anapeza mu Harana; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.” (Genesis 12:5) Pambuyo pa kuyenda makilomita 89 kumadzulo kuchokera pa Harana, Abramu mwachiwonekere anaima pa malo okwezeka ku tsidya lija la Firate kuchokera ku malo apakati akale a malonda a Karikemesi. Pano apaulendo kaŵirikaŵiri amawoloka.
Tsiku lake? Nisani 14, 1943 B.C.E. Pa tsiku limodzimodzilo zaka 430 pambuyo pake, mbadwa za Abramu zidzakhala zikuwomboledwa kuchokera ku ukapolo wa Igupto. (Eksodo 12:40, 41) Ndipo pa tsiku limodzimodzilo chifupifupi zaka zikwi ziŵiri pambuyo pake, Mbewu yake Yesu Kristu, anadzapanga “pangano . . . kaamba ka ufumu,” pansi pa limene “mabanja onse a pa dziko lapansi” adzadalitsidwa!—Luka 22:1, 28, 29.
Ndi kachitidwe ka chikhulupiriro—kuwoloka Firate kwa Abramu—malonjezo a Mulungu kwa iye ayamba kugwira ntchito. Abramu angawone masomphenya a “mzinda wokhala ndi maziko enieni,” boma lolungama pa mtundu wa anthu. Inde, kukhala akukhala ndi zizindikiro zochepa, Abramu wayamba kuzindikira kakhazikitsidwe ka chifuno cha Mulungu m’kuwombola mtundu wa anthu womafa. Kuwala kwa ulosi kwawunikira kuyaka kwa chiyembekezo m’malingaliro ake!—Ahebri 11:10.
Mboni za Yehova lerolino ziri ndi maziko okulira kaamba ka chikhulupiriro kuposa amene anali nawo Abramu. Chitsimikiziro chokulira chimatsimikiza kuti “mzinda,” kapena Ufumu wa kumwamba, umene Abramu anadikira tsopano uli weniweni! Koma kodi chikhulupiriro mu iwo chimakufulumizani inu kulalikira mwachangu, kutsatira chitsogozo chopatsidwa ndi Mulungu, kulondola zonulirapo zauzimu m’malo mwa zosangalatsa zakuthupi? Motsimikizirika chimatero, popeza chimenecho ndicho chinali mtundu wa chikhulupiriro cha Abramu. Chikhulupiriro chake chinamufulumiza iye ku ntchito!
[Mawu a M’munsi]
a Mbale wa Abramu Nahori anatsala kumbuyo, mwinamwake kuti amalize kusamalira malonda ake kapena zinthu zina zaumwini. Koma pambuyo pake mbadwa za Nahori zinachokanso ku Uri ndi kulambira Yehova mu Harana.—Genesis 11:31; 24:1-4, 10, 31; 27:43; 29:4.
[Mapu/Zithunzi patsamba 28]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Ulendo wa Abrahamu
Uri
Harana
Karikemesi
KANANI
Nyanja ya Mediterranean
[Mawu a Chithunzi]
Based on a map copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel
[Chithunzi]
Firate pafupi ndi Uri
[Chithunzi]
Harana lerolino
[Chithunzi]
Firate pafupi ndi Karikemesi