Kodi Tiziwaona Bwanji Anthu Pamene Tsiku la Yehova Likuyandikira?
“Ambuye sazengereza nalo lonjezano, . . . komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”—2 PETRO 3:9.
1, 2. (a) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu masiku ano? (b) Kodi tingadzifunse mafunso otani?
ATUMIKI a Yehova ali ndi ntchito ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19) Pamene tikugwira ntchito imeneyi ndi kuyembekeza “tsiku lalikulu la Yehova,” tifunika kuwaona anthu monga mmene iye amawaonera. (Zefaniya 1:14) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu? Mtumwi Petro anati: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Mulungu amawaona anthu monga oti angathe kulapa. Iye “afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Inde, Yehova amasangalala ‘woipa akaleka njira yake nakhala ndi moyo.’—Ezekieli 33:11.
2 Kodi ife timawaona anthu monga mmene Yehova amawaonera? Mofanana ndi iyeyo, kodi timaona kuti anthu a fuko ndi mtundu uliwonse angathe kukhala “nkhosa za pabusa pake”? (Salmo 100:3; Machitidwe 10:34, 35) Tiyeni tione zitsanzo ziŵiri zimene zikusonyeza kufunika koona anthu monga mmene Mulungu amawaonera. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, chiwonongeko chinali pafupi, ndipo atumiki a Yehova anawauziratu za chiwonongekocho. Zitsanzo zimenezi n’zofunika kwambiri pamene tikudikira tsiku lalikulu la Yehova.
Abrahamu Anaona Anthu Monga Mmene Yehova Amawaonera
3. Kodi Yehova anawaona bwanji anthu a ku Sodomu ndi Gomora?
3 Chitsanzo choyamba ndi cha Abrahamu, kholo lakale lokhulupirika, ndi mizinda yoipa ya Sodomu ndi Gomora. Yehova atamva “kulira kwa Sodomu ndi Gomora,” sanawononge mizindayo ndi anthu onse amene anali mmenemo nthaŵi yomweyo. Anayamba kaye wayendera m’mizindayo. (Genesis 18:20, 21) Anatumiza angelo aŵiri ku Sodomu kumene anakakhala m’nyumba ya Loti, munthu wolungama. Usiku umene angelowo anafika, “anthu a m’mudzimo . . . anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m’mbali zonse,” kufuna kuti agonane ndi angelowo. Inde, kuipa kwa anthu a mumzindawo kunatsimikizira kuti unayenereradi kuwonongedwa. Komabe, angelowo anauza Loti kuti: “Kodi muli nawo ena pano? Mkamwini, ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi, ndi onse ali nawo m’mudzi muno, utuluke nawo m’malo muno.” Yehova anakonza njira yopulumutsira anthu ena mumzindawo, koma mapeto ake, Loti ndi ana ake aakazi aŵiri okha ndi amene anapulumuka.—Genesis 19:4, 5, 12, 16, 23-26.
4, 5. N’chifukwa chiyani Abrahamu anawapemphera anthu a ku Sodomu, ndipo kodi mmene iye anali kuwaonera anthu zinali zofanana ndi mmene Yehova anali kuwaonera?
4 Tsopano, tiyeni tibwerere m’mbuyo m’nthaŵi imene Yehova anaulula cholinga chake choyendera m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Ndi nthaŵi imeneyo pamene Abrahamu anapempha kuti: “Kapena alipo olungama makumi asanu mkati mwa mudzi; kodi mudzawononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo? Musamatero ayi, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuti olungama akhale monga oipa; musamatero ayi; kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?” Abrahamu anagwiritsa ntchito mawu akuti “musamatero ayi” kaŵiri. Chifukwa cha zimene Abrahamu anaona pamoyo wake, ankadziŵa kuti Yehova sangawononge olungama pamodzi ndi oipa. Yehova atanena kuti sadzawononga Sodomu ngati munali “olungama makumi asanu mkati mwa mudzi,” Abrahamu anachepetsa pang’onopang’ono nambalayo mpaka kufika pa anthu khumi okha.—Genesis 18:22-33.
5 Kodi Yehova akanamvetsera zimene Abrahamu anali kupempha ngati zinali zosagwirizana ndi maganizo ake? Mwachionekere sakanatero. Mosakayika, Abrahamu monga “bwenzi la Mulungu” ankadziŵa mmene Yehova anali kuwaonera anthu ndipo iye analinso kuwaona chimodzimodzi. (Yakobo 2:23) Pamene Yehova anafuna kuti awononge Sodomu ndi Gomora, anali wofunitsitsa kuganizira zimene Abrahamu anapempha. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Atate wathu wakumwamba ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’
Yona Anaona Anthu Mosiyana Kwambiri ndi Mmene Yehova Anawaonera
6. Kodi Anineve anachita chiyani Yona atawalalikira?
6 Tsopano tiyeni tione chitsanzo chachiŵiri. Chimenechi ndi chitsanzo cha Yona. Apa tsopano mzinda umene Yehova anati auwononga unali wa Nineve. Mneneri Yona anauzidwa kulengeza kuti kuipa kwa mzindawo ‘kunakwera pamaso pa Yehova.’ (Yona 1:2) Nineve, kuphatikiza ndi midzi imene inali m’mbali mwake, unali mzinda waukulu, “wa ulendo wa masiku atatu.” Yona kenako atamvera ndi kukaloŵa mumzindawo, analengeza kuti: “Atsala masiku makumi anayi ndipo Nineve adzapasuka.” Atamva zimenezi, “anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli.” Mfumu ya Nineve nayonso inalapa.—Yona 3:1-6.
7. Kodi Yehova anawaona bwanji Anineve amene analapa?
7 Zinali zosiyana kwambiri ndi mmene anthu a ku Sodomu anachitira. Kodi Yehova anawaona bwanji Anineve amene analapawo? Yona 3:10 amati: “Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.” Yehova “analeka” mlingaliro lakuti anasintha zimene anafuna kuchitira Anineve chifukwa chakuti anasintha njira zawo. Miyezo ya Mulungu sinasinthe, koma Yehova anasintha maganizo ake ataona kuti Anineve alapa.—Malaki 3:6.
8. N’chifukwa chiyani Yona anakwiya?
8 Kodi Yona atazindikira kuti mzinda wa Nineve suwonongedwa, anaona zinthu monga mmene Yehova anazionera? Ayi, chifukwa tikuuzidwa kuti: “Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.” N’chiyaninso chimene Yona anachita? Nkhaniyo imati: “Anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! si ndiwo mawu anga ndikali m’dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisi, pakuti ndinadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.” (Yona 4:1, 2) Yona ankawadziŵa makhalidwe a Yehova. Komabe panthaŵiyi, mneneriyu anakwiya ndipo sanaone anthu olapa a ku Nineve monga mmene Mulungu anawaonera.
9, 10. (a) Kodi Yehova anaphunzitsa chiyani Yona? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yona n’kupita kwa nthaŵi anawaona anthu a ku Nineve monga mmene Yehova anali kuwaonera?
9 Yona anatuluka mu Nineve n’kumanga thandala, ndiyeno n’kukhala pa mthunzi wake kuti ‘mpaka aone chochitikira mudzi.’ Yehova anameretsa msatsi kuti umuchitire mthunzi Yona. Koma tsiku lotsatira, msatsiwo unafota. Yona atapsa mtima chifukwa cha zimenezo, Yehova anati: “Unachitira chifundo msatsiwo . . . Ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Nineve mudzi waukulu uwu; mmene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi aŵiri osadziŵa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?” (Yona 4:5-11) Yona anaphunzirapotu apa mmene Yehova amawaonera anthu.
10 Mmene Yona anachitira pamene Mulungu anafotokoza kuti ayenera kuchitira chifundo anthu a ku Nineve sizinalembedwe. Komabe, n’zoonekeratu kuti mneneriyo anasintha mmene anali kuwaonera Anineve amene analapawo. Tikunena zimenezi chifukwa chakuti Yehova anamugwiritsira ntchito kulemba nkhani youziridwa imeneyi.
Kodi Mumawaona Bwanji Anthu?
11. Kodi Abrahamu ayenera kuti akanawaona bwanji anthu amakono?
11 Masiku ano, tayandikira chiwonongeko china, kuwonongedwa kwa dongosolo la zinthu loipa lino pa tsiku lalikulu la Yehova. (Luka 17:26-30; Agalatiya 1:4; 2 Petro 3:10) Kodi Abrahamu akanawaona bwanji anthu amene ali m’dziko lino limene latsala pang’ono kuwonongedwa? Mwachionekere, akanadera nkhaŵa anthu amene sanamvebe ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mateyu 24:14) Abrahamu anapempha Mulungu mobwerezabwereza kuti mwina kungakhale anthu olungama ku Sodomu. Kodi ife timadera nkhaŵa anthu amene angathe kusiya njira za dziko limene Satana akulilamulirali ngati atapatsidwa mpata wolapa ndi kutumikira Mulungu?—1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 18:2-4.
12. N’chifukwa chiyani n’kosavuta kuona anthu amene timakumana nawo mu utumiki monga mmene Yona anaonera anthu, ndipo tingatani ngati zili choncho?
12 N’koyenera kufunitsitsa kuti zoipa zimene zikuchitikazi zithe. (Habakuku 1:2, 3) Komabe, n’kosavuta zedi kukhala ndi maganizo ngati a Yona, kusaganizira moyo wa anthu amene angathe kulapa. Zimenezi zimakhala choncho makamaka tikamakumana ndi anthu osalabadira, odana nafe, ngakhalenso aukali tikafika panyumba pawo kuti tiwauze uthenga wa Ufumu. Tingasiye kuwaganizira anthu amene Yehova adzawasonkhanitsa kuwachotsa m’dongosolo loipa la zinthu lino. (Aroma 2:4) Ngati titadzipenda mosamala kwambiri tipeza kuti timaona anthu monga mmene Yona anawaonera Anineve poyambirira, ngakhale tikusonyeza zimenezo pang’ono chabe, tingapemphe Yehova kuti atithandize kuwaona anthu monga mmene iye amawaonera.
13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amawaganizira anthu masiku ano?
13 Yehova amawaganizira anthu amene panopa sakumutumikira, ndipo amamvera pempho la anthu ake odzipatulira. (Mateyu 10:11) Mwachitsanzo, ‘adzachita chilungamo’ poyankha mapemphero awo. (Luka 18:7, 8) Ndiponso, Yehova adzakwaniritsa malonjezo ndi zolinga zake zonse panthaŵi yake. (Habakuku 2:3) Zina mwa zimenezi ndizo kuchotsa kuipa konse padziko lapansi, monga mmene anawonongera Nineve pamene anthu okhala mmenemo anayambiranso kuchita zinthu zoipa.—Nahumu 3:5-7.
14. Kodi tiyenera kumachita chiyani pamene tikudikira tsiku lalikulu la Yehova?
14 Kodi tidzadikirabe moleza mtima, kutanganidwa kuchita chifuniro chake, mpaka pamene dongosolo loipa la zinthu lino lidzachotsedwa pa tsiku lalikulu la Yehova? Sitikudziŵa kuti ntchito yolalikirayi iyenera kufika mpaka pati tsiku la Yehova lisanafike, koma tikudziŵa kuti mapeto asanafike, uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi mpaka Mulungu atakhutira. Ndipo mosakayika tiyenera kudera nkhaŵa “zofunika” zimene zidzasonkhanitsidwa pamene Yehova akupitiriza akudzaza nyumba yake ndi ulemerero.—Hagai 2:7.
Zochita Zathu Zimasonyeza Mmene Timawaonera Anthu
15. N’chiyani chingatithandize kuiona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri?
15 Mwina tikukhala m’dera limene anthu sakulabadira kwenikweni ntchito yathu yolalikira, ndipo sitingathe kusamukira kudera kumene kukufunika olengeza Ufumu ambiri. Tiyerekeze kuti anthu khumi angadzapezeke m’gawo lathu mapeto asanafike. Kodi timaona kuti anthu khumiwo ndi oyenerera kuwafunafuna? Yesu “anagwidwa m’mtima ndi chisoni” ataona makamu a anthu “popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Mwa kuphunzira Baibulo ndi kuŵerenga mosamala nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, tingamvetse bwino mavuto amene ali m’dzikoli. Ndiyeno zimenezi zidzatithandiza kumvetsa kwambiri kufunika kolalikira uthenga wabwino. Ndiponso, kugwiritsa ntchito moyamikira zofalitsa zothandizira kuphunzira Baibulo zimene timalandira kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kungathandize kuti tikhale ogwira mtima kwambiri polalikira m’gawo limene limalalikidwa kaŵirikaŵiri.—Mateyu 24:45-47; 2 Timoteo 3:14-17.
16. Kodi tingachite bwanji kuti utumiki wathu ukhale wopindulitsa kwambiri?
16 Kudera nkhaŵa anthu amene angathe kumvetsera uthenga wa m’Baibulo wopatsa moyo kumatilimbikitsa kuganizira nthaŵi ndi njira zosiyanasiyana zimene tingawafikire eninyumba mu utumiki wathu. Kodi timapeza kuti ambiri sali pakhomo tikafikapo? Ngati ndi choncho, tingachite zoti utumiki wathu ukhale wopindulitsa kwambiri mwa kusintha nthaŵi ndi malo a ntchito yathu yolalikira. Asodzi amapita kosodza nthaŵi imene angakaphe nsomba. Kodi sitingachite chimodzimodzi pantchito yathu yosodza mwauzimu? (Marko 1:16-18) Bwanji osayesa kulalikira madzulo ndiponso pa telefoni, ngati zimenezi n’zololeka? Ena apeza kuti kumsika, kuchitsime, kuchigayo, pamalo omwetsera mafuta galimoto, ndi kumasitolo ndi ‘malo osodzerako’ obala zipatso. Kuwaona anthu monga mmene Abrahamu anali kuwaonera kumaonekeranso pamene tigwiritsa ntchito mpata wolalikira mwamwayi.
17. Kodi tingalimbikitse bwanji amishonale ndi ena amene akutumikira m’mayiko ena?
17 Anthu ambirimbiri sanamvebe uthenga wa Ufumu. Kuwonjezera pa kulalikira kwathu, kodi tingasonyeze kuwaganizira anthu oterowo popanda kuchoka panyumba pathu? Kodi timawadziŵa amishonale kapena atumiki a nthaŵi zonse amene akutumikira kunja kwa dziko lathu? Ngati ndi choncho, zingakhale zothandiza kuwalembera makalata oyamikira ntchito yawo. Kodi zimenezo zingasonyeze bwanji kuganizira anthu? Makalata athu olimbikitsa ndiponso oyamikira angalimbikitse amishonalewo kukhalabe mu utumiki wawo, motero angathandize anthu ambiri kudziŵa choonadi. (Oweruza 11:40) Tingawapemphererenso amishonalewo pamodzi ndi anthu a m’mayiko ena amene akufuna choonadi. (Aefeso 6:18-20) Njira inanso imene tingasonyezere kuganizira anthu ndiyo mwa kupereka ndalama zothandizira pa ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova.—2 Akorinto 8:13, 14; 9:6, 7.
Kodi Mungathe Kusamuka?
18. Kodi Akristu ena achita chiyani kuti apititse patsogolo zinthu za Ufumu m’dziko limene akukhala?
18 Anthu amene asamukira kumene kukufunika olengeza Ufumu ambiri adalitsidwa chifukwa cha kudzipereka kwawo. Komabe, Mboni za Yehova zina ngakhale kuti sizinasamuke m’dziko lawo, zaphunzira chinenero china kuti zithandize mwauzimu anthu obwera m’dzikolo kuchokera m’mayiko ena. Zimenezi zakhala zopindulitsa kwambiri. Mwachitsanzo, Mboni zisanu ndi ziŵiri zimene zinali kuthandiza Matchaina mu mzinda wina ku Texas, m’dziko la America, zinalandira anthu okwana 114 ku mwambo wa Mgonero wa Ambuye mu 2001. Amene akuthandiza magulu oterowo aona kuti minda yawo yacha ndipo ikufunika kukolola.—Mateyu 9:37, 38.
19. Kodi mufunika kuchita chiyani ngati mukuganiza zosamukira kudziko lina kuti mukapititse patsogolo ntchito yolalikira Ufumu kumeneko?
19 Mwina inu ndi banja lanu mukuona kuti mungathe kusamukira kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Ndi nzeru kuyamba kaye ‘mwakhala pansi ndi kuŵerengera mtengo wake.’ (Luka 14:28) Zimenezi zimafunikadi makamaka pamene munthu akuganiza zopita ku dziko lina. Amene angaganize zochita zimenezi angachite bwino kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi ndidzatha kupezera zinthu zofunika banja langa? Kodi ndidzapeza ziphaso zoyendera zoyenera? Kodi ndimalankhula chinenero cha m’dziko limenelo, kapena kodi ndikufunitsitsa kuchiphunzira? Kodi ndaganizirapo za nyengo ndi chikhalidwe cha kumeneko? Kodi ndikakhaladi “wotonthoza mtima” osati wolemetsa kwa okhulupirira anzanga a m’dzikolo?’ (Akolose 4:10, 11) Pofuna kudziŵa kuti kuli kusoŵa kotani m’dziko limene mukuganiza zosamukirako, n’koyenera nthaŵi zonse kulembera kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova imene ikuyang’anira ntchito yolalikira m’dziko limenelo.a
20. Kodi Mkristu wina wachinyamata wachita zotani pothandiza okhulupirira anzake ndi anthu ena a m’dziko lachilendo?
20 Mkristu wina amene anali kugwira nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ku Japan anamva kuti pankafunika antchito aluso kuti akamange nyumba yolambiriramo ku Paraguay. Popeza anali wosakwatira ndiponso anali ndi mphamvu zaunyamata, anasamukira ku dzikolo ndipo anagwira ntchito kwa miyezi isanu ndi itatu. Ndi iye yekha amene anali kugwira ntchito nthaŵi yonse pamalopo. Ali kumeneko, anaphunzira Chispanya ndipo ankachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Anaona kuti pankafunikira olengeza Ufumu ambiri m’dzikolo. Ngakhale kuti anabwerera ku Japan, posakhalitsa anabwereranso ku Paraguay n’kuthandiza nawo kusonkhanitsira anthu m’Nyumba ya Ufumu yomwe anamanga nawoyo.
21. Kodi nkhaŵa yathu yaikulu iyenera kukhala iti ndipo tiyenera kuwaona bwanji anthu pamene tikudikira tsiku lalikulu la Yehova?
21 Mulungu adzaonetsetsa kuti ntchito yolalikira yachitika mokwanira, mogwirizana ndi zimene iye akufuna. Masiku ano, iye akufulumiza ntchito yokolola mwauzimu yomaliza. (Yesaya 60:22) Ndiyetu pamene tikudikira tsiku la Yehova tiyeni tigwire nawo ntchito yokololayi mwachangu ndi kuwaona anthu monga mmene Mulungu wathu wachikondi amawaonera.
[Mawu a M’munsi]
a Sizothandiza nthaŵi zonse kusamukira ku dziko limene ntchito yolalikira anailetsa kapena amaipondereza. Kuchita zimenezi kungaike pangozi ofalitsa Ufumu amene akugwira ntchitoyi mochenjera m’zochitika zoterozo.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi tiziwaona bwanji anthu pamene tikudikira tsiku la Yehova?
• Kodi Abrahamu anawaona bwanji anthu olungama amene akanatha kupezeka mu Sodomu?
• Kodi Yona anawaona bwanji anthu olapa a ku Nineve?
• Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuona anthu amene sanamvebe uthenga wabwino monga mmene Yehova amawaonera?
[Chithunzi patsamba 16]
Abrahamu anawaona anthu monga mmene Yehova amawaonera
[Chithunzi patsamba 17]
Yona anadzawaona Anineve amene analapa monga mmene Yehova anali kuwaonera
[Zithunzi patsamba 18]
Kudera nkhaŵa anthu kumatichititsa kuganizira nthaŵi ndi njira zosiyanasiyana zolalikira uthenga wabwino