Chilengedwe Chimalengeza Ulemerero wa Mulungu
“Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.”—SALMO 19:1.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani anthu sangathe kuona ulemerero wa Mulungu mwachindunji? (b) Kodi akulu 24 amam’patsa bwanji Mulungu ulemerero?
“SUNGATHE kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo.” (Eksodo 33:20) Yehova anatero pochenjeza Mose. Popeza anthu ali ndi thupi lanyama lofooka, sangathe kuona ulemerero wa Mulungu mwachindunji n’kukhala ndi moyo. Komabe, mtumwi Yohane anaonetsedwa m’masomphenya Yehova ali pa mpando Wake wachifumu waulemerero.—Chivumbulutso 4:1-3.
2 Mosiyana ndi anthu, zolengedwa zauzimu zokhulupirika zimatha kuona nkhope ya Yehova. Ena mwa iwo ndi “akulu makumi aŵiri mphambu zinayi” a m’masomphenya a Yohane akumwamba, amene akuimira a 144,000. (Chivumbulutso 4:4; 14:1-3) Kodi amatani akaona ulemerero wa Mulungu? Malinga ndi Chivumbulutso 4:11, iwo amalengeza kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”
Chifukwa chake ‘Alibe Choŵiringula’
3, 4. (a) Kodi n’chifukwa chiyani kukhulupirira Mulungu sikutsutsana ndi sayansi? (b) Kodi nthaŵi zina, n’chiyani chimachititsa ena kusakhulupirira Mulungu?
3 Kodi zimenezi zimakuchititsani kum’patsa Mulungu ulemerero? Anthu ambiri sakutero, ndipo ena mpaka amatsutsa zoti Mulungu aliko. Mwachitsanzo, katswiri wa sayansi ya zakuthambo wina analemba kuti: “Kodi n’zoona kuti ndi Mulungu amene anatilengera zinthu zonsezi? . . . N’zosamveka zimenezo. Kaya ena akhumudwa, koma ine ndimakhulupirira kuti zimenezo n’zabodza. . . . Si Mulungu amene analenga zinthu zonse.”
4 Kafukufuku wa sayansi ali ndi polekezera, amangodalira zimene anthu angaone kapena kuphunzira. Zina amangokhulupirira kapena kungopeka. Popeza “Mulungu ndiye mzimu,” n’zosatheka kumufufuza pogwiritsa ntchito njira za sayansi. (Yohane 4:24) Motero, n’chipongwe kunena kuti kukhulupirira Mulungu sikugwirizana ndi sayansi. Katswiri wina wa sayansi, Vincent Wigglesworth wa ku yunivesite ya Cambridge ananena kuti njira za sayansi nazonso “n’chipembedzo.” Chifukwa chiyani? “Njira za sayansi zimadaliranso kukhulupirira ndi mtima wonse kuti zinthu zolengedwa zimatsatira ‘malamulo a chilengedwe.’” Motero, munthu akamatsutsa chikhulupiriro choti kuli Mulungu amakhala akukana chikhulupirirochi koma akuvomereza chikhulupiriro chinacho. Nthaŵi zina, kusakhulupirira Mulungu kumaoneka kuti n’kungofuna kukana mwadala choonadi. Wamasalmo analemba kuti: ‘Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsa. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.’—Salmo 10:4.
5. N’chifukwa chiyani anthu osakhulupirira Mulungu alibe choŵiringula?
5 Koma sikuti anthu amakhulupirira Mulungu popanda zifukwa zake zokhulupirira, popeza pali umboni wochuluka woti Mulungu aliko. (Ahebri 11:1) Katswiri wina wa sayansi ya zakuthambo, Allan Sandage, anati: “Zikundivuta kukhulupirira kuti [chilengedwe] chokhala ndi dongosolochi chinakhalapo chifukwa choti zinthu zinazake zinasokonezeka. Payenera kuti pali winawake amene anakonza dongosololi. Mulungu sindimudziŵa, koma ayenera kuti ndi amene analenga zinthu zonse zodabwitsazi.” Mtumwi Paulo anauza Akristu ku Roma kuti ‘chilengedwere dziko lapansi aonekera bwino [makhalidwe a Mulungu] osaoneka ndiwo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza azindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo [osakhulupirira] adzakhale opanda mawu akuŵiringula.’ (Aroma 1:20) “Chilengedwere dziko lapansi,” makamaka kuyambira pamene anthu anzeru, omwe akanazindikira kuti Mulungu aliko, analengedwa, zaonekeratu kuti pali Mlengi wamphamvu zazikulu, Mulungu woyenera kumulambira. Motero, anthu amene akulephera kuvomereza ulemerero wa Mulungu alibe choŵiringula. Koma kodi chilengedwe chimapereka umboni wotani?
Zakumwamba Zimalengeza Ulemerero wa Mulungu
6, 7. (a) Kodi zakumwamba zimalengeza bwanji ulemerero wa Mulungu? (b) Kodi zakumwamba zimatumiza ‘miyeso’ n’cholinga chotani?
6 Salmo 19:1 limayankha kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” Davide anazindikira kuti nyenyezi ndi mapulaneti zimene zinawalitsa “thambo” kapena kuti mlengalenga, zinapereka umboni wosatsutsika wakuti kuli Mulungu waulemerero. Iye anapitiriza kuti: “Usana ndi usana uchulukitsa mawu, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.” (Salmo 19:2) Usana ndi usiku, zinthu zakumwamba zimasonyeza nzeru za Mulungu ndi mphamvu zake zolenga. Zili ngati kuti mawu ‘ochuluka’ olemekeza Mulungu akumveka kuchokera kumwamba.
7 Komabe, kuti munthu amve umboni umenewu pamafunika kuzindikira. “Palibe chilankhulidwe, palibe mawu; liwu lawo silimveka.” Komabe, umboni wosatulutsa mawu wa zinthu zakumwamba ndi wamphamvu kwambiri. “Muyeso wawo wapitirira pa dziko lonse lapansi, ndipo mawu awo kumalekezero a m’dziko muli anthu.” (Salmo 19:3, 4) Zili ngati kuti zakumwamba zimatumiza ‘miyeso’ pofuna kuonetsetsa kuti umboni wawo wosachita kutulutsira mawu wamveka padziko lonse lapansi.
8, 9. Kodi ndi zinthu zina ziti zodabwitsa zokhudza dzuŵa?
8 Kenako, Davide anafotokoza chinthu china chodabwitsa m’chilengedwe cha Yehova. Anati: “Iye anaika hema la dzuŵa mmenemo [m’mwamba], ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake, likondwera ngati chimphona kuthamanga m’njira. Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira kumalekezero ake: ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.”—Salmo 19:4-6.
9 Dzuŵa ndi locheperapo poyerekezera ndi nyenyezi zina. Komabe, ndi nyenyezi yaikulu, moti mapulaneti amene amazungulira dzuŵalo amaoneka aang’ono kwambiri. Buku lina limanena kuti dzuŵa ndi lolemera matani 2 biliyoni, biliyoni, biliyoni. Kulemera kumeneku kumaposeratu kutalitali kulemera kwa mapulaneti onse amene amazungulira dzuŵa kuwaphatikiza pamodzi. Mphamvu ya dzuŵa imachititsa kuti dziko lapansili lizizungulira dzuŵalo pa mtunda wa makilomita 150 miliyoni popanda kupatuka n’kupita kutali kapena kukokeka n’kuliyandikira kwambiri. Ndi mphamvu yochepa chabe ya dzuŵa imene imafika padziko lapansi koma ndi yokwanira kuti zamoyo zikhalepobe padzikoli.
10. (a) Kodi dzuŵa limaloŵa ndi kutuluka motani mu “hema” mwake? (b) Kodi limathamanga bwanji monga “chimphona”?
10 Wamasalmo anagwiritsa ntchito mawu okuluŵika pofotokoza za dzuŵa pamene ananena kuti dzuŵa ndi “chimphona” chimene chimathamanga kuchokera kumalekezero ena kufika malekezero ena masana, ndipo usiku chimakagona mu “hema.” Nyenyezi yaikulu imeneyi ikamaloŵa kumadzulo, munthu akamaiona ali padziko lapansi imaoneka ngati imapita mu “hema,” ngati kuti ikukapuma. Kum’maŵa imaoneka ngati ikutumphuka, n’kuwala kwambiri “ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake.” Popeza anali mbusa, Davide ankadziŵa kuti usiku kunali kuzizira kwambiri. (Genesis 31:40) Anali kukumbukira kuti dzuŵa linkamuchititsa kumva kutenthera mofulumira komanso kutenthetsa malo amene iye anali. Mwachionekere, silinali kutopa pa “ulendo” wake wochoka kum’maŵa kufika kumadzulo koma linali ngati “chimphona,” chokonzeka kubwerezanso ulendo wake.
Nyenyezi Ndiponso Milalang’amba Yochititsa Mantha
11, 12. (a) Kodi n’chiyani chochititsa chidwi pa mfundo yoti Baibulo limayerekezera nyenyezi ndi mchenga? (b) Kodi kuthambo n’kwakukulu motani?
11 Davide anaona nyenyezi zochepa chabe popeza analibe chipangizo choonera zinthu zakutali. Koma malinga ndi kafukufuku amene anachita posachedwapa, nyenyezi zimene zili kuthambo zimene zimaoneka pogwiritsa ntchito chipangizo choonera zinthu zakutali n’zochuluka zedi mwakuti titati tilembe nambala yake ingakhale 7 wotsatana ndi mazilo 22! Yehova anasonyeza kuti pali nyenyezi zambiri pamene anayerekezera kuchuluka kwa nyenyezi ndi “mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.”—Genesis 22:17.
12 Kwa zaka zambiri, akatswiri a sayansi ya zakuthambo ankaona “zigawo zazing’onozing’ono zooneka mwa chimbuuzi,” monga mmene iwowo ananenera. Asayansi anaganiza kuti “zinthu zozungulira” zimenezi zinali mu mlalang’amba wathu wa Milky Way. Mu 1924, anatulukira kuti chimodzi mwa zinthu zimenezi chimene chinali pafupi, dzina lake Andromeda, chinali mlalang’amba pachokha. Mlalang’ambawu uli pa mtunda umene kuwala kochokera pa mlalang’amba wathuwu wa Milky Way kungatenge zaka mamiliyoni aŵiri kuti kukafike kumeneko.a Asayansi tsopano amanena kuti n’kutheka kuti kuli milalang’amba mabiliyoni ambiri ndipo mlalang’amba uliwonse uli ndi nyenyezi zikwizikwi ndipo ina ili ndi nyenyezi mabiliyoni ambiri. Komabe, Yehova “aŵerenga nyenyezi momwe zili; azitcha mayina zonsezi.”—Salmo 147:4.
13. (a) Kodi ndi mfundo iti yochititsa chidwi pankhani ya magulu a nyenyezi? (b) Kodi pali umboni wotani wakuti asayansi sadziŵa “malemba a kuthambo”?
13 Yehova anafunsa Yobu kuti: “Kodi ungamange gulu [la nyenyezi] la Nsangwe? Kapena kumasula zomangira za [nyenyezi za] Akamwiniatsatana?” (Yobu 38:31) Gulu la nyenyezi ndilo nyenyezi zimene zayalana mwapadera. Ngakhale kuti nyenyezizo zingakhale zotalikirana kwambiri, pamalo pamene zilipo zimakhala pomwepo osasuntha, munthu akamaziona ali padziko lapansi. Popeza malo awowo ndi okhazikika, nyenyezi “zimathandiza kutsogolera anthu oyenda panyanja, zimathandiza akatswiri amene amapita kuthambo kudziŵa kuti chombo chayang’ana kuti mumlengalenga, ndiponso akamafuna kudziŵa nyenyezi.” (The Encyclopedia Americana) Komabe, palibe amene amamvetsetsa “zomangira” zimene zimachititsa kuti magulu a nyenyeziwo akhale pamodzi. Inde, mpaka pano, asayansi sangathe kuyankha funso limene linafunsidwa pa Yobu 38:33, kuti: “Kodi udziŵa malemba a kuthambo?”
14. Kodi mmene kuwala kumadzigaŵira n’zoimitsa mutu motani?
14 Asayansi sangathenso kuyankha funso lina limene Yobu anafunsidwa, lakuti: “Njira ili kuti yomukira pogaŵikana kuunika?” (Yobu 38:24) Wolemba mabuku wina anati funso limeneli ndi “funso la sayansi yamakono.” Mosiyana ndi zimenezi, anthu ena anzeru a ku Girisi ankaganiza kuti kuunika kapena kuti kuwala kumachokera m’maso mwa munthu. Chaposachedwapa, asayansi ankaganiza kuti kuwala kumapangika ndi tinthu tina take tating’onoting’ono. Ena amaganiza kuti kumayenda monga mmene amachitira mafunde. Masiku ano, asayansi amakhulupirira kuti kuwala kuli ngati mafunde komanso ngati tinthu tating’onoting’ono. Koma anthu sanafikebe pomvetsetsa bwino kuwala ndiponso mmene ‘kumadzigaŵira.’
15. Monga mmene anachitira Davide, kodi tiyenera kumva bwanji tikamaganizira za thambo la kumwamba?
15 Kuganizira zonsezi kungachititse munthu kumva monga mmene anachitira Davide, amene analemba kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?”—Salmo 8:3, 4.
Dziko ndi Zolengedwa Zake Zimam’patsa Yehova Ulemerero
16, 17. Kodi nyama za ‘m’malo ozama’ zimalemekeza bwanji Yehova?
16 Salmo 148 limafotokoza njira zina zimene chilengedwe chimalengezera ulemerero wa Mulungu. Vesi 7 imati: “Lemekezani Yehova kuchokera ku dziko lapansi, zinsomba inu, ndi malo ozama onse.” Inde, “malo ozama,” kapena kuti m’nyanja, muli zinthu zambiri zodabwitsa zimene zimasonyeza nzeru ndi mphamvu za Mulungu. Pali namgumi wina amene amalemera pafupifupi makilogalamu 120,000, kufanana ndi kulemera kwa njovu 30. Mtima wake wokha umalemera makilogalamu oposa 450, ndipo umatha kupopa magazi okwana makilogalamu 6,400 kuzungulira m’thupi lake. Kodi nyama zazikulu za m’madzi zimenezi zimayenda pang’onopang’ono ndiponso modzikwakwaza zikakhala m’madzimo? Ayi. “Zimayenda m’nyanja zikuluzikulu” pa liŵiro lalikulu, limatero lipoti la European Cetacean Bycatch Campaign. Kufufuza pogwiritsa ntchito zida zamlengalenga zounikira zinthu patali kunasonyeza kuti “nyama imodzi inayenda mtunda wa makilomita 16,000 m’miyezi 10.”
17 Nyama ya m’madzi yotchedwa bottle-nosed dolphin, nthaŵi zambiri imamira pansi pa nyanja mamita 45, koma mtunda wautali kwambiri umene nyama ya mtunduwu inamirapo ndi mamita 547. Kodi nyama imeneyi imatha bwanji kukhala ndi moyo itapita pansi penipeni pa madzi? Mtima wake umasiya kugwira ntchito kwambiri, ndipo magazi amapita kwambiri ku mtima, ku mapapo, ndi ku ubongo. Minofu yakenso ili ndi zinthu zina zimene zimasunga mpweya wofunika kwambiri kwa anthu ndi nyama. Nyama zina za m’madzi zotchedwa Elephant seal ndi anamgumi ena zingamire pansi kwambiri kuposa pamenepa. Magazini ya Discover inati: “M’malo molimbana ndi mphamvu ya madzi, nyamazi zimalola mphamvu ya madziyo kupsinyiratu mapapo awo.” Zimasungira mpweya wonse wofunika m’minofu yawo. Mwachionekere, nyama zimenezi zimachitira umboni moonekeratu kuti Mulungu wamphamvuyonse ndi wanzeru.
18. Kodi madzi a m’nyanja amasonyeza bwanji nzeru za Yehova?
18 Ngakhalenso madzi a m’nyanja amasonyeza nzeru za Yehova. Buku lakuti Scientific American linati: “Dontho lililonse la madzi ozama mamita 100 pamwamba pa nyanja zazikulu lili ndi tomera ting’onoting’ono tosaoneka ndi maso timene timayandama.” “Nkhalango yosaoneka” imeneyi imayeretsa mpweya wathu mwa kuchotsa mpweya wochuluka kwambiri wosafunika kwa anthu ndi zinyama. Tomera timeneti timatulutsa theka la mpweya wofunika kwambiri kwa anthu ndi zinyama umene timapumawu.
19. Kodi moto ndi chipale chofeŵa zimakwaniritsa bwanji zofuna za Yehova?
19 Salmo 148:8 limatchula “moto ndi matalala, chipale chofeŵa ndi nkhungu; mphepo ya namondwe, yakuchita mawu ake.” Inde, Yehova amagwiritsanso ntchito mphamvu za m’chilengedwe zopanda moyo pofuna kuchita chifuniro chake. Taganizirani za moto. M’zaka makumi angapo zapitazo, anthu ankaona kuti moto wa m’nkhalango umangowononga basi. Anthu ofufuza tsopano akukhulupirira kuti moto umathandiza pa zinthu zachilengedwe. Umachotsa mitengo yakale kapena imene yauma, umathandiza mbewu zambiri kuti zimere, umathandizira kuti nthaka izibwezeretsa chonde, ndiponso umachepetsa vuto la moto wolusa. Chipale chofeŵa n’chofunikanso kwambiri. Chimathirira nthaka ndiponso chimakhala ngati feteleza ku nthakayo, chimathandiza kuti mitsinje ikhale ndi madzi, ndiponso chimateteza zomera ndi nyama kuti zisazizidwe kwadzaoneni mpaka kufika pouma.
20. Kodi mapiri ndi mitengo zimathandiza bwanji athu?
20 Salmo 148:9 limatchula “mapiri ndi zitunda zonse; mitengo ya zipatso ndi ya mikungudza yonse.” Mapiri aakulu amachitira umboni wakuti Yehova ndi wamphamvu zazikulu. (Salmo 65:6) Koma mapiri ndi othandizanso m’mbali zina. Lipoti la bungwe la Institute of Geography mu mzinda wa Bern, ku Switzerland, linati: “Mitsinje yonse yaikulu padziko lapansi imachokera m’mapiri. Anthu oposa theka la anthu onse padziko lapansi amadalira madzi abwino amene amasonkhana m’mapiri . . . ‘Mathanki a madzi’ ameneŵa ndi ofunika kwambiri pa moyo wa anthu.” Ngakhalenso mitengo wamba yomweyi imapereka ulemerero kwa amene anaipanga. Lipoti la bungwe la United Nations Environment Programme linati mitengo “ndi yofunika kwambiri pa moyo wa anthu m’mayiko onse . . . Mitengo ina yambiri ndi yothandiza kwabasi pankhani ya zachuma chifukwa ndiyo magwero a zinthu monga matabwa, zipatso, mtedza, ndi utomoni kapena kuti mambidza. Anthu okwana 2 biliyoni padziko lonse amadalira nkhuni pophika chakudya ndiponso pounikira.”
21. Fotokozani mmene tsamba limaperekera umboni woti panagona luso polipanga.
21 Umboni wakuti pali Mlengi wanzeru umaoneka pa mmene mtengo unapangidwira. Taganizirani za tsamba. Tsamba lili ndi zinthu zina zonga mafuta kunja kwake zimene zimathandiza kuti tsambalo lisaume. Pamwamba pa tsamba, koma m’kati mwa mafutawo, pali tinthu tina ting’onoting’ono tosaoneka ndi maso. Tinthu timeneti tili ndi zinthu zina zobiriŵira, zimene zimatenga mphamvu ya kuwala. Ndiyeno masambawo amagwiritsa ntchito njira ina yovuta kuimvetsetsa n’kupanga chakudya. Mtengo umakoka madzi kudzera m’mizu yake ndipo madziwo amakafika ku masamba pogwiritsa ntchito njira ina yovutanso kuimvetsa. Kunsi kwa tsamba kuli timauna tambirimbiri timene timatsekuka ndi kutsekeka, ndipo zimenezi zimathandiza kuti mpweya umene tsambalo limafuna, umene ife timatulutsa tikamapuma, ulowe m’tsambalo. Kuwala kumapereka mphamvu imene imachititsa kuti madzi aja ndi mpweya uja zisakanikirane n’kupanga chakudya. Mtengowo tsopano umagwiritsa ntchito chakudya chimene wapanga wokha. Komabe, mosiyana ndi mafakitale a anthu opanga chakudya amene amatulutsa phokoso komanso amaoneka oipa, ntchito yopanga chakudya imene mitengo imachita sikhala yaphokoso ndipo mitengo imaoneka yokongola kwambiri. M’malo mowononga zinthu zachilengedwe, ntchitoyi imatulutsa mpweya wofunika kwambiri kwa anthu ndi nyama.
22, 23. (a) Kodi ndi zinthu zina zochititsa chidwi ziti zimene mbalame ndi nyama za pamtunda zili nazo? (b) Kodi ndi mafunso ena ati amene tifunika kukambirana?
22 Salmo 148:10 limatchula “nyama za kuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka.” Nyama zambiri zapamtunda ndi zamoyo zouluka zimasonyeza luso lodabwitsa. Mbalame ina ya kunyanja yonga bakha ingauluke mtunda wautali kwambiri (nthaŵi zina imauluka makilomita 40,000 m’masiku 90 okha). Mbalame ina yaing’ono yonga timba imachoka ku North America kukafika ku South America, ikuuluka kwa maola 80 osaima pena paliponse. Ngamira imasungira madzi, osati pa linunda lake monga mmene anthu ambiri amaganizira, koma m’mimba, zimene zimathandiza kuti ikhale kwa nthaŵi yaitali popanda kumva ludzu. N’zosadabwitsa kuti akatswiri okonza makina osiyanasiyana amaonetsetsa nyama pofuna kukonza makina kapena zinthu zina zatsopano. Wolemba mabuku wina, Gail Cleere, anati: “Ngati mukufuna kukonza chinthu chabwino. . . ndiponso kuti chisawononge zinthu zachilengedwe, mosakayika mungapeze chitsanzo chabwino kwambiri m’zinthu zachilengedwe.”
23 Inde, chilengedwe chikulengezadi ulemerero wa Mulungu. Kuyambira pa nyenyezi za kumwamba mpaka pa zomera ndi nyama, chilichonse chimalemekeza Mlengi wawo mwa njira yawoyawo. Koma nanga bwanji anthufe? Kodi tingalemekeze bwanji Mulungu monga mmene chilengedwe chikuchitira?
[Mawu a M’munsi]
a Kuwala kumathamanga makilomita 300,000 pa sekondi imodzi.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani anthu amene amatsutsa zoti kulibe Mulungu alibe choŵiringula?
• Kodi nyenyezi ndi mapulaneti zimapatsa bwanji Mulungu ulemerero?
• Kodi nyama zam’madzi ndi zapamtunda zimapereka bwanji umboni woti kuli Mlengi wachikondi?
• Kodi mphamvu za m’chilengedwe zopanda moyo zimachita bwanji chifuniro cha Yehova?
[Chithunzi patsamba 10]
Asayansi amati nyenyezi zimene zingathe kuoneka ndi zochuluka moti nambala yake ndi pafupifupi 7 wotsatana ndi mazilo 22
[Mawu a Chithunzi]
Frank Zullo
[Chithunzi patsamba 12]
Nyama zotchedwa bottle-nosed dolphin
[Chithunzi patsamba 13]
Chidutswa cha chipale chofeŵa
[Mawu a Chithunzi]
snowcrystals.net
[Chithunzi patsamba 13]
Mwana wa mbalame yonga bakha