Ukwati Womwe Umapindulitsa Mamiliyoni Omwe Ali ndi Moyo Tsopano
“Pakuti achita ufumu [Yehova, “NW”] Mulungu wathu, Wamphamvuyonse. . . . Tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.”—CHIBVUMBULUTSO 19:6, 7.
1. Ndi liti pamene nyimbo yaulosi ya Chibvumbulutso 19:6-8 idzayamba kuyimbidwa, ndipo nchifukwa ninji?
MAWU osangalatsa amenewa amapanga mbali ya nyimbo yaulosi ya chilakiko. Ndiliti pamene iyo idzayamba kuimbidwa? Pambuyo pa chiwonongeko cha mdani wakalekale wa kulambira kwa Yehova—“Babulo Wamkulu,” “mkazi wachigololo wamkulu” wophiphiritsira yemwe amaimira mitundu yonse ya chipembedzo chonyenga. Chiweruzo chiyenera kuperekedwa pa iye chifukwa cha njira mu imene iye waimira molakwika Mulungu. Iye wasokeretsa chotani nanga mtundu wa anthu mwa kudziloŵetsamo kwake mu ndale zadziko, umbombo wake wa kukondetsa zinthu zakuthupi, ndi udani wake wakupha alambiri owona a Yehova!—Chibvumbulutso 17:1-6; 18:23, 24; 19:1, 2; Yakobo 4:4.
2. (a) Ndimotani mmene Yehova adzabweretsera chiwonongeko cha Babulo Wamkulu? (b) M’malo motamanda Yehova, nchiyani chomwe osakaza a chipembedzo chonyenga adzachita?
2 Posachedwapa, Yehova Mulungu adzaika icho m’mitima ya atsogoleri a ndale zadziko kuwononga iye. (Chibvumbulutso 17:12, 16, 17) Koma owononga a chipembedzo chonyenga sadzagwirizanamo m’kuimba nyimbo yaikulu ya chilakikoyo. M’malomwake, pansi pa chisonkhezero cha Satana, nthaŵi zina wodziŵika monga Gogi, iwo adzawukira ochita chipembedzo chowona, omwe amakhala pa mtendere ndi kudzisunga iwo eni opatuka kuchokera ku kuipa kwa dziko iri.—Yesaya 2:2-4; Ezekieli 38:2, 8-12; Yohane 17:14; Yakobo 1:27.
3. Ndi kaamba ka zifukwa zotani zimene atumiki aumunthu a Yehova adzagwirizana m’nyimbo ya kumwamba?
3 Kuwukira konyoza Mulungu kumeneku kochitidwa ndi olamulira a ndale zadziko kudzatulukamo m’nkhondo ya Armagedo, yomwe idzabweretsa mapeto otheratu ku mitundu yokana chipembedzo. Chotsatira, chisonkhezero choipa cha Satana ndi ziwanda zake chidzachotsedwa pa dziko lapansi. (Chibvumbulutso 16:14, 16; 19:11-21; 20:1, 2) Ndi mitima yodzazidwa ndi chiyamikiro, anthu onse opulumuka adzagawanamo m’kuimba kwa kumwamba kwakuti: “Tamandani Ya, anthu inu, chifukwa Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulira monga mfumu.” (Chibvumbulutso 19:6, NW) Ndithudi, zochitika zogwedeza dziko zoterozo zidzapereka chizindikiro cha kuyambika kwa nyengo yatsopano. Yehova adzakhala atayeretsa ulamuliro wake ndi kuchotsa pa dziko lapansi onse omwe amatokosa kulamulira kwake. Pomalizira nthaŵi idzakhala itafika kaamba ka ukwati wakumwamba. Monga mmene nyimbo yaulosiyo ikupitirizira: “Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa [Yehova]; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.”—Chibvumbulutso 19:7, 8.
4. (a) Ndani omwe akuchitiridwa chithunzi ndi Mwanawankhosa ndi “mkazi” wake? (b) Ndi mafunso otani amene akufunsidwa pano, ndipo ndimotani mmene tingapezere mayankho?
4 Mwanawankhosa sali wina kuposa Yesu Kristu wolemekezedwa, ndipo “mkazi” wake ali chiŵerengero chathunthu cha atsatiri ake okhulupirika odzozedwa a 144,000 tsopano ogwirizana naye m’mwamba. Anzake a mu ukwati a kumwamba amenewa onse pamodzi amapanga ziŵalo zokwanira za Ufumu wa Mulungu, womwe udzakweza mtundu wa anthu, kuphatikizapo akufa owukitsidwa, ku ungwiro waumunthu. (Chibvumbulutso 5:8-10; 14:1-4; 20:4, 12, 13; 21:3-5, 9, 10; 22:1-3) Kodi zochitika zotsogolera ku ukwati wodalitsidwa umenewo zidzakhala zachipambano? Kodi ndimotani mmene mungapindulire kuchokera ku ukwati umenewo? Kuti tipeze mayankho ku mafunso amenewo, tiyeni tisanthule zochitika zozungulira ukwati wa Isake, monga momwe zalembedwera mu Genesis mutu 24.
Mkwatibwi Wosankhidwa Mwaumulungu kaamba ka Isake
5, 6. Nchifukwa ninji Abrahamu anawumirira kuti Isake asakwatire m’Kanani, ndipo ichi chiri chitsogozo chabwino kaamba ka yani lerolino? (1 Akorinto 7:39)
5 Cholembedwacho chikuyamba ndi Abrahamu akupereka malangizo kwa wolamulira banja lake, mwachidziŵikire Eliezere. (Genesis 15:2; 24:2) “Ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova,” anatero Abrahamu, “kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana akazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pawo. Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isake mkazi.”—Genesis 24:3, 4.
6 Kodi nchifukwa ninji Abrahamu anali wowumirira chotero kuti mwana wake wamwamuna sakayenera kukwatira m’Kanani? Chifukwa chakuti Akanani anali mbadwa za Kanani, yemwe anatembereredwa ndi Nowa. (Genesis 9:25) M’kuwonjezerapo, Akanani anadziŵika kaamba ka machitachita awo oipitsidwa, ndipo chofunika koposa, iwo sanalambire Yehova. (Genesis 13:13; Levitiko 18:3, 17-28) Momvetsetseka, Abrahamu anafuna mwana wake wamwamuna kukwatira winawake wochokera ku banja lake, mbadwa za Semu, yemwe analandira dalitso lowuziridwa la Nowa. (Genesis 9:26) Ndi chitsogozo chabwino chotani nanga mmene ichi chiriri kaamba ka Akristu omwe akusankha kukwatira lerolino!—Deuteronomo 7:3, 4.
7. Ndimotani mmene Abrahamu anakonzekeretsera Eliezere kaamba ka ntchito yake?
7 Chotero Eliezere ananyamuka pa ulendo wa makilomita oposa 800 kupita ku Mesopotamiya. Iye anapita wokonzekera bwino, ndi ngamila khumi zodzala ndi mphatso. (Genesis 24:10) M’kuwonjezerapo, iye akanakhoza kusinkhasinkha pa mawu olimbikitsa chikhulupiriro awa a mbuye wake: “Yehova Mulungu wa kumwamba . . . adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.”—Genesis 24:7.
8, 9. (a) Nchiyani chomwe chinachitika pamene Eliezere anafika mu mzinda wa Nahori? (b) Kodi ndi mwa chiyeso chotani mmene mkwatibwi woyenerera anasankhidwira?
8 Potsirizira pake, iye anafika pa mzinda wa Nahori kumpoto kwa Mesopotamiya. Eliezere analola ngamila zotopazo kugwada pansi kuti zipumule pa chitsime kunja kwa mzindawo. Inali nthaŵi ya masana pamene akazi anali kutunga madzi—mwaŵi wabwino, ndithudi, kaamba ka Eliezere kuyang’ana kaamba ka wothekera kukhala mkwatibwi! Koma kodi iye akayenera kukhala mkazi wa mtundu wanji? Wokongola koposa? Ayi. Eliezere choyambirira anali wokondweretsedwa mwa mkazi wokhala ndi umunthu waumulungu. Ichi chinavumbulidwa ndi pemphero lachikhulupiriro lodzichepetsa limene iye tsopano anapereka: “Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lerolino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu. Tawonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m’mudzi atuluka kudzatunga madzi; ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo chotero ndidzadziŵa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.”—Genesis 24:11-14.
9 Chimenecho ndithudi chinali chiyeso chabwino. Mogwirizana ndi The New Encyclopædia Britannica, ngamila ya ludzu mopambanitsa ingamwe ‘malita 95 a madzi mu mphindi 10.’ Mwinamwake ngamila za Abrahamu sizinali za ludzu motero, koma akazi a nthaŵi imeneyo mosakaikira anadziŵa unyinji wa madzi kaamba ka nyamayo. Motsimikizirika, chikatenga mkazi wachifundo koposa, wopanda dyera, waluso kudzipereka kutunga madzi kaamba ka ngamila zotopa khumi za mlendo.
10, 11. (a) Kodi pemphero la Eliezere linayankhidwa m’njira yozizwitsa yotani? (b) Ndimotani mmene Rebeka anasonyezera mikhalidwe yokhumbirika? (c) Ndimotani mmene Eliezere anachitira?
10 Eliezere asanamalize nkomwe pemphero lake, ilo linayankhidwa, monga momwe cholemberacho chikulongosolera: “Anatuluka Rebeka, . . . Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m’mawonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziŵa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera. Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang’ono a m’mtsuko mwako. Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m’manja mwake namwetsa iye. Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse. Ndipo anafulumira nathira madzi a m’mtsuko wake m’chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamila zake zonse.”—Genesis 24:15-20.
11 Eliezere ‘anamyang’anira iye’ pamene anawona yankho lozizwitsa limeneli ku pemphero lake. Pamene namwali woyenera kutamandidwayo anamaliza, mwamunayo anafupa mkaziyo mphete yagolidi ndi zingwinjiri ziŵiri za m’manja ndi kufunsa kuti: “Ndiwe mwana wa yani?” Pamene anapeza kuti anali mwana wa mkulu wake wa Abrahamu, Eliezere anaweramira pansi kwa Yehova m’kulambira kwaulemu, nanena kuti: “Ayamikike Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu amene sanasiya mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zowona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m’njira ya ku nyumba ya abale ake a mbuyanga.”—Genesis 24:21-27.
12. Ndimotani mmene nkhaniyo inatsirizidwira ku nyumba kwa Rebeka?
12 Rebeka mosangalatsidwa anathamangira kunyumba kukawuza banja lake. Pambuyo pake, pamene atate ndi mlongo wa Rebeka anamva kuchokera pakamwa penipeni pa Eliezere chifuno cha ulendo wake ndi mmene Yehova anayankhira pemphero lake, iwo anavomereza popanda kusinkhasinkha kuti Rebeka ayenera kukhala mkazi wa Isake. “Ndipo panali pamene anamva mawuwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi. Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zokometsera zagolidi, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.”—Genesis 24:52, 53.
Chivomerezo cha Mkwatibwi ndi Anamwali Ake
13. Ndimotani mmene chosankha cha Yehova chinatsimikiziridwira kukhala cholondola?
13 Kodi ndimotani mmene Rebeka anawonera mwaŵi wa kusankhidwa mwaumulungu kukhala mkwatibwi wa Isake? Tsiku lotsatira chinachake chinachitika chomwe chinavumbula malingaliro ake owona a mkati. Pokhala atamaliza chifuno cha ulendo wake, Eliezere anakhumba kubwerera kwa mbuye wake popanda kuchedwa. Koma banja la Rebeka linafuna kuti mkwatibwiyo akhale nawo kwa chifupifupi masiku khumi. Chotero chinaikidwa kwa Rebeka kugamulapo ngati iye anali wokonzekera kupita mwamsanga. “Ndidzanka,” iye anatero. Kuvomereza kusiya banja lake mwamsanga ndi kupanga ulendo kupita ku dziko lakutali ndi cholinga chokakwatiwa ndi mwamuna amene anali asanamuwonepo nkomwe chinali chisonyezero chowonekera cha chikhulupiriro m’chitsogozo cha Yehova. Icho chinatsimikizira kuti iye anali chosankha cholondola.—Genesis 24:54-58.
14. (a) Kodi Rebeka anatsagana ndi ndani? (b) Kodi ndi mtundu wanji wa ulendo umene iwo anayang’anizana nawo?
14 Rebeka anali ndi otsagana nawo pa ulendo wake. Monga momwe cholemberacho chikulongosolera: “Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ake, nakwera pa ngamila.” (Genesis 24:61) Chotero gulu la ngamilalo linanyamuka pa ulendo wowopsya wa makilomita oposa 800 kupyola gawo lachilendo. “Avereji ya liŵiro la ngamila zosenza katundu,” likulongosola tero bukhu lakuti The Living World of Animals, “iri chifupifupi makilomita 4 pa ora limodzi.” Ngati ngamila za Abrahamu zinayenda pa liŵiro limenelo kwa maora asanu ndi atatu pa tsiku, chingakhale chinawatengera iwo masiku oposa 25 kufika ku malo awo opita ku Negeb.
15. (a) Ndi chitsanzo chabwino chotani chimene tikuwona mwa Eliezere, Rebeka, ndi anamwali ake? (b) Kodi chochitikacho chikuphiphiritsira chiyani?
15 Eliezere, Rebeka, ndi anamwali ake anakhulupirira kotheratu m’chitsogozo cha Yehova, chitsanzo chabwino kaamba ka Akristu lerolino! (Miyambo 3:5, 6) M’kuwonjezerapo, cholemberacho chiri drama yaulosi yolimbikitsa chikhulupiriro. Monga momwe tawonera, Abrahamu amaimira Yehova Mulungu, yemwe anapereka Mwana wake wokondedwa, Isake Wamkulu, kotero kuti anthu ochimwa angapeze moyo wosatha. (Yohane 3:16) Kukonzekera kwa ukwati wa Isake kunabwera nthaŵi ina iye atapulumutsidwa ku imfa pa guwa loperekerako nsembe. Chinali cholosera kukonzekera kaamba ka ukwati wa kumwamba, kukonzekera komwe kunayamba mofunitsitsa pambuyo pa kuwukitsidwa kwa Yesu.
Ukwati wa Isake Wamkulu
16. (a) Ndimotani, moyenerera, mmene mtumiki wa Abrahamu akuchitira chithunzi mzimu woyera wa Mulungu? (b) Ndi funso lotani lomwe lingafunsidwe ponena za mzimu ndi mkwatibwi?
16 Dzina la Eliezere limatanthauza kuti “Mulungu Wanga Ndi Mthandizi.” M’dzina ndi m’kachitidwe, iye moyenerera akuchitira chithunzi mzimu woyera wa Abrahamu Wamkulu, Yehova Mulungu, umene Iye anatumiza ku dziko lino la kutali, dziko lathu lapansi, kudzasankha mkwati woyenerera kaamba ka Isake Wamkulu, Yesu Kristu. (Yohane 14:26; 15:26) Gulu la mkwatibwi liri “mpingo,” wopangidwa ndi ophunzira a Yesu omwe adzozedwa ndi mzimu woyera monga ana auzimu a Mulungu. (Aefeso 5:25-27; Aroma 8:15-17) Monga mmene Rebeka analandirira mphatso za mtengo, momwemonso ziŵalo zoyambirira za mpingo Wachikristu pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. zinalandira mphatso zozizwitsa m’kuchitira umboni chiitano chawo chaumulungu. (Machitidwe 2:1-4) Mofanana ndi Rebeka, iwo mofunitsitsa asiya maunansi a kudziko ndi akuthupi ndi cholinga chakuti potsirizira pake akagwirizane ndi Mkwati wawo wakumwamba. Kuyambira pa nthaŵi imene chiŵalo chirichonse cha gulu la mkwatibwi chaitanidwa kufikira imfa yawo, iwo ayenera kuchinjiriza unamwali wawo wauzimu pamene akuyenda kupyola dziko lowopsya, lachinyengo la Satana. (Yohane 15:18, 19; 2 Akorinto 11:3; Yakobo 4:4) Lodzazidwa ndi mzimu woyera, gulu la mkwatibwi mokhulupirika likuitana ena kutengako mbali mu makonzedwe a Yehova kaamba ka chipulumutso. (Chibvumbulutso 22:17) Kodi mumatsatira chitsanzo chake mwa kuvomerezanso ku chitsogozo cha mzimuwo?
17. (a) Nchiyani chomwe ngamila khumi zikuchitira chithunzi? (b) Nchiyani chomwe chiyenera kukhala mkhalidwe wathu kulinga ku Baibulo ndi kulinga ku zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo zokonzekeredwa ndi gulu la mkwatibwi? (Machitidwe 17:11)
17 Gulu la mkwatibwi limawona kukhala cha mtengo wapamwamba chomwe chikuchitiridwa chithunzi ndi ngamila khumi. Chiŵerengero cha khumi chikugwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kutanthauza ungwiro kapena kukwanira m’chigwirizano ndi zinthu za pa dziko lapansi. Ngamila khumizo zingayerekezedwe ku Mawu a Mulungu okwanira ndi angwiro, kupyolera mwa amene gulu la mkwatibwi limalandira chakudya chauzimu ndi mphatso zauzimu. (Yohane 17:17; Aefeso 1:13, 14; 1 Yohane 2:5) Ikumachitira ndemanga pa kumwetsa madzi ngamila kwa Rebeka, Nsanja ya Olonda ya November 1, 1948, (m’Chingelezi) inapanga kugwiritsira ntchito uku ku gulu la mkwatibwilo: “Iwo mwachikondi amalingalira Mawu a Mulungu omwe amabweretsa wochulukira wa mzimu wake kwa iwo. Iwo amatenga chikondwerero m’Mawu ake olembedwa, kuwapereka iwo ndi kuwakhalitsa atsopano mwa kusamalira ku iwo ndi kusonyeza kudera nkhaŵa kowona mtima kaamba ka uthenga wake ndi chifuno, kufunafuna kukhulupirira iwo.” Monga chitsanzo cha ichi, otsalira a gulu la mkwatibwi mwachikondi apangitsa kukhalako kwa mamiliyoni, New World Translation of the Holy Scriptures yokonzedwanso chatsopano. Kaya matembenuzidwe abwino amenewa alimo m’chinenero chanu kapena ayi, kodi inu mumasonyeza chiyamikiro mwa kusanthula Baibulo mokhazikika limodzi ndi zothandizira phunziro zoperekedwa ndi gulu la mkwatibwi?—2 Timoteo 3:16.
Ukwati wa Mwanawankhosa Uyandikira
18. Nchifukwa ninji anamwali a Rebeka moyenerera akuchitira chithunzi mabwenzi a mkwatibwi lerolino?
18 M’masiku ano omalizira a dziko la Satana, otsalira a gulu la mkwatibwi agwirizana ndi “khamu lalikulu,” loyerekezedwa ndi “anamwali” a Rebeka. Mofanana ndi m’nkhani ya Rebeka, awa mopambana amaposa gulu la mkwatibwi lokwanira mwa chiŵerengero cha 144,000. Iwo ali “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za Yesu Kristu. (Chibvumbulutso 7:4, 9; Yohane 10:16) Monga anamwali okhulupirika a mkwatibwiyo, iwo ayeneranso kukhala omasuka kuchokera ku kuipitsidwa ndi dziko loipa la Satana. Iwo nawonso ayenera kuvomereza ku zitsogozo za mzimu wa Yehova ndi Mawu ake monga momwe zalongosoledwera kwa iwo ndi gulu la mkwatibwi. Koma mphoto yawo iri yosiyana. Ngati iwo apirira m’kuchirikiza kokhulupirika kwa mkwatibwi wa Kristu, iwo adzapulumuka mapeto a dziko la Satana ndi kukhala ndi mwaŵi wosangalatsa wa kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso ya pa dziko lapansi.—Chibvumbulutso 21:3, 4.
19. Nchiyani chomwe chinachitika pamene Rebeka ndi anamwali ake anafikira mapeto a ulendo wawo?
19 Kodi Rebeka ndi “anamwali ake” mwachipambano anafikira chonulirapo chawo? Inde. Monga momwe Baibulo likusimbira kuti: “Ndipo Isake anatuluka kulingalira m’munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, tawona, ngamila zinalinkudza. Ndipo Rebeka anatukula maso ake, ndipo pamene anawona Isake anatsika pa ngamila.” Pambuyo pakuti Eliezere analongosola ulendo wake wachipambano, Isake analandira Rebeka monga mkazi wake ndipo “anamkonda iye.”—Genesis 24:63-67.
20. Ndi chochitika chotani cha kusangalala chomwe chikuphiphiritsidwa ndi ukwati wa Isake?
20 Mofananamo, chifuno cha Yehova ponena za mkwatibwi wa Kristu sichingalephere. (Yesaya 55:11) Posachedwapa, Babulo Wamkulu ataweruzidwa ndi kuwonongedwa, omalizira a otsalira a mkwatibwi adzamaliza ulendo wawo. Nthaŵi idzafika kaamba ka iwo kulekanitsidwa ndi mabwenzi awo anamwali ndi kugwirizana mu ukwati kwa Isake Wamkulu m’mwamba. Ndi chochitika chachikulu cha kusangalala cha chilengedwe chaponseponse chotani nanga mmene icho chidzakhalira!—Chibvumbulutso 19:6-8.
21. Pamene kaindeinde wa ukwati wakumwamba akuyandikira, nchiyani chomwe tonsefe tiyenera kumachita?
21 Pa nthaŵi ino, mamiliyoni akudzidalitsa iwo eni mwa kuvomereza ku utumiki wa otsalira a mkwatibwi omacheperachepera. Onse a iwo asanamalize ntchito yawo ya pa dziko lapansi mu imfa, kusakazidwa kwa ulamuliro wa dziko wonga mkazi wachigololo wa chipembedzo chonyenga kudzazindikiritsa kuyambika kwa “masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko.” Nthaŵi yomwe yatsalako yafupika. Ngati mufuna kudzapulumuka, ndi chofunika chotani nanga kugawanamo m’kupereka malamulo aumulunguwo! (Mateyu 24:14, 21; Marko 13:10; Luka 21:15; Yohane 13:34) Malamulo oterowo ali ndi kugwira ntchito kwapadera m’nthaŵi zathu zovuta. Chotero, kaya ndinu a otsalira a mkwatibwi kapena “khamu lalikulu” la anamwali ake, pitirizani kumvera Yehova ku ulemerero wake ndi chimwemwe chanu chosatha. Ndi chokulira chotani nanga mmene icho chikakhalira kaamba ka khamu lalikulu, lomwe likuŵerengedwa kale monga mabwenzi a Mulungu, kupitirizabe kukhala ndi moyo pamene Yehova ‘akupanga zinthu zonse zatsopano’ ndi madalitso osatha akusefukira ku mamiliyoni m’dziko lapansi la paradaiso!—Chibvumbulutso 21:5; 22:1, 2, 17.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Ndi zochitika zosangalatsa zotani zomwe ziyenera kuchitika posachedwapa?
◻ Nchiyani chomwe chikutsimikizira kuti ukwati wakumwamba udzakhala chipambano chotheratu?
◻ Kodi Eliezere ndi ngamila khumi angayerekezedwe ndi chiyani?
◻ Ndani lerolino omwe akufanana ndi Rebeka ndi anamwali ake?
◻ Nchiyani chomwe tikuphunzira kuchokera ku zochitika zotsogolera ku ukwati wa Isake?