Anachita Chifuniro cha Yehova
Kupezera Isake Mkazi
MWAMUNA wokalambayo ali khale pafupi ndi chitsime anali wotopa. Iye ndi anyamata ake limodzi ndi ngamila zawo khumi anali atayenda ulendo wautali kuchokera chapafupi ndi Beereseba kumka kumpoto kwa Mesopotamiya—mtunda woposa makilomita 800.a Tsopano popeza kuti anali atafika kumene anali kupita, wapaulendo wolema ameneyu anapuma kuti asinkhesinkhe za ntchito yake yovutayo. Kodi mwamuna ameneyu anali yani, ndipo nchifukwa ninji anayenda ulendo wosautsa umenewu?
Mwamunayo anali mtumiki wa Abrahamu, “wamkulu wa pa nyumba yake.” (Genesis 24:2) Ngakhale kuti sanatchulidwe dzina m’nkhaniyi, mwachionekere ameneyu anali Eliezere, amene Abrahamu nthaŵi ina anamutcha ‘wobadwa m’nyumba mwake’ amene anaoneka kukhala m’mzera ‘wodzaloŵa m’malo mwake.’ (Genesis 15:2, 3) Ndithudi, pamenepo nkuti Abrahamu ndi Sara anali adakali opanda mwana. Tsopano mwana wawo, Isake, anali wazaka 40 zakubadwa, ndipo ngakhale kuti Eliezere sanalinso woloŵa m’malo wamkulu wa Abrahamu, anakhalabe mtumiki wake. Chotero analola pamene Abrahamu anapereka pempho lovuta. Linali lotani kodi?
Ntchito Yovuta
M’tsiku la Abrahamu ukwati unakhudza osati banja lokha komanso fuko lonse, kapena mtundu wa makolo. Chotero unali mwambo kwa makolo kuti azisankhira ana awo wokwatirana naye. Komabe, pofunafuna mkazi wa mwana wake, Isake, Abrahamu anayang’anizana ndi chothetsa nzeru. Kuloŵa ukwati ndi Mkanani kunali kosatheka chifukwa cha mikhalidwe yawo yopanda umulungu. (Deuteronomo 18:9-12) Ngakhale kuti unali mwambo mwamuna kukwatira wa m’fuko lake, achibale a Abrahamu anali kukhala kutali pamtunda wamakilomita mazana ambiri chakumpoto kwa Mesopotamiya. Iye sakanalola kuti Isake asamukirenso komweko, popeza kuti Yehova analonjeza Abrahamu kuti: ‘Ndidzapatsa mbewu zako dziko ili,’ dziko la Kanani. (Genesis 24:7) Choncho, Abrahamu anati kwa Eliezere: “Udzamke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kutengera mwana wanga Isake mkazi.”—Genesis 24:4.
Atatsiriza ulendo wautaliwo, Eliezere anapuma chapafupi ndi chitsime namasinkhasinkha za ntchito yake. Anazindikira kuti posachedwa akazi adzayamba kubwera kuchitsime kudzatunga madzi a madzulo. Choncho anachonderera Yehova kuti: “Namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo chotero ndidzadziŵa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu.”—Genesis 24:14.
Adakali chipempherere, mkazi wachichepere wochititsa kaso wotchedwa Rebeka anafika. “Ndimwetu madzi pang’ono a m’mtsuko mwako.” Eliezere anatero kwa iye. Rebeka analola, kenako anati: “Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse.” Kumenekotu kunali kudzipereka kwenikweni, popeza kuti ngamila yaludzu ingamwe malita 95 amadzi m’mphindi khumi chabe! Kaya ngamila za Eliezere zinali zaludzu kwambiri kapena iyayi, Rebeka ayenera kukhala atadziŵa kuti utumiki umene anadzipereka kuuchita unali wovuta. Ndithudi, “anafulumira nathira madzi a m’mtsuko wake m’chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamila zake zonse.”—Genesis 24:15-20.
Atazindikira chitsogozo cha Yehova, Eliezere anampatsa Rebeka mphete ya golidi ndi zingwinjiri ziŵiri za golidi mtengo wake pafupifupi $1,400 m’mitengo ya lero. Pamene Rebeka anamuuza kuti anali chidzukulu cha Nahori, mbale wa Abrahamu, Eliezere anapereka pemphero lachiyamiko kwa Mulungu. “Yehova wanditsogolera m’njira ya ku nyumba ya abale ake a mbuyanga,” anatero. (Genesis 24:22-27) Eliezere anatsogoleredwa ku banja la Rebeka. Posakhalitsa, Rebeka anadzakhala mkazi wa Isake, ndipo anakhala ndi mwaŵi wakudzakhala kholo lachikazi la Mesiyayo, Yesu.
Maphunziro Kwa Ife
Yehova anadalitsa Eliezere m’kuyesayesa kwake mwapemphero kupezera Isake mkazi wowopa Mulungu. Pajatu, kumbukirani kuti ukwati wa Isake unali wokhudzana mwachindunji ndi chifuno cha Mulungu cha kutulutsa mbewu kupyolera mwa Abrahamu. Chotero nkhani imeneyi siyenera kutipangitsa kugamula kuti aliyense amene adzapempherera mkazi adzapatsidwa mozizwitsa. Komabe, ngati timamatira ku mapulinsipulo a Yehova, iye adzatipatsa nyonga kuti tipirire zitokoso za m’mbali zonse ziŵiri m’moyo—ukwati kapena umbeta.—1 Akorinto 7:8, 9, 28; yerekezerani ndi Afilipi 4:11-13.
Eliezere anafunikira kuyesetsa ndithu kuchita zinthu m’njira ya Yehova. Ifenso tingaone kuti kugonjera ku miyezo ya Yehova sikokhweka nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, kungakhale kovuta kupeza ntchito yolembedwa imene simadodometsa ntchito ya teokrase, mnzathu wamuukwati wowopa Mulungu, mabwenzi omangirira, zosangulutsa zosaluluzika. (Mateyu 6:33; 1 Akorinto 7:39; 15:33; Aefeso 4:17-19) Komabe, Yehova angachirikize aja amene amakana kulolera kuswa mapulinsipulo a Baibulo. Baibulo limalonjeza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6.
[Mawu a M’munsi]
a Polingalira kuyenda kwa ngamila, ulendowo ungakhale utatenga masiku oposa 25.