Mukati Inde Akhaledi Inde
“Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.”—MAT. 5:37.
1. Kodi Yesu ananena kuti chiyani pa nkhani yolumbira? N’chifukwa chiyani ananena zimenezo?
SIKUTI Akhristu oona amafunika kulumbira nthawi zonse pofuna kusonyeza kuti zimene akunena ndi zoona. Zili choncho chifukwa amatsatira mawu a Yesu akuti: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde.” Apa Yesu ankatanthauza kuti Akhristu ayenera kuchita zimene anena. Asananene mawuwa, Yesu ananena kuti: “Usamalumbire n’komwe.” Ananena zimenezi chifukwa chakuti anthu ambiri ali ndi chizolowezi chomangolumbira pa zinthu zimene akudziwa kuti sachita. Kodi chimachitika n’chiyani ngati munthu walumbira koma osachita zimene wanenazo? Munthuyo angasonyeze kuti ndi wosadalirika ndiponso kuti akutsogoleredwa ndi “woipayo.”—Werengani Mateyu 5:33-37.
2. Kodi kulumbira kulikonse n’koipa? Fotokozani.
2 Kodi Yesu ankatanthauza kuti kulumbira kulikonse n’koipa? Ayi. Monga taonera mu nkhani yoyamba ija, Yehova Mulungu ndiponso Abulahamu, yemwe anali mtumiki wake wokhulupirika, analumbira pa zinthu zofunika kwambiri. Chilamulo cha Mulungu chinkanenanso kuti anthu ayenera kulumbira pofuna kuthetsa nkhani zina. (Eks. 22:10, 11; Num. 5:21, 22) Choncho Mkhristu akhoza kulumbira posonyeza kuti alankhula zoona zokhazokha m’khoti. Nthawi zina, angafunikenso kulumbira potsimikizira anzake kuti achitadi zinthu zina kapena pothandiza kuthetsa vuto linalake. Yesu atalumbiritsidwa ndi mkulu wa ansembe, iye sanatsutse koma ananena zoona zokhazokha pa maso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. (Mat. 26:63, 64) Yesu sankafunika kulumbira kwa aliyense. Koma pofuna kusonyeza kuti zomwe akunena n’zoona, ankakonda kuyamba ndi mawu akuti: “Ndithudi [kapena kuti “Ndithu, ndithu”] ndikukuuzani anthu inu.” (Yoh. 1:51; 13:16, 20, 21, 38) Tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira kwa Yesu, Paulo ndiponso anthu ena amene “Inde” wawo ankakhaladi Inde.
YESU NDI CHITSANZO CHABWINO KWAMBIRI
3. Kodi Yesu analonjeza chiyani m’pemphero lake? Nanga Yehova anayankha bwanji pemphero la Mwana wake?
3 “Taonani! Ine ndabwera . . . kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.” (Aheb. 10:7) Ponena mawu amenewa m’pemphero, Yesu anasonyeza kuti akudzipereka kwa Mulungu kuti achite zinthu zonse monga Mbewu yolonjezedwa. Izi zinaphatikizapo ‘kuvulazidwa chidendene’ ndi Satana. (Gen. 3:15) Palibe munthu winanso amene anadzipereka kuti achite zinthu zovuta kwambiri ngati zimenezi. Poyankha pempheroli, Yehova analankhula kuchokera kumwamba ndipo mawu ake anasonyeza kuti amakhulupirira kwambiri Mwana wakeyu. Koma sanapemphe Yesu kuti alumbire potsimikiza kuti achitadi zimene walonjeza.—Luka 3:21, 22.
4. Kodi Yesu anachita chiyani kuti “Inde” wake akhaledi Inde?
4 Yesu ankaonetsetsa kuti nthawi zonse “Inde” wake azikhaladi Inde. Atate wake anamupatsa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa anthu amene Mulunguyo anawakokera kwa Mwana wake. (Yoh. 6:44) Yesu sanalole kuti chilichonse chimusokoneze pa ntchitoyi. Baibulo limasonyeza kuti Yesu ankachitadi chifuniro cha Mulungu mogwirizana ndi zimene analonjeza. Limanena kuti: “Malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani, akhala Inde kudzera mwa iye.” (2 Akor. 1:20) Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pokwaniritsa zimene analonjeza kwa Atate wake. Tsopano tiyeni tikambirane za munthu wina amene anayesetsa kutsanzira Yesu.
PAULO ANKACHITA ZIMENE WANENA
5. Kodi mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chotani kwa ife?
5 “Ndichite chiyani, Ambuye?” (Mac. 22:10) Saulo, yemwe anadzakhala Paulo, anafunsa funsoli poyankha zimene Ambuye Yesu anamuuza. Pa nthawiyi, anaona Yesu m’masomphenya akumuletsa kuzunza Akhristu. Izi zitachitika, Saulo analapa, kubatizidwa ndiponso kuvomera kugwira ntchito yochitira umboni za Yesu kwa anthu amene sanali Ayuda. Kuyambira nthawi imeneyi, Paulo ankatchula Yesu kuti “Ambuye” ndipo ankamumvera moyo wake wonse. (Mac. 22:6-16; 2 Akor. 4:5; 2 Tim. 4:8) Paulo sanali ngati anthu ena amene Yesu anawafunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani mumandiitana kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osachita zimene ndimanena?” (Luka 6:46) Yesu amafuna kuti anthu amene amamutchula kuti “Ambuye” azionetsetsa kuti “Inde” wawo akhaledi Inde, ngati mmene anachitira Paulo.
6, 7. (a) N’chifukwa chiyani Paulo anasintha ulendo wake wopita ku Korinto? N’chifukwa chiyani tinganene kuti panalibe chifukwa chonenera kuti iye anali wosadalirika? (b) Kodi tiziona bwanji anthu amene ali pa udindo wotitsogolera?
6 Paulo ankalalikira uthenga wa Ufumu mwakhama m’madera ambiri a ku Asia Minor ndiponso ku Ulaya. Iye anakhazikitsa mipingo yambiri ndipo ankaiyendera. Pa nthawi ina, iye anaona kuti ndi bwino kulumbira posonyeza kuti zimene analemba ndi zoona. (Agal. 1:20) Anthu ena ku Korinto atanena kuti Paulo ndi wosadalirika, iye analemba kuti: “Mulungu ndi wodalirika kuti mawu athu kwa inu asakhale Inde kenako Ayi.” (2 Akor. 1:18) Pamene Paulo ankalemba zimenezi anali atachoka ku Efeso ndipo anali pa ulendo wopita ku Korinto kudzera ku Makedoniya. Iye ankafuna kuti ayambe wabwerera ku Korinto asanapite ku Makedoniya. (2 Akor. 1:15, 16) Koma nthawi zina munthu angasinthe zochita pa zifukwa zina. Mwachitsanzo, oyang’anira oyendayenda a masiku ano angasinthe ndandanda yawo yoyendera mipingo. Iwo amasintha pa zifukwa zamwadzidzidzi osati tizifukwa ting’onoting’ono tongokomera iwowo. Paulo anasintha ulendo wopita ku Korinto chifukwa chofuna kuthandiza mpingowo. N’chifukwa chiyani tikutero?
7 Paulo atakonza zoti apite ku Korinto, anamva kuti Akhristu kumeneko sakugwirizana ndiponso akulekerera chiwerewere. (1 Akor. 1:11; 5:1) Pofuna kukonza zinthu, iye anawalembera kalata yake yoyamba imene inali ndi malangizo amphamvu. Kenako, m’malo mopita ku Korinto atachoka ku Efeso, Paulo anaganiza zopatsa abale ake nthawi kuti agwiritse ntchito malangizowo. Anachita zimenezi n’cholinga choti akadzapitako, ulendo wake udzakhale wolimbikitsa kwambiri. Kuti awatsimikizire za chifukwa chimene anasinthira ulendo wake, iye analemba m’kalata yake yachiwiri kuti: “Mulungu akhale mboni pa moyo wanga kuti chifukwa chimene sindinabwererebe ku Korintoko n’chakuti sindinafune kuti ndidzawonjezere chisoni chanu.” (2 Akor. 1:23) Tisakhale ngati anthu amene ankanena kuti Paulo ndi wosadalirika. M’malomwake, tiyeni tizilemekeza anthu amene aikidwa pa udindo kuti atitsogolere. Paulo anatengera chitsanzo cha Khristu. Ifenso tingachite bwino kutengera chitsanzo cha Paulo.—1 Akor. 11:1; Aheb. 13:7.
ANTHU ENA OMWE NDI ZITSANZO ZABWINO
8. Kodi Rabeka anapereka chitsanzo chotani?
8 “Inde ndipita.” (Gen. 24:58) Awa ndi mawu amene Rabeka ananena kwa mayi ake ndiponso mchimwene wake. Kunali kuvomera kuti achoka kwawo tsiku lomwelo n’kutsagana ndi mlendo pa ulendo wamakilomita 800 kuti akakhale mkazi wa Isaki. (Gen. 24:50-58) Rabeka anachitadi zimene ananena ndipo anakhala mkazi wa Isaki. Iye anali mkazi wokhulupirika ndiponso woopa Mulungu. Rabeka anali mlendo wokhala m’mahema kwa moyo wake wonse m’Dziko Lolonjezedwa. Iye anadalitsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwake. Anadzakhala kholo la Yesu Khristu, yemwe ndi Mbewu yolonjezedwa.—Aheb. 11:9, 13.
9. Kodi Rute anasonyeza bwanji kuti “Ayi” wake analidi Ayi?
9 “Ayi musatero, ife tipita nanu kwanu.” (Rute 1:10) Rute ndi Olipa, omwe anali akazi amasiye achimowabu, ndi amene ananena mawuwa kwa Naomi, yemwe anali mpongozi wawo. Naomi analinso wamasiye ndipo anali kubwerera kwawo ku Betelehemu. Iye atachonderera akazi awiriwa kuti asapite nawo, Olipa anabwerera kwawo. Koma mawu a Rute oti “Ayi” anakhaladi Ayi. (Werengani Rute 1:16, 17.) Iye anapitiriza kutsatira mokhulupirika apongozi akewa n’kulolera kusiya achibale ndiponso chipembedzo chake chonyenga cha ku Mowabu. Rute anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ndipo anadalitsidwa pokhala m’gulu la akazi asanu amene Mateyu anawatchula pa mndandanda wa makolo a Khristu.—Mat. 1:1, 3, 5, 6, 16.
10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesaya anapereka chitsanzo chabwino kwa ife?
10 “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Yesaya asananene zimenezi, anaona masomphenya aulemerero. Anaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu pamwamba pa kachisi wa Isiraeli. Iye akuyang’anitsitsa zimenezi, anamva Yehova akunena kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?” Yehova ankafuna munthu woti akapereke uthenga wake kwa anthu ake osamvera. Yesaya anavomera ndipo anachitadi zimene ananena. Iye anatumikira mokhulupirika monga mneneri kwa zaka zoposa 46. Anapereka mauthenga achiweruzo cha Mulungu ndiponso onena za malonjezo osangalatsa akuti kulambira koona kudzabwezeretsedwa.
11. (a) Kodi nkhani yakuti “Inde” wathu azikhaladi Inde ndi yofunika bwanji? (b) Kodi m’Baibulo muli zitsanzo ziti za anthu amene sanachite zimene ananena?
11 N’chifukwa chiyani Yehova anaika zitsanzozi m’Mawu ake? Kodi nkhani yakuti “Inde” wathu azikhaladi Inde ndi yofunika bwanji? Baibulo limachenjeza mosapita m’mbali kuti anthu “osasunga mapangano . . . n’ngoyenera imfa.” (Aroma 1:31, 32) M’Baibulo mulinso anthu amene “Inde” wawo sanali Inde. Ena mwa iwo ndi Farao wa ku Iguputo, Mfumu Zedekiya ndiponso Hananiya ndi Safira. Koma zinthu sizinawayendere bwino onsewa ndipo ndi chenjezo kwa ife.—Eks. 9:27, 28, 34, 35; Ezek. 17:13-15, 19, 20; Mac. 5:1-10.
12. N’chiyani chingatithandize kuti tizichitadi zimene tanena?
12 ‘M’masiku otsiriza’ ano, anthu ambiri ndi “osakhulupirika” ndiponso “ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.” (2 Tim. 3:1-5) Tiyenera kuyesetsa kupewa anthu ngati amenewa. M’malomwake, tizisonkhana nthawi zonse ndi anthu amene amayesetsa kuti “Inde” wawo akhaledi Inde.—Aheb. 10:24, 25.
“INDE” WANU WOFUNIKA KWAMBIRI
13. Kodi “Inde” wofunika kwambiri wa Akhristu ndi uti?
13 Lonjezo lofunika kwambiri limene anthufe timapanga ndi lokhudza kudzipereka kwa Mulungu. Anthu amene akufuna kudzikana okha n’cholinga choti akhale ophunzira a Yesu amafunsidwa maulendo atatu kuti atsimikize ngati akufunadi kuchita zimenezo. (Mat. 16:24) Mwachitsanzo, akulu awiri akamakambirana ndi munthu amene akufuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa, amamufunsa kuti, “Kodi mukufunadi kukhala wa Mboni za Yehova?” Kenako munthuyo akafika poti akufuna kubatizidwa, akulu amakumana naye n’kumufunsa kuti, “Kodi munadzipereka kwa Yehova m’pemphero?” Pomaliza, tsiku la ubatizo likafika, onse okabatizidwa amafunsidwa kuti, “Pa maziko a nsembe ya Yesu Khristu, kodi munalapa machimo anu ndi kudzipereka kwa Yehova kuti muchite chifuniro chake?” Anthu okabatizidwawo amavomera pamaso pa anthu onse kuti “Inde.” Apa amalonjeza kuti azitumikira Mulungu kwamuyaya.
14. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati nthawi ndi nthawi?
14 Kaya mwabatizidwa posachedwapa kapena mwakhala mukutumikira Mulungu kwa zaka zambiri, nthawi ndi nthawi muyenera kudzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi ndimatsanzira Yesu Khristu pochitadi zimene ndinalonjeza kwa Yehova? Kodi ndikumverabe Yesu poika patsogolo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu?’—Werengani 2 Akorinto 13:5.
15. Kodi “Inde” wathu ayenera kukhaladi Inde pa nkhani zina ziti?
15 Kuti tichitedi zimene tinalonjeza Mulungu, tiyenera kukhala okhulupirika pa nkhani zinanso. Mwachitsanzo, kodi muli pa banja? Ngati zili choncho, munalonjeza kuti muzikonda ndi kusamalira mwamuna kapena mkazi wanu. Ndiyetu muyenera kuchitadi zimenezi. Kodi mwasaina pangano lokhudza ndalama kapena fomu yofunsira utumiki? Ngati zili choncho, muyenera kuchitadi zimene mwalonjeza. Kodi mwavomera kukadya kunyumba ya munthu wosauka? Musasinthe ngati mwaitanidwa ndi munthu wina wopeza bwino. Kodi mwalonjeza munthu wina mu utumiki kuti mudzabwererako? Ngati ndi choncho, “Inde” wanu ayenera kukhaladi Inde. Mukamatero, Yehova adzadalitsa utumiki wanu.—Werengani Luka 16:10.
TINGATHANDIZIDWE NDI MFUMU NDIPONSO MKULU WA ANSEMBE WATHU
16. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati talephera kuchita zimene tinalonjeza?
16 Baibulo limanena kuti anthu opanda ungwirofe “timapunthwa nthawi zambiri,” makamaka pa zolankhula zathu. (Yak. 3:2) Kodi tiyenera kutani tikazindikira kuti sitinachite zimene tinalonjeza? M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli, munthu amene “walankhula mosalingalira bwino” ankakhala ndi mwayi wochitiridwa chifundo. (Lev. 5:4-7, 11) Mwayi umenewu uliponso kwa Akhristu amene alankhula mosalingalira bwino. Ngati tiulula kwa Yehova m’pemphero kuti talephera kuchita zimene tinalonjeza, iye adzatikhululukira mwachifundo. Yesu Khristu, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe wathu, adzatithandiza kukonzanso ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Yoh. 2:1, 2) Koma kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Mulungu, tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti talapadi. Mwachitsanzo, tisakhale ndi chizolowezi chosachita zimene talonjeza ndiponso tiziyesetsa kukonza zimene zalakwika chifukwa cholankhula mosalingalira bwino. (Miy. 6:2, 3) Kunena zoona, ndi bwino kuganiza kaye tisanalonjeze zinthu zimene mwina sitingakwanitse.—Werengani Mlaliki 5:2.
17, 18. Kodi anthu amene amayesetsa kuchita zimene alonjeza akuyembekezera zinthu zosangalatsa ziti?
17 Atumiki a Yehova amene amayesetsa kuchita zimene alonjeza akuyembekezera zinthu zosangalatsa kwambiri. Odzozedwa 144,000 adzalandira moyo wosafa kumwamba, kumene “adzalamulira monga mafumu limodzi [ndi Yesu] zaka 1,000.” (Chiv. 20:6) Koma anthu mamiliyoni ambiri adzakhala m’Paradaiso padziko lapansi n’kumalamulidwa ndi Khristu. Pa nthawiyo, adzathandizidwa kuti matupi awo komanso maganizo awo akhale angwiro.—Chiv. 21:3-5.
18 Tikadzakhala okhulupirika pa chiyeso chomaliza pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu, sitidzakayikiranso zonena za munthu aliyense. (Chiv. 20:7-10) Munthu akanena kuti “Inde” azidzakhaladi Inde ndipo akati “Ayi” azidzakhaladi Ayi. Aliyense wokhala ndi moyo pa nthawi imeneyo azidzatsanzira Atate wathu wachikondi, Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachoonadi.”—Sal. 31:5.