TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | RABEKA
“Inde Ndipita”
RABEKA anali atayenda kwa milungu ingapo kuchokera kwawo ku Harana, mzinda womwe unali kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Kanani. Pa nthawiyi n’kuti dzuwa litatsala pang’ono kulowa. Ulendowu unali wa pa ngamila ndipo chifukwa cha kutalika kwa mtunda womwe anayenda, Rabeka ayenera kuti anafika pozolowera kuyenda pa nyamayi. Apa n’kuti atayandikira kwambiri kwawo kwa Isaki, ndipo n’kutheka kuti ankadzifunsa mafunso ambirimbiri okhudza moyo wake. Mwina ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzaonananso ndi anthu a m’banja langa?’
Atadutsa chigawo chachikulu cha dziko la Kanani, anayamba kuyenda m’misewu yokumbikakumbika ya ku Negebu. (Genesis 24:62) N’kutheka kuti atayandikira kumeneku, Rabeka anayamba kuona nkhosa. Dzikoli linalibe nthaka yabwino komabe kunkapezeka msipu wambiri wodyetsera ziweto. Koma mtumiki wa Abulahamu, yemwe anatumidwa kukatenga Rabeka ankazidziwa bwino njira za m’derali. Ndipo n’zosakayikitsa kuti pa nthawiyi ankangoona kuchedwa kuti akafotokozere mbuye wake nkhani yosangalatsa yakuti Rabeka akhala mkazi wa Isaki. Komano Rabeka ayenera kuti anayambanso kudzifunsa kuti, ‘Ndizikhala bwanji m’dziko limeneli? Kodi Isakiyo ndi wooneka bwanji? Popeza kuti sitinaonanepo, andikondadi akangondiona? Nanga ineyo andisangalatsa?’
Masiku ano, makolo ambiri sasankhira ana awo mwamuna kapena mkazi woti akwatirane naye. Koma m’mayiko ena maukwati oterewa si achilendo. Kaya kwanuko zimenezi zimachitika kapena ayi, mungavomereze kuti pa nthawiyi Rabeka anakhala ngati wangomangidwa m’masamba. Koma zimene anachitazi polola ukwati umenewu, zikusonyeza kuti anali munthu wolimba mtima komanso wa chikhulupiriro cholimba. Nafenso timafunika kukhala ndi makhalidwe amenewa zinthu zikasintha pa moyo wathu. Koma tiyeni tionenso makhalidwe ena abwino amene Rabeka anali nawo.
“NDITUNGIRANSO MADZI NGAMILA ZANU”
Rabeka anakulira ku Mesopotamiya mumzinda wina wotchedwa Harana. Makolo ake anali osiyana ndi anthu ambiri a ku Harana. Tikutero chifukwa iwo ankalambira Yehova pomwe anthu ena ankalambira Sini, yemwe anali mulungu wa mwezi.—Genesis 24:50.
Rabeka anali mtsikana wokongola kwambiri, wolimbikira ntchito komanso wakhalidwe labwino. Ngakhale kuti kwawo kunali kolemera komanso kunali antchito ambiri, Rabeka sanali waulesi ndipo makolo ake sankamusasatitsa. Iye ankagwira ntchito zomwe atsikana ena onse ankagwira monga kutunga madzi a banja lonse. Tsiku lililonse dzuwa likapendeka, Rabeka ankanyamula mtsuko waukulu paphewa n’kupita kuchitsime kukatunga madzi.—Genesis 24:11, 15, 16.
Ndiyeno tsiku lina Rabeka anatenga mtsuko wake monga mmene ankachitira nthawi zonse n’kupita kuchitsime. Atatunga madzi, panafika munthu wina wachikulire. Munthuyo anamupempha mwaulemu kuti: “Chonde ndipatse madzi a mumtsuko wako ndimweko pang’ono.” Rabeka anadziwa kuti munthuyu wayenda ulendo wautali. Ndiyeno anatsitsa mtsuko paphewa lake n’kumupatsa madziwo kuti amwe. Kenako Rabeka anaona kuti munthuyo ali ndi ngamila 10. Ngamilazo zinali zitagona pafupi ndi chomwera ziweto chomwe chinalibe madzi. Rabeka anazindikira kuti munthuyu akuchita naye chidwi ndipo nayenso ankafunitsitsa kumuthandiza. Iye anauza munthuyo kuti: “Nditungiranso madzi ngamila zanu mpaka zitamwa mokwanira.”—Genesis 24:17-19.
Onani kuti Rabeka sanangonena kuti atungira madzi ngamilazo koma ananena kuti mpaka zitamwa mokwanira. Ngamila ikakhala ndi ludzu kwambiri imatha kumwa madzi okwana malita 95. Ngati ngamila zonse 10 zinali ndi ludzu kwambiri, ndiye kuti Rabeka anayenera kutunga madziwo kwa nthawi yaitali. Koma zikuoneka kuti ngamilazi sizinali ndi ludzu kwambiri.a Koma kodi Rabeka ankadziwa zimenezi pamene ankanena kuti atunga madziwo? Ayi. Kungoti iye ankafunitsitsa kuthandiza munthu wachikulireyo ngakhale kuti sankamudziwa. Munthuyo analola zoti Rabeka atungire madzi ngamilazo. Ndiyeno atayamba kutunga madziwo, mlendoyo ankangochita naye chidwi chifukwa ankagwira ntchitoyo modzipereka kwambiri.—Genesis 24:20, 21.
Tingaphunzire zambiri pa zimene Rabeka anachitazi. Masiku ano anthu ambiri ndi odzikonda. Ndipotu Baibulo linaneneratu kuti anthu adzakhala “odzikonda,” kapena kuti osafuna kuthandiza ena. (2 Timoteyo 3:1-5) Koma Rabeka sanali wodzikonda chifukwa anathandiza munthu yemwe sankamudziwa n’komwe. Choncho kuti Akhristu azipewa mtima wodzikonda ayenera kuganizira kwambiri zimene Rabeka anachitazi.
N’zosakayikitsa kuti Rabeka anaona kuti mlendoyo akumuyang’ana mwachidwi. Komatu sikuti munthuyu anali ndi zolinga zolakwika. Iye anachita zimenezi posonyeza kusangalala komanso kudabwa ndi zimene mtsikanayo ankachita. Ndiyeno Rabeka atamaliza kutunga madzi, mlendoyo anamupatsa mphatso zamtengo wapatali. Kenako anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe mwana wa ndani? Chonde ndiuze. Kodi kunyumba kwa bambo ako kuli malo oti tikhoza kugonako?” Atamuuza dzina la bambo ake, munthuyo anasangalala kwambiri. Rabeka nayenso anasonyeza kuti ankafunitsitsa kulandira mlendoyo kunyumba kwawo moti anamuuzanso kuti: “Chakudya cha ziweto tili nacho chambiri, komanso malo ogona alipo.” Pamenepatu anamuganizira mlendoyo chifukwa analinso ndi anthu ena pa ulendowu. Kenako, Rabeka anathamanga kuti akauze mayi ake zimene zachitikazo.—Genesis 24:22-28, 32.
N’zoonekeratu kuti makolo a Rabeka anamuphunzitsa kulandira bwino alendo. Limeneli ndi khalidwe linanso lomwe ndi losowa kwambiri masiku ano. Koma kuti tizilandira bwino alendo, tiyenera kutsanzira mtima wabwino umene Rabeka anali nawo. Kuti zimenezi zitheke, tizikhulupirira kwambiri Mulungu. Iye amafuna kuti anthu amene amamulambira azikhala opatsa, chifukwa nayenso ndi wopatsa. Yehova amasangalala kwambiri tikamapatsa ena zinthu, ngakhale anthu omwe sangatibwezere chilichonse.—Mateyu 5:44-46; 1 Petulo 4:9.
“UKAM’TENGERE MWANA WANGA MKAZI”
Kodi mlendo amene anakumana ndi Rabeka anali ndani? Anali mtumiki wa Abulahamu ndipo n’kutheka kuti anali Eliezere.b Abulahamu anali mchimwene wa agogo a Rabeka ndipo n’chifukwa chake Betuele, yemwe anali bambo ake a Rabeka, anamulandira bwino mtumiki wa Abulahamuyu. Banja la Betuele litakonzera alendowa chakudya, mtumiki wa Abulahamu uja anakana kudya. Ananena kuti adya pokhapokha akanena zimene wabwerera. (Genesis 24:31-33) Tangoganizirani mmene mtumikiyu anasangalalira kufotokoza cholinga cha ulendo wake. Iye anasangalala chifukwa choti anaona umboni woti Yehova Mulungu wake wamudalitsa kwambiri pa ulendo wofunikawu.
N’kutheka kuti bambo ake a Rabeka komanso mchimwene wake Labani, ankamvetsera mwatcheru Eliezere akuwafotokozera nkhaniyi. Iye anawafotokozera kuti Yehova anadalitsa kwambiri mbuye wake Abulahamu. Anawafotokozeranso kuti Sara, mkazi wa mbuye wake anabereka mwana dzina lake Isaki, yemwe adzalandire cholowa cha bambo ake. Kenako anawauza kuti Abulahamu wamutuma kuti adzafunire Isaki mkazi pakati pa abale ake a ku Harana.—Genesis 24:34-38.
Eliezere asananyamuke ku Negebu, Abulahamu anamulumbiritsa kuti asatengere mwana wake mkazi kuchokera m’dziko la Kanani. Abulahamu anachita zimenezi chifukwa chakuti Akanani sankalemekeza komanso kulambira Yehova Mulungu. Iye ankadziwa kuti m’tsogolo, Yehova adzawononga Akananiwo chifukwa cha makhalidwe awo oipa. Komanso sankafuna kuti mwana wake Isaki agwirizane ndi anthu oipawa n’kumachita nawo makhalidwe onyansa. Ankadziwanso kuti mwana wake anali munthu wofunika kwambiri pothandiza kuti zimene Mulungu analonjeza zikwaniritsidwe.—Genesis 15:16; 17:19; 24:2-4.
Eliezere anapitiriza kufotokozera anthuwo kuti atafika pachitsime chomwe chili kufupi ndi ku Harana, anapemphera kwa Yehova Mulungu. Iye anapempha Yehova kuti am’thandize kusankha mkazi wabwino woti akwatirane ndi Isaki. Kodi Yehova akanamuthandiza bwanji? Eliezere anapempha Mulungu kuti mkaziyo abwere kuchitsimeko ndipo akam’pempha madzi akumwa, atungirenso madzi ngamila zake. (Genesis 24:12-14) Rabeka ndi amene anabweradi kuchitsimeko n’kuchita zonse zimene Eliezere anapemphazi. Ndiye tangoganizani mmene Rabeka anamvera pamene Eliezere ankafotokoza nkhaniyi. N’kutheka kuti ankamva ali chapatali.
Betuele ndi Labani anachita chidwi ndi zimene Eliezere anawafotokozera. Ndipo anamuuza kuti: “Zimenezi zachokera kwa Yehova.” Malinga ndi mwambo wa pa nthawiyo, Betuele ndi Labani anavomereza nthawi yomweyo kuti Rabeka akhale mkazi wa Isaki. (Genesis 24:50-54) Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Rabeka anangomusankhira zochita?
Milungu ingapo izi zisanachitike, Eliezere anafunsa Abulahamu kuti: “Bwanji ngati mkaziyo sakabwera nane?” Abulahamu anamuyankha kuti: “Udzamasuka ku lumbiroli.” (Genesis 24:39, 41) Makolo a Rabeka anaona kuti ndi bwino kuti amve kaye maganizo a mwana wawoyo. Komano Eliezere anasangalala kwambiri ataona kuti makolo a Rabeka agwirizana ndi zimene anawafotokozerazo, moti anapempha kuti tsiku lotsatira atenge Rabeka kupita naye ku Kanani. Ngakhale zinali choncho, makolo a Rabeka ankafuna kuti mwana wawoyo asananyamuke, akhale nayebe kwa masiku 10. Koma pofuna kutsimikizira, anauza Eliezere kuti: “Tiyeni timuitane mtsikanayo kuti timve zimene iyeyo anene.”—Genesis 24:57.
Sizinali zophweka kuti Rabeka asankhe zochita pa nkhaniyi. Kodi akanayankha zotani? Kodi akanachonderera bambo ake komanso mchimwene wake kuti asamulole kupita kudziko la Kanani popeza kunali kuchilendo? Kapena akanavomera poganizira kuti unali mwayi wake kuti atsatire malangizo ochokera kwa Yehova? Ngakhale kuti sankayembekezera zimenezi, Rabeka anasonyeza kuti anali wokonzeka kusintha zinthu pa moyo wake. Choncho ananena kuti: “Inde ndipita.”—Genesis 24:58.
Kunena zoona, Rabeka anali mtsikana wachitsanzo chabwino pa nkhani yodzipereka pochita zimene Mulungu amafuna. N’zoona kuti masiku ano m’madera ambiri makolo sasankhira ana awo munthu woti akwatirane naye. Koma tingaphunzire zambiri kwa Rabeka. Iye sankangofuna kuchita zinthu zomwe zingamusangalatse, koma zomwe zingasangalatse Mulungu wake Yehova. Masiku anonso, Baibulo limatipatsa malangizo abwino omwe angatithandize kusankha bwino munthu woti tikwatirane naye. Limatithandizanso kudziwa zimene tingachite kuti tikhale mwamuna kapena mkazi wabwino. (2 Akorinto 6:14, 15; Aefeso 5:28-33) Nafenso tingachite bwino kwambiri kutsanzira Rabeka poyesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna.
“KODI MUNTHU AKUBWERA APOYO NDANI?”
Anthu onse a m’banja la Betuele anatsanzikana ndi Rabeka komanso anamudalitsa. Kenako Rabeka, atsikana antchito komanso Debora, yemwe anali mlezi wake, ananyamuka limodzi ndi Eliezere ndiponso anyamata ake. (Genesis 24:59-61; 35:8) Ulendo wopita ku Kanani unali wa makilomita 800 kapena kupitirira ndipo mwina anayenda kwa milungu itatu. Ngakhale kuti Rabeka ankazidziwa bwino ngamila, sizinali zophweka kuti ayende ulendo wautaliwu pa ngamila, chifukwa anali asanazolowere. Baibulo silinena kuti banja la Betuele linali ndi ngamila, koma limasonyeza kuti banjali linkaweta nkhosa. (Genesis 29:10) Ndipotu nthawi zambiri anthu omwe angoyamba kumene kuyenda pa ngamila amadandaula ngakhale atangoyenda mtunda wochepa.
Zikuoneka kuti Rabeka ankafunitsitsa Eliezere atamuuza zambiri zokhudza Isaki ndi banja lake. Tayerekezani kuti ndi madzulo ndipo anthuwa akupumira ulendowu kwinaku akuwotha moto. Ndiyeno Eliezere akufotokozera Rabeka zimene Yehova analonjeza Abulahamu kuti adzadalitsa mitundu yonse ya anthu kudzera m’banja la Abulahamu. Rabeka ayenera kuti anasangalala kwambiri atadziwa kuti Yehova adzakwaniritsa lonjezoli kudzera mwa Isaki, yemwe ankayembekezera kuti akhala mwamuna wake.—Genesis 22:15-18.
Kenako, monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhaniyi, Rabeka komanso anthu ena aja anayandikira kwawo kwa Isaki. Ndiyeno atatsala pang’ono kufika, Rabeka anaona mnyamata wina akuyenda m’munda. Mnyamatayo ankaoneka kuti akuganizira zinazake. Baibulo limanena kuti Rabeka ataona mnyamatayo, “mwamsanga anatsika pangamila.” Zikuoneka kuti sanachite kudikira kuti ngamilayo igwade kaye. Kenako anafunsa Eliezere kuti: “Kodi munthu akubwera apoyo kuchokera m’tchire kudzakumana nafe ndani?” Ndiye atamuuza kuti ndi Isaki, Rabeka anatenga nsalu n’kudziphimba kumutu. (Genesis 24:62-65) Kodi anachitiranji zimenezi? Anachita zimenezi posonyeza ulemu kwa Isaki, yemwe ankayembekezera kuti akhala mwamuna wake. Anthu ena masiku ano angaone kuti ulemu umene Rabeka anasonyezawu ndi wachikale. Komabe zimene anachitazi zikusonyeza kuti Rabeka anali munthu wodzichepetsa kwambiri. Ndiye nafenso, kaya ndife mwamuna kapena mkazi, tiyenera kuyesetsa kutengera khalidwe labwino limeneli.
Pa nthawiyi Isaki anali ndi zaka 40. Komanso n’kuti patadutsa zaka pafupifupi zitatu kuchokera pamene Sara, yemwe anali mayi ake anamwalira ndipo Isaki anali adakali ndi chisoni. Zimenezi zikusonyeza kuti Isaki anali wachikondi ndipo ankawakonda kwambiri mayi ake. Rabeka analidi mkazi woyenera kwa Isaki chifukwa anali wolimbikira ntchito, wodziwa kulandira alendo ndiponso wodzichepetsa. Ndiyeno kodi Isaki atamuona Rabeka anatani? Baibulo limati, “Anam’konda kwambiri.”—Genesis 24:67; 26:8.
Ngakhale kuti padutsa zaka 3,900 chichitikireni zimenezi, nafenso tingaphunzire zambiri kwa Rabeka. Monga taonera, Rabeka anali ndi makhalidwe abwino kwambiri monga kulimbikira ntchito, kulandira bwino alendo ndi kudzichepetsa. Choncho, aliyense kaya ndi wamkulu, mwana, amene ali pabanja kapena ayi, tiyenera kuyesetsa kutsanzira chikhulupiriro cha Rabeka.
a Zimenezi zinachitika chakumadzulo. Ndipo nkhaniyi sisonyeza kuti Rabeka anakhalitsa kwambiri kuchitsimeko kapenanso kuti anakafika kwawo anthu atagona. Sisonyezanso kuti winawake anamulondola kuchitsimeko ataona kuti akuchedwa kubwera.
b Ngakhale kuti mtumikiyu sanatchulidwe dzina m’nkhaniyi, n’kuthekadi kuti anali Eliezere. Pa nthawi imene Abulahamu analibe mwana, ankafuna kuti cholowa chake chidzaperekedwe kwa Eliezere chifukwa anali mtumiki wake wamkulu komanso wokhulupirika.—Genesis 15:2; 24:2-4.